-
Mmene Yehova Amatithandizira Kuti Tizipirira MosangalalaNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2022 | November
-
-
YEHOVA AMATITSOGOLERA
8. Mu nthawi ya Ayuda, kodi lemba la Yesaya 30:20, 21 linakwaniritsidwa bwanji?
8 Werengani Yesaya 30:20, 21. Pamene asilikali a Babulo anazungulira mzinda wa Yerusalemu kwa chaka ndi hafu, mavuto omwe anthu ankakumana nawo anangofika pozolowereka ngati chakudya ndi madzi. Koma mogwirizana ndi vesi 20 ndi 21, Yehova anawalonjeza Ayudawo kuti ngati atalapa komanso kusintha zochita zawo, iye adzawapulumutsa. Potchula Yehova monga ‘Mlangizi Wamkulu,’ Yesaya analonjeza anthuwo kuti Yehova adzawaphunzitsa mmene angamamulambirire movomerezeka. Mawu amenewa anakwaniritsidwa pamene Ayuda anamasulidwa ku ukapolo. Yehova anasonyeza kuti analidi Mlangizi wawo Wamkulu, ndipo malangizo omwe ankawapatsa anathandiza kuti akwanitse kubwezeretsa kulambira koona. Ifenso masiku ano tili ndi mwayi kuti Yehova ndi Mlangizi wathu Wamkulu.
-
-
Mmene Yehova Amatithandizira Kuti Tizipirira MosangalalaNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2022 | November
-
-
10. Kodi timamva bwanji “mawu kumbuyo [kwathu]”?
10 Yesaya anatchula njira yachiwiri yomwe Yehova amatiphunzitsira ponena kuti: “Makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwako.” Apa mneneriyu anafotokoza Yehova monga mlangizi watcheru yemwe akuyenda kumbuyo kwa ophunzira ake n’kumawalozera njira patsogolo pawo komanso kuwapatsa malangizo. Masiku ano timamva mawu a Mulungu kuchokera kumbuyo kwathu. Motani? Mawu a Mulungu analembedwa m’Baibulo kalekale ife tisanabadwe, choncho tikamawawerenga zimakhala ngati tikumva mawu a Mulungu kumbuyo kwathu.—Yes. 51:4.
11. Kuti tizipirira mosangalala, kodi tiyenera kuchita chiyani, nanga n’chifukwa chiyani?
11 Kodi tingatani kuti tizipindula ndi malangizo omwe Yehova amatipatsa kudzera m’gulu lake ndi m’Mawu ake? Onani kuti Yesaya anatchula zinthu ziwiri. Choyamba iye anati, “njira ndi iyi.” Chachiwiri anati, “yendani mmenemu.” (Yes. 30:21) Si zokwanira kungodziwa “njira.” Timafunikanso ‘kuyendamo.’ Kudzera m’Mawu a Yehova, monga mmene gulu lake limawafotokozera, timadziwa zomwe Mulungu amafuna kuti tizichita. Timaphunziranso mmene tingagwiritsire ntchito zomwe timaphunzirazo. Kuti tizipirira mosangalala potumikira Yehova, timafunika kuchita zinthu ziwiri zonsezi. Tikamachita zimenezo m’pamene tingakhale otsimikiza kuti Yehova adzatidalitsa.
-