Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jr mutu 4 tsamba 43-53
  • Samalani, Mtima Ndi Wonyenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Samalani, Mtima Ndi Wonyenga
  • Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MTIMA WOMWE NDI WONYENGA UNGATHE KUTISOCHERETSA
  • MMENE YEHOVA AMATIUMBIRA
  • LOLANI KUTI YEHOVA AKUUMBENI
  • Kodi Tsiku Lililonse Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • “Sindingathe Kukhala Chete”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • “Tsopano Uwauze” Mawu Awa
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Kodi Mumasankha Anthu Otani Kuti Akhale Anzanu?
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
Onani Zambiri
Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
jr mutu 4 tsamba 43-53

Mutu 4

Samalani, Mtima Ndi Wonyenga

1, 2. N’chifukwa chiyani n’zovuta kudziwa mmene mtima wathu wophiphiritsa ulilidi?

TAYEREKEZERANI kuti tsiku lina m’bandakucha musanadzuke, mukumva kupweteka kwambiri m’chifuwa ndiponso mukubanika. Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndi matenda a mtima?’ Kunyalanyaza vutolo sikungakuthandizeni, koma mungafunike kuchitapo kanthu mwamsanga. Mwina mungafunike kuuza anthu ena kuti apite nanu kuchipatala kuti mukalandire thandizo. Adokotala angakuyezeni bwinobwino, mwina mpaka angagwiritse ntchito makina ounikira mmene mtima ukugwirira ntchito. Ngati adokotalawo atadziwa vuto lanu n’kukuthandizani mwamsanga, angapulumutse moyo wanu.

2 Nanga bwanji za mtima wathu wophiphiritsa? N’zovuta kudziwa mmene mtima wathu wophiphiritsa ulili. Chifukwa chiyani? Timawerenga m’Baibulo kuti: “Mtima ndi wonyenga kwambiri kuposa china chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa. Ndani angaudziwe?” (Yer. 17:9) Choncho, mtima wathu ungatinyenge n’kutichititsa kuganiza kuti tilibe vuto lililonse mwauzimu, ngakhale kuti anthu ena angaone zizindikiro za vuto linalake n’kumatidera nkhawa. Koma n’chifukwa chiyani mtima wathu ungatinyenge? N’chifukwa chakuti ndife anthu ochimwa ndipo mtima wathu ungamatilimbikitse kuchita zinthu zolakwika. Komanso Satana pamodzi ndi dzikoli angatilepheretse kuona mmene mtima wathuwo ulilidi. Choncho chitsanzo cha Yeremiya ndiponso cha anthu a ku Yuda a m’nthawi yake, chitithandiza kuona kufunika kofufuza mitima yathu.

3. Kodi ndi zinthu ziti zimene zasanduka milungu kwa anthu ambiri?

3 Zimene Ayuda ambiri ankachita zinasonyeza kuti mitima yawo inali ndi vuto lauzimu. Iwo anasiya kulambira Mulungu woona yekha n’kuyamba kulambira milungu ya Akanani, ndipo chikumbumtima chawo sichinkawavutitsa. Ndiyeno Yehova anafunsa anthuwo kuti: ‘Kodi milungu yanu imene mwadzipangira ili kuti? Imeneyo ibwere kwa inu ngati ingathe kukupulumutsani pa nthawi ya tsoka. Pakuti milungu yanu yachuluka mofanana ndi mizinda yanu.’ (Yer. 2:28) Ifeyo masiku ano, timakhulupirira kuti sitikulambira milungu yonyenga. Komabe, buku lina lotanthauzira mawu limati mawu akuti “mulungu” amatanthauza “munthu kapena chinthu chofunika kwambiri.” Anthu ambiri m’dzikoli amaona kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo wawo ndi ntchito yawo, thanzi lawo, banja lawo, ngakhalenso ziweto zawo. Ena amaona kuti chinthu chofunika kwambiri pa moyo wawo ndi masewera olimbitsa thupi, anthu otchuka, zipangizo zamakono, kuyenda maulendo osiyanasiyana, kapena miyambo yawo. Ndipo anthu ambiri amatanganidwa ndi zinthu zimenezi n’kunyalanyaza ubwenzi wawo ndi Mlengi. Kodi zimenezi zingakhudzenso Akhristu oona ngati mmene zinalili ndi Ayuda a m’nthawi ya Yeremiya?

MTIMA WOMWE NDI WONYENGA UNGATHE KUTISOCHERETSA

4. Kodi Ayuda ena ankanena moona mtima pamene ankati, ‘N’chifukwa chiyani mawu a Yehova sanakwaniritsidwebe, tsopanotu akwaniritsidwe’?

4 Mwina mungachite chidwi ndi mmene zinthu zinalili pamene Yeremiya ananena kuti mtima ungathe kuchita china chilichonse choipa. Iye anadziwa kuti anthu ankanena kuti: “N’chifukwa chiyani mawu a Yehova sanakwaniritsidwebe? Tsopanotu akwaniritsidwe.” (Yer. 17:15) Koma kodi anthuwo ankanena zimenezi moona mtima? M’chaputala chimenechi cha Yeremiya, mawu ake oyambirira akunena kuti: “Tchimo la Yuda lalembedwa ndi chitsulo chogobera. Lalembedwa ndi cholembera cha dayamondi m’mitima yawo.” Vuto lalikulu la Ayudawo linali lakuti ‘ankakhulupirira mwa munthu aliyense wochokera kufumbi, ankadalira mphamvu za dzanja la munthu, komanso mitima yawo inapatuka kuchoka kwa Yehova.’ Iwo ankachita zinthu mosiyana kwambiri ndi anthu ochepa omwe ankakhulupirira Mulungu komanso kumudalira kuti awatsogolere ndi kuwapatsa madalitso.—Yer. 17:1, 5, 7.

5. Kodi Ayuda a m’nthawi ya Yeremiya anachita chiyani Yehova atawapatsa malangizo?

5 Zimene Ayuda ambiri anachita atamva mawu amene Mulungu anawauza zinasonyeza kuti mitima yawo inali ndi vuto. (Werengani Yeremiya 17:21, 22.) Mwachitsanzo, iwo sankayenera kugwira ntchito zawo zatsiku ndi tsiku pa tsiku la Sabata, koma ankafunika kupuma n’kumachita zinthu zauzimu. Ayuda a m’nthawi ya Yeremiyawo sankayenera kuchita malonda kapena kugwira ntchito zina pa tsiku la Sabata. Koma zimene anachita atamva zimene Mulungu anawauza zinasonyeza mmene mtima wawo unalili. Baibulo limatiuza kuti: “Iwo sanamvere kapena kutchera khutu moti anapitiriza kuumitsa khosi lawo kuti asamve ndi kulandira mwambo.” Ngakhale kuti ankadziwa malamulo a Mulungu, iwo anasankha kuchita zinthu zosemphana ndi malamulowo, moti ankagwira ntchito pa tsiku la Sabata.—Yer. 17:23; Yes. 58:13.

6, 7. (a) Kodi Mkhristu angaganize bwanji mopanda nzeru masiku ano ngakhale kuti gulu la kapolo wokhulupirika likutipatsa malangizo? (b) Kodi maganizo amenewo angakhudze bwanji cholinga chathu chopezeka pamisonkhano nthawi zonse?

6 Masiku ano, sititsatira lamulo losunga Sabata. Komabe, tingapeze phunziro lotichenjeza tikaona zimene Ayudawo anachita ndi lamulo limeneli, zomwe zinasonyeza mmene mitima yawo inalili. (Akol. 2:16) Pofuna kuchita chifuniro cha Mulungu, ifeyo tasiya kuchita zofuna za mtima wathu kapena zinthu zosafunikira kwenikweni. Ndipo tikudziwa kuti kungakhale kupusa kwambiri ngati munthu atasankha kutumikira Mulungu mmene munthuyo akufunira, mosemphana ndi zimene Mulungu akufuna. Komanso mwina tikudziwa anthu ambiri amene anadzipereka ndi mtima wonse kuchita chifuniro cha Mulungu, ndipo chifukwa cha zimenezi, moyo wawo ndi wosangalala kwambiri. Komabe, kodi nthawi zina tingasocheretsedwe bwanji?

