Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi pangano la Chilamulo linatha pamene Yesu anafa pa mtengo, ndipo ndi liti pamene linalowedwa m’malo ndi pangano latsopano?
Ambiri afunsa mafunso amenewa, akumakhala m’maganizo ndi zochitika zitatu: Kufa kwa Yesu pa mtengo wozunzirapo pa masana a Nisani 14, 33 C.E., kupereka kwake mtengo wa mwazi wake wa moyo m’mwamba, ndi kutsanulira kwake kwa mzimu woyera pa tsiku la Pentekoste wa 33 C.E. Mwa Malemba, chikuwoneka kuti pangano la Chilamulo linatha ndipo linalowedwa m’malo ndi pangano latsopano pa Pentekoste. Tiyeni tiwone nchifukwa ninji ichi chiri tero.
Yehova ananeneratu kuti, m’kupita kwa nthaŵi, iye akalowa m’malo pangano la Chilamulo ndi “pangano latsopano” lomwe likalola kaamba ka chimo kukhululukidwa kotheratu, chomwe sichinali chotheka pansi pa Chilamulo. (Yeremiya 31:31-34) Ndi liti pamene kulowa m’malo kumeneko kukachitika?
Pangano lakalelo, pangano la Chilamulo, linafunikira choyamba kuchotsedwa kukhala litakwaniritsa chifuno chake. (Agalatiya 3:19, 24, 25) Mtumwi Paulo analemba kuti: “[Mulungu] adatikhululukira ife zolakwa zonse; adatha kutifafanizira cha pa ifecho cholembedwa m’zochitikazo chimene chinali chotsutsana nafe: ndipo Anachichotsera pakatipo ndi kukhomera ichi [pa mtengo wozunzirapo, NW].” (Akolose 2:13, 14) Kodi chimenecho chimatanthauza kuti pa nthaŵi imene Yesu anamwalira, pangano la Chilamulo linalowedwa m’malo ndi pangano latsopano?
Ayi, popeza kuti pangano latsopano linayenera kuyambitsidwa ndi mwazi wa nsembe yoyenerera ndi mtundu watsopano, Israyeli wauzimu. (Ahebri 8:5, 6; 9:15-22) Yesu anaukitsidwa pa Nisani 16, ndipo masiku 40 pambuyo pake iye anakwera kumwamba. (Machitidwe 1:3-9) Masiku khumi pambuyo pa kukwera kwake, kapena pa tsiku la Pentekoste, Yesu anatsanulira pa atumwi ake “mzimu woyera wolonjezedwa” womwe iye analandira kuchokera kwa Atate wake, ndipo Israyeli wauzimu anakhalako. (Machitidwe 2:33) Kupyolera mwa Nkhoswe, Yesu Kristu, Mulungu akupanga pangano latsopano ndi Israyeli wauzimu.
M’chiyang’aniro cha zinthu zambiri zolumikizidwa pamodzi zimenezi, ndi pa nthaŵi iti imene pangano la Chilamulo linalowedwa m’malo ndi pangano latsopano?
Wina sanganene kuti Chilamulocho chinatha ndi imfa ya Yesu. Mkati mwa masiku 40 pambuyo pa kuwukitsidwa kwa Yesu ku moyo wauzimu koma akali pa dziko lapansi, ophunzira ake anali adakali kusungabe Chilamulo. Kuwonjezerapo, mbali yofunika ya Chilamulocho inali kupita kwa mkulu wansembe m’Malo Opatulikitsa kamodzi chaka chirichonse. Chimenecho chinachitira chithunzi kuukitsidwa kwa Yesu kupita kumwamba. Kumeneko, pamaso pa Mulungu, iye, monga Nkhoswe wa pangano latsopano, akapereka mtengo wa nsembe ya dipo lake. (Ahebri 9:23, 24) Ichi chinatsegula njira kaamba ka pangano latsopano kuyambitsidwa m’kukwaniritsa Yeremiya 31:31-34.
Pangano latsopano linayamba kugwira ntchito pamene Yehova anachita kanthu pa kulandira kwake kwa nsembe ya dipo. Iye anatsanulira mzimu wake woyera pa ophunzira okhulupirika a Yesu kubweretsa m’kukhalapo kwa mtundu watsopano, Israyeli wauzimu, wopangidwa ndi awo okhala m’pangano kaamba ka Ufumu. (Luka 22:29; Machitidwe 2:1-4) Ichi chinasonyeza kuti Mulungu anali atathetsa pangano la Chilamulo, kumalikhomera ilo mophiphiritsira pa mtengo umene Yesu anafera. Chotero pangano la Chilamulo linatha pamene kugwira ntchito, kapena kuyambitsidwa, kwa pangano latsopano kunachitika pa kubadwa kwa mtundu watsopano, Israyeli wauzimu, pa Pentekoste wa 33 C.E.—Ahebri 7:12; 8:1, 2.
Kupyola pa yankho loyambirira limenelo ku funsolo, mungadziŵe kuti Mulungu sanatembenukire kotheratu Israyeli wakuthupi pamapeto a pangano la Chilamulo ndi umboni wa kuyambika kwa pangano latsopano pa Pentekoste wa 33 C.E. Mwachitsanzo, m’chigwirizano ndi pangano la Abrahamu, Yehova anasonyeza chiyanjo chapadera kulinga kwa Ayuda, akunja osadulidwa, ndi Asamariya mkati mwa “mlungu” wa 70 womwe unatha mu 36 C.E. (Genesis 12:1-3; 15:18; 22:18; Danieli 9:27; Machitidwe 10:9-28, 44-48) Chinatenga nthaŵi ngakhale kwa Akristu ena Achiyuda odzozedwa kusinthira ku chenicheni chakuti pambuyo pa 33 C.E. sichinali choyenera kusunga Chilamulo; tingawone ichi kuchokera pa funso lobweretsedwa ku bungwe lolamulira mu 49 C.E. (Machitidwe 15:1, 2) Kulekeka kotheratu kwa Chilamulocho kunatsimikiziridwa mosakanika mu 70 C.E., pamene kachisi ndi zolembera za mbiri yakale zogwirizana ndi Chilamulo zinathetsedwa, kuwonongedwa ndi Aroma.—Mateyu 23:38.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.