Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 1/1 tsamba 10-18
  • Masiku Otsiriza—Nthaŵi ya Kututa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Masiku Otsiriza—Nthaŵi ya Kututa
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nthaŵi ya Kututa
  • Ripoti la Chaka
  • Nthaŵi Zofulumira
  • Ziyembekezo kaamba ka Kukula Kowonjezereka
  • Osati kwa Utali Wokulira
  • Limbikirani ntchito yotuta!
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Zotsatira za Ntchito Yolalikira—“M’mindamo Mwayera Kale Ndipo M’mofunika Kukolola”
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
  • “Babulo Wamkulu Wagwa”
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Sangalalani Ndi Ntchito Yotuta!
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 1/1 tsamba 10-18

Masiku Otsiriza​—Nthaŵi ya Kututa

“Ndipo ndinapenya, tawonani, mtambo woyera; ndi pamtambo padakhala wina monga mwana wa munthu, wakukhala naye korona wagolidi pamutu pake, ndi m’dzanja lake zenga lakuthwa.”​—CHIVUMBULUTSO 14:14.

1. Ndi ziti zomwe ziri zinthu zina zomwe zapanga zana lino kukhala lapadera?

NDI nthaŵi yowopsya chotani nanga mmene zana lino la 20 lakhalira! Mtundu wa anthu wayenera kupirira nkhondo ziŵiri zowopsya za dziko. Dziko limodzi pambuyo pa linzake lakhala likugwetsedwa ndi kuwukira. Njala yapangitsa kuvutika kwambiri kuposa ndi kalelonse m’mbiri ya munthu. Kusatsimikizirika kwa chuma, upandu, kuwononga, ndi matenda ochititsa mantha kwawopsyeza ubwino wa aliyense. Panthaŵi imodzimodziyo, munthu wapanga kupita patsogolo kwakukulu kwa sayansi. Iye wakonza mphamvu za atomu ndipo ngakhale kuyenda pa mwezi. Ndithudi, mbadwo wathu uli wapadera m’njira zambiri. Mosasamala kanthu za chimenecho, chinthu chimodzi chimakhala chowonekera monga chinthu chofunika kwambiri cha nthaŵi yathu, ndipo pambali pa icho zinthu zina zonse zimakhala zosawonekera.

2. Ndi chochitika chotani choloseredwa ndi Danieli chinayenera kuchitika m’nthaŵi yathu?

2 Chochitika chopanga mbiri chowona chimenechi chinanenedweratu kalelo m’zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E. ndi mneneri Danieli. Mvetserani ku ripoti lake louziridwa mwaumulungu: “Ndinawona m’masomphenya a usiku, tawonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake. Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire.”​—Danieli 7:13, 14.

3. (a) Ndani amene ali “Nkhalamba ya kale lomwe,” ndipo nchiyani chimene iye anapereka kwa “winawake monga mwana wa munthu”? (b) Kodi ndani ameneyu “wonga mwana wa munthu,” ndipo ndimotani mmene atsogoleri a chipembedzo a Chiyuda anavomerezera pamene Yesu anapanga chizindikiritso chimenechi?

3 “Nkhalamba ya kale lomwe” ali Yehova Mulungu. Danieli akumuwona iye “m’mitambo ya kumwamba,” kunena kuti, m’mabwalo a mizimu yosawoneka, akupereka ufumu kwa “winawake wonga mwana wa munthu.” Ndani yemwe ali “winawake” ameneyo? Yesu anayankha funso limenelo kalelo mu 33 C.E. pamene iye anali kuyesedwa pamaso pa Bwalo Lalikulu la milandu. Mkulu wansembe wa Chiyuda anamuika iye pansi pa chilumbiro kuti anene kaya iye anali Kristu kapena ayi. M’kuyankha, Yesu mopanda mantha anagwiritsira ntchito ulosi wa Danieli kwa iyemwini, akumanena kuti: “Kuyambira tsopano mudzawona Mwana wa munthu ali kukhala ku dzanja lamanja la mphamvu, ndi kufika pa mitambo ya kumwamba.” M’malo mowerama kwa Mfumu yosankhidwa ya Yehova, wansembe wamkuluyo anamuzenga mlandu wa kuchita mwano. Kenaka, atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda anakakamiza Pontiyo Pilato kumpatsa Yesu chilango cha imfa.​—Mateyu 26:63-65; 27:1, 2, 11-26.

4. Ndi liti pamene Yesu analandira chisoti cha ufumu, ndipo mosasamala kanthu za chitsutso chotani?

4 Kuyesera kumeneku kwa kusokoneza mawu a Yesu kunalephera pamene iye anaukitsidwa kuchokera kwa akufa ndi kukwera kumwamba kukadikirira kaamba ka nthaŵi yoyenera ya Yehova ya kumpatsa iye ufumu. (Machitidwe 2:24, 33, 34; Masalmo 110:1, 2) Nthaŵi imeneyo inafika mu 1914. Mogwirizana ndi zizindikiro zonse, kumapeto kwa chaka chimenecho, Yesu analandira chisote cha ufumu kuchokera kwa “Nkhalamba ya kale lomwe” ndipo anayamba kulamulira. (Mateyu 24:3-42) Ufumu wobadwa chatsopanowo unayang’anizana ndi chitsutso chowawa. Koma atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda a m’zana loyamba, mphamvu zonse za mitundu zosonkhanitsidwa, ndipo ngakhale Satana ndi ziwanda zake sanali okhoza kuletsa chifuno cha Mulungu kukwaniritsidwa. (Masalmo 2:2, 4-6; Chivumbulutso 12:1-12) Mu 1914 nyimbo ya kumwamba inaimbidwa pa nthaŵi yake yeniyeni: “Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.” (Chivumbulutso 11:15) Chiyambire tsiku limenelo, takhala tikukhala “m’masiku otsiriza” a dongosolo iri loipa la kachitidwe ka zinthu.​—2 Timoteo 3:1.

Nthaŵi ya Kututa

5. (a) Mogwirizana ndi ulosi wa Danieli, ndani amene adzatumikira Mfumu yovekedwa chisoti yatsopanoyo? (b) Ndi masomphenya otani amene Yohane anawona omwe anakhudzanso Yesu monga Mfumu yovekedwa chisoti yachatsopanoyo?

5 Mogwirizana ndi ulosi wa Danieli, pamene Yesu alandira chisote chake chaufumu “anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi amanenedwe onse [adzamtumikira.]” Kodi chimenechi chingachitike motani ngati mtundu wonse wa anthu umukana iye monga Mfumu? Masomphenya a chitsanzo ovumbulutsidwa kwa mtumwi Yohane amasonyeza yankho. Yohane akutiuza ife zimene iye anawona: “Tawonani! mtambo woyera, ndi pamtambo padakhala wina monga Mwana wa munthu, wakukhala naye korona wagolidi pamutu pake, ndi m’dzanja lake zenga lakuthwa.” (Chivumbulutso 14:14) Mofanana ndi masomphenya a Danieli, Yesu pano akuwonedwa atakhala pamtambo ndipo akuzindikiritsidwa monga “winawake . . . wonga Mwana wa munthu.” Iye wavala chisote chaufumu, koma m’dzanja mwake sali ndi ndodo yachifumu koma zenga la wotuta. Nchifukwa ninji?

6. Ndi ntchito yotani imene Yehova akulamulira Yesu woikidwa ufumu chatsopanoyo kudzilowetsamo?

6 Yohane akupitiriza: “Ndipo mngelo wina anatuluka m’Kachisi, wofuula ndi mawu akulu kwa Iye wakukhala pamtambo, ‘Tumiza zenga lako ndi kumweta, pakuti yafika nthaŵi yakumweta; popeza dzinthu za dziko zachetsa.’” Yesu, ngakhale kuti ali Mfumu, amamverabe malangizo operekedwa kuchokera kwa Yehova “m’malo opatulika a kachisi.” Chotero pamene Yehova amlangiza iye kuyamba ntchito yotuta mkati mwa masiku otsiriza, iye amamvera. Yesu “anaponya zenga lake pa dziko, ndipo dzinthu za dziko zinamwetedwa.”​—Chivumbulutso 14:15, 16; Ahebri 9:24; 1 Akorinto 11:3.

7. (a) Nchiyani chimene chiri “zotuta za dziko lapansi”? (b) Nchiyani chimene chinali chiyambi cha “kututa” kumeneku?

7 Nchiyani chimene chiri “kututa kwa dziko lapansi”? Iko kuli anthu amene amabwera kuchokera ku dongosolo la usatana la kachitidwe ka zinthu iri kudzatumikira Yehova ndi Mfumu yake yoikidwa. Kututako kumayamba ndi kusonkhanitsidwa kwa otsalira a 144,000 omwe adzalamulira limodzi ndi Yesu mu ufumu wake wa kumwamba. (Mateyu 13:37-43) Awa ali “Israyeli wa Mulungu,” “zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.” Iwo agulidwa kuchokera kwa “anthu a mafuko onse ndi manenedwe onse ndi mitundu yonse.” (Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 14:4; 5:9, 10) M’njira imeneyi, munthu aliyense payekha kuchokera kwa “anthu onse, mitundu ndi manenedwe” amayamba kutumikira Yesu woikidwa ufumuyo.

8. (a) Ndi m’chaka chiti pamene kusonkhanitsa kwa omalizira a odzozedwa mwachiwonekere kunafika kumapeto? (b) Ndimotani, mogwirizana ndi masomphenya ena a Yohane, mmene ntchito yotuta ikapitirizira?

8 Komabe, iwo sali okha. Yohane m’masomphenya ena, akuwona kuikidwa chizindikiro kwa omalizira a 144,000. (Chivumbulutso 7:1-8) Mwachiwonekere, kusonkhanitsidwa kwa awa kunatheratu pofika 1935. Koma kenaka, Yohane akusimba kuti, iye akuwona “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:9-17) Chotero ntchito yotuta ikupitiriza pamene ambiri kuchokera “kwa anthu, mitundu ndi manenedwe” akuyamba kutumikira Yesu monga Mfumu.

9. Ndani amene ali achatsopano amenewo, ndipo kodi ndi maulosi ena ati amene amatchula kuwonekera kwawo mkati mwa “masiku otsiriza”?

9 Achatsopano amenewa amayang’ana kutsogolo ku kusangalala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi pansi pa Mfumu yoikidwa ya Yehova. (Masalmo 37:11, 29; 72:7-9) Kusonkhanitsidwa kwawo kunanenedweratu mu unyinji wa maulosi ena. Yesaya, mwachitsanzo, ananeneratu kuti “m’masiku otsiriza” mitundu idzanka kunyumba ya Yehova. (Yesaya 2:2, 3) Hagai analosera kugwedezeka kwa mitundu mkati mwa kumene “zofunika za amitundu onse zidzafika.” (Hagai 2:7) Zekariya analankhula za “amuna khumi a manenedwe onse amitundu” omwe adzazigwirizanitsa iwo eni kwa anthu a Mulungu. (Zekariya 8:23) Kuwonjezerapo, Yesu iyemwini analosera ponena za “khamu lalikulu” limeneli. Iye ananena kuti: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake. Ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse, ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi. Nadzakhalitsa nkhosa ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere.”​—Mateyu 25:31-33.

10. (a) Ndi mwanjira yotani mmene “zotuta za dziko lapansi” zikututidwira? (b) Ndani okha amene akugwirizana ndi angelo m’ntchito imeneyi?

10 Inde, mtundu wonse wa anthu ukusanthulidwa kuwona ndani amene ali “nkhosa” ndi amene ali “mbuzi.” Ndimotani mmene ntchito yosanthula imeneyi ikukwaniritsidwira? M’masomphenya a Yohane, “kututa kwa dziko lapansi” kukumwetedwa m’chigwirizano ndi uthenga wamphamvu wolalikidwa ndi angelo. Mngelo mmodzi akulalikira uthenga wa “mbiri yabwino yosatha.” Wina akulengeza kugwa kwa “Babulo Wamkulu.” Ndipo wachitatu akuchenjeza motsutsana ndi kulambira “chirombo,” dongosolo la kachitidwe ka zinthu la ndale zadziko la Satana. (Chivumbulutso 14:6-10) Zowona, palibe aliyense amene anamva mawu enieni a angelo amenewa. Koma iwo amvapo uthenga wolinganako womwe ukutulutsidwa ndi anthu okhulupirika. (Mateyu 24:14; Yesaya 48:20; Zekariya 2:7; Yakobo 1:27; 1 Yohane 2:15-17) Chotero, momvekera, uthengawo ukuwulutsidwa ndi pakamwa pa anthu pansi pa chitsogozo cha angelowo. Munthu amazindikiridwa monga ‘nkhosa’ kapena monga ‘mbuzi’ mwanjira imene amavomerezera ku uthenga waungelowo. Mkati mwa zana lino la 20, kokha Mboni za Yehova zagwirizana ndi angelowo m’ntchito yofunika kwambiri imeneyi.

11. Kodi kubukitsa uthenga waungelo kumeneku kuli kofunika motani?

11 Kufalitsidwa kwa mauthenga amenewa iri ntchito yotsendereza koposa chirichonse chomwe chikuchitidwa lerolino. Palibe kupita patsogolo kwa ndale zadziko kapena zopeza za usayansi zomwe zimafika pafupi ndi kufunikako. Mauthenga amenewa amaloza njira ku mayankho a mavuto onse a mtundu wa anthu ndipo amanena za chipulumutso chosatha cha anthu okhulupirika. Ndipo, chofunika koposa, iwo amachita ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova.

Ripoti la Chaka

12, 13. Perekani tsatanetsatane wina kuchokera ku ripoti la chaka amene amasonyeza kuti “kututa” kwakukulu kwasonkhanitsidwa kale.

12 Chimenecho ndicho chifukwa chake Mboni za Yehova zimayang’ana kutsogolo chaka chirichonse ku kuŵerenga ripoti la chaka la ntchito ya gulu la Yehova. Iwo amasangalala kuwona chitsimikiziro chopitirizabe cha dalitso lake pa ntchito yawo. Ngati musanthula ripoti la 1987, lolembedwanso pa masamba 12 mpaka 15 a magazini ino, mudzawona kuti angelo ndi anthu ogwira nawo ntchito anali okangalika koposa chaka chatha.

13 Mbiri yabwino inamvedwa m’maiko 210​—ndithudi, ‘fuko lirilonse ndi mitundu ndi manenedwe’ yomwe iri yofikirika pa nthaŵi ino. (Marko 13:10) Ndiponso, monga chiŵerengero chapamwamba 3,395,612 anagwirira ntchito limodzi kukwaniritsa chimenecho​—kuposa ndi kale lonse m’mbiri ya Chikristu. Ziŵerengerozo ziri zosangalatsa ngakhale m’maiko ena. Mu United States, chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha 773,219 chinafikiridwa. Maiko ena aŵiri, Brazil ndi Mexico, anawona ziŵerengero zapamwamba za 216,216 ndi 222,168 lirilonse; ndipo asanu ndi limodzi owonjezereka, Britain, Germany, Italy, Japan, Nigeria, ndi Philippines, anachitira ripoti ziŵerengero zapamwamba mu unyinji woposa 100,000. Kumbali ina, pali maiko ena amene ali ndi chiŵerengero cha anthu chokulira ndipo kokha zikwi zochepa za ofalitsa kapena ocheperapo. Ntchito ya miyoyo yokhulupirika imeneyi irinso yofunika kwambiri pamene iwo akukalamira kupangitsa kuwala kwa chowonadi kuwonekera pansi pa mikhalidwe yovuta.​—Mateyu 5:14-16.

14. Ndi anthu a mtundu wanji amene akusonkhanitsidwa mu gulu la Yehova?

14 Ndithudi, anthu a Mulungu sali okondweretsedwa m’chiwonjezeko kokha chifukwa cha icho chokha. Iwo amadziŵa, ngakhale kuli tero, kuti onse a awo achatsopano obwera ku gulu la Yehova ali “zinthu zofunika” m’maso mwa Yehova. Ambiri anali “kulira ndi kuusa moyo pa zonyansa zonse” zimene anachitira umboni m’Chikristu cha Dziko. (Ezekieli 9:4) Iwo akunka ku “phiri la Yehova” chifukwa akufuna kulangizidwa m’njira za Mulungu. (Yesaya 2:2, 3) Ndi chitsimikiziro champhamvu chotani nanga cha dalitso la Yehova​—kuti m’dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu loipa ndi lokondetsa zinthu za kuthupi, mazana a zikwi za atsopano amadziwonetsera iwo eni chaka chirichonse monga “zinthu zofunika” za Yehova!

Nthaŵi Zofulumira

15. (a) Kodi gawo loti likwaniritsidwe ndi ntchito yolalikira liri lalikulu motani? (b) Mogwirizana ndi masomphenya a Yohane, kodi “khamu lalikulu” liri lokangalika motani?

15 Ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova iri yofulumira. Nchifukwa ninji? Kaamba ka chinthu chimodzi, gawo liri lalikulu. “Mbiri yabwino” iyenera kulengezedwa “kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” (Chivumbulutso 14:6) M’fanizo la Yesu, anthu a “mitundu yonse” akugawidwa mu “nkhosa” ndi “mbuzi.” Pali ntchito yambiri yoti ichitidwe. Ndi choyenera chotani, nanga, kuti “khamu lalikulu” lowonedwa ndi Yohane likulemekeza Mulungu “usana ndi usiku m’kachisi wake.” (Chivumbulutso 7:15) M’kukwaniritsa masomphenya amenewa, “khamu lalikulu” limeneli, likumagwira ntchito mogwirizana ndi abale awo odzozedwa, anachitira ripoti kuwononga chiwonkhetso cha maora 739,019,286 m’ntchito yolalikira chaka chatha​—chiŵerengero chomwe chiri chifupifupi chachikulu kwambiri kuchiyerekezera. Kuzungulira padziko lonse, ichi chinaimira avereji ya maora 18 pa mwezi pa wofalitsa aliyense. Yerekezani ichi ndi avereji ya maora 12 pa mwezi zaka khumi zokha zapita, ndipo mungawone kuti liŵiro la ntchito yolalikira likuwonjezereka. Ndimotani mmene avereji yanu yaumwini imafananira ndi avereji ya dziko lonse?

16. (a) Ndi iti imene iri njira yabwino ya “kulalikira mawu . . . panthaŵi yake”? (b) Ndi angati amene anagawana m’ntchito imeneyi chaka chatha?

16 Dziŵani, kachiŵirinso, chiŵerengero chapamwamba cha apainiya othandizira ndi okhazikika: 650,095. Ichi chikutanthauza kuti panali apainiya ambiri m’munda chaka chatha kuposa ndi mmene analiri ofalitsa mu chaka cha 1955. Kodi munali mmodzi wa apainiya amenewo? Ngati ndi tero, munapeza njira yabwino koposa ya kugwiritsira ntchito mwaumwini uphungu wa Paulo wakuti: “Lalika mawu, chita nawo panthaŵi yake.” (2 Timoteo 4:2) Bwanji osakonzekera kugawanamo mu utumiki wa upainiya kwa chifupifupi mwezi umodzi mkati mwa chaka chautumiki cha 1988?

Ziyembekezo kaamba ka Kukula Kowonjezereka

17. Ndi ziŵerengero zotani zimene zimasonyeza kuti chiyembekezero kaamba ka chiwonjezeko cha mtsogolo chiri chabwino?

17 Chiyembekezo kaamba ka kukula kwa mtsogolo chiri mowonadi chapamwamba. Chiŵerengero cha maphunziro a Baibulo a panyumba chinali 3,005,048​—ndipo wophunzira Baibulo aliyense ali ‘chinthu chofunika’ chothekera! Kuwonjezerapo, 8,965,221 anapezekapo pa chikondwerero cha Mgonero wa Ambuye mu April watha. Ambiri a awo amene anapezekapo sanali Mboni za Yehova. Ena anali okondwerera chatsopano. Iwo analandiridwa kwambiri ndipo akulimbikitsidwa kupitiriza kupanga kupita patsogolo kwabwino. Ena angakhale anapezeka pa zochitika zoterozo nthaŵi zambiri kumbuyoko. Iwo mwachiwonekere anasangalala kukhala ndi Mboni koma sanachimve chifuno cha kuchita zambiri kuposa apo.

18. Mogwirizana ndi maulosi a Yesu ndi Zekariya, nchiyani chimene munthu afunikira kuchita kuti aŵerengedwe monga mmodzi wa “nkhosa” za Yehova?

18 Otero ayenera kuyamikiridwa kaamba ka chikondwerero chawo m’chowonadi cha Baibulo. Koma kumbukirani, m’fanizo la Yesu “nkhosa” zimene zinapita ku moyo wosatha ali awo amene anasonyeza kuthandiza kulinga kwa abale odzozedwa a Yesu ndi kugwirizana nawo. (Mateyu 25:34-40, 46) Mu ulosi wa Zekariya, chiŵerengero chathunthu cha “amuna khumi” chikulengeza popanda kusinkhasinkha: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) Iwo samangokhala kokha ndi mkhalidwe waubwenzi. Iwo “amagwira” anthu a Mulungu ndi kupita ndi iwo, kudzipereka iwo eni kutumikira Mulungu wa awa. M’tsiku lathu, ichi chimaphatikizapo kukhala wodziloŵetsa kotheratu m’gulu la Yehova.

Osati kwa Utali Wokulira

19, 20. (a) Mogwirizana ndi masomphenya a Yohane, nchiyani chimene chidzachitika pamene kusonkhanitsa kwa “zotuta za dziko lapansi” kwatsirizidwa? (b) Kodi ichi chidzatanthauza chiyani kaamba ka onse amene sadzigonjetsera iwo eni kwa Yesu monga Mfumu?

19 Ntchito yotuta iri yofulumira kaamba ka chifukwa chachiŵiri. Posachedwapa idzatsirizidwa. (Mateyu 24:32-34) Nchiyani chimene kenaka chidzachitika? Ŵerengani chimene chidzatsatira m’masomphenya a Yohane: “Ndipo mngelo wina anatuluka m’kachisi ali m’mwamba, nakhala nalo zenga lakuthwa nayenso. Ndipo mngelo wina anatuluka pa guwa la nsembe, ndiye wakukhala nawo ulamuliro pamoto. Nafuula ndi mawu a akulu kwa iye wakukhala nalo zenga lakuthwa, nanena: ‘Tumiza zenga lako lakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m’dziko, pakuti mphesa zake zapsya ndithu.’ Ndipo mngelo anaponya zenga lake ku dziko nadula mphesa za m’munda wa m’dziko, naziponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu.”​—Chivumbulutso 14:17-19.

20 Pambuyo pa kusonkhanitsa zotuta za “zinthu zofunika”, sipadzakhala chifukwa chowonjezereka chirichonse kwa dziko lakale loipa iri kupitiriza kukhalapo. “Mphesa za m’munda wa dziko,” dongosolo lonse la dziko iri la kachitidwe ka zinthu la usatana, lidzadulidwa ndi kuwonongedwa. Panthaŵi imeneyo, ngakhale otsutsa adzakakamizidwa kuzindikira Mfumu yoikidwa ya Yehova. Yohane analemba kuti: “Tawonani! adzadza [Yesu] m’mitambo ndipo diso lirilonse lidzampenya iye, iwonso amene anampyoza, ndipo mafuko onse a padziko adzamlira iye.” (Chivumbulutso 1:7; Mateyu 24:30) Kenaka, mawu a Yesu kwa atsogoleri a chipembedzo a Chiyuda, omwe anali kutsogolo kwambiri pakati pa “awo omwe anampyoza iye,” adzakwaniritsidwa. (Mateyu 26:64) Ndithudi atsogoleri onyenga a chipembedzo amenewo sadzaukitsidwa “kudzawona” Yesu mwaumwini. (Mateyu 23:33) Koma onse amene lerolino amasonyeza mzimu umenewo ndi kukana kulandira Mfumu yoikidwa ya Yehova adzakakamizidwa kumdziŵa iye pamene iye adzabwera kudzawononga mitundu pa Amargedo.​—Chivumbulutso 19:11-16, 19-21.

21. Nchifukwa ninji anthu a Mulungu ayenera kugwira ntchito molimbika m’chigwirizano ndi angelo a kumwamba?

21 Ndithudi, chipulumutso cha munthu aliyense payekha chiri pa ngozi. Tiri ndi thayo lalikulu m’kukhala ogwira ntchito ndi angelo. Koma iwo uli mwaŵi waukulu chotani nanga! Lolani kuti tipitirize kugwira ntchito molimbika m’chigwirizano ndi angelo a kumwamba pamene tikukalamira kupeza onse onga nkhosa, “zinthu zofunika” za Yehova, ntchito yotuta isanatsirizidwe.

Kodi Mungalongosole?

◻ Nchiyani chimene chiri chochitika chachikulu m’zana lino la 20?

◻ Nchiyani chimene chiri “zotuta za dziko lapansi,” ndipo ndimotani mmene izo zikusonkhanitsidwira?

◻ Nziti zomwe ziri zina za zizindikiro za “nkhosa” za Yehova?

◻ Ndimotani mmene ripoti la chaka likusonyezera dalitso la Yehova pa ntchito yotuta?

◻ Nchifukwa ninji ntchito yolalikira iri yofulumira?

[Tchati pamasamba 12-15]

RIPOTI LAUTUMIKI LA CHAKA CHA 1987 LA MBONI ZA YEHOVA DZIKO LONSE

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena