Yehova Amafupa Chikhulupiriro ndi Kulimba Mtima
“Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa. M’ng’anjo yotentha ya moto, nadzatilanditsa m’dzanja lanu, mfumu.”—DANIELI 3:17.
1. Ndi phunziro lotani lomwe linawunikiridwa m’nkhani yapitayo, ndipo nchifukwa ninji kusanthulanso kwa zochitikazo kungakhale kopindulitsa?
YEHOVA MULUNGU, Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, waphunzitsa olamulira a dziko maphunziro ofunika kwambiri ponena za ukulu wake. M’nkhani yapitayo, tinawona mmene ichi chinali chowona m’zochitika zolembedwa mu mitu isanu ndi umodzi yoyambirira ya bukhu la Danieli. Zolembera zimodzimodzizi zingasanthulidwe tsopano kuwona chimene tingaphunzire kuchokera ku izo m’kusunga mawu owuziridwa a mtumwi Paulo: “Zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha Malembo tikhale ndi chiyembekezo.”—Aroma 15:4.
2, 3. Ndi ndani omwe anali pakati pa awo otengedwda ukapolo ndi Mfumu Nebukadinezara, ndipo ndi mapeto otani amene tingafikire kuchokera ku matanthauzo a maina awo?
2 Munali m’chaka cha 617 B.C.E., mkati mwa kulamulira kwachidule kwa Yehoyakini, mwana wa Mfumu Yehoyakimu, kuti Mfumu Nebukadinezara analamulira kuti achichepere abwino koposa ndi anzeru koposa Achiyuda abweretsedwe ku Babulo. Pakati pa awa panali Danieli, Hananiya, Misaeli, ndi Azariya.—Danieli 1:3, 4, 6.
3 Kuŵeruza mwa matanthauzo a maina awo, chiri chachidziŵikire kuti mosasamala kanthu za mikhalidwe yoipa yomwe inali m’Yuda pa nthaŵiyo, achichepere achihebri anayi amenewa anali ndi makolo owopa Mulungu. “Danieli” amatanthauza “Woŵeruza Wanga Ali Mulungu.” Dzina la Hananiya limatanthauza kuti “Yehova Wasonyeza Chiyanjo; Yehova Wakhala Wachisomo.” Dzina la Misaeli mothekera limatanthauza kuti “Ndani Afanana Ndi Mulungu?” kapena “Ndani amene ali ku mbali ya Mulungu?” Ndipo dzina la Azariya limatanthauza kuti “Yehova Wathandiza.” Mosakaikira maina awo enieniwo anali chida kwa iwo kukhala okhulupirika kwa Mulungu mmodzi wowona. M’malo mwa maina amenewa, Akasidi anawatcha Ahebri achichepere anayiwo kukhala Belisazara, Sadrake, Mesake, ndi Abedinego. Ndithudi, akumakhala akapolo ku mphamvu yachilendo, iwo analibe chosankha ponena za maina amene owagwirawo anagwiritsira ntchito m’kulozera kwa iwo.—Danieli 1:7.
Chikhulupiriro ndi Kulimba Mtima Ziikidwa ku Chiyeso
4. Ndi chiyani chomwe chikusonyeza kuti Yehova anafuna kuti anthu ake atenge mosamalitsa malamulo ake ponena za nyama zosadetsedwa ndi zodetsedwa?
4 Si kokha kuti makolo awo owopa Mulungu anapatsa Ahebri anayiwo chiyambi chabwino m’moyo mwa maina amene anawapatsa iwo koma iwo angakhalenso anawalela iwo mosamalitsa molingana ndi Chilamulo cha Mose, kuphatikizapo mbali zake za kadyedwe. Yehova Mulungu iyemwini analingalira izi kukhala zofunika koposa kotero kuti chinali pambuyo pa kundandalitsa zoletsa zambiri zofananazo pamene iye ananena kuti: “Mudzikhala oyera, pakuti ine ndine woyera.”—Levitiko 11:44, 45.
5. Ndimotani mmene kulera kwabwino kwa achichepere Achihebri anayi kunaikidwira ku chiyeso?
5 Kulera kwabwino kumeneku kwa achichepere Achihebri anayi amenewo mwamsanga kunaikidwa ku chiyeso. Tero motani? Chifukwa chakuti iwo “anaikiridwa gawo la chakudya cha mfumu tsiku ndi tsiku ndi la vinyo wakumwa iye.” (Danieli 1:5) Iwo anadziŵa kuti pakati pa zinthu zoletsedwa ndi Chilamulo cha Mose panali zakudya zonga ngati nkhumba, kalulu, oysters, ndi nkhunga. Ngakhale nyama zimene Chilamulo chinalola zinali zokaikiritsa m’mabwalo a Chibabulo, popeza kuti panalibe njira ya kudziŵira ngati izo zinakhetsedwa mwazi moyenerera. Pa mbali ya icho, nyama zoterozo zingakhale zinadetsedwa ndi miyambo yachikunja.—Levitiko 3:16, 17.
6. Ndimotani mmene Ahebri anayiwo anavomerezera ku chiyesocho?
6 Nchiyani chomwe Ahebri anayiwo akadachita? Timaŵerenga kuti Danieli, ndipo mosakaikira atatuwonsa, anatsimikizira mu mtima mwake kusadzidetsa iyemwini ndi chakudya choterocho. Chotero, “anafunsira” zomera m’nthaka m’malo mwa chakudya cha mfumu ndi madzi m’malo mwa vinyo wake. Nkhani ya chimene chimakoma siinalowe m’maganizo mwawo. Icho ndithudi chinatenga chikhulupiriro ndi kulimba mtima kuwumirira nkhani imeneyi. Chabwino, popeza kuti Yehova anali wokondweretsedwa mwa achichepere anayi amenewa, iye anawona ku icho kuti mkulu wa adindo anali wa chiyanjo kulinga kwa Danieli. Ngakhale kuli tero, mkulu ameneyu anali ndi mantha kuvomereza chifunsiro cha Danieli akumawopa chiyambukiro chimene chakudya choterocho chikakhala nacho pa umoyo wa Danieli. Chotero Danieli anafunsa kuti iwo avomerezedwe kuyesedwa ndi chakudya chimenechi kwa masiku khumi. Iye anali ndi chikhulupiriro champhamvu chakuti kumvera Lamulo la Mulungu sikukampatsa iye kokha chikumbumtima chabwino komanso kukatsimikizira kukhala kopindulitsa mwa umoyo. Monga chotulukapo cha kaimidwe kawo, Ahebri anayiwo mosakaikira anayenera kupirira kuseka kokulira.—Danieli 1:8-14; Yesaya 48:17, 18.
7. Ndimotani mmene achichepere Achihebri amenewo anafupidwira kaamba ka kaimidwe kawo kolimba mtima?
7 Chinatenga chikhulupiriro ndi kulimba mtima kwa Ahebri anayiwo kupanga nkhani ya chakudya chawo. Koma iwo anafupidwa motani nanga kaamba ka kuchita chimenecho, popeza kuti pamapeto pa masiku khumi, iwo anawoneka onenepa ndi a umoyo kuposa wina aliyense wa enawo! Yehova anali kuwapatsa iwo chidziŵitso, luntha, ndi nzeru, kotero kutu pamene iwo anawonekera pamaso a mfumu pamapeto pa nyengo yawo ya kuphunzitsidwa ya zaka zitatu, iye anawapeza iwo “akuposa nthaŵi khumi alembi ndi openda onse mu ufumu wake wonse.”—Danieli 1:20.
8. Ndi phunziro lotani limene lilimo kaamba ka atumiki a Yehova lerolino?
8 Pali phunziro mu ichi kaamba ka atumiki onse a Yehova Mulungu lerolino. Ahebri achichepre amenewo angakhale analingalira kuti ziletso za chakudya za Chilamulo cha Mose sizinali zofunika koposa, ndithudi osati zitayerekezedwa ndi Malamulo Khumi kapena malamulo onena za nsembe kapena mapwando a pa chaka. Koma ayi, Ahebri okhulupirikawo anali odera nkhaŵa ndi kukhala ndi moyo ku mbali zonse za Lamulo la Mulungu. Ichi chimaitanira ku maganizo prinsipulo limene Yesu ananena, monga mmene lalembedwera pa Luka 16:10: “Iye amene akhulupirika m’chaching’onong’ono alinso wokhulupirika m’chachikulu, ndipo iye amene sali wosalungama m’chaching’onong’ono alinso wosalungama m’chachikulu.”—Yerekezani ndi Mateyu 23:23.
9. Ndimotani mmene Mboni zina zasonyezera kulimba mtima kofananako lerolino?
9 Nthaŵi zambiri Mboni za Yehova zimasonyeza chikhulupiriro chofananacho ndi kulimba mtima, monga ngati pamene chibwera ku kufunsa owalemba ntchito awo kaamba ka nthaŵi yopumula kukapezeka pa msonkhano wachigawo. Ndipo kwa nthaŵi ndi nthaŵi, kupatulidwa kumapangidwa m’nkhani yawo. Mboni zofuna kulowa m’mathayo a upainiya kapena kukhala apainiya othandizira zalondola chikhumbo chawo kaamba ka ntchito ya pa kanthaŵi ndipo mobwerezabwereza zapatsidwa mwaŵi umenewu.
10. Ndi phunziro lotani limene liripo kaamba ka makolo omwe ali Mboni mu zonsezi?
10 Ndi phunziro labwino chotani nanga limene makolo owopa Mulungu lerolino angaphunzire kuchokera ku kuphunzitsa kowonekera kwa achichepere anayi Achihebriwo! Pamene makolo Achikristu ndithudi akhala ndi zikondwerero zauzimu za ana awo pamtima, iwo adzaika izi choyamba m’miyoyo yawo yeniyeniyo, m’kugwirizana ndi Mateyu 6:33. Kenaka iwo angayembekezere kuti ana awo adzakhala okhoza kutsutsa ziyeso ndi zididikizo za anzawo a msinkhu wofanana ndi aphunzitsi a ku sukulu osonkhezera kukondwerera masiku a kubadwa kapena matchuthi kapena kuswa maprinsipulo a Malemba m’njira zina. Makolo owopa Mulungu amenewa mwakutero amatsimikizira Miyambo 22:6 kukhala yowona.
Mopanda Mantha Kumasulira Maloto a Nebukadinezara
11. Ndimotani mmene ife lerolino tingatsanzirire zitsanzo za Danieli ndi mabwenzi ake atatu?
11 Mutu wachiŵiri wa Danieli umatipatsa ife chitsanzo china cha chikhulupiriro ndi kulimba mtima. Pamene Danieli anamva za lamulo la mfumu la kuwononga anthu anzeru onse a ku Babulo chifukwa chakuti sanakhoze kumuuza iye loto lake ndi tanthauzo lake, kodi Danieli ndi mabwenzi ake atatuwo anakhala odera nkhaŵa? Motsimikizirika ayi! M’malomwake, ndi chikhulupiriro chokulira chakuti Yehova akampatsa iye chidziŵitso chimene mfumu inachifuna, Danieli anawonekera pamaso pa mfumu imeneyo ndi kufunsa kaamba ka nthaŵi ya kupereka yankho. Chifunsiro chimenechi chinaperekedwa. Kenaka Danieli ndi mabwenzi ake atatu anaipanga nkhaniyo kukhala mutu wa pemphero lofunitsitsa. Yehova anafupa chikhulupiriro chawo mwa kupereka chidziŵitso chofunidwacho. Pamenepo, Danieli anapereka pemphero la mtima wonse la chiyamiko kwa Yehova. (Danieli 2:23) Ndipo kumasulira loto kwa Danieli kwa mutu 4 kunafunikira kuti iye awuze Mfumu Nebukadinezara kuti iye akathera zaka zisanu ndi ziŵiri akukhala monga nyama ndi nyama za kuthengo. Ichi chinaitanira kaamba ka chikhulupiriro ndi kulimba mtima konga kumene anthu a Mulungu ayenera kusonyeza lerolino m’kulengeza uthenga wamphamvu wa kubwezera Kwake molimbana ndi dziko la Satana.
‘Kulaka Mphamvu ya Moto’
12, 13. Mutu 3 wa Danieli umalongosola chiyeso chotani chimene chinayang’anizana ndi mabwenzi atatu a Danieli?
12 Danieli mutu 3 umapereka chimodzi cha zochitika zowonekera kwambiri za cholembera cha Baibulo zosonyeza mmene Yehova anafupira chikhulupiriro ndi kulimba mtima kodabwitsa kumbali ya atumiki Achihebri atatuwo. Tangolingalirani chochitikacho. Nduna zazikulu zonse za Babulo zasonkhanitsidwa pa chigwa cha dura. Pamaso pawo paimirira chifano cha msinkhu wa mamita 27 ndi thunthu la mamita 2.7. Kuti asangalatse malingaliro awo, mfumuyo yapangitsa gulu loyimba kukhalapo. Pa kumvekera kwa kuyimba, awo osonkhanawo akayenera ‘kugwa pansi ndi kulambira chifano cha golidi chimene mfumu Nebukadinezara anachiimika. Ndipo yense amene sakagwa pansi ndi kulambira pa nthaŵi yomweyo adzaponyedwa m’nganjo yotentha ndi moto’—Danieli 3:5, 6.
13 Palibe kukaikira ponena za icho: Kukana kumvera lamulo limenelo kunaitanira kaamba ka chikhulupiriro chachikulu ndi kulimba mtima. Koma kukhala ‘okhulupirika m’chaching’ono’ kunawakonzekeretsa iwo kukhala ‘okhulupirika m’chachikulu.’ Chenicheni chakuti kaimidwe kawo kakakhoza kuika Ayuda ena m’ngozi sichinalingaliridwe. Iwo sakagwada pansi ndi kulambira chifanocho. Kukana kwawo kosabisika kunawonedwa ndi ena oyanjana nawo awo a nsanje, omwe sanataye nthaŵi m’kusimba ichi kwa mfumu.
14. Ndimotani mmene Nebukadinezara anavomerezera ku kukana kwawo kugwada, ndipo ndimotani mmene iwo anayankhira lamulo lake lamphamvu?
14 Mu “mkwiyo ndi ukali,” Nebukadinezara analamulira kuti Ahebri atatuwo abweretsedwe kwa iye. Funso lake, “Kodi mutero dala?” limasonyeza kuti chinali chosamvetsetseka kwa iye kuti iwo angakane kugwada ndi kulambira chifano cha golidicho. Iye anali wofunitsitsa kukwapatsa iwo mwaŵi wina, koma ngati iwo akakanabe, iwo akayenera kuponyedwa m’ng’anjo yotentha ndi moto. “Ndipo,” inatero mfumu yodzikweza ya Babulo, “mulungu amene adzakulanditsani m’manja mwanga ndani?” Ndi kulimba mtima kowona ndi chikhulupiriro mwa Yehova, Ahebri atatuwo mwaulemu anayankha mfumuyo: “Sikufunikira kuti tikuyankheni pa mlandu uwu. Mulungu wathu amene timtumikira akhoza kutilanditsa m’ng’anjo ya moto . . . , Mfumu, koma akapanda kutero, dziŵani, mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu, kapena kulambira fano la golidi mudaliimikalo.”—Danieli 3:13-18.
15. Ndi kachitidwe kotani kamene Nebukadinezara anatenga?
15 Ngati Nebukadinezara anali atakwiya kumbuyoko, iye ayenera kukhala anali waukali kwenikweni tsopano, popeza kuti timaŵerenga kuti “mawonekedwe a nkhope yake anasandulikira” Ahebri atatuwo. (Danieli 3:19) Losonyeza ukali wake linali lamulo lake la kusonkhezera ng’anjo nthaŵi zisanu ndi ziŵiri kuposa nthaŵi zonse. Kenaka amuna ena amphamvu m’gulu lake lankhondo anatenga Ahebri atatuwo ndi kuwaponya iwo m’ng’anjo ya motoyo. Malawi anali akulu kwenikweni kotero kuti anapha amuna amene anachita ntchitoyi.
16. Ndimotani mmene chikhulupiriro cha Ahebri atatu chinafupidwira?
16 Koma ndi choziziwitsa chotani nanga chimene mfumuyo inalandira pamene anawona osati kokha amuna atatu koma anayi akuyendayenda pakati pa motowo athunthu osavulazidwa! Pamene mfumuyo inaitana Ahebri atatuwo kuti atuluke, iye anapeza kuti panalibe ngakhale tsitsi la pamutu pawo lomwe linawawuka ndipo kununkha kwa utsi sikunali ngakhale pa zovala zawo. Ndi mokulira chotani nanga mmene Yehova anafupira chikhulupiriro chawo ndi kulimba mtima! Mosakaikira chitsanzo chawo chinali chimodzi chimene mtumwi Paulo anali nacho m’maganizo pamene anandandalitsa pakati pa mtambo waukulu wa mboni zomwe “zinalaka mphamvu ya moto.” (Ahebri 11:34) Ndi chitsanzo chabwino chotani nanga chimene iwo akhala kaamba ka atumiki onse a Yehova kuyambira pa nthawiyo!
17. Ndi zitsanzo zofananako zabwino zotani zimene tiri nazo lerolino?
17 Lerolino, atumiki a Yehova sakuyang’anizidwa ndi chiwopsyezo cha ng’anjo yeniyeni ya moto. Koma nthaŵi zambiri ochulukira koposa akhala ndi umphumphu wawo utaikidwa ku chiyeso mokulira pamene chibwera ku kusonyeza ulemu wolambira kaamba ka ziphiphiritso za utundu. Ena akhala ndi kukhulupirira kwawo kutayesedwa pamene chibwera ku kugula kardi ya chipani cha ndale zadziko kapena kugwirizana ndi magulu ankhondo. Yehova wawachirikiza anthu otero onsewo, kuwatheketsa iwo kuyang’anizana ndi chitokoso ku umphumphu wawo mwachipambano ndipo chotero kutsimikizira Mdyerekezi kukhala wabodza ndi Yehova kukhala Mulungu wowona.
Chitsanzo China cha Chikhulupiriro ndi Kulimba Mtima
18. Ndimotani mmene Belisazara anasonyezera chitonzo kaamba ka Yehova, Mulungu wa Ayuda, monga mmene zinalembedwera pa Danieli mutu 5, maversi 3, 4?
18 Komabe chitsanzo china cha kukhulupirika ndi kulimba mtima chalembedwa m’bukhu la Danieli, mu mutu 5. Belisazara, mfumu ya Babulo, anali kusangalala ndi phwando lalikulu lopatulika la chipembedzo ndi zikwi za akulu ake, akazi ake, ndi akazi ang’ono. Mwadzidzidzi, dzanja lolemba lachilendo linawonekera pa khoma. Ichi chinadabwitsa mfumuyo kotero kuti mfundo za m’chiwuno mwake zinaguluka ndipo mawondo ake anawombana. Kachiŵirinso, Danieli, mtumiki wa Mulungu wowona, anaitanidwa kaamba ka kumasulira chifukwa chakuti amuna anzeru onse a Babulo analephera.
19. Nchiyani chomwe chinali chowonekera pamene Danieli anamasulira dzanja lolemba pa khoma?
19 Kuimirira yekha pamenepo m’malo a ulemelero ndi owopsyawo sikunamuwopsyeze Danieli kapena kumupangitsa iye kupeputsa uthenga wake kapena kutaya chiyang’aniro cha nkhaniyo. Woima bwino ndi wa bata, ndi kalankhulidwe komvekera, kolemekezeka, iye anapereka umboni ponena za Mulungu wake. Wosakhutiritsidwa kokha ndi kumasulira kwa dzanja lolembalo, Danieli anakumbutsa mfumuyo kuti Yehova Mulungu anali atachepetsa agogo ake amuna mwa kupangitsa iwo kukhala monga nyama ya kuthengo kufikira anafikira pa kuzindikira kuti Mulungu Wam’mwambamwamba ali Wolamulira wa ufumu wa anthu. “Chinkana munazidziŵa izi zonse,” Danieli anawuza Belisazara, ‘inu simunadzichepetsa koma munabwera nazo zotengera za nyumba ya Yehova ndi kulemekeza milungu ya golidi, siliva, mkuwa, chitsulo, mtengo, ndi mwala yomwe siwona, siimva, kapena kudziŵa. Koma Mulungu kwa amene m’dzanja lake muli njira zanu zonse, simunamulemekeza. Chifukwa chake, lamulo iri latuluka kuchokera kwa iye. Mwayesedwa muzoyesera ndi kupezeka woperewera, ndipo ufumu wanu wagawidwa ndi kupatsidwa kwa Amedi ndi Aperesiya.’ Inde, kachiŵirinso Danieli anakhazikitsa chitsanzo chabwino koposa m’chikhulupiriro ndi kulimba mtima kaamba ka atumiki a Mulungu lerolino.—Danieli 5:22-28.
20. Mkati mwa kulamulira kwa Dariyo, ndi chitsanzo chowonjezereka cha chikhulupiriro chachikulu chotani chimene Danieli anakhazikitsa?
20 Kubwera ku mutu 6 wa Danieli, tiri ndi chitsanzo chimodzi chowonjezereka chabwino cha chikhulupiriro ndi kulimba mtima. Mfumu Dariyo inali tsopano wolamulira ndipo inamupanga Danieli mmodzi wa olamulira akulu atatu a ufumuwo. Ena, ochitira nsanje Danieli, anakakamiza mfumuyo kupereka lamulo lakuti pa masiku 30 wina aliyense asapange pembedzero kwa winawake kusiyapo kokha mfumuyo. Iwo anazindikira kuti iyi inali njira yokha yomwe akapezera chotsutsana ndi Danieli. Iye ananyalanyaza lamulolo ndi kupitirizabe kupemphera m’chipinda chake chapamwamba ndi zenera lotsegula, akumayang’ana ku Yerusalemu. Akumapezedwa wolakwa mwa kulakwira lamulo la mfumu, Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango m’chigwirizano ndi chilanga choperekedwa ndi lamulo. Kachiŵirinso Mulungu anafupa Danieli kaamba ka chikhulupiriro chake ndi kulimba mtima. Motani? Monga mmene Ahebri 11:33 amachiikira icho, Yehova “analetsa pakamwa pa mikango.”
21. M’chiyang’aniro cha zitsanzo zabwino za chikhulupiriro ndi kulimba mtima zolembedwa mu mitu isanu ndi umodzi yoyambirira ya bukhu la Danieli, nchiyani chomwe chiyenera kukhala chigamulo chathu champhamvu?
21 Ndi zochitika zolimbikitsa chikhulupiriro chotani nanga zimene Danieli mitu 1 mpaka 6 amalongosola! Ndi mokulira chotani nanga mmene Yehova Mulungu amafupira awo amene amasonyeza chikhulupiriro ndi kulimba mtima! Ku mbali ina, ichi chinawoneka mwa kukhala kwawo okwezeka ndipo kumbali ina, mwa kukumana kwawo ndi zipulumutso zozizwitsa. Zowonadi, tingapeze chitonthozo ndi chiyembekezo kuchokera ku zokumana nazo za mboni zokhulupirika zimenezi pamene tiyang’anizana ndi ziyeso. Nkulekeranji, popeza zinthu zimenezi zinalembedwa kaamba ka chifuno chimenechi! Lolani kuti ife, chotero, tigamulepo kukhala atsanziri abwino a chikhulupiriro ndi kulimba mtima koteroko.—Aroma 15:4; Ahebri 6:12.
Mafunso a Kubwereramo
◻ Maina a achichepere Achihebri anayiwo amalingalira chiyani ponena za kuleredwa kwawo?
◻ Kuyang’anizana ndi chiyeso kwa chakudya kwa Ahebri kuli ndi phunziro lotani kaamba ka ife?
◻ Ndimotani mmene atumiki a Yehova lerolino akhalira ndi umphumphu wawo utayesedwa monga mmene anachitira Ahebri atatu?
◻ Ndimotani mmene Danieli anasonyezera chikhulupiriro ndi kulimba mtima m’kuchitira umboni kwa Belisazara?
[Chithunzi patsamba 17]
Danieli ndi mabwenzi ake anaphunzira kunena kuti ayi