7 Mkhristu angayambe kuganiza molakwika kuti mtima wake sungamunyenge ngati mmene zinachitikira ndi anthu ambiri a m’nthawi ya Yeremiya. Mwachitsanzo, bambo angaganize kuti, ‘Ndiyenera kuyesetsa kuti asandichotse ntchito n’cholinga choti ndizitha kusamalira banja langa,’ ndipo zimenezi n’zomveka. Nanga bwanji ngati maganizo amenewa angamuchititse kuganiza kuti, ‘Ndikufunika kuwonjezera maphunziro kuti ndipeze ntchito yabwino kapena kuti asandichotse ntchito’? Zimenezinso zingaoneke ngati zomveka, ndipo zingamuchititse kuganiza kuti, ‘Masiku anotu zinthu zasintha, ndipo kuti zinthu zikuyendere bwino, ukufunikira maphunziro a kukoleji kapena kuyunivesite. Ukatero sangakuchotse ntchito.’ Zimenezi zikungosonyezeratu kuti n’zosavuta kuti munthu ayambe kunyalanyaza malangizo anzeru ndi abwino ochokera ku gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, pa nkhani yowonjezera maphunziro, ndipo munthuyo angasiye kufika pamisonkhano. Pa nkhani yowonjezera maphunziroyi, Akhristu ena aumbidwa ndi dzikoli pang’ono ndi pang’ono ndipo ayamba kuganiza ndi kuona zinthu mofanana ndi anthu a m’dzikoli. (Aef. 2:2, 3) Koma Baibulo limatichenjeza mosapita m’mbali kuti: “Musalole kuti dzikoli likukanikizireni m’chikombole chake.”—Aroma 12:2, Phillips.a

Zithunzi patsamba 46

Kodi mtima wanu wakunyengani ndipo simukupezeka pamisonkhano?

8. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingachititse Akhristu ena kuyamba kunyada? (b) N’chifukwa chiyani kungodziwa mfundo zokhudza Mulungu ndiponso zochita zake sikokwanira?

8 N’zodziwikiratu kuti Akhristu ena m’nthawi ya atumwi anali ndi chuma, mwinanso anali otchuka ndithu m’dzikoli. N’chimodzimodzinso ndi Akhristu ena masiku ano. Kodi iwo ayenera kuona bwanji zinthu zimene ali nazo, ndipo enafe tiyenera kuwaona bwanji Akhristu otero? Yehova anapereka yankho kudzera mwa Yeremiya. (Werengani Yeremiya 9:23, 24.) M’malo modzitamandira ndi zinthu zimene ali nazo, munthu wanzeru amakumbukira mfundo yakuti chinthu chofunika kwambiri n’kudziwa Wolamulira wa Chilengedwe Chonse. (1 Akor. 1:31) Komabe, kodi kumvetsa bwino njira za Yehova komanso kumudziwa bwino kumatanthauza chiyani? Tikudziwa kuti anthu a m’nthawi ya Yeremiya ankadziwa dzina la Mulungu. Iwo ankadziwanso zimene Yehova anachita populumutsa makolo awo pa Nyanja Yofiira, polowa m’Dziko Lolonjezedwa, m’nthawi ya Oweruza, ndiponso m’nthawi ya ulamuliro wa mafumu okhulupirika. Ngakhale zinali choncho, iwo sankamudziwa bwino Yehova komanso sankamukhulupirira kwenikweni. Komabe iwo ankanena kuti: “Ine ndilibe mlandu uliwonse. Ndithudi mkwiyo [wa Mulungu] wandichokera.”—Yer. 2:35.

N’chifukwa chiyani kudziwa mfundo yakuti mtima wathu ndi wonyenga n’kofunika kwambiri? Kodi mtima wathu tingaufufuze bwanji kuti tidziwe mmene Mulungu, amene amafufuza mtima wa munthu aliyense, akutionera?

MMENE YEHOVA AMATIUMBIRA

Chithunzi patsamba 48

Kodi mukulola kuti Yehova akuumbeni?

9. Kodi tingatsimikize bwanji kuti mtima wathu ungathe kusintha, ndipo chofunika n’chiyani kuti usinthe?

9 Ayuda amene Yeremiya anawauza uthenga wochokera kwa Mulungu ankafunika kusintha mitima yawo. Zimenezo zinali zotheka chifukwa Mulungu ananena za anthu amene adzabwerere kwawo kuchokera ku ukapolo, kuti: “Ndidzawapatsa mtima wodziwa kuti ine ndine Yehova. Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo pakuti adzabwerera kwa ine.” (Yer. 24:7) Masiku anonso n’zotheka kuti anthu asinthe mitima yawo. Ndipotu ambiri mwa ife tingathe kusintha kuti mtima wathu ukhale wabwino mwauzimu. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kuchita zinthu zitatu zofunika kwambiri. Tiziphunzira Mawu a Mulungu mwakhama, tiziganizira mozama zimene Mulungu akutichitira pa moyo wathu, ndiponso tizigwiritsa ntchito mfundo zimene tikuphunzira zokhudza iyeyo. Mosiyana ndi anthu a m’nthawi ya Yeremiya, tizilolera kuti mitima yathu iziunikidwa ndi Mulungu, amene amafufuza mtima wa munthu aliyense. Ndipo ifeyo tingafufuze tokha mtima wathu pogwiritsa ntchito Baibulo komanso poona mmene Yehova watithandizira. (Sal. 17:3) Choncho, tingasonyeze kuti ndife anzeru tikamadzifufuza mwanjira imeneyi.

