Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jr mutu 13 tsamba 154-167
  • “Yehova Wachita Zimene Anali Kuganiza”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Yehova Wachita Zimene Anali Kuganiza”
  • Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • N’CHIFUKWA CHIYANI YEREMIYA ANKAKHULUPIRIRA MAULOSI A YEHOVA?
  • MAULOSI AMENE YEREMIYA ANANENA N’KUWAONA AKUKWANIRITSIDWA
  • MAULOSI AMENE ANAKWANIRITSIDWA YEREMIYA ATAMWALIRA
  • MAULOSI AMENE AKUKUKHUDZANI
  • “Sindingathe Kukhala Chete”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Kodi Mumasankha Anthu Otani Kuti Akhale Anzanu?
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • Kodi Tsiku Lililonse Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
  • “Ndaika Mawu Anga M’kamwa Mwako”
    Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
Onani Zambiri
Zimene Mulungu Akutiuza Kudzera mwa Yeremiya
jr mutu 13 tsamba 154-167

Mutu 13

“Yehova Wachita Zimene Anali Kuganiza”

1. Kodi mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa, Yeremiya ananena chiyani chokhudza maulosi a Yehova?

ABABULO anali atawononga mzinda wa Yerusalemu n’kuutentha ndi moto, ndipo Yeremiya ankati akayang’ana kumzindawo, ankangoona utsi wokhawokha, womwe unali koboo, m’mwamba. Iye ayenera kuti ankakumbukira mmene anthu a mumzindawo ankalirira momvetsa chisoni pamene ankaphedwa ndi adani awo. Mulungu anali atamuuza kale kuti zimenezo zidzachitika, ndipo zinachitikadi ndendende. Ataona zimenezi, mneneriyu ananena mwachisoni kuti: “Yehova wachita zimene anali kuganiza.” Mzinda wa Yerusalemu unawonongedwa momvetsa chisoni kwambiri.—Werengani Maliro 2:17.

2. Kodi Yeremiya anaona kukwaniritsidwa kwa ulosi uti wakalekale?

2 Zoonadi, Yeremiya anaona kukwaniritsidwa kwa maulosi ambiri amene Mulungu anapereka kwa anthu ake, kuphatikizapo maulosi ena akale. Zaka zambiri m’mbuyomu, Mose anauza Aisiraeli zimene zidzawachitikire akasankha kumvera Mulungu kapena kusamumvera. Iye anawauza kuti akamumvera adzalandira “dalitso” ndipo akapanda kumumvera adzalandira “temberero.” Yehova ankafunira anthu ake zabwino ndipo ankafuna kuti iwo alandire madalitso. Koma iwo akanapanda kumumvera akanalandira matemberero oopsa kwambiri. Mose anachenjeza Aisiraeliwo kuti aliyense amene adzanyalanyaze kapena kutsutsa malamulo a Yehova, zinthu sizidzamuyendera bwino moti mpaka ‘adzadya mnofu wa ana ake aamuna ndi ana ake aakazi.’ Ndipo nayenso Yeremiya anabwereza chenjezo limeneli. (Deut. 30:19, 20; Yer. 19:9; Lev. 26:29) Mwina ena angadzifunse kuti, ‘Kodi zinthu zoopsa choncho zinachitikadi?’ Inde, zinachitika. Ababulo atazungulira mzinda wa Yerusalemu, chakudya chinatheratu mumzindawo ndipo anthu anayamba kudya ana awo. Yeremiya ananena kuti: “Ngakhale amayi, amene amakhala achifundo, afika pophika ana awo ndi manja awo. Anawo akhala ngati chakudya chotonthoza anthu pa nthawi ya kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.” (Maliro 4:10) Izitu zinali zoopsa kwambiri.

3. N’chifukwa chiyani Mulungu ankatumiza aneneri kwa anthu ake?

3 Koma sikuti Yehova ankatumiza aneneri, monga Yeremiya, kuti azikangolengeza zoti anthu osamvera adzawonongedwa. Mulungu ankafuna kuti anthu akewo ayambirenso kumutumikira mokhulupirika. Iye ankafuna kuti anthu ochimwa alape, ndipo Ezara ananena mfundo imeneyi pamene anati: “Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwatumizira machenjezo kudzera mwa amithenga ake. Anawatumiza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo ndiponso malo ake okhala.”—2 Mbiri 36:15; werengani Yeremiya 26:3, 12, 13.

Chithunzi patsamba 154

4. Kodi Yeremiya ankamva bwanji mumtima akaganizira uthenga umene ankalengeza?

4 Mofanana ndi Yehova, Yeremiya nayenso ankamvera chisoni anthu a mtundu wake. Mungaone zimenezi m’mawu amene Yeremiyayo ananena mzinda wa Yerusalemu utangotsala pang’ono kuwonongedwa. Iye ankavutika kwambiri mumtima akaganizira kuti anthu ambiri mumzindawo anali atatsala pang’ono kuwonongedwa. Anthuwo akanatha kupewa tsoka limeneli akanamvera uthenga wa Yeremiya. Taganizirani mmene Yeremiya ankamvera mumtima pamene ankalengeza uthenga wochokera kwa Mulungu. Iye analira kuti: “M’mimba mwanga ine, m’mimba mwanga! Ndikumva kupweteka kwambiri mumtima mwanga. Mtima wanga ukuvutika. Sindingathe kukhala chete pakuti ndamva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, chizindikiro chochenjeza cha nkhondo.” (Yer. 4:19) Yeremiya sakanatha kungokhala chete osachenjeza anthu za tsoka limenelo, lomwe linali litayandikira kwambiri.

N’CHIFUKWA CHIYANI YEREMIYA ANKAKHULUPIRIRA MAULOSI A YEHOVA?

5. N’chifukwa chiyani Yeremiya sankakayikira maulosi amene ankalengeza?

5 N’chifukwa chiyani Yeremiya sankakayikira kuti zimene ankaloserazo zidzachitikadi? (Yer. 1:17; 7:30; 9:22) Iye anali ndi chikhulupiriro komanso ankaphunzira Malemba, ndipo zimenezi zinamutsimikizira kuti Yehova ndi Mulungu yemwe amanena maulosi oona. Mbiri ya anthu inkatsimikizira kuti Yehova amatha kulosera zinthu zomwe zingaoneke ngati zosatheka kwa anthu, monga za kumasulidwa kwa Aisiraeli kuchoka ku ukapolo ku Iguputo. Yeremiya ankadziwa bwino nkhani ya kumasulidwa kwa Aisiraeli yomwe inalembedwa m’buku la Ekisodo, komanso mawu amene Yoswa, yemwe anaona zimenezi ndi maso ake, ananena. Yoswa anakumbutsa Aisiraeli anzake kuti: “Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.”—Yos. 23:14.

6, 7. (a) N’chifukwa chiyani muyenera kuchita chidwi ndi maulosi amene Yeremiya ankalengeza? (b) Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuti musamakayikire uthenga umene mumalengeza?

6 Ndiye kodi n’chifukwa chiyani inuyo muyenera kupitiriza kuganizira mozama maulosi amene Yeremiya ankalengeza? Chifukwa choyamba n’chakuti Yeremiya sankakayikira zoti Yehova adzakwaniritsa mawu akewo. Chachiwiri n’chakuti zinthu zina zimene Mulungu analosera kudzera mwa Yeremiya zikukwaniritsidwa panopa, ndipo muonanso zina zikukwaniritsidwa m’tsogolo muno. Chifukwa chachitatu n’chakuti Yeremiya anali mtumiki wa Mulungu wapadera kwambiri. Izi zili choncho chifukwa iye analengeza mauthenga ochuluka kwambiri ochokera kwa Mulungu, komanso anali wakhama ndiponso wodzipereka kwambiri polengeza mauthengawo. Ndipo katswiri wina wa Baibulo ananena kuti: “Tikayerekezera Yeremiya ndi aneneri ena, iye amaoneka kuti anali wotchuka kwambiri.” Zoonadi, Yeremiya anali mneneri wodziwika kwambiri pakati pa anthu a Mulungu moti anthu ena atamva Yesu akulankhula, ankaganiza kuti anali Yeremiya.—Mat. 16:13, 14.

7 Mofanana ndi Yeremiya, inuyo mukukhala m’nthawi imene maulosi ofunika kwambiri a m’Baibulo akukwaniritsidwa, ndipo mukufunika kukhulupirira kuti Mulungu adzakwaniritsadi malonjezo ake onse. (2 Pet. 3:9-14) Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kuchita zimenezi? Muyenera kupitiriza kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni kuti muzikhulupirirabe kuti Mawu a Mulungu aulosi ndi odalirika kwambiri. Ngati njira imodzi yokuthandizani kuchita zimenezi, m’mutu uno tikambirana maulosi angapo amene Yeremiya analosera n’kuwaona akukwaniritsidwa. Komanso tikambirana maulosi ena amene anakwaniritsidwa iye atamwalira. Ndipo pali maulosi ena amene akukukhudzani panopa komanso akukhudza tsogolo lanu. Choncho zimene tikambirane m’mutu uno zikuthandizani kukhulupirira kwambiri Mawu aulosi a Yehova ndiponso kuti iye ‘adzachita zimene akuganiza.’—Maliro 2:17.

N’chifukwa chiyani Mulungu anatumiza aneneri? Nanga n’chifukwa chiyani inuyo mukukhulupirira maulosi oti oipa awonongedwa posachedwa?

MAULOSI AMENE YEREMIYA ANANENA N’KUWAONA AKUKWANIRITSIDWA

8, 9. Kodi mfundo imodzi imene imachititsa kuti Baibulo likhale buku lapadera ndi iti?

8 Masiku ano, pali anthu ambiri amene amayesera kulosera za m’tsogolo. Ena mwa anthu amenewa ndi akatswiri azachuma, andale, azanyengo ndi anthu ochita zamatsenga. Mwina mwaonapo kuti anthu amenewa amavutika kulosera molondola ngakhale zinthu zing’onozing’ono zimene zingachitike m’masiku kapena milungu yochepa. Komatu mfundo imodzi imene imachititsa kuti Baibulo likhale lapadera kwambiri, ndi yoti maulosi ake ndi olondola. (Yes. 41:26; 42:9) Maulosi onse a Yeremiya, kaya onena za zinthu zimene zinali zitatsala pang’ono kuchitika kapena zam’tsogolo kwambiri, ndi olondola. Ambiri mwa maulosiwo ankakhudza anthu osiyanasiyana komanso mayiko. Choyamba, tiyeni tikambirane maulosi angapo a Yeremiya amene anakwaniritsidwa iye adakali ndi moyo.

9 Kodi ndani masiku ano amene angalosere mmene zinthu zidzakhalire m’dzikoli pakapita chaka chimodzi kapena ziwiri? Mwachitsanzo, kodi ndi katswiri uti woona zochitika m’mayiko osiyanasiyana amene anganene molondola ngati padzakhale kusintha kwa olamulira? Mouziridwa ndi Mulungu, Yeremiya analosera kuti ufumu wa Babulo udzagonjetsanso madera ena ambiri n’kuyamba kuwalamulira. Iye ananena kuti ufumu wa Babulo unali ngati “kapu yagolide” imene Yehova adzagwiritse ntchito potsanulira mkwiyo wake padziko la Yuda komanso pamizinda ndi anthu oyandikana ndi dzikoli, kuti anthuwo akhale akapolo a Ababulowo. (Yer. 51:7) Ndipo Yeremiya ndi anthu ena a m’nthawi yake anaona zimenezi zikuchitikadi.—Yerekezerani ndi Yeremiya 25:15-29; 27:3-6; 46:13.

10. Kodi Yehova analosera chiyani chokhudza mafumu anayi a Yuda?

10 Yehova anagwiritsanso ntchito Yeremiya kuti alosere zimene zidzachitikire mafumu anayi a Yuda. Ponena za Yehoahazi, kapena kuti Salumu, mwana wa Mfumu Yosiya, Mulungu analosera kuti adzatengedwa kupita ku ukapolo ndipo sadzabwereranso ku Yuda. (Yer. 22:11, 12) Zimenezi zinachitikadi. (2 Maf. 23:31-34) Mulungu ananenanso kuti Yehoyakimu, amene anadzalowa m’malo Yehoahazi, “adzaikidwa m’manda ngati mmene amaikira bulu wamphongo.” (Yer. 22:18, 19; 36:30) Baibulo silinena mmene Yehoyakimu anafera kapena zimene zinachitika ndi mtembo wake, koma limasonyeza kuti mwana wake Yehoyakini analowa m’malomwake pa nthawi imene Ababulo anazungulira mzinda wa Yerusalemu. Yeremiya analoseranso kuti Yehoyakini (amene amadziwikanso kuti Koniya kapena Yekoniya) adzatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo ndipo adzafera komweko. (Yer. 22:24-27; 24:1) Ndipo zimenezi zinachitikadi. Nanga bwanji za Zedekiya, mfumu yomaliza ya Yuda? Yeremiya analosera kuti Zedekiya adzaperekedwa m’manja mwa adani ndipo adaniwo sadzamuchitira chifundo. (Yer. 21:1-10) Kodi n’chiyani chimene chinam’chitikira? Adaniwo anamugwiradi ndipo anapha ana ake aamuna iye akuona, anamuvulaza maso n’kumuchititsa khungu, kenako anamutenga n’kupita naye ku Babulo ndipo anafera komweko. (Yer. 52:8-11) Zoonadi, maulosi onsewa anakwaniritsidwa.

11. Kodi Hananiya anali ndani, ndipo Yehova ananeneratu kuti n’chiyani chidzamuchitikire?

11 Muchaputala 28 cha Yeremiya timawerenga kuti mu ulamuliro wa Zedekiya, Hananiya yemwe anali mneneri wonyenga, anatsutsa mawu amene Yehova ananena kudzera mwa Yeremiya akuti Ababulo adzapitiriza kulamulira mzinda wa Yerusalemu. Hananiya ananyalanyaza mawu a Mulungu n’kumalengeza kuti goli la ukapolo limene Nebukadinezara anaika pa Yuda ndi mitundu ina lidzathyoledwa. Koma motsogoleredwa ndi Yehova, Yeremiya anaulula bodza la Hananiya, ndipo anabwereza kunena kuti mitundu yambiri idzatumikira Ababulo. Kenako anauza mneneri wonyengayo kuti amwalira chaka chisanathe, ndipo zimenezi zinachitikadi.—Werengani Yeremiya 28:10-17.

12. Kodi anthu ambiri m’nthawi ya Yeremiya ankaganiza chiyani akamva mfundo yaikulu ya uthenga waulosi wa mneneriyu?

12 Komabe mfundo yaikulu ya uthenga waulosi umene Mulungu anapatsa Yeremiya inali yokhudza kuwonongedwa kwa mzinda wa Yerusalemu. Mobwerezabwereza, Yeremiya ankachenjeza kuti ngati Ayudawo salapa machimo awo, monga kupembedza mafano, kuchita zinthu mopanda chilungamo komanso kuchita chiwawa, mzinda wawo wa Yerusalemu udzawonongedwa. (Yer. 4:1; 16:18; 19:3-5, 15) Koma anthu ambiri a m’nthawi ya Yeremiya ankaganiza kuti Yehova sangachite zimenezo. Iwo ankaganiza kuti Mulungu sangalole kuti mzinda wa Yerusalemu uwonongedwe, chifukwa kunali kachisi wake wopatulika. Komatu Yehova sanama ndipo anachita zimene zinali m’maganizo mwake.—Yer. 52:12-14.

Chithunzi patsamba 160

Makolo: Gwiritsani ntchito zitsanzo za Arekabu, Ebedi-meleki, ndi Baruki kuti muthandize ana anu kukhala ndi chikhulupiriro cholimba

13. (a) Kodi zochitika masiku ano zikufanana bwanji ndi zimene zinkachitika m’nthawi ya Yeremiya? (b) N’chifukwa chiyani muyenera kuchita chidwi ndi zimene Mulungu analonjeza anthu osiyanasiyana m’nthawi ya Yeremiya?

13 Zimene zikuchitikira atumiki a Mulungu masiku ano zikufanana ndi zimene zinkachitikira atumiki a Yehova okhulupirika m’nthawi ya Yeremiya. Tikudziwa kuti posachedwapa Yehova awononga anthu onse amene safuna kumvera machenjezo ake. Komabe, tingalimbikitsidwe ndi malonjezo ake aulosi, ngati mmene analimbikitsidwira Ayuda m’nthawi ya Yeremiya, amene ankalambira Mulungu mokhulupirika. Komanso Arekabu ankatsatira mokhulupirika malangizo a Yehova ndiponso a kholo lawo, ndipo Mulungu anawalonjeza kuti adzapulumuka mzinda wa Yerusalemu ukamawonongedwa. Iwo anapulumukadi, ndipo umboni wa zimenezi ndi wakuti patapita nthawi, Baibulo linanena za “Malikiya mwana wamwamuna wa Rekabu,” amene anathandiza nawo pa ntchito yomanganso mpanda wa Yerusalemu pa nthawi imene Nehemiya anali bwanamkubwa. (Neh. 3:14; Yer. 35:18, 19) Yehova anatsimikizira Ebedi-meleki kuti nayenso adzapulumuka chifukwa chakuti ankakhulupirira Mulungu ndiponso anathandiza Yeremiya. (Yer. 38:11-13; 39:15-18) Komanso, Mulungu analonjeza kuti Baruki, amene anali mnzake wa Yeremiya, adzalandira ‘moyo wake monga chofunkha.’ (Yer. 45:1, 5) Ndiye kodi ndi mfundo iti imene mukuipeza pamene mwaona kuti maulosi onsewa anakwaniritsidwa? Kodi mukuganiza kuti Yehova adzakuchitirani chiyani mukakhalabe wokhulupirika?—Werengani 2 Petulo 2:9.

Kodi Ebedi-meleki, Baruki komanso Arekabu anapindula bwanji atadziwa mfundo yakuti Mulungu amakwaniritsa maulosi ake nthawi zonse? Nanga inuyo mumamva bwanji mukaganizira maulosi amenewo?

MAULOSI AMENE ANAKWANIRITSIDWA YEREMIYA ATAMWALIRA

14. N’chifukwa chiyani ulosi wa Mulungu wokhudza Babulo unali wochititsa chidwi?

14 Mulungu analosera kuti kuwonjezera pa kugonjetsa dziko la Yuda, Nebukadinezara adzagonjetsanso dziko la Iguputo. (Yer. 25:17-19) Mwina zimenezi zinkaoneka kuti n’zosatheka chifukwa chakuti dziko la Iguputo pa nthawiyo linali lamphamvu kwambiri, moti linkalamuliranso dziko la Yuda. (2 Maf. 23:29-35) Mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa, Ayuda amene anatsala mumzindawo anakonza zoti achokemo n’kupita ku Iguputo n’cholinga choti azikakhala motetezeka kumeneko. Iwo ankafuna kuchita zimenezi ngakhale kuti Yehova anali atawachenjeza komanso anali atawauza kuti akapitiriza kukhala m’dziko la Yuda, iye adzawadalitsa. Ndipo Mulungu anawachenjezanso kuti ngati iwo angathawire ku Iguputo, ndiye kuti lupanga limene ankaliopalo lidzawapeza komweko. (Yer. 42:10-16; 44:30) Sitikudziwa ngati Yeremiya anaona Ababulo akugonjetsa dziko la Iguputo, chifukwa iye sananene zimenezi m’mabuku ake. Koma zimene tikudziwa n’zoti zomwe Yehova analosera zinachitikiradi Aisiraeli amene anathawira ku Iguputo, pamene Ababulo ankagonjetsa dzikoli kumayambiriro kwa zaka za m’ma 500 B.C.E.—Yer. 43:8-13.

15, 16. Kodi mawu a Mulungu oti anthu ake adzamasulidwa ku ukapolo anakwaniritsidwa bwanji?

15 Yeremiya analoseranso kuti ufumu wa Babulo, umene unadzagonjetsa dziko la Iguputo, nawonso udzatha. Kutatsala zaka 100 kuti zimenezi zichitike, Yeremiya analosera molondola kuti ufumu wa Babulo udzatha mwadzidzidzi. Kodi iye anati chiyani? Mneneri wa Mulunguyu analosera kuti madzi amene ankateteza mzinda wa Babulo “adzauma,” ndipo asilikali ake amphamvu sadzamenya nkhondo. (Yer. 50:38; 51:30) Maulosi amenewa anakwaniritsidwa ndendende pamene Amedi ndi Aperisi anaphwetsa mtsinje wa Firate n’kuwoloka mosavuta, kenako analowa mumzindawo n’kugonjetsa Ababulo modzidzimutsa. Mukaganizira zimenezi, simungakayikire zoti ulosi wakuti mzindawo udzakhala bwinja ndipo anthu sadzakhalamonso, unakwaniritsidwa. (Yer. 50:39; 51:26) Mpaka pano, pamalo pamene panali mzinda wamphamvu wa Babulo pali bwinja lokhalokha, ndipo zimenezi zikutsimikizira kuti zomwe Mulungu walosera zimachitikadi.

16 Kudzera mwa Yeremiya, Yehova ananeneratu kuti Ayuda adzatumikira Ababulo kwa zaka 70, ndipo kenako iye adzapulumutsa anthu akewo n’kuwabwezeretsa kudziko lawo. (Werengani Yeremiya 25:8-11; 29:10.) Danieli ankakhulupirira ulosi umenewu ndi mtima wonse, ndipo anaugwiritsa ntchito kuti adziwe kutalika kwa nthawi imene mzinda wa Yerusalemu udzakhale uli ‘wowonongedwa.’ (Dan. 9:2) Nayenso Ezara ananena kuti: “Yehova analimbikitsa mtima wa Koresi mfumu ya Perisiya” kuti agonjetse Ababulo n’kulamula Ayuda kuti abwerere kudziko lawo. Yehova anachita zimenezi kuti “mawu [ake] kudzera mwa Yeremiya akwaniritsidwe.” (Ezara 1:1-4) Ayuda ochokera ku ukapolowo ayenera kuti anasangalala kwambiri chifukwa anayamba kukhala mwamtendere m’dziko lawo n’kuyambiranso kulambira Mulungu woona, monga mmene Yeremiya analoserera.—Yer. 30:8-10; 31:3, 11, 12; 32:37.

17. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu a Yeremiya onena za “kulira mofuula” ku Rama ayenera kuti ankanena zimene zinachitika pa nthawi ziwiri zosiyana?

17 Yeremiya analembanso maulosi amene anadzakwaniritsidwa m’tsogolo kwambiri. Iye anati: “Yehova wanena kuti, ‘Mawu amveka ku Rama. Kwamveka kulira mofuula ndiponso momvetsa chisoni. Rakele akulirira ana ake. Iye wakana kutonthozedwa pamene akulirira ana ake, chifukwa ana akewo kulibenso.’” (Yer. 31:15) Zikuoneka kuti mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa mu 607 B.C.E., Ayuda amene anagwidwa ukapolo anasonkhanitsidwa mumzinda wa Rama, umene unali pamtunda wa makilomita pafupifupi 8, kumpoto kwa mzinda wa Yerusalemu. N’kutheka kuti ena mwa akapolowo anaphedwa ku Rama. Zimene zinachitikazi ziyenera kuti zinachititsa kuti ulosiwu ukwaniritsidwe koyamba, ndipo zinali ngati Rakele akulirira “ana” ake amene aphedwa. Koma patapita zaka zoposa 600, Mfumu Herode analamula kuti ana akhanda a ku Betelehemu aphedwe. Mateyu, amene analemba nawo Uthenga Wabwino, ananena kuti Yeremiya analosera kuti anthu adzalira momvetsa chisoni chifukwa cha kuphedwa kwa anawo.—Mat. 2:16-18.

Chithunzi patsamba 163

Kodi Aedomu ali kuti masiku ano?

18. Kodi ulosi wa Mulungu wonena za Edomu unakwaniritsidwa bwanji?

18 Pali ulosi winanso umene unakwaniritsidwa m’nthawi ya atumwi. Kudzera mwa Yeremiya, Mulungu analoseranso kuti dziko la Edomu lidzakhala m’gulu la mayiko amene adzawonongedwe ndi Ababulo. (Yer. 25:15-17, 21; 27:1-7) Koma Mulungu analoseranso zinthu zina zimene zinayenera kudzachitikira Edomu. Iye ananena kuti dziko la Edomu lidzakhala ngati mizinda ya Sodomu ndi Gomora. Zimenezitu zinatanthauza kuti m’dzikoli simudzakhalanso anthu mpaka kalekale. (Yer. 49:7-10, 17, 18) Izi zinachitikadi ndendende. Kodi mukuganiza kuti mayina akuti Edomu kapena Aedomu angapezeke kuti masiku ano? Kodi angapezeke pamapu a mayiko amene alipo masiku ano? Ayi. Mayina amenewa kawirikawiri amapezeka m’mabuku a mbiri yakale ya m’Baibulo kapena pamapu osonyeza mayiko a m’nthawi imeneyo. Flavius Josephus anafotokoza kuti Aedomu anakakamizidwa kulowa chipembedzo chachiyuda m’zaka za m’ma 100 B.C.E. Kenako, Yerusalemu atawonongedwa mu 70 C.E., mtundu umenewu unatheratu.

19. Kodi buku la Yeremiya likusonyeza bwanji kuti Mulungu amakwaniritsadi maulosi?

19 Monga mmene mukuonera, machaputala ambiri m’buku la Yeremiya ali ndi maulosi okhudza anthu osiyanasiyana kapena mitundu ya anthu. Ambiri mwa maulosi amenewa anakwaniritsidwa kale. Mukaganizira mfundo imeneyi, muyenera kuchita chidwi ndi buku la Yeremiya n’kukhala wofunitsitsa kuliphunzira, chifukwa mfundoyi ikukukuuzani chinthu chofunika kwambiri chokhudza Mulungu wanu wamkulu. Chinthu chake n’chakuti Yehova anachita zimene zinali m’maganizo mwake, ndipo adzachitanso zimene zidakali m’maganizo mwake. (Werengani Yesaya 46:9-11.) Mfundoyi ingakuthandizeni kuti muzikhulupirira kwambiri maulosi a m’Baibulo. Ndipotu maulosi ena amene Yeremiya analemba akukhudza inuyo mwachindunji ndiponso tsogolo lanu. Choncho m’ndime zotsala za mutu uno, tikambirana ena mwa maulosi amenewa.

Kodi ndi maulosi ena ati amene anakwaniritsidwa Yeremiya atamwalira, ndipo n’chifukwa chiyani maulosi amenewa ali ofunika kwa inu?

MAULOSI AMENE AKUKUKHUDZANI

20-22. N’chifukwa chiyani tinganene kuti maulosi ena a m’Baibulo, kuphatikizapo a m’buku la Yeremiya, amakwaniritsidwa kangapo? Fotokozani.

20 Nthawi zina ulosi umodzi wa m’Baibulo ungakwaniritsidwe kangapo. Chitsanzo cha zimenezi ndi ulosi womwe ukupezeka mu yankho limene Yesu anauza ophunzira ake atamufunsa za chizindikiro cha ‘kukhalapo kwake ndi cha mapeto a nthawi ino.’ (Mat. 24:3) Ulosiwo unakwaniritsidwa koyamba mu 66 C.E. mpaka mu 70 C.E. Koma n’zoonekeratu kuti mbali zina za ulosiwu zidzakwaniritsidwa pa “chisautso chachikulu” chimene chikubwera padziko lonse loipali. Chisautso chimenechi “sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha dziko mpaka tsopano, ndipo sichidzachitikanso.” (Mat. 24:21) M’mabuku amene Yeremiya analemba muli maulosi enanso amene anayenera kukwaniritsidwa kangapo. Ena mwa maulosiwa anakwaniritsidwa koyamba mu 607 B.C.E. Koma patapita nthawi, maulosiwa anakwaniritsidwanso, monga taonera ndi ulosi wokhudza “Rakele akulirira ana ake.” (Yer. 31:15) Ndipotu ena mwa maulosi amene Yeremiya analemba akukhudza nthawi yathu ino, ndipo kukwaniritsidwa kwake kukukukhudzani inuyo mwachindunji.

21 Mungaone umboni wa zimenezi m’buku la Chivumbulutso. Mouziridwa, mtumwi Yohane anatchula za maulosi akale amene Yeremiya ananena okhudza kutha kwa ufumu wa Babulo mu 539 B.C.E. M’buku la Chivumbulutso, iye ananena ulosi wofanana ndi umenewu, womwe ukuyenera kukwaniritsidwa m’njira yaikulu kwambiri. Chitsanzo chimodzi cha ulosi umene Yeremiya ananena, womwe ukuyenera kukwaniritsidwanso m’nthawi yathu ino, ndi chonena za kugwa kwa “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi zipembedzo zonyenga zonse pamodzi. (Chiv. 14:8; 17:1, 2, 5; Yer. 50:2; 51:8) Anthu a Mulungu akuyenera ‘kutuluka mwa iye’ n’cholinga choti asalandire nawo chilango chake. (Chiv. 18:2, 4; Yer. 51:6) Madzi a mzinda umenewo, omwe akuimira anthu omwe ali mu Babulo Wamkuluyu, kapena kuti anthu amene akumutsatira, ‘adzauma.’—Yer. 51:36; Chiv. 16:12.

22 Ulosi wina umene ukwaniritsidwe m’tsogolo muno ndi wokhudza zimene Mulungu walonjeza, zoti adzawononga chipembedzo chonyenga chifukwa chimazunza anthu ake. Yehova ‘adzabwezera [Babulo Wamkulu] mogwirizana ndi zonse zimene anachita.’ (Yer. 50:29; 51:9; Chiv. 18:6) Ndipo m’dziko lophiphiritsa la chipembedzo chonyenga simudzakhala chilichonse, koma dziko lonselo lidzakhala bwinja.—Yer. 50:39, 40.

23. Kodi Yeremiya analosera zinthu zotani zokhudza kulambira koona, zomwe zinachitika m’zaka za m’ma 1900?

23 Monga mmene mwaonera, maulosi amene Yeremiya ankanena ankakhalanso ndi mfundo zolimbikitsa. Mwachitsanzo, iye analosera zoti m’nthawi yathu ino, kulambira koona kudzayambiranso padziko lapansili. Kumasulidwa kwa Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo kunachitira chithunzi kumasulidwa kwa anthu a Mulungu m’nthawi yathu ino kuchoka mu Babulo Wamkulu. Zimenezi zinachitika pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba. Mwauzimu, Yehova anathandiza anthu ake kuti ayambirenso kulambira koona, ndipo zimenezi zinawachititsa kuyamikira Mulungu komanso kukhala anthu osangalala. Iye wadalitsa ntchito imene iwo akuigwira mwakhama pothandiza ena kuti ayambe kumulambira ndiponso kuti azidyetsedwa mwauzimu ndi chakudya cha mwanaalirenji. (Werengani Yeremiya 30:18, 19.) Komanso inuyo mwaona nokha m’nthawi yathu ino kuti Yehova wakwaniritsa zimene analonjeza anthu ake kuti adzawapatsa abusa, kutanthauza amuna okhwima mwauzimu, amene amasamaliradi nkhosa ndi kuziteteza.—Yer. 3:15; 23:3, 4.

24. Kodi Yeremiya ananena mawu amphamvu ati, omwe atsala pang’ono kukwaniritsidwa?

24 Uthenga umene Yeremiya anauza anthu a Mulungu akale sikuti unali ndi mfundo zolimbikitsa zokha ndi malonjezo abwino opita kwa anthu okhulupirika, koma unalinso ndi chenjezo loti anthu onse osakhulupirika, omwe sankafuna kukonza ubwenzi wawo ndi Yehova, adzawonongedwa. Zilinso chimodzimodzi masiku ano. Tingaone mosavuta kuti zimene Yeremiya anachenjeza momveka bwino zatsala pang’ono kukwaniritsidwa. Iye anati: “Pa tsiku limenelo padzakhala anthu ophedwa ndi Yehova kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kufikanso kumalekezero ena a dziko lapansi. Sadzawalira maliro, kuwasonkhanitsa pamodzi, kapena kuwaika m’manda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.”—Yer. 25:33.

25. Kodi anthu a Mulungu masiku ano ali ndi udindo wotani?

25 Zoonadi, mofanana ndi Yeremiya, ifenso tikukhala m’nthawi yovuta komanso yapadera kwambiri. Monga mmene zinalili m’nthawi yake, masiku anonso zimene munthu angachite akamva uthenga wa Yehova zingamuchititse kudzalandira moyo kapena kudzawonongedwa. N’zoona kuti masiku ano anthu a Mulungu si aneneri. Sitinauziridwe ndi Yehova kuti tiwonjezere mfundo zina pa mawu ake amene akupezeka m’Baibulo, omwe sangalephere kukwaniritsidwa. Komabe, tapatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu masiku onse mpaka kufika pamapeto pa nthawi ino. (Mat. 28:19, 20) Ife sitikufuna ‘kuba mawu a Yehova’ pobisira anthu zinthu zimene zatsala pang’ono kuchitika. (Werengani Yeremiya 23:30.) Ndife otsimikiza ndi mtima wonse kuti tiuze anthu mosabisa, zonse zimene mawu a Mulungu akunena. Ndipotu ambiri mwa maulosi amene Mulungu anauza Yeremiya kuti alengeze, akwaniritsidwa kale. Zimenezi zikutitsimikizira kuti maulosi amene atsalawo adzakwaniritsidwa popanda kukayikira kulikonse. Choncho, tiyenera kuuza anthu kuti Mulungu sadzalephera kuchita ‘zimene akuganiza ndiponso zimene analamula kalekale.’—Maliro 2:17.

Chithunzi patsamba 166

‘Musabe mawu a Yehova’ pobisa zimene zikuyenera kuchitika posachedwapa

26. Kodi pali ulosi wina uti womwe tiukambirane?

26 Sitinganene kuti tamaliza kuphunzira za Yeremiya ndi uthenga wake waulosi ngati sitinaphunzire za malonjezo ofunika kwambiri a Yehova okhudza “pangano latsopano” limene iye anachita ndi anthu ake. Mulungu analemba malamulo okhudza pangano limeneli m’mitima ya anthuwo. (Yer. 31:31-33) Ulosi umenewu ndiponso kukwaniritsidwa kwake, zomwe zikukukhudzani inuyo mwachindunji, tiukambirana m’mutu wotsatirawu.

M’nthawi yathu ino, kodi ndi maulosi ati a m’buku la Yeremiya amene akwaniritsidwa? Nanga mumaona bwanji maulosi amene sanakwaniritsidwebe?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena