Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 11/15 tsamba 8-9
  • Danieli Anatumikira Mulungu Mosalekeza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Danieli Anatumikira Mulungu Mosalekeza
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Upo Wachiŵembu
  • Danieli Achirimikabe
  • Phunziro kwa Ife
  • Alanditsidwa ku Mano a Mikango!
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Danieli Anaponyedwa M’dzenje la Mikango
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Danieli m’Dzenje la Mikango
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yehova Alonjeza Danieli Mphotho Yodabwitsa
    Samalani Ulosi wa Danieli!
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 11/15 tsamba 8-9

Anachita Chifuniro cha Yehova

Danieli Anatumikira Mulungu Mosalekeza

SIZIMACHITIKA kaŵirikaŵiri kuti mbiri ingosintha mwadzidzidzi. Komabe, zimenezo zinachitika mu 539 B.C.E., pamene Ufumu wa Babulo unagwetsedwa ndi Amedi ndi Aperisi m’maola oŵerengeka okha. Pofika chakacho, Danieli mneneri wa Yehova anali atakhala ndi moyo monga Myuda wogwidwa ukapolo ku Babulo kwa zaka pafupifupi 80. Danieli, mwinamwake wa m’zaka zake za ma 90, anali atatsala pang’ono kuyang’anizana ndi chiyeso chachikulu koposa cha umphumphu wake kwa Mulungu.

Babulo atagwa, poyamba zinthu zinaoneka ngati zikuyenda bwino kwa Danieli. Mfumu yatsopano inali Dariyo Mmedi, mwamuna wazaka 62 zakubadwa amene anayanja Danieli. Chimodzi cha zinthu zoyamba zimene Dariyo anachita monga mfumu chinali kusankha akalonga 120 ndi kukweza amuna atatu kukhala akuluakulu aboma apamwamba.a Danieli anali mmodzi wa anthu atatu amenewo oyanjidwa. Pozindikira kukhoza kuchita zinthu kwapadera kwa Danieli, Dariyo analingaliradi zompatsa malo a nduna yaikulu! Komabe, panthaŵiyo, kanthu kena kanachitika kamene kanasintha mwadzidzidzi malingaliro a mfumuyo.

Upo Wachiŵembu

Akuluakulu aboma anzake a Danieli, limodzi ndi gulu lalikulu la akalonga, anafikira mfumu ndi lingaliro lina lamachenjera. Anachonderera Dariyo kuti akhazikitse lamulo lonena kuti: “Aliyense akapempha kanthu kwa mulungu aliyense, kapena kwa munthu aliyense masiku makumi atatu, osati kwa inu nokha, mfumu, adzaponyedwa m’dzenje la mikango.” (Danieli 6:7) Zingakhale zitaoneka kwa Dariyo monga ngati kuti amuna ameneŵa anali kusonyeza lumbiro la kukhulupirika kwawo kwa iye. Mwina angakhale atalingaliranso kuti, pokhala kuti anali wa kudziko lina, lamulo limeneli lidzamthandiza kulimbitsa malo ake monga mtsogoleri wa ufumuwo.

Komabe, akuluakulu aboma ndi akazembewo sanatchule lamuloli kwa mfumu kaamba ka ubwino wake. Iwo “anayesa kumtola chifukwa Danieli, kunena za ufumuwo; koma sanakhoza kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo sanaona chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.” Chotero anthu achiŵembuwa anati: “Sitidzamtola chifukwa chilichonse Danieli amene, tikapanda kumtola ichi pa chilamulo cha Mulungu wake.” (Danieli 6:4, 5) Podziŵa kuti Danieli anali kupemphera kwa Yehova tsiku ndi tsiku, anafunafuna njira yochititsira zimenezo kukhala mlandu woyenerera chilango cha imfa.

Mwinamwake akuluakulu aboma ndi akalongawo anada Danieli chifukwa chakuti “anaposa [iwo] ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang’anira ufumu wonse.” (Danieli 6:3) Kuona mtima kwa Danieli kungakhale kutachititsa kuipidwa naye pa kulimbana kwake ndi chinyengo ndi kulanda. Mulimonse mmene zinalili, amuna ameneŵa anakhutiritsa mfumu kuti isaine lamulolo, kulipanga kukhala mbali ya “malamulo a Amedi ndi Aperisi, amene sasinthika.”​—Danieli 6:8, 9.

Danieli Achirimikabe

Kodi Danieli analeka kupemphera kwa Yehova atadziŵa za lamulo latsopanolo? Kutalitali! Anapemphera kwa Mulungu katatu patsiku atagwada m’chipinda chapamwamba cha nyumba yake, “monga umo amachitira kale lonse.” (Danieli 6:10) Pamene anali kupemphera, adani ake “anasonkhana . . . napeza Danieli alikupemphera ndi kupembedza pamaso pa Mulungu wake.” (Danieli 6:11) Pamene anauza mfumu za nkhaniyo, Dariyo anavutika mtima chifukwa chakuti lamulo limene analisaina linaloŵetsa Danieli mu mlandu. Nkhaniyo imati, “nayesetsa mpaka poloŵa dzuŵa kumlanditsa.” Komabe mfumuyo sikanathanso kuchotsa lamulo limene inakhazikitsa. Chotero anatengera Danieli ku dzenje la mikango, mwachionekere malo okumbika kapena a pansi pa nthaka. “Mulungu wako amene umtumikira kosalekeza, iyeyu adzakulanditsa,” mfumuyo inamtsimikizira Danieli motero.​—Danieli 6:12-16.

Pambuyo posapeza tulo usiku ndi kusala kudya, Dariyo anafulumira kumka ku dzenjelo. Danieli anali moyo ndiponso wosapwetekedwa! Mfumu inachitapo kanthu nthaŵi yomweyo. Inaponyera adani a Danieli ndi mabanja awo m’dzenje la mikango monga chilango. Dariyo analengezanso mu ufumu wake wonse kuti “m’maiko onse a ufumu wanga anthu anjenjemere, naope pamaso pa Mulungu wa Danieli.”​—Danieli 6:17-27.

Phunziro kwa Ife

Danieli anali chitsanzo chabwino cha kukhulupirika. Ngakhale mfumu, imene sinali yolambira Yehova, inaona kuti Danieli anatumikira Iye “kosalekeza.” (Danieli 6:16, 20) Phata la liwu lachiaramaiki lotembenuzidwa kuti “kusalekeza” makamaka limatanthauza “kuyenda mozungulira.” Limapereka lingaliro la kupitiriza. Zimenezi zimafotokoza bwino chotani nanga umphumphu wosasweka wa Danieli kwa Yehova!

Danieli anakulitsa chizoloŵezi cha kuchita zinthu mosalekeza poyambirira pomwe asanaponyedwe m’dzenje la mikango. Monga wogwidwa ukapolo wachichepere ku Babulo, iye anakana chakudya kapena zakumwa zoletsedwa ndi Chilamulo cha Mose kapena zodetsedwa ndi miyambo yachikunja. (Danieli 1:8) Pambuyo pake, iye analengeza molimba mtima uthenga wa Mulungu kwa Mfumu Nebukadinezara yachibabulo. (Danieli 4:19-25) Patangotsala maola oŵerengeka okha kuti Babulo agwe, Danieli mopanda mantha analengeza za chiweruzo cha Mulungu kwa Mfumu Belisazara. (Danieli 5:22-28) Chotero pamene Danieli anayang’anizana ndi dzenje la mikango, iye anapitiriza kuyenda m’njira yokhulupirika imene anakhazikitsa.

Inunso mungatumikire Yehova mosalekeza. Kodi ndinu wachichepere? Pamenepo chitanipo kanthu tsopano lino kukulitsa chizoloŵezi cha kuchita zinthu mosalekeza mwa kukana mayanjano oipa a dzikoli ndi khalidwe lake loipitsa. Ngati mwakhala mukutumikira Mulungu kwa nthaŵi ina, sungani chizoloŵezi cha kupirira mokhulupirira. Musagonje, pakuti chiyeso chilichonse chimene timayang’anizana nacho chimatipatsa mwaŵi wa kusonyeza Yehova kuti tili otsimikiza mtima kumtumikira mosalekeza.​—Afilipi 4:11-13.

[Mawu a M’munsi]

a Mawu akuti “kalonga” (kwenikweni kutanthauza “wotetezera Ufumu”) amanena za kazembe woikidwa ndi mfumu yachiperisi kuti atumikire wolamulira wamkulu pa chigawo china. Monga woimira waboma wa mfumu, iye anali ndi thayo la kukhometsa misonkho ndi kutumiza ndalama za misonkhoyo kwa mfumu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena