Ponena zoponya anthu mung’anjo yamoto, mbiri ya mzinda wa wakale wa Babulo, imafotokoza za nkhaniyi mobwerezabwereza. Mbiriyi imafotokozanso za anthu ena omwe analandira chilangochi pambuyo poti mfumu yapereka chilolezo. Munkhani ina yakale yomwe inalembedwa m’nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Nebukadinezara, inafotokoza za chilango chomwe akuluakulu ena aboma anapatsidwa chifukwa chonyoza milungu ya ku Babulo. Nkhaniyo imati: “ Awonongeni, awotcheni, awambeni . . . mu uvuni . . . afuke utsi, moto wawo ulilime kwambiri ndipo pafuke utsi wambiri kuti asakhalenso ndi moyo.”