CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YESAYA 29-33
“Mfumu Idzalamulira Mwachilungamo”
Yesu, yemwe ndi Mfumu, amapereka “akalonga” kapena kuti akulu amene amasamalira nkhosa
Mofanana ndi “malo ousapo mvula yamkuntho,” iwo amayesetsa kuteteza nkhosa ngati zikuzunzidwa komanso amazilimbikitsa zikafooka
Mofanana ndi “mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi,” iwo amatsitsimula nkhosa zimene zili ndi ludzu poziphunzitsa mfundo zolondola za choonadi
Mofanana ndi “mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma,” iwo amatonthoza nkhosa pozipatsa malangizo olimbikitsa a m’Baibulo