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani Yeremiya anapita kukaona woumba mbiya? (b) N’chiyani chimachititsa Yehova kuumba anthu mwanjira inayake?

10 Satana amafuna kuumba anthu pokanikizira anthu onse m’chikombole chimodzi. Koma Mulungu akamaumba anthu amaganizira mmene munthu aliyense payekha alili. Chitsanzo pa nkhani imeneyi ndi zimene Yeremiya anaona. Tsiku lina, Mulungu anamuuza kuti apite kunyumba ya woumba mbiya. Kumeneko anapeza woumba mbiyayo akugwira ntchito yake. Ndiyeno chiwiya chimene ankaumbacho chitawonongeka, iye anapanga chiwiya china ndi dongo lomwelo, limene linali lidakali lofewa. (Werengani Yeremiya 18:1-4.) N’chifukwa chiyani Yeremiya anauzidwa kuti akaonerere zimenezi, ndipo ifeyo tikuphunzirapo chiyani pamenepa?

11 Yehova anafuna kusonyeza Yeremiya ndi Aisiraeli kuti Iye ali ndi mphamvu zoumba anthu mmene Iye akufunira. Koma kodi Mulungu amachita bwanji ndi dongo limene akuumba? Mosiyana ndi anthu oumba mbiya, Yehova salakwitsa, kapena kuwononga mwachisawawa ziwiya zimene waumba ndi manja ake. Zimene iye amasankha kuchita ndi anthu zimadalira zimene anthuwo akuchita pamene akuwaumba.—Werengani Yeremiya 18:6-10.

12. (a) Kodi Yehoyakimu anachita chiyani Yehova atayesetsa kumuumba? (b) Kodi mukuphunzira chiyani pa nkhani ya Yehoyakimu?

12 Nanga kodi Yehova amaumba bwanji munthu aliyense payekha? Njira yaikulu imene akugwiritsa ntchito masiku ano, ndi Baibulo. Munthu akamawerenga Mawu a Mulungu ndi kuchita zimene akuwerengazo, amasonyeza kuti iye ndi munthu wotani, ndipo Mulungu angamuumbe. Tsopano tiyeni tione chitsanzo cha Mfumu Yehoyakimu kuti tione mmene anthu a m’nthawi ya Yeremiya ayenera kuti ankaumbidwira pa nkhani za moyo watsiku ndi tsiku. Chilamulo chinanena kuti: “Usachitire chinyengo waganyu.” Mfumuyi sinamvere zimenezi koma inkadyera masuku pamutu Aisiraeli anzake powagwiritsa ntchito yomanga “nyumba yaikulu” osawapatsa malipiro. (Deut. 24:14; Yer. 22:13, 14, 17) Ndiyeno Mulungu anayesetsa kuti aumbe Yehoyakimu pogwiritsa ntchito mawu Ake, omwe ankawatumiza kudzera mwa aneneri. Komabe mfumuyo inatsatira maganizo a mumtima wake wonyenga ndipo inati, “Sindidzamvera.” Choncho iye anapitiriza kuchita zinthu zoipa, zomwe anayamba kuzichita kale kwambiri ali mnyamata. Motero Mulungu anati: “[Yehoyakimu] adzaikidwa m’manda ngati mmene amaikira bulu wamphongo. Adzamukoka . . . ndi kukamutaya kunja.” (Yer. 22:19, 21) Ndiyetu munthu angasonyeze kupusa kwambiri ngati atamanena kuti: ‘Ndi mmene ndilili, sindingasinthe.’ Masiku ano, Mulungu sakutumiza aneneri ngati Yeremiya, koma amatipatsa malangizo. Gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru limatithandiza kuti tizimvetsa mfundo za m’Baibulo ndi kuzigwiritsa ntchito. Mfundo zimenezi zingakhudze mbali zosiyanasiyana za moyo wa tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, zingakhudze mmene timavalira ndi kudzikongoletsera, kapena nyimbo ndi mavinidwe a paukwati kapena paphwando lina. Kodi tidzalolera kuti Mawu a Mulungu atiumbe?

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani anthu omwe anali ndi akapolo ku Yerusalemu anavomereza kumasula akapolo awo achiheberi? (b) Kodi n’chiyani chinasonyeza mmene mtima wa anthu omwe anali ndi akapolowo unalilidi?

13 Taonani chitsanzo china. Ababulo anaika Zedekiya pa mpando wachifumu ku Yuda, kuti azilamulira pansi pa ulamuliro wawo. Koma kenako Zedekiya anawagalukira, ngakhale kuti Mulungu, kudzera mwa Yeremiya anamulangiza kuti asachite zimenezo. (Yer. 27:8, 12) Ababulo ataona zimene iye anachitazo, anabwera n’kuzungulira mzinda wa Yerusalemu. Mfumuyi ndi akalonga ake anaganiza kuti achitepo kanthu posonyeza kumvera Chilamulo n’cholinga choti Mulungu awachitire chifundo. Popeza Zedekiya ankadziwa kuti akapolo achiheberi ankayenera kumasulidwa m’chaka cha 7 cha ukapolo wawo, iye anachita pangano ndi anthu onse a mu Yerusalemu kuti amasule akapolo awo. (Eks. 21:2; Yer. 34:14) Apa zikuonekeratu kuti Zedekiya ndi anthu ake anasintha mwadzidzidzi n’kuyamba kutsatira Chilamulo cha Mulungu pongofuna kuti Mulunguyo awateteze kwa adani awo omwe anali atazungulira mzinda wa Yerusalemu.—Werengani Yeremiya 34:8-10.

14 Kenako, gulu lankhondo la ku Iguputo linabwera kudzathandiza anthu a ku Yerusalemu, ndipo Ababulo atamva zimenezi, anachoka. (Yer. 37:5) Ndiyeno kodi anthu amene anali atamasula akapolo awo aja anachita chiyani tsopano? Anagwiranso anthuwo n’kuwakakamiza kuti akhalenso akapolo awo. (Yer. 34:11) Apa mfundo ndi yakuti, Ayuda ataona kuti ali m’mavuto, anayamba kuchita zinthu zooneka ngati akutsatira malamulo a Mulungu. Mwina iwo ankaganiza kuti kuchita zimenezo kukanachititsa kuti akhululukidwe machimo omwe ankachita poyamba. Koma mavutowo atatha, iwo anayambiranso kuyenda m’njira zawo zoipa. Ngakhale kuti ankanamizira kutsatira mfundo za m’Chilamulo, zimene anachita pambuyo pake zinasonyezeratu zimene zinali mumtima mwawo kuti sankafuna kutsatira malangizo a m’Mawu a Mulungu ndiponso kuumbidwa ndi mawuwo.

Kodi mungaphunzirepo chiyani pa zimene Yeremiya analemba zokhudza woumba mbiya? Kodi Yehova amatiumba bwanji masiku ano?

LOLANI KUTI YEHOVA AKUUMBENI

15. Kodi mungakonde kuti Yehova akuumbeni mpaka kufika pati? Fotokozani.

15 Mothandizidwa ndi mpingo wapadziko lonse wa Yehova, tingathe kudziwa mfundo za m’Baibulo zimene zimakhudzana ndi nkhani inayake mwachindunji. Mwachitsanzo, tingadziwe zoyenera kuchita ngati zikuoneka kuti m’bale wina amatichitira zinthu zosatisangalatsa. (Aef. 4:32) Mwina tikhoza kuvomereza ndithu kuti malangizo a m’Baibulo pa nkhaniyi ndi oona ndiponso anzeru. Komabe, kodi ifeyo tidzakhala dongo lotani? Kodi tidzaloleradi kuumbidwa ndi Yehova? Ngati mtima wathu uli wabwino, tidzasintha mosavuta ndipo Yehova, yemwe ndi Woumba Mbiya Wamkulu, adzatiumba kuti tikhale chiwiya choyenerera chomwe iye angachigwiritse ntchito. (Werengani Aroma 9:20, 21; 2 Timoteyo 2:20, 21.) M’malo mosonyeza mtima wangati wa Yehoyakimu kapena wa anthu omwe anali ndi akapolo m’masiku a Zedekiya, ifeyo tilolere kuti Yehova atiumbe n’kukhala chiwiya chogwiritsidwa ntchito yolemekezeka.

16. Kodi Yeremiya ankadziwa mfundo iti ya choonadi yofunika kwambiri?

16 Nayenso Yeremiya anaumbidwa ndi Mulungu. Koma kodi mneneriyu anasonyeza mtima wotani? Tingadziwe mtima umene anasonyeza tikaona zimene iye ananena. Mneneriyu anavomereza kuti: “Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.” Kenako anapempha kuti: “Ndikonzeni, inu Yehova.” (Yer. 10:23, 24) Achinyamata, kodi mudzatsanzira Yeremiya? N’zachidziwikire kuti pali zinthu zambiri zimene muyenera kusankha pa moyo wanu. Achinyamata ena amafuna ‘kuwongolera okha mapazi awo.’ Koma kodi inuyo mudzadalira Mulungu kuti akutsogolereni posankha zochita pa moyo wanu? Mofanana ndi Yeremiya, kodi inuyo mudzavomereza modzichepetsa kuti zochita za anthu zasonyeza kuti iwo alibe ulamuliro wowongolera mapazi awo? Muzikumbukira mfundo yakuti: Mukamafunafuna malangizo a Mulungu, iye adzakutsogolerani.

17-19. (a) N’chifukwa chiyani Yeremiya anayenda ulendo wautali wopita kumtsinje wa Firate? (b) Kodi Yeremiya ayenera kuti anayesedwa bwanji pa nkhani ya kumvera? (c) Kodi zimene Yeremiya anachita ndi lamba uja zinathandiza bwanji?

17 Yeremiya ankafunika kumvera malangizo a Mulungu pa utumiki wake. Kodi inuyo mukanakhala Yeremiya, mukanamvera malangizo alionse amene mukanapatsidwa? Nthawi inayake, Yehova anauza Yeremiya kuti atenge lamba wansalu n’kumumanga m’chiuno mwake. Kenako Mulungu anauza mneneriyu kuti apite kumtsinje wa Firate. Kuti mumvetse kutalika kwa ulendo umene Yeremiya anafunika kuyenda, mungayang’ane pamapu, ndipo muona kuti iye ankafunika kuyenda ulendo wautali makilomita pafupifupi 500. Atafika kumtsinjeko, Yeremiya ankafunika kubisa lambayo mumng’alu wa m’phanga kenako n’kubwerera ku Yerusalemu. Ndiyeno patapita nthawi, Mulungu anamuuza kuti apitenso kumtsinjeko n’kukatenga lamba uja. (Werengani Yeremiya 13:1-9.) Maulendo onse amene Yeremiya anafunikira kuyendawa, anali mtunda wautali makilomita pafupifupi 2,000. Anthu ena otsutsa nkhani za m’Baibulo sakhulupirira kuti Yeremiya anayendadi mtunda wautali choncho, womwe ukanamutengera miyezi ingapo.b (Ezara 7:9) Komabe, zimenezi n’zomwe Mulungu ananena ndipo Yeremiya anazichitadi.

18 Yerekezerani kuti mukuona mneneriyu akuyenda kudutsa m’mapiri a ku Yudeya. Ndiyeno malinga ndi njira imene anadutsa, mwina anafika m’chipululu chomwe chili pafupi ndi mtsinje wa Firate. Cholinga cha ulendo wonsewu n’kukabisa lamba wansalu basi. Ndipo anthu akwawo ayenera kuti ankafunsana za iye ataona kuti papita nthawi yaitali mneneriyu asakuoneka. Koma mneneriyu atabwerera, anthuwo anaona kuti iye alibe lamba wansalu uja. Kenako Mulungu anamuuza kuti ayendenso ulendo wautali kwambiriwo kuti akatenge lamba uja, yemwe pa nthawiyo anali atawola “moti sakanagwiranso ntchito iliyonse.” Tangoganizirani zimenezi. Zikanakhala zosavuta kuti iye ayambe kuganiza kuti: ‘Apa tsopano zanyanya. Sindikuona chifukwa chilichonse chochitira zimenezi.’ Koma iye sanaganize zimenezo chifukwa anali ataumbidwa ndi Mulungu. M’malo monyinyirika, iye anachita zonse zimene Mulungu anamuuza.

Chithunzi patsamba 53

N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera malangizo a Yehova, ngakhale pamene sitikuwamvetsa bwino?

19 Pambuyo pa ulendo wachiwiriwu m’pamene Mulungu anamufotokozera bwinobwino chifukwa chake anachita zimenezi. Yehova anauza Yeremiya kuti achite zimenezi ndi lamba wansaluyo kuti athandize anthuwo kumvetsetsa uthenga wamphamvu umene mneneriyo analengeza wakuti: “Anthu oipa amenewa akukana kumvera mawu anga. Iwo akupitirizabe kuumitsa mitima yawo ndipo akutsatira milungu ina kuti aitumikire ndi kuigwadira. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba ameneyu amene sangagwirenso ntchito iliyonse.” (Yer. 13:10) Imeneyi inali njira yogwira mtima kwambiri yomwe Yehova anagwiritsa ntchito pophunzitsa anthu ake. Zimene Yeremiya anachita pomvera Yehova kuchokera pansi pa mtima, ngakhale pa nkhani imene inkaoneka ngati yaing’ono, zinathandiza kwambiri pamene Mulungu ankayesetsa kuphunzitsa anthu mowafika pamtima.—Yer. 13:11.

20. N’chifukwa chiyani anthu ena angadabwe ndi zimene mukuchita pomvera Mulungu, koma kodi mungatsimikizire za chiyani?

20 Masiku ano, Mulungu sauza Akhristu kuti ayende mtunda wautali makilomita ambirimbiri ngati njira yophunzitsira. Koma mwina moyo wanu wachikhristu ungachititse anzanu kapena anthu amene mwayandikana nawo nyumba kuyamba kudabwa, ngakhalenso kukunyozani kumene. Mwina anthuwo angachite zimenezi chifukwa cha mmene mumavalira ndi kudzikongoletsera, maphunziro akusukulu amene munasankha, ntchito imene munasankha kugwira, ngakhalenso mmene mumaonera zakumwa zoledzeretsa. Kodi mudzatsimikiza ndi mtima wonse kumvera malangizo a Mulungu ngati mmene anachitira Yeremiya? Zimene mumasankha kuchita chifukwa choti munalolera mtima wanu kuumbidwa ndi Mulungu, zingachititse kuti anthu ena amvetsere uthenga wabwino. Mulimonse mmene zingakhalire, kumvera malangizo a Yehova opezeka m’Mawu ake ndiponso kutsatira malangizo operekedwa ndi gulu la kapolo wokhulupirika, kudzakuthandizani kuti zinthu zikuyendereni bwino mpaka kalekale. Mukhoza kukhala ngati Yeremiya, n’kupewa kutsogoleredwa ndi mtima wonyenga. Choncho, tsimikizani ndi mtima wonse kuti mudzalolera kuumbidwa ndi Mulungu, ndipo lolani kuti iye akuumbeni kukhala chiwiya cholemekezeka chimene iye adzachigwiritsa ntchito mpaka kalekale.

N’chifukwa chiyani m’pofunika kwambiri kulimbana ndi maganizo olakwika ochokera mumtima wathu wopanda ungwirowu, mayesero ochokera kwa Satana ndiponso ochokera m’dzikoli?

a Baibulo lina lachingelezi limene linasindikizidwa mu 2005 (NET Bible) palemba limeneli limati: “Musafanane ndi dzikoli.” Pofotokoza mmene munthu angafananire ndi dzikoli, mawu a m’munsi a pavesi limeneli, amati: “Pali zinthu ziwiri zimene zimachititsa munthu kuti afanane ndi dzikoli. Choyamba, dziko limachititsa munthuyo kuti afanane nalo iye asakudziwa, ndipo pa nthawi yomweyo, munthuyo amachita kufuna yekha kuti afanane nalo. Choncho zikuoneka kuti nthawi zambiri kuti munthu afike pofananadi ndi dzikoli, zinthu ziwiri zonsezi zimachitika nthawi imodzi.”

b Anthu ena amaganiza kuti Yeremiya anauzidwa kupita pafupi osati kumtsinje wa Firate. N’chifukwa chiyani amaganiza choncho? Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti: “Chifukwa chachikulu chimene anthu amatsutsira zimenezi n’choti amaganiza kuti Mulungu sakanapempha mneneriyu kuti ayende maulendo awiri ataliatali omwe atchulidwawa, kuchokera ku Yerusalemu kupita kumtsinje wa Firate.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena