Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w91 8/15 tsamba 24-27
  • Yehova “Ndiye Wankhondo”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova “Ndiye Wankhondo”
  • Nsanja ya Olonda—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Msampha​—Wocheredwera Aisrayeli Kapena Farao?
  • Yehova Athirira Yoswa Nkhondo
  • Nkhondo ku Kisoni
  • Kulaka Gogi ndi Gulu Lake
  • “Chirimikani, Ndipo Penyani Chipulumutso cha Yehova”
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kuoloka Nyanja Yofiira
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kuchokera pa Tabori Kutsikira ku Chilakiko!
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Pa Nyanja Yofiira Panachitika Zodabwitsa Kwambiri
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1991
w91 8/15 tsamba 24-27

Yehova “Ndiye Wankhondo”

MAKAMU aukatswiri koposa a gulu lankhondo Lachiigupto anafafanizidwa. Mitembo ya apagareta ndi apakavalo inali yanda! ikugavira m’mbali mwa Nyanja Yofiira, ndipo zida zankhondo zinali mbwee pagombe. Amuna a Israyeli otsogozedwa ndi Mose, anaimba mokondwera nyimbo yachilakiko kumati: ‘Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m’nyanja. Yehova ndiye wankhondo; dzina lake ndiye Yehova.’​—Eksodo 15:1, 3.

Chilakiko cha Yehova pa Nyanja Yofiira chinalidi chisonyezero cha kupambana kwake m’nkhondo. Israyeli anatuluka m’Igupto m’mpangidwe wankhondo koma ndi zida zochepa zomenyera nkhondo. Yehova anawatsogolera ndi mtambo umene usiku unakhala mtambo wamoto, kuchokera ku Ramese mpaka ku ‘malekezero a chipululu’ ku Etamu. (Eksodo 12:37; 13:18, 20-22) Ndiyeno Yehova anati kwa Mose: ‘Lankhula ndi anthu a Israyeli, kuti abwerere m’mbuyo nagone patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja yamchere, patsogolo pa Baala-Zefoni. . . . Ndipo Farao dzanena za ana a Israyeli, Azimidwa dziko, chipululu chawatsekera. . . . Ndipo . . . adzaŵalondola.’ (Eksodo 14:1-4) Momvera, Israyeli anatembenuka ndi kupita ku Pihahiroti. Azondi a Farao anasimba za kusokonezeka kowonekerako, ndipo monga momwe kunaloseredwera, Farao anakonzekeretsa gulu lake lankhondo kuti lilondole.​—Eksodo 14:5-9.

Msampha​—Wocheredwera Aisrayeli Kapena Farao?

Pochingidwa ndi mapiri kumbali zonse ziŵiri, nyanja kutsogolo, ndipo Aigupto kumbuyo, Aisrayeli ochita manthawo anawonekera kukhala atagwidwa m’msampha, chotero anafuulira kwa Mulungu kaamba ka chithandizo. Akusonkhanitsa anthuwo, Mose anati: ‘Musawope, chirimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero; pakuti Aigupto mwawaona leroŵa, simudzawaonanso konse. Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.’ (Eksodo 14:10-14) Mogwirizana ndi lonjezolo, ‘mtambo njo uja unachoka patsogolo pawo, nuima pambuyo pawo; nuloŵa pakati pa ulendo wa Aigupto ndi ulendo wa Aisrayeli. . . . Ndipo ulendo wina sunayandikizana ndi unzake usiku wonse.’​—Eksodo 14:15-20.

Monga momwedi Yehova analangizira, Mose anatambasulira ndodo yake ku nyanja ‘naigaŵa’ kuti Aisrayeli athaŵe. Ndipo chozizwitsa chowopsa chinachitikadi! (Eksodo 14:16, 21) Chimphepo cholimba chochokera kummaŵa chinayamba kugaŵa madzi a Nyanja Yofiira, chikumapanga njira yotakata kwambiri kutheketsa mtundu wonsewo​—chigulu cha anthu pafupifupi mamiliyoni atatu​—kudutsa m’mpangidwe wankhondo. Kulamanzere ndi kulamanja kwa mzera wa Aisrayeli, madzi “ounjikana” anaima ngati makoma aŵiri aakulu.​—Eksodo 15:8.

Motsogozedwa ndi kuunika kwa mtambo wamoto umenewo, Aisrayeli anathaŵa mwakuyenda panthaka ya panyanja youmitsidwa ndi mphepo. Pofika m’maŵa, munthu wokhala kunthungo wa Aisrayeli anawolokera kutsidya lina. ‘Ndipo Aigupto anawalondola, naloŵa pakati pa nyanja powatsata, ndiwo akavalo onse a Farao, magareta ake, ndi apakavalo ake.’ Olondolawo analoŵa m’msampha!​—Eksodo 14:23.

‘[Yehova] anavuta ulendo wa Aigupto. Nagulula [magudumu a, NW] magareta awo, nawayendetsa molemetsa.’ Tsopano Mose anatambasulira dzanja lake ku nyanja, ndipo ‘nyanja inabwerera m’mayendedwe ake.’ Makoma amadzi anagwa nayamba kumiza Aigupto. Iwo anayesa kuthaŵa, “ndipo Yehova anakutumula [iwo] mkati mwa nyanja.” Palibe ndimmodzi yense anapulumuka! Mwachisangalalo Aisrayeli anaimba nyimbo yawo yachilakiko kwa Yehova.​—Eksodo 14:24–15:3; Salmo 106:11.

Yehova Athirira Yoswa Nkhondo

Yehova anatsimikizira kukhala “wankhondo” m’nkhondo zinanso. Nkhondo ina inali ku Ai. Kuukira mzindawo koyamba kunalephera chifukwa cha kulakwa kwakukulu kwa Akani. Pamene mlanduwo unawongoleredwa, Yehova anapereka malangizo ankhondo kwa Yoswa.​—Yoswa 7:1, 4, 5, 11-26; 8:1, 2.

Potsatira malangizo a Yehova, Yoswa anaika olalira kumbuyo kwa mzindawo usiku, kumbali yakumadzulo. Gulu lake lalikulu linatsogozedwa kumpoto ku chigwa kunja kwa Ai pafupi kwenikweni ndipo linawonekera lokonzekera kuukira kwachindunji. Amuna a Ai analoŵa m’msampha. Pokhala okondweretsedwa ndi chilakiko cha kulimbana kwawo kwapapitapo, iwo anaguduka kutuluka m’mzinda nalunjika kukalimbana ndi Aisrayeli. Akunamizira kuthaŵa, Aisrayeli anabwerera ku ‘njira ya kuchipululu,’ akukokera adaniwo kutali ndi Ai.​—Yoswa 8:3-17.

Panthaŵi yoyenerera yeniyeni, Yehova anati kwa Yoswa: “Tambasula nthungo iri m’dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m’dzanja lako.” Powona chizindikiro chimenechi, amuna olalirawo anaukira mzindawo, kuupereka ku lupanga ndi moto. Pakuwona utsiwo, magulu a adani kunjako anazizira m’mawondo kotheratu. Akubwerera kuti aukire, Yoswa anatsekereza adaniwo pakati pa magulu ake ankhondo aŵiriwo. Kodi chinali chilakiko chaumunthu? Ayi. Aisrayeli anapambana chifukwa chakuti, monga momwe Yoswa pambuyo pake anawauzira: “Yehova Mulungu wanu ndiye anakuthirirani nkhondo.”​—Yoswa 8:18-27; 23:3.

Nkhondo ku Kisoni

Kupambana kwa Yehova m’nkhondo kunasonyezedwanso ku Chigwa cha Kisoni, pafupi ndi Megido. Yabini, mfumu Yachikanani inatsendereza Israyeli kwa zaka 20. Gulu lake lankhondo, lotsogozedwa ndi Sisera, linaphatikizapo magareta ankhondo 900 okhala ndi mazenga ku magudumu awo​—gulu lankhondo lowonekera kukhala losakhoza kulakidwa masikuwo.​—Oweruza 4:1-3.

Mosasamala kanthu za zimenezo, Yehova anauza Woweruza Baraki kupyolera mwa Debora, mneneri wamkazi, kusonkhanitsa amuna ankhondo zikwi khumi pamwamba pa Phiri la Tabori kutokosa magulu ankhondo a Yabini. Sisera anachitapo kanthu mofulumira motsutsana ndi anthu ankhondowo omawonjezereka, akuthamanga kuchokera ku Haroseti kumka ku chigwa cha Kisoni, pakati pa Phiri la Tabori ndi Megido. Mosakaikira iye anaganiza kuti pano pamalo atyatyatya, asirikali oyenda pansi a Israyeli okhala ndi zida zochepa sakakhala ndi mpata wolimbana ndi magareta ake. Komabe, sanazindikire kuti akalimbana ndi Mdani wakumwamba.​—Oweruza 4:4-7, 12, 13.

Yehova analamula Baraki kuchoka pamalo okwezeka otetezereka a Tabori kutsikira m’chigwa, machenjera omwe anagwetsera magulu ankhondo a Sisera m’nkhondo. Ndiyeno Yehova anaukira! Madzi osefukira anasintha bwalo lankhondolo kukhala matenjetenje, kulepheretsa magulu ankhondo a Sisera kuyenda. Ndi chisokonezo chobukapo, asirikali oyenda pansi a Israyeli mosavuta anagonjetsa kotheratu mdani wawoyo. “Gulu lonse lankhondo la Sisera linagwa ndi lupanga, sanatsala munthu ndi mmodzi yense.” Mkokomo wamadzi a Kisoni unamiza magareta a Akanani ndipo mwina unakokolola mitembo ina.​—Oweruza 4:14-16; 5:20, 21.

Kulaka Gogi ndi Gulu Lake

Zochitika zamakedzana zimenezi zinachitira chithunzi chilakiko cha Yehova chachikulu koposa chomwe chikubwera. Chomwe chiri pafupi kwenikweni ndicho nkhondo imene idzachitika mu “zaka zotsiriza.” Malinga ndi ulosi wa Ezekieli, Gogi, chizindikiro cha “mkulu wa dziko,” Satana Mdyerekezi, adzasonkhanitsa gulu lankhondo loukira lamitundu yonse. Adzatsogolera magulu ake ankhondo kuukira “mapiri a Israyeli” ophiphiritsira, ndiko kuti, malo okwezeka auzimu a “Israyeli wa Mulungu” Wachikristu.​—Ezekieli 38:1-9; Yohane 12:31; Agalatiya 6:16.

Kodi nchiyani chimene chikusonkhezera Gogi kupanga kuukira kotheratu kumeneku pa anthu a Mulungu? Ulosiwo umaloza ku mkhalidwe wawo wauzimu wamtendere, ndi wokhupuka. Gogi akunena kuti: ‘Ndidzakwera kumka ku dziko la midzi yopanda malinga, ndidzamka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mipingiridzo, kapena zitseko; kulanda ndi kufunkha . . . [za] anthu . . . odziwonera zoŵeta ndi chuma.’​—Ezekieli 38:10-12.

Mwachisawawa, anthu a Yehova sali achuma mwakuthupi. Komabe, iwo amakundika chuma chauzimu chochuluka monga chotulukapo cha ntchito yawo yolalikira ya padziko lonse. ‘Khamu lalikulu . . . lochokera mwa mtundu uliwonse’ loposa mamiliyoni anayi tsopano, lasonkhanitsidwa. (Chibvumbulutso 7:9, 10) Ndichuma chotani nanga! Satana​—wokwiitsidwa ndi kukhupuka kwauzimu kumeneku​—akuyesayesa kufafaniza anthu a Mulungu.

Ndithudi, mwakubwera pamalo ophiphiritsira a dziko la Israyeli, Gogi, akuukira Yehova Mulungu mwiniyo. “Ukali wanga udzakwera m’mphuno mwanga,” atero Yehova, yemwe adzabwezerera anthu ake. Makamu ankhondo a Gogi adzasokonezeka m’chipwirikiti. ‘Munthu aliyense lupanga lake lidzawombana nalo la mbale wake.’ Kenaka Yehova adzamasula mphamvu zake zowononga​—‘mvumbi waukulu, ndi matalala aakulu, moto ndi sulfure.’ Monga pa Nyanja Yofiira, ku Ai, ndi Kisoni, Yehova kachiŵirinso adzamenyera anthu ake nkhondo ndi kulemekeza dzina lake. ‘Ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziŵika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.’​—Ezekieli 38:18-23.

Cholembedwa cha m’mbiri cha nkhondo za Yehova m’nthaŵi zamakedzana chimatipatsa chifukwa chakukhalira ndi chidaliro chotheratu m’chilakiko chamtsogolo mkati mwa ‘chisautso chachikulu.’ (Mateyu 24:21, 22) Pokhala wolamulira wa nthaŵi zonse, Yehova ali wokhoza kuganiza koposa adani ake ndi kuyendetsa zinthu kuti apulumutse anthu ake. Ndithudi, kudzakhala monga momwe Yesaya analoserera kuti: ‘Yehova adzatuluka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wankhondo; Iye adzafuula, inde adzakuwa zolimba; adzachita zamphamvu pa adani ake.’ (Yesaya 42:13) Pamaso pa Mboni zake, iye kunthaŵi zosatha adzakhalabe YEHOVA, “NDIYE WANKHONDO”!​—Eksodo 15:3.

[Mapu patsamba 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Njira ya ulendo wotchedwa Eksodo kuchokera ku Igupto

GOSENI

Memphis

Ramese

Sukoti

Migidoli

Pihahiroti

Etamu

[Zithunzi patsamba 26]

Pano, m’dera la Ai, Yehova anatsogolera Yoswa ndi anthu Ake ku chilakiko chodabwitsa

Madzi a Kisoni anasefukira mofulumira, a kumathandizira kugonjetsa adani a Yehova

[Mawu a Chithunzi]

Zithunzithunzi: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena