Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lff phunziro 32
  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulira Panopa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulira Panopa
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • FUFUZANI MOZAMA
  • ZOMWE TAPHUNZIRA
  • ONANI ZINANSO
  • Kodi Ulosi wa M’Baibulo Umatiuza Zotani pa Nkhani ya Chaka cha 1914?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira?—Gawo 2
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Boma la Mulungu Liyamba Ulamuliro Wake
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Ufumu wa Mulungu Umaposa Mafumu Onse
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff phunziro 32
Phunziro 32. Yesu Khristu wanyamula ndodo yachifumu ndipo akulamulira dziko lapansi.

PHUNZIRO 32

Ufumu wa Mulungu Ukulamulira Panopa

Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa

Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira kumwamba m’chaka cha 1914. Chaka chimenechi n’chimenenso masiku otsiriza a ulamuliro wa anthu anayamba. Kodi timadziwa bwanji zimenezi? Tiona ulosi wina wa m’Baibulo, zinthu zimene zakhala zikuchitika padzikoli ndiponso makhalidwe amene anthu akhala akusonyeza kuyambira mu 1914.

1. Kodi Baibulo linalosera chiyani?

Buku la m’Baibulo la Danieli linalosera kuti Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulira pamapeto pa “nthawi zokwanira 7.” (Danieli 4:16, 17) Patapita zaka zambiri Yesu anatchula nthawiyi kuti “nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu,” ndipo anaphunzitsa kuti nthawiyi inali isanafike kumapeto. (Luka 21:24) Monga mmene tionere nthawi zokwanira 7 zimenezi zinatha mu 1914.

2. Kodi kuchokera mu 1914, ndi zinthu ziti zomwe zakhala zikuchitika padzikoli, nanga anthu akhala akusonyeza makhalidwe otani?

Ophunzira a Yesu anafunsa kuti: “Kodi . . . chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” (Mateyu 24:3) Poyankha, Yesu anawafotokozera zinthu zambiri zimene zidzachitike iye akadzayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba. Zina mwa zinthu zimenezi ndi monga nkhondo, njala komanso zivomezi. (Werengani Mateyu 24:7.) Baibulo linaloseranso kuti ‘m’masiku otsiriza’ anthu adzakhala ndi makhalidwe oipa omwe adzachititse kuti moyo ukhale wovuta kwambiri. (2 Timoteyo 3:1-5) Zinthu zimenezi zakhala zikuchitika kwambiri kuyambira mu 1914.

3. N’chifukwa chiyani padzikoli pakuchitika zinthu zoipa kwambiri kungochokera pamene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira?

Yesu atangokhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, anapita kukamenyana ndi Satana komanso ziwanda zake. Satana anagonja pa nkhondoyi. Baibulo limanena kuti: “Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.” (Chivumbulutso 12:9, 10, 12) Satana ndi wokwiya kwambiri chifukwa akudziwa kuti awonongedwa posachedwapa. Iye ndi amene akuchititsa kuti padzikoli pakhale mavuto ambiri chonchi. Zimenezi zikutithandiza kumvetsa chifukwa chake zinthu zafika poipa kwambiri padzikoli. Koma chosangalatsa n’chakuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onsewa.

FUFUZANI MOZAMA

Fufuzani kuti muone zimene zimatithandiza kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914 komanso mmene zimenezi zimatikhudzira.

4. Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914

Onerani VIDIYO.

VIDIYO: Ufumu wa Mulungu Unayamba Kulamulira mu 1914 (5:02)

Mulungu anachititsa kuti Mfumu Nebukadinezara ilote maloto a zinthu zomwe zidzachitike m’tsogolo. Zimene Danieli ananena pomasulira malotowo zinasonyeza kuti malotowo anali okhudza ulamuliro wa Nebukadinezara komanso Ufumu wa Mulungu.​—Werengani Danieli 4:17.a

Werengani Danieli 4:20-26, kenako mugwiritse ntchito tchati kuti muyankhe mafunso otsatirawa:

  • (A) Kodi Nebukadinezara anaona chiyani m’maloto ake?​—Onani vesi 20 ndi 21.

  • (B) N’chiyani chimene chinachitikira mtengo umene analota?​—Onani vesi 23.

  • (C) N’chiyani chimene chinachitika kumapeto kwa “nthawi zokwanira 7”?​—Onani vesi 26.

Kugwirizana kwa Maloto a Mtengo ndi Ufumu wa Mulungu

ULOSI (Danieli 4:20-36)

Ufumu

(A) Mtengo waukulu

Mtengo wautali kwambiri.

Ufumu unasiya kulamulira

(B) “Gwetsani mtengowo,” ndipo ‘padutse nthawi zokwanira 7’

AChitsa cha mtengo chavekedwa chitsulo ndi mkuwa.

Ufumu unayambiranso kulamulira

(C) “Mudzayambiranso kulamulira mu ufumu wanu”

Mtengo wautali kwambiri.

Pamene ulosiwu unkakwaniritsidwa koyamba . . .

  • (D) Kodi mtengo unkaimira ndani?​—Onani vesi 22.

  • (E) Chinachitika n’chiyani kuti asiye kaye kulamulira?​—Werengani Danieli 4:29-33.

  • (F) N’chiyani chinachitikira Nebukadinezara “nthawi zokwanira 7” zitatha?​—Werengani Danieli 4:34-36.

KUKWANIRITSIDWA KOYAMBA

Ufumu

(D) Nebukadinezara, Mfumu ya Babulo

Mfumu Nebukadinezara yaima modzimva.

Ufumu unasiya kulamulira

(E) Pambuyo pa chaka cha 606 B.C.E., Nebukadinezara anapenga ndipo sanathe kulamulira kwa zaka 7

Nebukadinezara akudya udzu ngati nyama.

Ufumu unayambiranso kulamulira

(F) Nebukadinezara anachira misala yake ija ndipo anayambiranso kulamulira

Mfumu Nebukadinezara yayang’ana kumwamba itatambasula manja ake.

Pamene ulosiwu unkakwaniritsidwa kachiwiri . . .

  • (G) Kodi mtengo unkaimira ndani?​—Werengani 1 Mbiri 29:23.

  • (H) Chinachitika n’chiyani kuti asiye kaye kulamulira? Nanga timadziwa bwanji kuti ufumuwo unali usanayambebe kulamulira pa nthawi imene Yesu anali padzikoli?​—Werengani Luka 21:24.

  • (I) Ndi liti pamene ufumuwu unayambiranso kulamulira, nanga unayamba kulamulira kuti?

KUKWANIRITSIDWA KWACHIWIRI

Ufumu

(G) Mafumu a Isiraeli amene ankaimira ulamuliro wa Mulungu

Mafumu a Isiraeli omwe analamulira pa nthawi zosiyanasiyana akhala pamipando yachifumu. Kuwala kochokera kumwamba kukuwaunikira.

Ufumu unasiya kulamulira

(H) Yerusalemu anawonongedwa zomwe zinachititsa kuti mafumu a Isiraeli asiye kaye kulamulira kwa zaka 2,520

Mzinda wa Yerusalemu ukupsa ndi moto mu 607 B.C.E. Kenako pakudutsa zaka 2,520.

Ufumu unayambiranso kulamulira

(I) Yesu akuyamba kulamulira kumwamba monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu

Yesu ali kumwamba ndipo akulamulira dziko lapansi kuyambira mu 1914 C.E. Kuwala kochokera kochokera kwa iye kukuunikira dziko lapansi.

Kodi nthawi zokwanira 7 zikuimira nthawi yaitali bwanji?

Mavesi ena a m’Baibulo amatithandiza kumvetsa bwino zimene mavesi ena akutanthauza. Mwachitsanzo, buku la Chivumbulutso limanena kuti nthawi zitatu ndi hafu n’zofanana ndi masiku 1,260. (Chivumbulutso 12:6, 14) Choncho nthawi zokwanira 7 ndi kuwirikiza kawiri masiku 1,260 zomwe ndi masiku 2,520. Nthawi zina m’Baibulo mawu akuti tsiku amaimira chaka. (Ezekieli 4:6) Ndi mmenenso zilili ndi nthawi zokwanira 7 zotchulidwa m’buku la Danieli. Nthawizi zimaimira zaka 2,520.

5. Dzikoli lasintha kwambiri kuyambira mu 1914

Onerani VIDIYO.

VIDIYO: Dzikoli Lasintha Kwambiri Kuyambira mu 1914 (1:10)

Yesu ananeneratu zinthu zomwe zidzachitike padzikoli akadzangokhala Mfumu. Werengani Luka 21:9-11, kenako mukambirane funso ili:

  • Pa zinthu zimene zatchulidwa palembali, ndi ziti zimene inuyo munaona zikuchitika kapena kumva kuti zachitika?

Mtumwi Paulo anafotokoza makhalidwe amene anthu adzakhale nawo m’masiku otsiriza. Werengani 2 Timoteyo 3:1-5, kenako mukambirane funso ili:

  • Malinga ndi lembali, ndi makhalidwe ati amene inuyo mukuona kuti anthu akusonyeza kwambiri masiku ano?

Zithunzi: Zithunzi zosonyeza zomwe zikuchitika padzikoli ndiponso makhalidwe a anthu m’masiku otsiriza. 1. Mkulu wa asilikali akulankhula mofuula ataimika manja m’mwamba. 2. Nyumba zagwa chifukwa cha chivomezi. 3. Ndege za nkhondo. 4. Gulu la anthu likuyenda litavala mamasiki. 5. Nyumba zosanja ziwiri zaphulitsidwa ndi zigawenga ku New York ndipo zikuyaka. 6. Munthu akudzibaya mankhwala osokoneza bongo. 7. Mwamuna wakunga chibakera ndipo akukalipira mkazi wake. 8. Mowa komanso mankhwala osiyanasiyana. 9. Azimayi avala zovala ndi zodzikongoletsera zapamwamba ndipo akudzijambula. 10. DJ akuika nyimbo ku dansi. 11. Munthu yemwe akuchita nawo zionetsero akuponya bomba.

6. Muzisonyeza kuti mumakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira

Werengani Mateyu 24:3, 14, kenako mukambirane mafunso awa:

  • Kodi ndi ntchito yofunika kwambiri iti imene ikusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira?

  • Mungatani kuti muyambe kugwira nawo ntchitoyi?

Ufumu wa Mulungu ukulamulira panopa ndipo posachedwapa uyamba kulamulira dziko lonse lapansi. Werengani Aheberi 10:24, 25, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi aliyense wa ife ayenera kuchita chiyani pamene ‘tikuona kuti tsikulo likuyandikira’?

Zithunzi: 1. Wophunzira Baibulo ali pamisonkhano ya Mboni za Yehova. 2. Wophunzira Baibulo yemweyo akulalikira mnzake.

Mungatani mutakhala kuti mwaphunzira mfundo inayake yomwe ikhoza kuthandiza komanso kupulumutsa anthu?

MUNTHU WINA ANGAKUFUNSENI KUTI: “N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amakonda kunena kuti chaka cha 1914 ndi chapadera?”

  • Kodi mungamuyankhe bwanji?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Ulosi wa m’Baibulo komanso zinthu zimene zikuchitika padzikoli, zikusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira. Tikamalalikira ndi kuchita nawo misonkhano yampingo timasonyeza kuti timakhulupirira zimenezi.

Kubwereza

  • N’chiyani chinachitika kumapeto kwa nthawi zokwanira 7 zotchulidwa m’buku la Danieli?

  • N’chiyani chimakutsimikizirani kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914?

  • Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira panopa?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Onani zimene olemba mbiri ndiponso anthu ena amanena zokhudza mmene dzikoli linasinthira kuyambira mu 1914.

“Nthawi Imene Makhalidwe Analowa Pansi Kwambiri” (Galamukani!, April 2007)

Werengani kuti muone mmene ulosi wopezeka pa Mateyu 24:14 unakhudzira moyo wa munthu wina.

“Ndinkakonda Kwambiri Masewera a Baseball Kuposa Chilichonse” (Nsanja ya Olonda Na. 3 2017)

Kodi timadziwa bwanji kuti ulosi umene umapezeka m’buku la Danieli chaputala 4 umanena za Ufumu wa Mulungu?

“Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira? (Gawo 1)” (Nsanja ya Olonda, October 1, 2014)

N’chiyani chikusonyeza kuti “nthawi zokwanira 7” zimene zinatchulidwa m’buku la Danieli chaputala 4, zinatha mu 1914?

“Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira? (Gawo 2)” (Nsanja ya Olonda, November 1, 2014)

a Werengani nkhani ziwiri zomalizira zomwe zili pagawo lakuti, Onani Zinanso m’phunziroli.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena