-
Ufumu UkulamuliraNsanja ya Olonda (Yophunzira)—2022 | July
-
-
10. (a) Kodi timaona zinthu ziti mu ulamuliro wa Britain ndi America zomwe ulosi wa Danieli unaneneratu? (b) Kodi tiyenera kusamala ndi chiyani? (Onani bokosi lakuti, “Samalani ndi Dongo.”)
10 Choyamba, mosiyana ndi maulamuliro ena amphamvu padziko lonse otchulidwa m’masomphenyawa, ulamuliro wa Britain ndi America sukuimiridwa ndi zinthu zolimba ngati golide kapena siliva, koma chitsulo chosakanizika ndi dongo. Dongolo likuimira “ana a anthu” kapena kuti anthu wamba. (Dan. 2:43) Monga mmene timaonera masiku ano, zochita za anthu pa nkhani ya zisankho, ziwonetsero, kumenyera maufulu komanso kukhazikitsa mabungwe zimachititsa kuti ulamuliro womalizawu uzivutika kukwaniritsa zolinga zake.
-