Mutu 2
Danieli—Buku Limene Likuzengedwa Mlandu
1, 2. Kodi buku la Danieli likuzengedwa mlandu m’lingaliro lotani, ndipo muganiza n’chifukwa chiyani kuli kofunika kupenda umboni wotchinjiriza bukulo?
YEREKEZANI kuti muli m’khothi, kudzamvera mlandu wofunika kwambiri umene ukuzengedwa. Munthu wina waimirira ndipo akuimbidwa mlandu wa chinyengo. Loya wa boma akunenetsa kuti munthuyo alidi ndi mlandu. Komabe, wosumiridwayo ali ndi mbiri ya zaka zambiri yokhala munthu wokhulupirika. Kodi simungafune kumva umboni wake wodzitchinjiriza?
2 Inunso muli mumkhalidwe umodzimodziwo ponena za buku la Danieli. Wolemba wake anali mwamuna wodziŵika kwambiri chifukwa cha kukhulupirika kwake. Bukulo lotchedwa ndi dzina lake lakhala lodalirika kwambiri kwa zaka zikwizikwi. Limaonetsa lokha kuti ndi mbiri yakale yoona, yolembedwa ndi Danieli, mneneri wachihebri amene anakhalako m’zaka za zana la 7 ndi la 6 B.C.E. Kuŵerengera zaka kolondola kwa m’Baibulo kumasonyeza kuti buku lakelo likusimba zochitika za m’nyengo yoyambira pafupifupi 618 mpaka 536 B.C.E. ndipo linamalizidwa pafupifupi m’chaka chomalizirachi. Chikhalirecho bukulo likuimbidwa mlandu. Mabuku otchedwa insaikulopediya ndi mabuku ena a maumboni amasonyeza, kapena kunenetsa ndithu kuti bukulo n’lachinyengo.
3. Pankhani yakuti buku la Danieli n’loona kapena ayi, kodi The New Encyclopædia Britannica ikunenapo chiyani?
3 Mwachitsanzo, The New Encyclopædia Britannica imavomereza kuti buku la Danieli nthaŵi ina “anthu ambiri ankalikhulupirira kukhala mbiri yoona, yokhala ndi ulosi wodalirika.” Buku la Britannica limenelo limanena kuti, koma zoona zake n’zakuti, buku la Danieli “linadzalembedwa pambuyo pake pamene mtunduwo unagwa m’vuto—pamene Ayuda ankazunzidwa koopsa ndi [Mfumu ya Suriya] Antiyokasi 4 Epifanasi.” Insaikulopediyayo imati buku la Danieli linalembedwa pakati pa 167 ndi 164 B.C.E. Buku lokhalokhalo limanenanso kuti wolemba buku la Danieli sakulosera zenizeni zam’tsogolo ayi, koma akungofotokoza “zochitika za m’nthaŵi yakale m’njira yosonyeza ngati maulosi odzachitika m’tsogolo.”
4. Kodi buku la Danieli linayamba liti kutsutsidwa, ndipo n’chiyani chakolezera chitsutso chofanana m’zaka mazana aposachedwapa?
4 Kodi maganizo oterowo amachokera kuti? Kutsutsa buku la Danieli si kwatsopano. Kunayambira kalekale m’zaka za zana lachitatu C.E. ndi wafilosofi wotchedwa Porphyry. Mofanana ndi ena ambiri mu Ufumu wa Roma, iyeyo anaopsezedwa ndi mphamvu yomwe Chikristu chinali nayo. Analemba mabuku 15 amene cholinga chake chinali kufooketsa chipembedzo “chatsopanocho.” Buku la nambala 12 linali lotsutsa buku la Danieli. Porphyry anati bukulo linali lachinyengo, lolembedwa ndi Myuda m’zaka za zana lachiŵiri B.C.E. Chitsutso chofanana chinafika m’zaka za mazana a 18 ndi 19. M’kuona kwa akatswiri ofufuza Baibulo limodzinso ndi olimbikitsa nzeru zaumunthu, ulosi—kulosera zochitika zam’tsogolo—ndi chinthu chosatheka. Danieli anakhala chandamale chachikulu cha mtsutso umenewo. Kwenikweni, tingatero kuti iye limodzi ndi buku lake anali kuzengedwa mlandu m’khothi. Akatswiri otsutsawo anati ali ndi umboni wokwanira wotsimikiza kuti bukulo silinalembedwe ndi Danieli panthaŵi imene Ayuda anali mu ukaidi ku Babulo, koma linalembedwa ndi munthu wina zaka mazana angapo pambuyo pake.a Zitsutso zoterozo zinachuluka kwambiri moti wolemba mabuku wina analemba buku lolandula zitsutsozo lotchedwa Daniel in the Critics’ Den.
5. N’chifukwa chiyani kuli kofunika kutsimikiza kuti buku la Danieli lilidi loona?
5 Kodi akatswiri otsutsawo ali ndi umboni wochirikiza zonena zawozo zimene akuzinena mwachidaliro choncho? Kapena kodi umboniwo ukuchirikizadi zifukwa zimene akuzipereka? Apa pali nkhani zazikulu zimene zikuloŵetsedwapo. Si mbiri yokha ya buku lakale limeneli komanso tsogolo lathu likuloŵetsedwapo. Ngati buku la Danieli n’lachinyengo, ndiye kuti malonjezo ake onena za tsogolo la anthu angokhala mawu opanda pake. Koma ngati lili ndi maulosi enieni, ndithudi mudzakhala ndi chidwi choti muphunzire tanthauzo la maulosiwo kwa ife lerolino. Mogwirizana ndi mfundo zimenezo, tiyeni tipende ziukiro zina zimene zaperekedwa pa Danieli.
6. Kodi n’chinenezo chotani chimene nthaŵi zina chimaperekedwa ponena za mbiri ya m’buku la Danieli?
6 Mwachitsanzo, titenge chinenezo chopezeka m’buku lotchedwa The Encyclopedia Americana: “Zochitika zambiri za m’nthaŵi zakale [monga nthaŵi ya ukaidi wa ku Babulo] zasimbidwa molakwa kwambiri” m’buku la Danieli. Kodi zimenezo n’zoona? Tiyeni tione chimodzichimodzi cha zolakwa zitatu zimene akunena.
NKHANI YA KUSOŴEKA KWA UFUMU
7. (a) N’chifukwa chiyani kutchula Belisazara kwa Danieli kunakhala kofunika kwambiri kwa otsutsa Baibulo kwa nthaŵi yaitali? (b) Kodi chinachitika n’chiyani ku chikhulupiriro chakuti Belisazara anali munthu wongopeka?
7 Danieli analemba kuti Belisazara, “mwana” wa Nebukadinezara, anali kulamulira monga mfumu m’Babulo pamene mzindawo unagwetsedwa. (Danieli 5:1, 11, 18, 22, 30) Akatswiri ofufuzawo anatsutsa mawu ameneŵa kwanthaŵi yaitali, chifukwa chakuti dzina la Belisazara sanalipeze kwina kulikonse kupatulapo m’Baibulo. M’malo mwake, olemba mbiri akale anatchula Nabonidasi, woloŵa m’malo mwa Nebukadinezara, kukhala womalizira pa mafumu a Babulo. Choncho, mu 1850, Ferdinand Hitzig ananena kuti mwachionekere, Belisazara anangopekedwa ndi wolembayo. Koma kodi ganizo la Hitzig limenelo silikuoneka kwa inu kuti anangodya mfulumira? Ndi iko komwe, kodi kusapezeka kwa dzina la mfumu imeneyi—makamaka m’nyengo imene zolemba za mbiri yakale zinali zosoŵa kwambiri—kungakhaledi umboni wakuti iye sanakhaleko? Chabwino, mu 1854 zolembapo zadongo zing’onozing’ono zinafukulidwa m’mabwinja a mzinda wa Babulo wakale wotchedwa Uri, dera limene panopo ndi kumwera kwa Iraq. Zolemba zozokota zimenezo za Mfumu Nabonidasi zinaphatikizapo pemphero lake lopempherera “Bel-sar-ussur, mwana wanga wamwamuna wamkulu.” Ngakhale akatswiri otsutsawo anakakamizika kuvomereza: Uyu anali Belisazara wa m’buku la Danieli.
8. Kodi kunena kwa Danieli kuti Belisazara anali mfumu yolamulira kwatsimikiziridwa motani kukhala koona?
8 Komabe, otsutsawo sanakhutire. “Zimenezi sizikutsimikiza chilichonse,” analemba motero wina dzina lake H. F. Talbot. Iyeyo anati mwana wotchulidwa m’zolemba zozokotazo akhoza kukhala mwana wamba, koma Danieli akum’sonyeza kukhala mfumu yolamulira. Komabe, patangopita chaka chimodzi zonena za Talbot zitafalitsidwa, zolembapo zina zadongo zinafukulidwa zimene zinafotokoza kuti Belisazara anali ndi alembi ndiponso antchito ena m’nyumba mwake. Ameneyo sakanakhala mwana wamba ayi! Potsirizira pake, zolembapo zina zadongo zinaphera mphongo nkhaniyo, zikumanena kuti panthaŵi ina Nabonidasi nthaŵi zina amachoka m’Babulo kwa zaka zingapo ndithu. Zolembapo zimenezi zinasonyezanso kuti m’nthaŵi zimenezo, iye “anali kuikiza ufumu” wa Babulo m’manja mwa mwana wake wamwamuna wamkulu (Belisazara). Panthaŵi zoterozo, Belisazara amakhaladi mfumu—wolamulira limodzi ndi atate wake.b
9. (a) Kodi Danieli ayenera anatanthauza kuti Belisazara anali mwana wa Nebukadinezara m’lingaliro lotani? (b) N’chifukwa chiyani otsutsa ali olakwa ponena kuti Danieli sakunena chilichonse chokhudzana ndi kukhalako kwa Nabonidasi?
9 Posakhutirabe, otsutsa ena akudandaula kuti Baibulo limatchula Belisazara, kuti mwana wa Nebukadinezara, osati mwana wa Nabonidasi. Ndiponso ena akuumirira kuti Danieli sakutchula china chilichonse chokhudzana ndi kukhalako kwa Nabonidasi. Komabe, zitsutso ziŵiri zonsezo zimagwa pozipenda. Zikuoneka kuti Nabonidasi, anakwatira mwana wa Nebukadinezara. Zimenezo zikutanthauza kuti Belisazara anali mdzukulu wa Nebukadinezara. Chihebri ndi Chialamu zilibe mawu akuti “gogo wamwamuna” kapena “mdzukulu wamwamuna”; “mwana” akhoza kutanthauza “mdzukulu” kapena ngakhale “mbadwa.” (Yerekezani ndi Mateyu 1:1.) Ndiponso, nkhani ya m’Baibulo imasonyeza kuti Belisazara akhoza kutchedwa mwana wa Nabonidasi. Belisazara atachita mantha kwambiri poona mawu olembedwa ndi dzanja pakhoma ochititsa manthawo, mothedwa nzeru anapereka udindo wachitatu mu ufumuwo kwa aliyense amene akanatha kumasulira mawuwo. (Danieli 5:7) N’chifukwa chiyani anapereka udindo wachitatu osati wachiŵiri? Zimenezo zikusonyeza kuti udindo woyamba ndi wachiŵiri panali kale anthu. Ndipo analipowo ndi Nabonidasi ndi mwana wake, Belisazara.
10. N’chifukwa chiyani buku la Danieli limaunika zambiri ponena za ufumu wa Babulo kuposa olemba mbiri ena akale?
10 Choncho pamene Danieli atchula Belisazara, si umboni wakuti bukulo ndi mbiri yakale “yosimbidwa molakwa kwambiri.” Mosiyana n’zimenezo, ngakhale kuti cholinga cha Danieli sichinali kulemba mbiri ya Babulo—akutipatsabe chithunzi chounika zochuluka kuposa olemba mbiri akale monga Herodotus, Xenophon, ndi Berossus. Kodi n’chiyani chinatheketsa Danieli kulemba zinthu zimene iwowo anaziphonya? Chifukwa iye anali komweko ku Babulo. Buku lakelo n’lolembedwa ndi mboni yoona ndi maso, osati wina wongonamizira wa m’zaka mazana ambiri pambuyo pake.
KODI DARIYO MMEDI ANALI YANI?
11. Malinga n’kunena kwa Danieli, kodi Dariyo Mmedi anali ndani, koma kodi anthu anenanji za iye?
11 Danieli akusimba kuti Babulo atagwa, mfumu ina yotchedwa “Dariyo Mmedi” inayamba kulamulira. (Danieli 5:31) Dariyo Mmedi sanapezeke akutchulidwa ndi dzina kwina kulikonse m’mbiri yolemba kapena m’zofukula m’mabwinja. Motero, The New Encyclopædia Britannica imanena kuti Dariyo ameneyu “n’ngwopeka.”
12. (a) N’chifukwa chiyani otsutsa Baibulo ayenera kudziŵa bwino lomwe, m’malo moumirira kuti Dariyo Mmediyo sanakhaleko konse? (b) Kodi mfundo yothekera yodziŵikitsa Dariyo Mmedi n’chiyani, ndipo ndi umboni wotani wosonyeza zimenezo?
12 Akatswiri azamaphunziro ena akhala osamala kwambiri. Ndi iko komwe, otsutsawo nthaŵi ina ankanena kuti Belisazara “n’ngwopeka.” Mosakayika, nkhani ya Dariyo idzathanso chimodzimodzi. Miyala yolembapo mawu ozokota yasonyeza kale kuti Koresi Mperisiyayo sanatchedwe “Mfumu ya Babulo” panthaŵi imene anagonjetsa mzindawo. Wofufuza wina anapereka maganizo akuti: “Amene anatchedwa ‘Mfumu ya Babulo’ anali mfumu yaing’ono pansi pa ulamuliro wa Koresi, osati Koresi mwiniyo.” Kodi mwina Dariyo linali dzina la ulamuliro, kapena dzina laulemu, la nduna yamphamvu yachimedi yosiyidwa kukhala yoyang’anira Babulo? Ena akuti n’kutheka kuti Dariyo anali mwamuna wina wotchedwa Gubaru. Koresi anaika Gubaru kukhala gavana m’Babulo, ndipo zolemba za mbiri yakale zimatsimikizira kuti iye analamulira ndi mphamvu yaikulu kwambiri. Mwala wina wolembedwa mawu ozokota umanena kuti iye anasankha magavana ena ang’onoang’ono m’Babulo. Chosangalatsanso n’chakuti, Danieli akunena kuti Dariyo anasankha akalonga ang’onoang’ono okwanira 120 kuti alamulire mu ufumu wa Babulo.—Danieli 6:1.
13. Kodi pali chifukwa chomveka chotani chimene Dariyo Mmedi akutchulidwira m’buku la Danieli koma osati m’zolemba za mbiri yakale?
13 M’kupita kwa nthaŵi, umboni wolunjikirapo wa kudziŵika kwenikweni kwa mfumuyi ungayambe kuoneka. Komabe, kusanenapo kanthu kwa ofukula m’mabwinja pankhani imeneyi sikuli maziko onenera kuti Dariyo anali “wopeka,” kapena onenera kuti buku lonse la Danieli ndi chinyengo. N’kwanzeru kuona zolemba za Danieli kukhala monga umboni woperekedwa ndi munthu woona ndi maso woulula zambiri kuposa zolemba za mbiri yakale zimene zidakalipobe.
ULAMULIRO WA YEHOYAKIMU
14. N’chifukwa chiyani tikunena kuti palibe kuphonyetsa pakati pa Danieli ndi Yeremiya potchula zaka za ulamuliro wa Mfumu Yehoyakimu?
14 Pa Danieli 1:1 timaŵerenga kuti: “Chaka chachitatu cha Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo adadza ku Yerusalemu, naumangira misasa ya nkhondo.” Otsutsawo akunena kuti lemba limeneli n’lolakwa chifukwa likuoneka kuti likutsutsana ndi Yeremiya, amene akuti chaka chachinayi cha Yehoyakimu chinali chaka choyamba cha Nebukadinezara. (Yeremiya 25:1; 46:2) Kodi Danieli anali kutsutsadi Yeremiya? Mwa kumva zoŵonjezera, nkhaniyi imamveketsedwa bwino mosavuta. Nthaŵi yoyamba Yehoyakimu atalongedwa ufumu ndi Farao Neko mu 628 B.C.E, ankangotsatira zonse zonena wolamulira wa Aiguptoyo. Zimenezi zinali pafupifupi zaka zitatu Nebukadinezara asanaloŵe m’malo mwa atate wake pampando wachifumu wa Babulo, mu 624 B.C.E. Posakhalitsa (mu 620 B.C.E.), Nebukadinezara anaukira ndi kugonjetsa Yuda, naika Yehoyakimu kukhala mfumu yaing’ono yolamulira pansi pa Babulo. (2 Mafumu 23:34; 24:1) Kwa Myuda wokhala m’Babulo, “chaka chachitatu” cha Yehoyakimu chikanakhalanso chaka chachitatu cha ufumu wake waung’onowo kwa Babulo. Danieli analemba zinthuzo akuziona motero. Komabe, Yeremiya analemba malinga n’kuona kwa Ayuda okhala ku Yerusalemu komweko. Choncho anati ulamuliro wa Yehoyakimu unayamba pamene Farao Neko anam’longa ufumu.
15. N’chifukwa chiyani kuli kopanda maziko olimba kutsutsa zaka zotchulidwa pa Danieli 1:1?
15 Kunena zoona, kusiyana konenedwa kumeneku kumangolimbitsa umboni wakuti Danieli analembera buku lakelo ku Babulo ali pakati pa akaidi achiyuda. Komanso pali kuphonya kwina kwakukulu pamfundo imeneyi yotsutsa buku la Danieli. Kumbukirani kuti n’kwachionekere kuti wolemba buku la Danieli analinso ndi buku la Yeremiya ndipo analigwiritsa ntchito. (Danieli 9:2) Ngati wolemba buku la Danieli analidi wopeka wochenjera, monga momwe otsutsawo amanenera, kodi iye daladala akanalemba zotsutsana ndi buku lodalirika chotero la Yeremiya—ndipo m’vesi loyambirira lenilenilo la buku lake? Sakanayerekeza n’komwe!
MAUMBONI OSONYEZA ZOONA ZENIZENI
16, 17. Kodi umboni wa zofukula m’mabwinja wachirikiza motani zolembedwa m’buku la Danieli ponena za (a) Kuimika fano kwa Nebukadinezara loti anthu onse alilambire? (b) Kudzitukumula kwa Nebukadinezara ponena za ntchito zake zomanga m’Babulo?
16 Tiyeni tsopano tichotse maganizo athu ku maumboni otsutsa tione maumboni ochirikiza. Taganizirani maumboni ena m’buku la Danieli osonyeza kuti wolemba wake ndi munthu amene anali kuona zochitika za m’nthaŵi imene anali kulemba.
17 Kudziŵa kwa Danieli zinthu zobisika za m’Babulo wakaleyo kuli umboni wovuta kuutsutsa wakuti zolemba zakezo zilidi zoona. Mwachitsanzo, Danieli 3:1-6 amanena kuti Nebukadinezara anaimika fano lalikulu loti anthu onse alilambire. Ofukula zam’mabwinja apeza umboni wina wakuti mfumu imeneyi inayesetsa kuphunzitsa anthu ake kudzipereka kwambiri m’machitachita ochirikiza mtundu wawo ndi chipembedzo. Ndiponso, Danieli akulemba za mzimu wodzitukumula wa Nebukadinezara chifukwa cha ntchito zake zomanga zambiri. (Danieli 4:30) Kusiyana ndi kale, masiku ano akatswiri ofukula zam’mabwinja atsimikizira kuti Nebukadinezara ndiyedi anachita ntchito yomanga yaikulu yochitidwa m’Babulo. Ponena za kudzitukumula—unalidi moyo wake, mpaka anachita kulemba dzina lake pa njerwa zomangira zenizenizo! Otsutsa Danieli sangafotokoze mmene wopeka amene akum’ganizirayo wa m’nthaŵi za Amakabeo (167-63 B.C.E.) akanadziŵira za ntchito zomanga zimenezo—patapita zaka pafupifupi mazana anayi chichitikire ntchitozo, komanso kale kwambiri akatswiri ofukula zam’mabwinja asanaziunike.
18. Kodi nkhani ya Danieli yosonyeza kusiyana kwa chilango pansi pa ulamuliro wa Babulo ndi wa Perisiya kumasonyeza motani kulondola kwake kwa nkhaniyo?
18 Buku la Danieli limavumbulanso kusiyana kwina kwakukulu pakati pa malamulo a Babulo ndi a Amedi ndi Aperisiya. Mwachitsanzo, pansi pa malamulo a Babulo anzake a Danieli atatu aja anaponyedwa m’ng’anjo ya moto chifukwa chokana kumvera lamulo la mfumu. Patapita zaka makumi angapo, Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango chifukwa chokana kumvera lamulo la Perisiya limene linatsutsana ndi chikumbumtima chake. (Danieli 3:6; 6:7-9) Ena ayesa kutsutsa nkhani ya ng’anjo ya motoyo akumati ndi nthano chabe, koma akatswiri ofukula zam’mabwinja apeza kalata yeniyeni yochokera ku Babulo wakaleyo imene ikutchula bwino lomwe mtundu wa chilango chimenecho. Komabe, kwa Amedi ndi Aperisiya, moto unali chinthu chopatulika. Choncho anagwiritsa ntchito mitundu ina ya chilango. N’chifukwa chake sitiyenera kudabwa poŵerenga za dzenje la mikango.
19. Kodi buku la Danieli likusonyeza bwino lomwe kusiyana kotani pakati pa malamulo a Babulo ndi a Medi ndi Perisiya?
19 Pakuonekanso kusiyana kwina. Danieli akusonyeza kuti Nebukadinezara pa iye yekha ankatha kukhazikitsa malamulo ndi kuwasintha nthaŵi ina iliyonse. Dariyo sankatha kuchita chilichonse kuti asinthe “malamulo a Amedi ndi Aperisiya”—angakhale amene anawakhazikitsa iye mwini! (Danieli 2:5, 6, 24, 46-49; 3:10, 11, 29; 6:12-16) Wolemba mbiri yakale John C. Whitcomb analemba kuti: “Mbiri yakale imaikira umboni za kusiyana kumeneku pakati pa Babulo, kumene lamulo linali pansi pa mfumu, ndi Amedi ndi Aperisiya, kumene mfumu inali pansi pa lamulo.”
20. Kodi Danieli akufotokoza zinthu zotani ponena za madyerero a Belisazara zimene zikusonyeza kuti iye amadziŵa bwino lomwe miyambo ya Ababulo?
20 Nkhani ya madyerero adzaoneni a Belisazara, yolembedwa m’Danieli chaputala 5, imaunika zambiri. Mwachionekere, phwandolo linayamba ndi kudya pang’onopang’ono koma ndi kumwa kwambiri, chifukwa vinyo akutchulidwa kangapo ndithu. (Danieli 5:1, 2, 4) Ndipo zithunzi zozokota za maphwando ofananawo zimasonyeza kuti vinyo yekha ndiye ankamwedwapo. Pamenepa, n’kwachionekere kuti vinyo anali wofunika kwambiri pamaphwando ngati amenewo. Danieli akutchulanso kuti akazi analipo pamadyereropo—akazi aang’ono a mfumu komanso akazi ake apambali. (Danieli 5:3, 23) Zofukulidwa m’mabwinja zimachirikiza mwambo wa Ababulo umenewo. Mchitidwe woti akazi azikhala limodzi ndi amuna pamaphwando unali wosaloleka kwa Ayuda ndi Agiriki m’nthaŵi ya Amakabeo. Mwina ndicho chifukwa chake mabaibulo achigiriki oyambirira otchedwa Septuagint samawatchula akaziwo m’buku la Danieli.c Komabe, wopeka buku la Danieli yemwe akum’ganizirayo akanakhala pakati pa anthu amodzimodziwo otengera chikhalidwe cha Ahelene (Agiriki), ndipo mwinanso m’nyengo imodzimodziyo, mmene Septuagint inalembedwa!
21. Kodi chifukwa chomveka n’chotani chimene chinapangitsa Danieli kudziŵa kwambiri za nthaŵi ndi miyambo ya Ababulo pamene Ayuda anali mu ukaidi?
21 Ponena za zinthuzo, pakuoneka kukhala posatheka kuti Britannica ingafotokoze wolemba buku la Danieli monga wokhala ndi chidziŵitso “chopereŵera zedi ndi chosalondola” ponena za nthaŵi ya ukaidi imeneyo. Ndi motani mmene wopeka nkhani aliyense wokhalako pambuyo pa zaka mazana ambiri akanadziŵira bwino choncho miyambo ya Ababulo ndi Aperisiya? Kumbukiraninso kuti maufumu onse aŵiriwo anali atatha kalekale zisanafike zaka za zana lachiŵiri B.C.E. Mwachidziŵikire, panthaŵiyo panalibe akatswiri ofukula zam’mabwinja; komanso Ayuda apanthaŵiyo sanadzionetsere kukhala odziŵa za zikhalidwe za mitundu ina ndi mbiri zawo. Kokha Danieli mneneriyo, mboni yoona ndi maso ya nthaŵi ndi zochitika zimene anazifotokoza, ndiye akanalemba buku la m’Baibulolo lotchedwa ndi dzina lake.
KODI MAUMBONI AKUNJA AMATSIMIKIZIRA KUTI BUKU LA DANIELI N’LOPEKA?
22. Kodi otsutsawo amanenanji za malo a buku la Danieli m’mabuku ovomerezeka a Malemba Achihebri?
22 Umodzi mwa maumboni ofala kwambiri ogwiritsidwa ntchito potsutsa buku la Danieli ndiwo malo amene linaikidwapo m’Malemba Achihebri ovomerezeka. Arabi akale anaika mabuku a Malemba Achihebri m’magulu atatu: Lamulo, Aneneri, ndi Zolemba Zina. Sanaike Danieli pakati pa Aneneri, koma pakati pa Zolemba Zina. Otsutsawo akuti, zimenezi zikutanthauza kuti bukulo silinkadziŵika panthaŵi imene amasonkhanitsa mabuku ena a aneneri. Akuganiza kuti linaikidwa pakati pa Zolemba Zina chifukwa zimenezo zinasonkhanitsidwa pambuyo pake.
23. Kodi Ayuda akale analiona motani buku la Danieli, ndipo timadziŵa motani zimenezo?
23 Komabe, si ofufuza Baibulo onse amene amakhulupirira kuti arabi akalewo anagaŵa Baibulo mwa mtundu wolekanitsiratu umenewo kapena kuti buku la Danieli linachotsedwapo pa mabuku a Aneneri. Koma ngakhale ngati arabiwo anandandalikadi Danieli pakati pa Zolemba Zina, kodi chimenecho chikanatsimikizira kuti bukulo linadzalembedwa nthaŵi ina pambuyo pake? Iyayi. Akatswiri ena odalirika azamaphunziro apereka zifukwa zingapo zosonyeza chimene arabiwo angakhale atachotsera buku la Danieli pakati pa mabuku a Aneneri. Mwachitsanzo, mwina anatero chifukwa bukulo linawakhumudwitsa iwo kapena chifukwa anaona Danieli kukhala wosiyana ndi aneneri ena pokhala ndi udindo m’dziko lachilendo. Mulimonse mmene zingakhalire, nkhani yaikulu ndi iyi: Ayuda akale ankalilemekeza kwambiri buku la Danieli ndipo ankaliona kukhala limodzi la mabuku ovomerezekadi. Komanso, umboniwo ukusonyeza kuti mabuku ovomerezeka a Malemba Achihebri anali atakwanira kalekale zisanafike zaka za zana lachiŵiri B.C.E. Mabuku ena owonjezera pambuyo pake sanaloledwe konse, kuphatikizapo mabuku ena olembedwa m’zaka za zana lachiŵiri B.C.E.
24. Kodi buku lowonjezera lotchedwa Mphunzitsi wa Mpingo lagwiritsidwa ntchito motani kutsutsira buku la Danieli, ndipo n’chiyani chikusonyeza kuti kalingaliridwe kameneko n’kolakwa?
24 Chodabwitsa n’chakuti, limodzi la mabuku okanidwa amenewo lagwiritsidwa ntchito kutsutsira buku la Danieli. Buku lowonjezera lotchedwa Mphunzitsi wa Mpingo, lolembedwa ndi Jesus Ben Sirach, mwachionekere linalembedwa pafupifupi mu 180 B.C.E. Otsutsa amakonda kunena kuti Danieli palibepo pa mndandanda wautali wopezeka m’bukulo wa anthu olungama. Amalingalira kuti Danieli sanali kudziŵika panthaŵiyo. Akatswiri azamaphunziro ambiri amakhulupirira maganizo ameneŵa. Koma talingalirani izi: Mndandanda umodzimodziwo ulibenso Ezara ndi Moredekai (ngwazi zenizeni m’maso mwa Ayuda atabwerako ku ukaidi ku Babulo), Yehosafati Mfumu yabwinoyo, komanso Yobu, mwamuna wolungamayo; pa oweruza onse, mndandandawo umangotchulapo Samueli yekha basi.d Kodi tingakhulupiriredi kuti amuna onsewo n’ngopeka, kokha chifukwa sakupezeka pamndandandawo, umenenso suphatikizapo onse, komanso wopezeka m’limodzi la mabuku osavomerezeka? Lingaliro limenelo n’losagwira m’pang’ono pomwe.
UMBONI WAKUNJA WOCHIRIKIZA BUKU LA DANIELI
25. (a) Kodi Josephus anaikira motani umboni wakuti zolembedwa m’buku la Danieli n’zoona? (b) Nanga m’motani mmene zolemba za Josephus zonena za Alesandro Wamkulu komanso zolembedwa m’buku la Danieli zikugwirizanira ndi mbiri yakale yodziŵika? (Onani mawu am’tsinde achiŵiri.) (c) Kodi umboni wa chilankhulo umachirikiza motani buku la Danieli? (Onani tsamba 26.)
25 Tiyeni titembenukirenso ku umboni wochirikiza. Kwanenedwa kuti palibe buku lina lililonse la Malemba Achihebri limene lili ndi umboni wokwanira kuposa buku la Danieli. Nachi chitsanzo: Josephus, Myuda wolemba mbiri yakale wotchukayo anaikira umboni wakuti bukulo n’loonadi. Iye ananena kuti Alesandro Wamkulu, m’nkhondo yake yomenyana ndi Perisiya m’zaka za zana lachinayi B.C.E., anabwera ku Yerusalemu, kumene ansembe anam’sonyeza kope la buku la Danieli. Alesandro mwiniyo ananena kuti mawu a ulosi wa Danieli amene anasonyezedwa kwa iye amanena za nkhondo yake youkira Perisiya.e Zimenezi ziyenera kukhala zitachitika pafupifupi zaka zana limodzi ndi theka “kupekako” kusanachitike malinga n’kunena kwa otsutsawo. N’zoona kuti otsutsawo am’tsutsanso Josephus ponena za ndime imeneyi. Ndipo am’tsutsanso ponena kuti maulosi ena a m’buku la Danieli anakwaniritsidwa. Komabe, malinga n’kunena kwa wolemba mbiri yakale Joseph D. Wilson, “[Josephus] mwinamwake anadziŵa zochuluka pankhaniyo kuposa ofufuza Baibulo onse padziko lapansi.”
26. Kodi mipukutu yotchedwa Dead Sea Scrolls yaonetsa motani kuti buku la Danieli n’loona?
26 Umboni wowonjezera wotsimikiza kuti buku la Danieli n’loonadi unaoneka pamene mipukutu yotchedwa Dead Sea Scrolls inapezeka m’mapanga a ku Qumran, ku Israyeli. Chodabwitsa n’chakuti zochuluka mwa zopezedwa mu 1952 zinali mipukutu ndi zidutswa za buku la Danieli. Zakale kwambiri zapezeka kukhala zakumapeto kwa zaka za zana lachiŵiri B.C.E. Choncho, ngakhale kale limenelo, buku la Danieli linali lodziŵika ndi lodaliridwa ndi anthu ambiri. The Zondervan Pictorial Encyclopedia of the Bible imanena kuti: “Mfundo yonena kuti buku la Danieli linalembedwa m’nyengo ya Amakabeo iyenera kusiyidwa tsopano, chifukwa chakuti sipakanakhala mpata wokwanira pakati pa kulembedwa kwa buku la Danieli ndi kuonekera kwa makope ake m’laibulale ya chipembedzo cha mpatuko cha Amakabeo.”
27. Kodi umboni wakale koposa n’ngwotani wakuti Danieli analidi munthu weniweni wodziŵika bwino m’nthaŵi ya ukaidi ku Babulo?
27 Komabe, uliponso umboni wina wakale kuposa pamenepo komanso wodalirika kwambiri wotsimikiza kuti buku la Danieli n’loona. Munthu wina wokhalako n’nthaŵi ya Danieli anali mneneri Ezekieli. Iyenso anatumikira monga mneneri m’nthaŵi ya ukaidi ku Babulo. Nthaŵi zambiri, buku la Ezekieli limatchula Danieli ndi dzina. (Ezekieli 14:14, 20; 28:3) Mavesi ameneŵa amasonyeza kuti ngakhale m’nthaŵi ya moyo wake, m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., Danieli anali wodziŵika kale monga mwamuna wachilungamo ndi wanzeru, woyenera kum’tchula limodzi ndi ena oopa Mulungu monga Nowa ndi Yobu.
MBONI YAIKULU KOPOSA
28, 29. (a) Kodi umboni wokhutiritsa koposa wina uliwonse ndi uti, wosonyeza kuti buku la Danieli lilidi loona? (b) Nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuvomereza umboni wa Yesu?
28 Chomalizira, tiyeni tione mboni yaikulu yoposa zina zonse yotsimikizira kuti buku la Danieli n’loonadi—ameneyo si wina aliyense koma Yesu Kristu. Pofotokoza za masiku otsiriza, Yesu anatchula “Mneneri Danieli” komanso umodzi mwa maulosi a Danieli.—Mateyu 24:15; Danieli 11:31; 12:11.
29 Tsopano ngati maganizo a ofufuza Baibulowo onena za m’nyengo ya Amakabeo anali oona, ndiye kuti chimodzi mwa zinthu ziŵiri chiyenera kukhala choona. Ndiye kuti Yesunso anangopusitsidwa ndi chinyengo chimenechi, apo ayi, ndiye kuti iye sananene konse mawu akewo amene Mateyu waagwira. Zonse ziŵirizi n’zonama. Ngati tingalephere kudalira Uthenga Wabwino wa Mateyu, zingatheke bwanji kuti tidalire mbali zina za Baibulo? Ngati tichotsa mawu amenewo, kodi si zoona kuti tikhoza kuchotsanso mawu ena m’Malemba Oyera? Mtumwi Paulo analemba kuti: ‘Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, . . . chikonzero.’ (2 Timoteo 3:16) Choncho, ngati Danieli anali wopeka, ndiye kuti Paulonso anali wotero! Kodi n’kutheka kuti Yesu anapusitsidwa? Kutalitali. Iye anali wamoyo kumwamba pamene buku la Danieli linali kulembedwa. Ndi iko komwe, Yesu anati: “Asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.” (Yohane 8:58) Pa anthu onse amene akhalapo ndi moyo, kwa Yesu kokha ndiko koyenera kuti tifunsire za kuona kwake kwa buku la Danieli. Koma sitifunikira kuchita kufunsa. Monga taona kale, umboni wake uli womvekera bwino lomwe.
30. Kodi Yesu anaperekanso umboni wina wotani woonetsa kuti buku la Danieli n’loonadi?
30 Yesu anasonyezanso kuona kwake kwa buku la Danieli panthaŵi imene anali kubatizidwa. Pamenepo iye anakhala Mesiya, akumakwaniritsa ulosi wa m’buku la Danieli wonena za masabata 69 a zaka. (Danieli 9:25, 26; onani Mutu 11 wa buku lino.) Ngakhale akanakhala oona maganizo akuti bukulo linalembedwa pambuyo pake, wolemba buku la Danieli anadziŵabe zam’tsogolo zaka pafupifupi 200 pasadakhale. Ndithudi, Mulungu sakanauzira munthu wonyenga kuti alosere maulosi oona m’dzina la chinyengo. Sakanatero konse, ndipo umboni wa Yesu uli wolandirika ndi mtima wonse kwa anthu a Mulungu okhulupirika. Ngati akatswiri onse, pamodzi ndi ofufuza onse padziko lapansi, akanati agundanitse mitu kuti atsutse buku la Danieli, umboni wa Yesu utha kuwatsutsabe onsewo, chifukwa iyeyo ndiye “mboni yokhulupirika ndi yoona.”—Chivumbulutso 3:14.
31. N’chifukwa chiyani ofufuza Baibulo ambiri sakukhutirabe kuti buku la Danieli n’loona?
31 Ngakhale umboni umenewu suli wokwanira kwa otsutsa Baibulo ambiri. Munthu atapenda nkhani imeneyi mofatsa bwino, sangachitire mwina koma kudabwa ngati pangafunikirenso umboni wina uliwonse woti uwakhutiritse. Polofesa wina pa Yunivesite ya Oxford analemba kuti: “Kupereka mayankho kokha sikukhutiritsa otsutsa, malinga ngati akhalapobe maganizo akuti ‘kulibe ulosi wouziridwa kuchokera kumwamba.’” Choncho maganizo awowo ndiwo akuwachititsa khungu. Koma zimenezo n’kusankha kwawo—ndi kutayikidwa kwawonso.
32. Kodi tidzadziŵa zotani popitiriza kuphunzira buku la Danieli?
32 Nanga bwanji za inuyo? Ngati mukuona kuti palibe chifukwa chenicheni chokayikira kuti buku la Danieli n’loona, ndiye kuti ndinu wokonzeka kuyenda paulendo wochititsa chidwi wotumba zinthu. Mudzaona kusangalatsa kwa nkhani zosimbidwa m’buku la Danieli, komanso kukopa maganizo kwa maulosi ake. Chofunika koposa, mudzapeza kuti chikhulupiriro chanu chizimka nachilimbirapo pamene muŵerenga mutu uliwonse. Kunena zoona, simudzagwiritsidwa mwala m’pang’ono ponse pomvetsera mosamalitsa ulosi wa Danieli!
[Mawu a M’munsi]
a Otsutsa ena akuyesa kufeŵetsa chinenezo chili pamwambacho chakuti bukulo n’lachinyengo mwa kunena kuti amene analemba bukulo ndi mwiniwake weniweni koma kuti anangosankha kugwiritsa ntchito dzina lopeka lakuti Danieli, monga mmene mabuku ena akale osavomerezeka analembedwera mogwiritsa ntchito mayina opekanso. Komabe, katswiri wina wofufuza Baibulo Ferdinand Hitzig ananenetsa kuti: “Ngati buku la Danieli linalembedwa ndi [munthu] wina, ikhala nkhani yosiyana. Likhala buku lachinyengo, ndipo cholinga chake chinali kugwira m’maso oliŵerenga a panthaŵi yomweyo, ngakhale kuti cholinga chake chinali chowapindulitsa.”
b Nabonidasi anali kwina pamene Babulo amagwa. Choncho, n’koyenera kunena kuti Belisazara anali mfumu panthaŵiyo. Akatswiri ofufuzawo akutsutsabe kuti zolemba za mbiri yakale sizikutchula Belisazara kukhala mfumu. Komabe, umboni wa nkhani zamakedzana umasonyeza kuti ngakhale gavana nthaŵi zina amatchedwa mfumu ndi anthu m’masiku amenewo.
c C. F. Keil, katswiri wa zamaphunziro komanso Mhebri analemba za Danieli 5:3 kuti: “LXX. panopo, komanso pa vesi 23, siitchula za akaziwo, malinga ndi mwambo wa Amakedoniya, Agiriki, ndi Aroma.”
d Mosiyana ndi zimenezo, mndandanda wouziridwa wa mtumwi Paulo wopezeka mu Ahebri chaputala 11, wotchula amuna ndi akazi okhulupirika, ukuoneka kuti umakhudza zochitika zolembedwa m’buku la Danieli. (Danieli 6:16-24; Ahebri 11:32, 33) Komabe, ngakhale mndandanda wa mtumwiwo sutchula onse. Alipo ambiri amene sanatchulidwe pamndandandawo, kuphatikizapo Yesaya, Yeremiya, ndi Ezekieli, koma zimenezo sizili umboni wakuti anthuwo sanakhaleko.
e Olemba mbiri ena aona kuti chimenecho chingakhale chifukwa chake Alesandro anali wokoma mtima kwambiri kwa Ayuda, amenenso anali paubwenzi kwa nthaŵi yaitali ndi Aperisiya. Panthaŵiyo, Alesandro anali pankhondo zowononga mabwenzi onse a Perisiya.
KODI MWAZINDIKIRA CHIYANI?
• Kodi buku la Danieli laimbidwa mlandu wanji?
• N’chifukwa chiyani zonena za anthu otsutsa buku la Danieli zilibe maziko olimba?
• Ndi umboni wotani umene umachirikiza kuti zolembedwa m’buku la Danieli n’zoona?
• Kodi ndi umboni wokhutiritsa koposa uti wakuti buku la Danieli n’loonadi?
[Bokosi patsamba 26]
Mfundo ya Chinenero
BUKU la Danieli linatha kulembedwa pafupifupi mu 536 B.C.E. Linalembedwa m’Chihebri ndi Chialamu, kuphatikizaponso mawu oŵerengeka achigiriki ndi achiperisiya. Kulemba kophatikiza zinenero koteroko n’kwachilendo m’zolemba zina, koma osati m’Malemba. Ngakhalenso buku la Ezara linalembedwa m’Chihebri ndi m’Chialamu. Komabe, otsutsa ena akuumirira kunena kuti wolemba Danieli anagwiritsa ntchito zinenerozo m’njira yosonyeza kuti anali kulemba panthaŵi inayake pambuyo pa 536 B.C.E. Wotsutsa wina, ambiri am’gwira mawu kukhala akunena kuti kugwiritsa ntchito mawu achigiriki m’buku la Danieli kumatsimikizira kuti linalembedwa m’nthaŵi ina pambuyo pake. Iyeyo ananena kuti Chihebri chimachirikiza mfundoyo ndipo Chialamu chimalola deti lapambuyo pake limenelo—ngakhale m’zaka za zana lachiŵiri B.C.E.
Komabe, si akatswiri azinenero onse amene akuvomereza. Ena anena kuti Chihebri cha m’buku la Danieli n’chofanana ndi chija cha m’mabuku a Ezekieli ndi Ezara koma n’chosiyana ndi chija chopezeka m’mabuku owonjezera monga lotchedwa Mphunzitsi wa Mpingo. Ponena za Chialamu m’buku la Danieli, talingalirani za zolembedwa ziŵiri zopezeka pakati pa mipukutu yotchedwa Dead Sea Scrolls. Zimenezonso zinalembedwa m’Chialamu ndipo zapezeka kukhala za m’zaka za zana loyamba ndi lachiŵiri B.C.E.—osati kale kwambiri pambuyo pa nthaŵi imene amaiganizira kuti m’pamene buku la Danieli analipeka. Koma akatswiri amaphunziro azindikira kusiyana kwakukulu pakati pa Chialamu cha m’zolembedwa zimenezo ndi cha m’buku la Danieli. Choncho, ena akuganiza kuti buku la Danieli liyenera kukhala lakale zaka mazana angapo kuposa zimene otsutsawo amanena.
Nanga bwanji za mawu achigiriki “ovutitsawo” opezeka m’buku la Danieli? Ena mwa mawuwo apezeka kuti ndi achiperisiya, osatinso achigiriki! Mawu okha amene akuwaganizira kukhala achigiriki ndi mayina atatu okha a zipangizo zoimbira. Kodi kukhalapo kwa mawu atatu ameneŵa kukutsimikiziradi kuti Danieli analembedwa pambuyo pake? Ayi. Akatswiri ofukula m’mabwinja apeza kuti chikhalidwe cha Agiriki chinali champhamvu kwambiri kwa zaka mazana ambiri Girisi asanakhale ulamuliro wa dziko lonse lapansi. Ndiponso, ngati buku la Danieli linalembedwa m’kati mwa zaka za zana lachiŵiri B.C.E., pamene chikhalidwe cha Agiriki ndi chinenero chawo zinali zamphamvu kwambiri, kodi n’zoona kuti ilo likanakhala ndi mawu atatu okha achigiriki? Kutalitali. Likanakhala nawo ambiri. Choncho, umboni wa chinenero umachirikiza mfundo yakuti buku la Danieli n’loonadi.
[Chithunzi chachikulu patsamba 12]
[Zithunzi patsamba 20]
(Pamwamba) Cholembapochi chikunena za kudzitama kwa Nebukadinezara za ntchito zake zomanga
(Pansi) Cholembapo cha m’kachisi wa ku Babulo chimatchula Mfumu Nabonidasi ndi mwana wake Belisazara
[Chithunzi patsamba 21]
Malinga n’kunena kwa Mbiri ya Nabonidasi, asilikali a Koresi analoŵa m’Babulo chosamenya nkhondo
[Zithunzi patsamba 22]
(Kumanja) “Nkhani ya Vesi ya Nabonidasi” ikunena kuti Nabonidasi anaikiza ulamuliro wake m’manja mwa mwana wake woyamba
(Kumanzere) Zolemba zachibabulo zonena za kuukira Yuda kwa Nebukadinezara