Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yehova Waulula “Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa”
    Nsanja ya Olonda—2012 | June 15
    • 9 Kwa nthawi yaitali, atumiki a Yehova akhala akuyesetsa kumvetsa tanthauzo la mapazi a chifaniziro chimenechi. Lemba la Danieli 2:41 limafotokoza msanganizo wa chitsulo ndi dongo monga “ufumu,” osati maufumu. Choncho dongolo likuimira zinthu zimene anthu ena amene ali pansi pa ulamuliro wa Britain ndi America akuchita. Zochita za anthuwa zimachititsa kuti ulamulirowu ukhale wosalimba poyerekezera ndi ulamuliro wa Roma, womwe unali ngati chitsulo. Dongolo likufotokozedwa ngati “ana a anthu,” kapena kuti anthu wamba. (Dan. 2:43) Anthu amene ali pansi pa ulamulirowu apanga magulu omenyera ufulu wosiyanasiyana. Anthu wamba amenewa achepetsa mphamvu za ulamuliro wa Britain ndi America kuti usakhale ngati chitsulo. Anthu ambiri amasiyana maganizo pa nkhani zokhudza boma ndipo olamulira ena amawina chisankho ndi mavoti ochepa. Zimenezi zimachititsa kuti olamulirawo asakhale ndi mphamvu zokwanira zochita zimene akufuna. Danieli anati: “Pa zinthu zina ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba.”​—Dan. 2:42; 2 Tim. 3:1-3.

  • Yehova Waulula “Zimene Ziyenera Kuchitika Posachedwapa”
    Nsanja ya Olonda—2012 | June 15
    • 11 Kodi chiwerengero cha zala zakumiyendo za chifanizirochi chili ndi tanthauzo lapadera? Taganizirani izi. M’masomphenya ena, Danieli anatchula ziwerengero za zinthu. Mwachitsanzo, anatchula chiwerengero cha nyanga pamitu ya zilombo zosiyanasiyana. Ziwerengero zimenezi zinali ndi tanthauzo lapadera. Koma pofotokoza chifanizirochi, Danieli sanatchule chiwerengero cha zala zake. Choncho zikuoneka kuti chiwerengero chake chilibe tanthauzo lapadera ngati mmene zilili ndi chiwerengero cha manja, miyendo ndi mapazi ake. Koma zimene Danieli anatchula n’zoti zalazo zidzakhala zachitsulo ndi dongo. Zimene Danieli anafotokoza zikutithandiza kuzindikira kuti ulamuliro wa Britain ndi America ndi umene udzakhale wamphamvu padziko lonse pamene “mwala” woimira Ufumu wa Mulungu udzaphwanya mapazi a chifanizirochi.​—Dan. 2:45.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena