Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 7/15 tsamba 28-30
  • Kodi Kalenda Yachiyuda Ili Yolondola Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kalenda Yachiyuda Ili Yolondola Motani?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukhazikitsa Poyambira
  • “Nyengo ya Kulenga”
  • Maziko a Kuŵerengera Nthaŵiko
  • Miyambo ndi Mamasuliridwe
  • Chotsala Chachipembedzo
  • Madeti
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Gawo 10: 537 B.C.E. kupita mtsogolo—Kudikirirabe Mesiya
    Galamukani!—1989
  • Mmene Ulosi wa Danieli Unasonyezera Nthawi Imene Mesiya Adzafike
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Nsanja ya Olonda—1994
w94 7/15 tsamba 28-30

Kodi Kalenda Yachiyuda Ili Yolondola Motani?

MALINGA ndi kalenda Yachiyuda, Lachinayi, September 16, 1993, linali tsiku laphwando la Rosh Hashanah. Mwa mwambo shofar, kapena mphalasa ya nyanga ya nkhosa yamphongo, inawombedwa panthaŵiyo kulengeza kuyambika kwa chaka chatsopano. Chakacho ndicho cha 5754 (kalenda Yachiyuda), ndipo chiyambira pa September 16, 1993, kufika pa September 5, 1994.

Pamenepo, tikuona kuti pali kusiyana kwa zaka 3,760 pakati pa kuŵerengera nthaŵi kwa Ayuda ndi kwa kalenda Yakumadzulo, kapena ya Gregory imene ikugwiritsiridwa ntchito mofala tsopano. Kodi nchifukwa ninji pali kusiyana kumeneku? Ndipo kodi kalenda Yachiyuda ndi yolondola motani?

Kukhazikitsa Poyambira

Njira iliyonse yoŵerengera nthaŵi iyenera kukhala ndi poyambira pake. Mwachitsanzo, Dziko Lachikristu limaŵerengera nthaŵi kuyambira m’chaka chimene Yesu Kristu analingaliridwa kukhala atabadwiramo. Madeti oyambira pamenepo amanenedwa kukhala a m’nyengo Yachikristu. Kaŵirikaŵiri amasonyezedwa ndi zilemba zakuti A.D., zotengedwa ku anno Domini Wachilatini, kutanthauza “m’chaka cha Ambuye.” Madeti a kumbuyoko nyengo imeneyo isanakhale amasonyezedwa ndi B.C., “Before Christ.”a Mofananamo Atchaina amwambo amaŵerengera nthaŵi kuyambira mu 2698 B.C.E., chiyambi cha ulamuliro wa Huang-Ti wa m’nthanthi, mfumu yotchedwa Yellow Emperor. Motero, February 10, 1994, linali chiyambi cha chaka chotsatira kayendedwe ka mwezi cha 4692 cha Atchaina. Nangano, bwanji ponena za kalenda Yachiyuda?

The Jewish Encyclopedia imati: “Njira yamakono yozoloŵereka kwa Ayuda yolembera deti la chochitika ndiyo kutchula chiŵerengero cha zaka zimene zapita kuyambira pa kulengedwa kwa dziko.” Njira imeneyi, yodziŵika kwa Ayuda monga Nyengo ya Kulenga, inayamba kugwiritsiridwa ntchito mofala pafupifupi m’zaka za zana lachisanu ndi chinayi C.E. Chotero, madeti pa kalenda Yachiyuda amayamba kaŵirikaŵiri ndi mawuwo A.M. Iwo amaimira anno mundi, amene ali chidule cha ab creatione mundi, kutanthauza “kuyambira pa kulengedwa kwa dziko.” Popeza kuti chaka chino ndi cha A.M. 5754, malinga ndi njira imeneyi yoŵerengera nthaŵi, “kulengedwa kwa dziko” kumalingaliridwa kukhala kutachitika zaka 5,753 zapitazo. Tiyeni tione mmene zimenezo zimapezedwera.

“Nyengo ya Kulenga”

Encyclopaedia Judaica (1971) imapereka mafotokozedwe aŵa: “M’kuŵerengera kosiyanasiyana kwa arabi ‘Nyengo ya Kulenga’ inayamba paphukuto m’chimodzi cha zaka zapakati pa 3762 ndi 3758 B.C.E. Komabe, kuyambira m’zaka za zana la 12 C.E., kunakhala kovomerezedwa kuti ‘Nyengo ya Kulenga’ inayamba mu 3761 B.C.E. (kunena molondola, pa Oct. 7 wa chakacho). Kuŵerengera kumeneku nkozikidwa pa kugwirizanitsidwa kwa kuŵerengera nthaŵi kosonyezedwa m’Baibulo ndi kaŵerengeredwe kopezeka m’mabuku Achiyuda apambuyo pa Baibulo.”

Njira imeneyi yoŵerengera madeti kuyambira pa “kulengedwa kwa dziko” kwakukulukulu njozikidwa pa mamasuliridwe aurabi onena za mbiri ya Baibulo. Chifukwa cha chikhulupiriro chawo chakuti dziko ndi zonse za momwemo zinalengedwa m’masiku enieni asanu ndi limodzi amaola 24, akatswiri aurabi, limodzinso ndi a Dziko Lachikristu, amalingalira kuti kulengedwa kwa munthu woyamba, Adamu, kunachitika m’chaka chimodzimodzi cha kulengedwa kwa dzikoli. Komabe, zimenezi nzosalondola konse.

Chaputala choyamba cha Genesis chimayamba mwa kunena kuti: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Ndiyeno chimapitiriza kulongosola zimene Mulungu anachita mu “masiku” asanu ndi limodzi otsatizana kusandutsa dziko lapansi kuchokera kumkhalidwe ‘wopanda kanthu’ kukhala malo oyenera okhalapo anthu. (Genesis 1:1, 2) Payenera kukhala patapita zaka mamiliyoni pakati pa mbali ziŵiri zimenezi. Ndiponso, masiku akulenga sanali nyengo zamaola 24, ngati kuti ntchito za Mlengi zinali zomangika ndi malire otero. Kunena kuti “tsiku” m’nkhaniyi lingakhale loposa pa maola 24 kukusonyezedwa ndi Genesis 2:4, amene amalankhula za nyengo zonse zakulenga kukhala “tsiku” limodzi. Panapita zaka zikwi zambiri pakati pa tsiku loyamba lakulenga ndi lachisanu ndi chimodzi, pamene Adamu analengedwa. Kuika deti la kulengedwa kwa Adamu panthaŵi imodzimodzi ndi ija ya miyamba yeniyeni ndi dziko lapansi sikuli kwa Malemba osatinso kwasayansi. Komabe, kodi kunadziŵidwa motani kuti “Nyengo ya Kulenga” inayamba mu 3761 B.C.E.?

Maziko a Kuŵerengera Nthaŵiko

Mwatsoka, ochuluka a mabuku Achiyuda amene anazikidwapo kuŵerengera kumene tikukambapo kulibenso. Limene lilipo ndi buku la kuŵerengera nthaŵi limene poyambirira linatchedwa Seder ʽOlam (Dongosolo la Dziko). Limakhulupiriridwa kuti linalembedwa ndi katswiri wa Talmud wa m’zaka za zana lachiŵiri C.E. Yose ben Halafta. Buku limeneli (limene pambuyo pake linatchedwa Seder ʽOlam Rabbah kulisiyanitsa ndi la mbiri yotchedwa Seder ʽOlam Zuṭa ya m’Zaka Zapakati) limapereka kuŵerengera nthaŵi kwa m’mbiri kuyambira pa Adamu kufikira pa chipanduko cha Ayuda cha m’zaka za zana lachiŵiri C.E. chopandukira Roma pansi pa Mesiya wonama Bar Kokhba. Kodi mlembiyo anapeza motani chidziŵitso chimenecho?

Pamene kuli kwakuti Yose ben Halafta anayesayesa kutsatira mbiri ya Baibulo, anawonjezera mamasuliridwe ake pamene lemba silinafotokoze bwino madeti oloŵetsedwamo. “Nthaŵi zambiri, . . . anapereka madetiwo malinga ndi mwambo, ndipo anaika, m’mbali mwake, maneno ndi halakot [miyambo] ya arabi oyambirira ndi a m’nthaŵi yake,” ikutero The Jewish Encyclopedia. Ena samachita chifundo mpang’ono pomwe m’kufufuza kwawo. The Book of Jewish Knowledge limati: “Anaŵerengera kuyambira pa Nyengo ya Kulenga ndipo, mogwirizana ndi zimenezo, anaika madeti ongopeka pa zochitika zosiyanasiyana Zachiyuda zimene zinalingaliridwa kukhala zitachitika kuyambira kwa Adamu, munthu woyamba, kufikira kwa Alexander Wamkulu.” Koma kodi ndimotani mmene mamasuliridwe ndi zoikamo zotero zinayambukirira kulondola ndi kuona kwa kuŵerengera nthaŵi Kwachiyuda? Tiyeni tione.

Miyambo ndi Mamasuliridwe

Mogwirizana ndi mwambo wa arabi, Yose ben Halafta anaŵerengera kuti kachisi wachiŵiri m’Yerusalemu anakhalako kwa zaka 420. Zimenezi zinazikidwa pa mamasuliridwe a arabi onena za ulosi wa Danieli wa “masabata makumi asanu ndi aŵiri,” kapena zaka 490. (Danieli 9:24) Nyengo imeneyi inagwiritsiridwa ntchito pa nthaŵi imene inapyola pakati pa kuwonongedwa kwa kachisi woyamba ndi kuwonongedwa kwa wachiŵiri. Akumachotsapo zaka 70 za ukapolo wa ku Babulo, Yose ben Halafta anadzapeza kuti kachisi wachiŵiri anakhalako kwa zaka 420.

Komabe, mamasuliridwe ameneŵa amaloŵa m’vuto lalikulu. Madeti onse aŵiri la kuwonongedwa kwa Babulo (539 B.C.E.) ndi lija la kuwonongedwa kwa kachisi wachiŵiri (70 C.E.) ali odziŵika m’mbiri. Chotero, nyengo ya kachisi wachiŵiri inayenera kukhala zaka 606 mmalo mwa zaka 420. Mwa kuika zaka 420 zokha pa nyengo imeneyi, kuŵerengera nthaŵi Kwachiyuda kumapeŵera ndi zaka 186.

Ulosi wa Danieli suli wonena za utali wa nthaŵi imene kachisi wa m’Yerusalemu akakhala. Mmalomwake, unaneneratu za nthaŵi pamene Mesiya akaonekera. Ulosiwo umasonyeza bwino lomwe kuti “kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, ku[ka]khala masabata asanu ndi aŵiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu aŵiri.” (Danieli 9:25, 26) Pamene kuli kwakuti maziko a kachisi anayalidwa m’chaka chachiŵiri cha kubwerera kwa Ayuda kuchokera muukapolo (536 B.C.E.), “lamulo” la kumanga mzinda wa Yerusalemu silinatuluke kufikira “chaka cha makumi aŵiri cha Aritasasta mfumu.” (Nehemiya 2:1-8) Mbiri yakudziko yolondola imatchula 455 B.C.E. kukhala chakacho. Kuŵerengera kumka kutsogolo ndi “masabata” 69, kapena zaka 483, kumatifikitsa mu 29 C.E. Imeneyo ndiyo inali nthaŵi ya kuonekera kwa Mesiya, pa ubatizo wa Yesu.b

Mfundo ina ya kumasulira kwa arabi imene inachititsa cholakwa chachikulu m’kuŵerengera nthaŵi Kwachiyuda imakhudza nthaŵi ya kubadwa kwa Abrahamu. Arabi anawonkhetsa zaka za mibadwo yotsatizana zolembedwa pa Genesis 11:10-26 naika zaka 292 kuyambira panyengo ya Chigumula kudzafika pa kubadwa kwa Abrahamu (Abramu). Komabe, vuto lili m’kumasulira kwa arabi vesi 26, limene limati: “Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi aŵiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harana.” Kuchokera pamenepa, mwambo Wachiyuda umapereka lingaliro lakuti Tera anali ndi zaka 70 pamene Abramu anabadwa. Komabe, vesilo silimatchula mwachindunji kuti Tera anabala Abrahamu ali pausinkhu wazaka 70. Mmalomwake, limangonena kuti anabala ana aamuna atatu atakhala ndi zaka 70.

Kuti tipeze usinkhu wolondola wa Tera pakubadwa kwa Abrahamu, timangofunikira kupitiriza kuŵerenga nkhani ya Baibuloyo. Kuyambira pa Genesis 11:32–12:4, timapeza kuti Tera atafa pausinkhu wa zaka 205, Abrahamu ndi banja lake anachoka ku Harana molamulidwa ndi Yehova. Panthaŵiyo Abrahamu anali ndi zaka 75. Chotero, Abrahamu ayenera kukhala anali atabadwa pamene Tera anali ndi zaka 130, mmalo mwa 70. Chotero, nyengoyo kuchokera pa Chigumula mpaka pa kubadwa kwa Abrahamu inali zaka 352, mmalo mwa zaka 292. Panopo kuŵerengera nthaŵi Kwachiyuda kuchiphonya ndi zaka 60.

Chotsala Chachipembedzo

Zolakwa ndi kusiyana kotero mu Seder ‘Olam Rabbah ndi mabuku ena a kuŵerengera nthaŵi a Talmud zachititsa manyazi kwambiri ndi makambitsirano ochuluka pakati pa akatswiri Achiyuda. Ngakhale kuti kuyesayesa kochuluka kwachitidwa kwa kugwirizanitsa kuŵerengera nthaŵi kumeneku ndi zoona zodziŵika za m’mbiri, sizinakhale zachipambano zonse. Chifukwa ninji sizinatero? “Kwakukulukulu cholinga chawo sichinali chamaphunziro koma chachipembedzo,” ikutero Encyclopaedia Judaica. “Mwambo unayenera kusungidwa zivute zitani, makamaka poyang’anizana ndi timagulu topatuka.” Mmalo mothetsa msokonezo wochititsidwa ndi miyambo yawo, akatswiri ena Achiyuda anayesa kululuza zolembedwa za Baibulo. Ena anayesa kupeza chichirikizo m’nthano ndi miyambo ya Ababulo, Aigupto, ndi Ahindu.

Chotero, olemba mbiri samaonanso “Nyengo ya Kulenga” kukhala buku la kuŵerengera nthaŵi lodalirika. Akatswiri Achiyuda oŵerengeka ndiwo angayese kulitetezera, ndipo ngakhale mabuku aukumu otero onga The Jewish Encyclopedia ndi Encyclopaedia Judaica amaliona lonse ndi lingaliro lonyumwa. Chifukwa chake, njira yamwambo Yachiyuda yoŵerengera nthaŵi kuyambira pa kulengedwa kwa dziko singaonedwe kukhala yolondola malinga ndi kaonedwe ka kuŵerengera nthaŵi kwa Baibulo, ndandanda yanthaŵi ya Yehova Mulungu ya ulosi womavumbuluka.

[Mawu a M’munsi]

a Umboni wa Baibulo ndiponso wa mbiri umasonya ku kubadwa kwa Yesu Kristu m’chaka cha 2 B.C. Chotero, kaamba ka kulondola, ambiri amasankha kugwiritsira ntchito mawuwo C.E. (Common Era) ndi B.C.E. (Before the Common Era), ndipo umu ndi mmene madeti asonyezedwera m’zofalitsa za Watch Tower Society.

b Kuti mupeze zoloŵetsedwamo, onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 2 masamba 614-16, 900-902, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena