Mutu 14
Pangano Latsopano Lingakupindulitseni
1. Kodi Yeremiya anakwaniritsa utumiki uti wokhala ndi mbali ziwiri?
UTUMIKI umene Yehova anapatsa Yeremiya unali ndi mbali ziwiri. Mbali yoyamba, iye anafunika ‘kuzula, kugwetsa, kuwononga ndi kupasula.’ Mbali yachiwiri inali yoti ‘amange ndiponso kubzala.’ Mneneriyu anakwaniritsa mbali yoyambayo poulula makhalidwe oipa kwambiri omwe Ayuda onyada ankachita. Iye anakwaniritsanso mbali imeneyi polengeza uthenga wachiweruzo cha Mulungu kwa Ayudawo komanso Ababulo. Komabe, maulosi amene Yeremiya ankalengeza analinso ndi mfundo zothandiza anthu kukhala ndi chiyembekezo. Iye analosera zoti zimene Mulungu wafuna kuti zimangidwe zidzamangidwadi, ndiponso zimene wafuna kuti zibzalidwe zidzabzalidwadi. Mwachitsanzo, Yeremiya ankakwaniritsa mbali yachiwiriyi ya utumiki wake pamene analengeza zoti Ayuda adzabwerera kudziko lakwawo.—Yer. 1:10; 30:17, 18.
2. N’chifukwa chiyani Yehova analanga anthu ake, ndipo anawalanga mpaka kufika pati?
2 Mfundo yomwe Yeremiya analengeza, yoti Ayuda adzabwerera kudziko lakwawo, sinatanthauze zoti Mulungu adzayamba kusasatitsa anthu akewo kapenanso kuti adzayamba kunyalanyaza mfundo zake zachilungamo. Izi zili choncho chifukwa Yeremiya anasonyeza kuti Mulungu adzapereka chilango kwa Ayuda ochimwa. (Werengani Yeremiya 16:17, 18.) M’nthawi ya Yeremiya, ndi anthu ochepa chabe amene ‘ankachita chilungamo’ kapena amene ankayesetsa kukhala ‘okhulupirika,’ moti Yehova anafika poganiza zosiya kuwalezera mtima. Iye anati: “Ndatopa nako kukumvera chisoni.” (Yer. 5:1; 15:6, 7) Ayudawo ‘anabwerera ku zolakwa zimene makolo awo ankachita kalekale, chifukwa makolowo anakana kumvera mawu’ a Yehova. Komanso iwo anakwiyitsa kwambiri Mulungu chifukwa ankalambira mafano, zomwe zinali ngati kuchita chigololo mwauzimu. (Yer. 11:10; 34:18) Choncho, Yehova anali wokonzeka kuthandiza anthu ake kuti asinthe njira zawo, ngakhale kufika powalanga “pamlingo woyenera.” Zimenezo zikanachititsa ena mwa anthuwo kuzindikira kuti analakwa ndipo akanabwerera kwa iye.—Yer. 30:11; 46:28.
3. N’chifukwa chiyani muyenera kuphunzira ulosi wonena za pangano latsopano?
3 Mulungu anagwiritsa ntchito Yeremiya kuti alosere za pangano latsopano. Pangano limeneli lingathandize anthu kupeza madalitso ambiri komanso osatha. Pamene tikukambirana maulosi amene Yeremiya analemba, ndi bwino kuti tikambiranenso za pangano losangalatsali. Pangano latsopanoli linayenera kulowa m’malo mwa pangano limene Mulungu anachita ndi Aisiraeli, atawatulutsa m’dziko la Iguputo, ndipo mkhalapakati wake anali Mose. (Werengani Yeremiya 31:31, 32.) Pamene Yesu Khristu ankayambitsa mwambo wa Mgonero wa Ambuye, anatchulanso za pangano latsopanoli, ndipo zimenezi zikusonyezeratu kuti tiyenera kuchita nalo chidwi. (Luka 22:20) Nayenso mtumwi Paulo anatchula za pangano limeneli m’kalata yake yopita kwa Aheberi. Iye anagwira mawu ulosi wa Yeremiya ndipo anatsindika kufunika kwa pangano latsopanoli. (Aheb. 8:7-9) Koma kodi pangano latsopano n’chiyani kwenikweni? N’chifukwa chiyani linafunikira? Nanga ndani amene akukhudzidwa ndi panganoli ndipo inuyo panokha mungapindule nalo bwanji? Tiyeni tione.
N’CHIFUKWA CHIYANI PANAFUNIKA PANGANO LATSOPANO?
4. Kodi pangano la Chilamulo linakwaniritsa chiyani?
4 Kuti pangano latsopanoli tilimvetse bwino, choyamba tiyenera kumvetsa cholinga cha pangano la Chilamulo, lomwe linali loyamba. Cholinga cha pangano loyambali chinali choti likwaniritse zinthu zingapo zabwino kwambiri zokhudza mtundu umene unkayembekezera Mbewu imene Mulungu analonjeza, yomwe ikanathandiza kuti anthu ambiri adalitsidwe. (Gen. 22:17, 18) Aisiraeli atavomereza pangano la Chilamulo, anakhala “chuma [cha Mulungu] chapadera.” Malinga ndi pangano limeneli, ansembe a mtundu wonsewo ankachokera m’fuko la Levi. Ndipo pamene Yehova ankachita pangano limenelo ndi mtundu wa Isiraeli paphiri la Sinai, anatchula za ‘ufumu wa ansembe ndiponso mtundu woyera,’ koma sanaulule nthawi imene ufumu ndiponso mtundu umenewu udzakhazikitsidwe komanso mmene udzakhazikitsidwire. (Eks. 19:5-8) Kuyambira pa nthawi imene Yehova anachita pangano la Chilamuloli mpaka pamene ufumu wa ansembe ndi mtundu woyera unakhazikitsidwa, panganoli linasonyezeratu kuti Aisiraeli sangakwanitse kutsatira mbali zonse za Chilamulo. Motero, panganoli linachititsa kuti machimo awo aonekere. Choncho mogwirizana ndi Chilamulo, nthawi zonse Aisiraeli ankafunika kupereka nsembe kuti aphimbe machimo awo. Komabe, zinali zoonekeratu kuti pankafunika nsembe ina yoposa nsembe zimenezi. Pankafunika nsembe yangwiro, imene ikanaperekedwa kamodzi kokha basi. Zoonadi, panafunika njira yodalirika imene ikanathandiza anthu kwamuyaya kuti machimo awo azikhululukidwa.—Agal. 3:19-22.
5. N’chifukwa chiyani Yehova analosera za pangano latsopano?
5 Choncho, tikuona chifukwa chake Mulungu anauzira Yeremiya kuti alosere za pangano lina, lomwe ndi pangano latsopano, ngakhale kuti pa nthawiyo pangano la Chilamulo linali likugwirabe ntchito. Popeza Yehova ndi wachikondi komanso wachifundo, iye anafuna kupeza njira yodalirika imene ikanathandiza mitundu yambiri ya anthu, osati mtundu umodzi wokha. Polosera za anthu amene akukhudzidwa ndi pangano latsopanoli, Mulungu ananena kudzera mwa Yeremiya kuti: “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.” (Yer. 31:34) Ngakhale kuti Mulungu analonjeza zimenezi m’nthawi ya Yeremiya, lonjezoli likukhudza anthu a mitundu yonse, omwe adzalandire madalitso abwino kwambiri. Kodi zimenezi zidzachitika bwanji?
6, 7. (a) Kodi anthu ena amamva bwanji akaganizira zoti iwo ndi ochimwa? (b) N’chifukwa chiyani mungalimbikitsidwe mukaphunzira za pangano latsopano?
6 Tidakali anthu opanda ungwiro ndipo zimene timachita nthawi zambiri zimatikumbutsa mfundo imeneyi. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina yemwe ankalimbana ndi tchimo linalake lalikulu. M’baleyu anati: “Ndinkayesetsa ndithu kuti ndisachitenso tchimolo, koma nthawi zina ndinkalephera, ndipo zinkandimvetsa chisoni kwambiri. Zikatero, ndinkaona kuti palibe chomwe ndingachite kuti Mulungu andikhululukire tchimolo, moti ndinkavutika kuti ndipemphere. Nthawi zina ndinkayamba kupemphera ndi mawu akuti, ‘Yehova, sindikudziwa ngati mungamve pempheroli, komabe . . . ’” Anthu ena amene akulephera kulimbana ndi tchimo linalake kapena amene achita tchimo lalikulu amaona ngati “mtambo waukulu” watchinga mapemphero awo kuti asafike kwa Mulungu. (Maliro 3:44) Enanso akhala akuvutika maganizo akakumbukira za tchimo limene anachita zaka zambiri m’mbuyomo. Ngakhalenso Akhristu achitsanzo chabwino nthawi zina amalankhula zinthu zimene kenako amamva nazo chisoni.—Yak. 3:5-10.
7 Aliyense wa ife asaganize kuti sangachite tchimo. (1 Akor. 10:12) Ngakhalenso mtumwi Paulo anavomereza kuti nthawi zina ankachimwa. (Werengani Aroma 7:21-25.) Choncho, kukumbukira za pangano latsopano kungatithandize pa nkhani imeneyi. Mulungu analonjeza zoti adzagwiritsa ntchito pangano latsopano pothandiza anthu m’njira zosiyanasiyana, ndipo njira imodzi yofunika kwambiri, ndi yoti sadzakumbukiranso machimo. Limenelitu ndi dalitso lalikulu zedi. Polosera zimenezi, Yeremiya ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri. Ifenso tingalimbikitsidwe kwambiri tikamapitiriza kuphunzira za pangano latsopanoli, ndiponso kuona mmene lingatithandizire.
N’chifukwa chiyani Mulungu anakhazikitsa pangano latsopano?
KODI PANGANO LATSOPANO N’CHIYANI?
8, 9. Kodi Yehova anafunika kuchita chiyani kuti athe kukhululukira anthu machimo awo?
8 Mukamamudziwa bwino Yehova, mumayambanso kuzindikira kuti iye ndi wokoma mtima kwambiri ndiponso wachifundo kwa anthu opanda ungwiro. (Sal. 103:13, 14) Polosera za pangano latsopano, Yeremiya ananena kuti Yehova ‘adzakhululukira anthu zolakwa zawo’ ndipo sadzakumbukiranso machimo awo. (Yer. 31:34) N’kutheka kuti Yeremiya ankadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu adzafunika kuchita zotani kuti athe kukhululukira anthu mwanjira imeneyi?’ Komabe, iye ayenera kuti anamvetsa kuti popeza Mulungu ankanena za pangano latsopano, ndiye kuti Mulunguyo adzachita mgwirizano winawake ndi anthu. Pogwiritsira ntchito pangano limenelo, Yehova adzakwaniritsa zinthu zimene anauza Yeremiya kuti alosere, ndipo zina mwa izo zinali zokhudza kukhululukira anthu. Koma mfundo zambiri zofotokoza mwatsatanetsatane mmene zinthu zimenezi zidzachitikire, sizinadziwike kufikira pamene Mulungu anaulula zinthu zina zokhudza chifuniro chake, kuphatikizapo zimene Mesiya adzachite.
9 Mwina munaonapo makolo amene amasasatitsa ana awo, osamawalanga. Kodi mukuganiza kuti Yehova angakhale ngati makolo amenewo? Ayi ndithu. Mfundo imeneyi imaonekera bwino tikaona zimene anachita pokhazikitsa pangano latsopano. M’malo mongofafaniza machimo a anthu, Mulungu anachita zonse zotheka kuti atsatire mfundo zake zolungama pokhazikitsa njira yodalirika yokhululukira machimo, ngakhale kuti zimenezi zinali zopweteka kwambiri kwa iye. Mukhoza kumvetsa bwino nkhani imeneyi powerenga zimene Paulo analemba zokhudza pangano latsopano. (Werengani Aheberi 9:15, 22, 28.) Paulo anatchula za “dipo lawo lowamasula,” ndipo anati “popanda kukhetsa magazi anthu sangakhululukidwe machimo awo.” M’pangano latsopano, magazi amene anakhetsedwa sanali magazi a ng’ombe zamphongo kapena mbuzi, zimene zinkaperekedwa nsembe mogwirizana ndi Chilamulo. Koma pangano latsopanoli linayamba kugwira ntchito chifukwa cha magazi a Yesu. Yehova angathe ‘kukhululukira anthu machimo ndiponso zolakwa zawo’ kwamuyaya pogwiritsira nsembe yangwiro imeneyo. (Mac. 2:38; 3:19) Koma kodi ndani amene anadzakhala nawo m’pangano latsopanoli n’kukhululukidwa machimo awo? Tikudziwa kuti sunali mtundu wa Ayuda. Yesu ananena kuti Mulungu adzawakana Ayuda, omwe ankapereka nsembe zanyama potsatira Chilamulo, ndipo adzasankha mtundu wina. (Mat. 21:43; Mac. 3:13-15) Mtundu umenewo unadzakhala “Isiraeli wa Mulungu,” yemwe wapangidwa ndi Akhristu odzozedwa ndi mzimu woyera. Kunena mwachidule, pangano la Chilamulo linali pakati pa Mulungu ndi Aisiraeli enieni, pamene pangano latsopano lili pakati pa Yehova Mulungu ndi Isiraeli wauzimu, ndipo Yesu ndiye Mkhalapakati wake.—Agal. 6:16; Aroma 9:6.
10. (a) Kodi “mphukira” ya Davide ndani? (b) Kodi anthu angapindule bwanji chifukwa cha “mphukira” imeneyi?
10 Yeremiya ananena kuti Mesiya amene anali kubwerayo ndi “mphukira” ya Davide, ndipo m’poyenereradi kuti anamufotokoza mwanjira imeneyi. Yeremiya asanamalize utumiki wake monga mneneri, mafumu ochokera ku banja la Davide anasiya kulamulira, zomwe zinali ngati kudulidwa kwa mtengo womwe mafumu amenewa ankachokerako. Komabe, chitsa chake chinali chikadali moyo. Patapita nthawi, Yesu anabadwira m’banja la ku mtundu wa Mfumu Davide. Iye ankadziwikanso ndi dzina lakuti “Yehova Ndiye Chilungamo Chathu,” ndipo dzinali likusonyeza kuti Mulungu amakonda kwambiri chilungamo. (Werengani Yeremiya 23:5, 6.) Yehova analola kuti Mwana wake wobadwa yekha azunzike padziko lapansi n’kufa. Kenako Yehova, potsatira chilungamo chake, anayamba kugwiritsira ntchito nsembe ya dipo imeneyo ya “mphukira” ya Davide, pokhululukira anthu. (Yer. 33:15) Nsembeyi inatsegula njira yoti anthu ena ayesedwe “olungama kuti akhale ndi moyo” ndiponso kuti adzozedwe ndi mzimu woyera n’kukhala nawo m’pangano latsopano. Umboni wina wosonyeza kuti Mulungu amakonda kwambiri chilungamo, ndi wakuti anthu ena amene sali nawo m’pangano limenelo mwachindunji, akhoza kupindula nalo ndipo akupinduladi, monga momwe tionere.—Aroma 5:18.
“Chilamulo cha Khristu” chimachititsa munthu kutumikira Yehova mofunitsitsa
11. (a) Kodi chilamulo cha pangano latsopano chinalembedwa pachiyani? (b) N’chifukwa chiyani anthu a “nkhosa zina” amachita chidwi ndi chilamulo cha pangano latsopano?
11 Kodi mungakonde kudziwa mbali zina zapadera za pangano latsopano? Kusiyana kumodzi kwakukulu pakati pa pangano latsopano ndi pangano la Chilamulo cha Mose, ndi malo omwe mapangano amenewa analembedwa. (Werengani Yeremiya 31:33.) Malamulo Khumi a pangano la Chilamulo analembedwa pamiyala, yomwe pamapeto pake inasowa. Mosiyana ndi zimenezi, Yeremiya analosera kuti chilamulo cha pangano latsopano chidzalembedwa m’mitima ya anthu, ndipo chidzakhalapo mpaka kalekale. Akhristu odzozedwa, amene ali nawo m’pangano latsopano, amayamikira kwambiri chilamulo chimenechi. Nanga bwanji za anthu a “nkhosa zina” omwe sali nawo m’pangano latsopano mwachindunji, koma akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi? (Yoh. 10:16) Nawonso amakonda kwambiri malamulo a Mulungu. Mwanjira ina, iwo ali ngati alendo omwe ankakhala ndi Aisiraeli ndipo ankatsatira Chilamulo cha Mose moti ankapindula kwambiri chifukwa chochita zimenezi.—Lev. 24:22; Num. 15:15.
12, 13. (a) Kodi chilamulo cha pangano latsopano n’chiyani? (b) N’chifukwa chiyani anthu amene amamvera “chilamulo cha Khristu” amatumikira Mulungu mwakufuna kwawo, osati mokakamizidwa?
12 Mungayankhe bwanji ngati mutafunsidwa kuti, ‘Kodi chilamulo chimenechi, chomwe chimalembedwa m’mitima ya Akhristu odzozedwa, n’chiyani?’ Chilamulo chimenechi chimatchedwanso “chilamulo cha Khristu.” Poyamba chinaperekedwa kwa Aisiraeli auzimu, amene ali m’pangano latsopano. (Agal. 6:2; Aroma 2:28, 29) Mungafotokoze “chilamulo cha Khristu” ndi mawu amodzi okha, akuti chikondi. (Mat. 22:36-39) Kodi Akhristu odzozedwa amatani kuti chilamulo chimenechi chilembedwe m’mitima yawo? Zinthu ziwiri zimene zimawathandiza kwambiri ndizo kuphunzira Mawu a Mulungu ndiponso kupemphera kwa Yehova. Choncho Akhristu onse oona, ngakhale amene sali nawo m’pangano latsopano koma akufuna kuti apindule nalo, ayenera kuchita zinthu ziwiri zimenezi nthawi zonse, chifukwa chakuti n’zofunika kwambiri pa kulambira koona.
13 “Chilamulo cha Khristu” chimatchedwanso ‘lamulo langwiro limene limabweretsa ufulu’ ndiponso “lamulo la mfulu.” (Yak. 1:25; 2:12) Anthu ambiri anabadwira mumtundu umene unali pansi pa Chilamulo cha Mose, koma palibe munthu amene amabadwa ali m’pangano latsopano kapena m’chilamulo cha Khristu. Pa anthu onse amene amamvera chilamulo cha Khristu, palibe amene amachita kukakamizidwa kuti azitumikira Mulungu. M’malomwake, anthu amenewa amasangalala kwambiri kudziwa kuti malamulo a Mulungu akhoza kulembedwa m’mitima mwawo. Amasangalalanso kudziwa kuti anthu masiku ano akhoza kuyamba kusangalala ndi madalitso osatha a m’pangano limene Yeremiya analoserali.
Kodi Mulungu anachita zotani kuti anthu azikhululukidwa machimo awo kudzera m’pangano latsopano? Kodi mungatani kuti muphunzire za chilamulo chimene chimalembedwa m’mitima?
ANTHU AMENE AMAPINDULA NDI PANGANO LATSOPANO
14. Kodi n’zoonekeratu kuti ndani amene amapindula ndi pangano latsopano?
14 Anthu ena ataphunzira zoti anthu 144,000 okha ndi amene ali nawo m’pangano latsopano, mwina anaganiza kuti okhawo ndi amene amapindula ndi panganoli. Mwina iwo anaganiza zimenezi chifukwa chakuti Akhristu odzozedwa, ndi anthu okhawo amene amayenera kudya mkate ndi kumwa vinyo pa mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Khristu, womwe umachitika chaka chilichonse. Pa mwambo umenewu, vinyo amaimira ‘magazi a pangano.’ (Maliko 14:24) Koma musaiwale kuti Yesu limodzi ndi anthu amene ali m’pangano latsopano, akupanga “mbewu” ya Abulahamu, ndipo kudzera mwa mbewu imeneyi, mitundu yonse idzadalitsidwa. (Agal. 3:8, 9, 29; Gen. 12:3) Choncho kudzera m’pangano latsopano, Yehova adzakwaniritsa lonjezo lake loti adzadalitsa anthu onse kudzera mwa “mbewu” ya Abulahamu.
15. Kodi Baibulo linalosera kuti odzozedwa adzagwira ntchito yotani?
15 Yesu Khristu, yemwe ndi mbali yoyamba ya mbewu ya Abulahamu, akutumikira monga Mkulu wa Ansembe. Iye anapereka nsembe yangwiro imene imachititsa kuti zikhale zotheka kuti anthu akhululukidwe machimo ndiponso zolakwa zawo. (Werengani Aheberi 2:17, 18.) Komabe, kalekale Mulungu ananena zoti padzakhala ‘ufumu wa ansembe ndi mtundu woyera.’ (Eks. 19:6) Mu mtundu wa Aisiraeli enieni, ansembe ndi mafumu ankachokera m’mafuko awiri osiyana. Choncho kodi zikanatheka bwanji kuti pakhale mtundu umene Mulungu analonjezawu, wokhala ndi mafumu omwenso ndi ansembe? Kalata yoyamba yomwe mtumwi Petulo analemba inkapita kwa anthu amene anali oyeretsedwa ndi mzimu. (1 Pet. 1:1, 2) Iye anati anthu amenewa anali “ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera.” (1 Pet. 2:9) Choncho Akhristu odzozedwa, omwe ali m’pangano latsopano, adzatumikira monga ansembe aang’ono. Tangoganizirani tanthauzo la zimenezi. Tsiku lililonse timavutika chifukwa cha uchimo, umene mpaka pano ‘ukulamulira monga mfumu.’ Koma anthu amene azidzatumikira monga ansembe aang’ono adzakhala oti nawonso anavutika mwanjira imeneyi. (Aroma 5:21) Iwo adzakhala akudziwa mmene munthu amamvera akalakwa n’kumavutika ndi chikumbumtima. Choncho, limodzi ndi Khristu, iwo azidzatimvetsa tikamadzayesetsa kulimbana ndi makhalidwe athu oipa obwera chifukwa cha uchimo.
16. Kodi lemba la Chivumbulutso 7:9, 14 lingalimbikitse bwanji anthu a “khamu lalikulu”?
16 Pa Chivumbulutso 7:9, 14, Yohane anaona “khamu lalikulu” la anthu “atavala mikanjo yoyera,” zomwe zikusonyeza kuti Mulungu amawaona kuti ndi oyera. Panopa khamu lalikulu limeneli likusonkhanitsidwa n’cholinga choti lidzathe kupulumuka ‘chisautso chachikulu.’ Choncho ngakhale panopa, Yehova amatha kuwaona anthu amenewa ngati olungama, monga mabwenzi ake. (Aroma 4:2, 3; Yak. 2:23) Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri. Ngati muli m’gulu la khamu lalikulu, musakayikire kuti Mulungu ndi wokonzeka kukuthandizani pamene mukuyesetsa kukhalabe oyera pamaso pake.
17. Kodi mfundo yakuti Yehova ‘sakumbukiranso’ machimo ikutanthauza chiyani?
17 Kodi chimachitika n’chiyani ndi machimo a anthu amene Mulungu amawakonda? Monga momwe taonera kale, Yehova ananena kudzera mwa Yeremiya kuti: “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.” (Yer. 31:34) Mulungu amakhululukira Akhristu odzozedwa pogwiritsira ntchito ‘magazi a pangano’ a nsembe ya Yesu. Komanso Mulungu amakhululukira machimo a anthu a khamu lalikulu pogwiritsira ntchito ‘magazi a pangano’ omwewo. Pamene Yeremiya ananena kuti Mulungu ‘sadzakumbukiranso’ machimo, sizikutanthauza kuti Mulunguyo amaiwaladi machimowo, kapena kuti amalephera kuwakumbukira. Koma zikutanthauza kuti Yehova akapereka chilango choyenera kwa munthu wochimwa yemwe walapa, kenako n’kumukhululukira, amakhala ngati wataya machimowo kumbuyo kwake. Mwachitsanzo, taganizirani za machimo amene Mfumu Davide anachita, okhudza Bati-seba ndi Uriya. Davide anapatsidwa chilango, ndipo anavutika ndi zotsatirapo za machimo akewo. (2 Sam. 11:4, 15, 27; 12:9-14; Yes. 38:17) Koma Mulungu sanapitirize kumuimba mlandu chifukwa cha machimo amenewo. (Werengani 2 Mbiri 7:17, 18.) Mogwirizana ndi zimene zili m’pangano latsopano, Yehova akakhululukira munthu machimo ake pogwiritsira ntchito nsembe ya Yesu, iye sawakumbukiranso.—Ezek. 18:21, 22.
18, 19. Kodi pangano latsopano lili ndi phunziro lotani kwa tonsefe lokhudza kukhululukirana machimo?
18 Monga mmene taonera, pangano latsopanoli likutisonyeza mbali yosangalatsa kwambiri ya mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ochimwa, kaya akhale odzozedwa amene ali m’pangano latsopano, kapena a khamu lalikulu amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo padziko lapansi. Choncho mukhoza kukhala otsimikiza kuti Yehova akakukhululukirani machimo, sadzakuimbaninso mlandu wa machimo amenewo. Chotero aliyense wa ife akhoza kuphunzirapo kanthu pa lonjezo la Mulungu limeneli lonena za pangano latsopano. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimayesetsa kutsanzira Yehova posakumbutsanso zolakwa za munthu wina zomwe ndinanena kuti ndinamukhululukira?’ (Mat. 6:14, 15) Tiyenera kutsatira mfundo imeneyi pa zolakwa zing’onozing’ono komanso zikuluzikulu, monga tchimo la chigololo limene mwamuna kapena mkazi wa Mkhristu anachita. Ngati munthu wosalakwayo wavomereza kukhululukira munthu wolapa yemwe anachita chigololo, kodi sipoyenera kuti ‘asakumbukirenso tchimolo’? N’zoona kuti sizophweka kuiwala zolakwa za munthu wina, koma imeneyi ndi njira imodzi imene tingatsanzirire Yehova.a
19 Tikhozanso kugwiritsira ntchito mfundo imeneyi, yomwe ikukhudzana ndi pangano latsopano, kwa munthu amene anachotsedwa mumpingo koma kenako analapa n’kubwezeretsedwa. Kodi mungamve bwanji poona kuti munthuyo walandiridwanso mumpingo, koma anakuchititsani kuti muluze ndalama kapena zinthu zinazake, kapenanso anakuipitsirani mbiri yanu mwanjira inayake? Kodi mfundo imene tikuipeza pa Yeremiya 31:34 ingakhudze bwanji maganizo athu ndiponso zochita zathu kwa munthuyo? Kodi tidzamukhululukira n’kupewa kumakumbutsanso zolakwa zimene anachitazo? (2 Akor. 2:6-8) Inde, anthu onse amene amayamikira pangano latsopano ayenera kuyesetsa kutsatira mfundo imeneyi pa moyo wawo.
Kodi mungagwiritse ntchito bwanji mfundo yokhudza kukhululukira ena imene tikuipeza m’pangano latsopano?
MADALITSO A PANGANO LATSOPANO, PANOPA KOMANSO M’TSOGOLO
20. Kodi mtima wanu ndi wosiyana motani ndi wa anthu ambiri a m’nthawi ya Yeremiya?
20 M’nthawi ya Yeremiya, Ayuda ambiri, mwa zochita zawo ankakhala ngati akunena kuti: “Yehova sadzachita zabwino kapena kuchita zoipa.” (Zef. 1:12) Ngakhale kuti iwo ankamudziwa ndithu Yehova ndiponso zimene iye amakonda, ankaganiza kuti iye sadzachitapo kanthu kalikonse komanso sakuyembekezera kuti anthuwo azitsatira mfundo zilizonse pa moyo wawo. Koma inuyo mukudziwa kuti palibe chimene Mulungu saona. Choncho mumamuopa chifukwa chomulemekeza, ndipo mumafunitsitsa kupewa kuchita choipa chilichonse. (Yer. 16:17) Komabe, mumadziwa kuti Yehova ndi Tate wabwino. Iye amaona zabwino zimene timachita, kaya anthu enanso akuziona kapena ayi.—2 Mbiri 16:9.
Amene atumikira Mulungu mokhulupirika adzasangalala ndi madalitso ake m’tsogolo
21, 22. Kodi n’chifukwa chiyani simukufunikiranso kuuzidwa kuti: “Mum’dziwe Yehova”?
21 Mfundo ina yofunika kwambiri m’pangano latsopano yafotokozedwa motere: “Ndidzaika chilamulo changa mwa iwo ndipo ndidzachilemba mumtima mwawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo . . . Munthu sadzaphunzitsanso mnzake kapena m’bale wake kuti, ‘Mum’dziwe Yehova!’ pakuti aliyense wa iwo adzandidziwa.” (Yer. 31:33, 34) Akhristu odzozedwa amene ali padziko lapansi masiku ano asonyeza kuti ali ndi chilamulo cha Mulungu mumtima mwawo. Iwo amakonda mfundo za choonadi zimene zili m’chilamulochi, m’malo modalira ziphunzitso za munthu wina aliyense. Ndipo iwo akhala akuphunzitsa mosangalala anthu a khamu lalikulu kuti nawonso adziwe bwino choonadi cha m’Baibulo. Choncho anthu a khamu lalikuluwa, omwe akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, afikanso podziwa Yehova ndi kumukonda. Iwo amamvera malangizo a Mulungu ndi mtima wonse ndiponso amakhulupirira malonjezo ake. Mwina inunso ndi mmodzi wa anthu oterewa. Mwamudziwa bwino Yehova ndipo muli naye pa ubwenzi wabwino. Limenelitu ndi dalitso lapadera kwambiri.
22 Kodi munachita zinthu zotani kuti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Yehova? Mwina mukukumbukira nthawi zimene munaona kuti Yehova anayankha mapemphero anu. Zinthu ngati zimenezo zinakuchititsani kuti mumudziwe bwino Mulungu, ndipo munayamba kumukonda kwambiri. Mwinanso munaona kuti iye akukuthandizani pa nthawi imene munakumbukira lemba linalake limene linakuthandizani kulimbana ndi mavuto enaake. Ndi bwino kumaona kuti zinthu zimenezi n’zamtengo wapatali. Mukapitiriza kuphunzira Mawu ake, mudzapitirizanso kumudziwa bwino, ndipo zimenezi zidzakuthandizani mpaka kalekale.
23. Kodi kudziwa Yehova kungakuthandizeni bwanji kuti musiye kumangodziimba mlandu popanda chifukwa?
23 Koma palinso dalitso lina limene tingakhale nalo panopa chifukwa cha pangano latsopanoli. Tikadziwa kuti Yehova amatikhululukira machimo athu chifukwa cha pangano limenelo, zingatithandize kuti tisiye kumangodziimba mlandu chifukwa cha zolakwa zimene tinachita. Mwachitsanzo, anthu ena amene anachotsapo mimba asanadziwe mfundo za Mulungu akhoza kumadziimba mlandu ndiponso kukhala achisoni chifukwa chakuti anapha mwadala mwana amene anali m’mimba mwawo. Ena amamvanso chimodzimodzi chifukwa chakuti anapha anthu pa nkhondo. Koma nsembe ya dipo ya Yesu, yomwe ndi maziko a pangano latsopano, imathandiza kuti anthu amene alapa mochokera pansi pa mtima akhululukidwe machimo awo. Choncho, kodi sitikuyenera kukhulupirira kuti ngati Yehova watikhululukira machimo athu, ndiye kuti amaona kuti nkhani imeneyo inatha? Sitiyenera kumangoganizirabe machimo amene Yehova anatikhululukira ndi mtima wonse.
24. Kodi nkhani imene ili pa Yeremiya 31:20 ingakulimbikitseni bwanji?
24 Pa lemba la Yeremiya 31:20 (Werengani.), timapeza umboni wooneka bwino kwambiri wosonyeza kuti Yehova amakhululukadi. Kutatsala zaka zambiri kuti nthawi ya Yeremiya ifike, Yehova analanga ufumu wakumpoto wa Isiraeli wa mafuko 10 (womwe ukutchedwa Efuraimu, fuko lomwe linali lodziwika kwambiri mu ufumuwu). Mulungu analanga anthu a mu ufumu umenewu chifukwa chakuti ankapembedza mafano, ndipo iwo anatengedwa n’kupita ku ukapolo. Komabe, Mulungu ankakonda kwambiri anthu amtundu umenewo ndipo anawasonyeza chikondi chachikulu. Iye ankawakonda kwambiri ngati ‘mwana wokondedwa.’ Akaganizira za iwo, m’mimba mwake ‘munkabwadamuka,’ kusonyeza kuti ankakhudzidwa kwambiri mumtima. Nkhani imeneyi, yomwe inalembedwa pofotokoza za pangano latsopano, ikusonyeza kuti Yehova amakhululukiradi ndi mtima wonse anthu amene alapa machimo awo.
25. N’chifukwa chiyani muyenera kuthokoza Yehova chifukwa chokhazikitsa pangano latsopano?
25 Lonjezo la Yehova lakuti adzakhululukira machimo kudzera m’pangano latsopano, lidzafika pachimake pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu. Yesu Khristu, limodzi ndi ansembe 144,000 amene iye akuwatsogolera, adzakhala atathandiza anthu okhulupirika kuti akhalenso angwiro. Pamapeto pa mayesero omaliza, anthu adzakhaladi oyenerera kukhala m’banja la Yehova la m’chilengedwe chonse, lomwe lidzapangidwe ndi atumiki ake apadziko lapansi ndiponso akumwamba. (Werengani Aroma 8:19-22.) Kwa zaka zambiri, anthu onse akhala akubuula chifukwa cholemedwa ndi uchimo. Koma pa nthawi imeneyo anthu onse a Yehova adzakhala ndi “ufulu waulemerero wa ana a Mulungu,” ndipo adzamasuka ku uchimo ndi imfa. Choncho musakayikire zoti mungapeze madalitso ochuluka kwambiri kudzera m’pangano latsopano, lomwe ndi njira imene Mulungu anasonyezera chikondi chachikulu. “Mphukira” ya Davide ingakuthandizeni kuyambira panopa mpaka kalekale ndipo mungakhale osangalala ndi ‘chilungamo m’dzikoli.’—Yer. 33:15.
Kodi pangano latsopano lingakupindulitseni bwanji panopa komanso m’tsogolo?
a Zimene Hoseya anachitira Gomeri zinachitira bwino chithunzi mfundo yakuti Mulungu ali ndi mtima wofunitsitsa kukhululukira anthu. Onani Nsanja ya Olonda ya November 15, 2005, tsamba 17 mpaka 21, komanso onani ndemanga za lemba la Hoseya 2:14-16, m’buku lachingelezi lakuti Live With Jehovah’s Day in Mind, tsamba 128 mpaka 130.