Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 8/15 tsamba 32
  • Kodi Chinameza Yona?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Chinameza Yona?
  • Nsanja ya Olonda—1993
Nsanja ya Olonda—1993
w93 8/15 tsamba 32

Kodi Chinameza Yona?

BAIBULO limatiuza kuti Yona, mneneri wa Yehova wokhala ndi moyo m’zaka za zana lachisanu ndi chinayi B.C.E., anathaŵa ntchito yotumidwa. Iyeyu anakwera chombo. Mkati mwa ulendo wa panyanja ya Mediterranean wa namondwe wamkulu, amalinyero anaponyera Yona m’madzi. “Yehova anaikiratu chinsomba chachikulu chimeze Yona; ndipo Yona anali m’mimba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku.”​—Yona 1:3-17.

Ena amanena kuti, ‘Nzosatheka! Palibe cholengedwa cha m’nyanja chimene chingameze munthu.’ Komatu namngumi wotchedwa sperm whale kapena white shark wamkulu angatero. Posachedwapa, National Geographic (December 1992) inanena za kuthekera kwina kwa zimenezo​—namngumi wotchedwa whale shark. Mtundu wa shark waukulu koposa umene ukudziŵidwa, ukhoza kukhala wa mamita 20 m’litali ndi kulemera matani 70.

“Mpangidwe wa mimba wodabwitsa wa whale shark umagwirizana bwino lomwe ndi nkhani ya Yona. Nkosavuta kudziyerekezera mukuloŵa mosadziŵa m’kamwa ka whale shark, kakakulu kwambiri . . . M’kamwa monga phanga ngakhale mwa whale shark yaing’ono mukhoza kukwana Ayona aŵiri.”

Whale shark imadya zinthu za m’nyanja zotchedwa kuti plankton ndi krill, zimene “zimapyola pammero ndi kuloŵa m’chipinda chachikulu chotamuka chimene chili mimba yokhala pafupi ndi mtima.” Komabe, kodi munthu angatulukemo motani? National Geographic imati: “Anamngumi a shark ali ndi njira yabwino yotulutsira zinthu zimene amameza zovuta kupukusika m’mimba . . . Shark ingathe mwapang’onopang’ono kuchotsa m’mimba mwake chinthucho mwa kutembenuza mimba yake ndi kuikankhira kunja kudzera m’kamwa. . . . Chotero, inu mungatuluke kunja ndi masanzi, woterera koma mwinamwake mutaphunzira kanthu kena.”

Lerolino anamngumi a whale shark samapezeka m’Mediterranean, ngakhale kuti apezeka kudera lakutali kumpoto kwa New York City. Kodi anamngumiwo analiko m’Mediterranean munthaŵi ya Yona? Kodi ndani amene angadziŵe kwenikweni? Baibulo silimatchula mwachindunji za mtundu wa cholengedwa chimene Yehova anagwiritsira ntchito, koma Yesu mwiniyo anatsimikizira kuti nkhani ya Yona njowona.​—Mateyu 12:39, 40.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Norbert Wu/​Peter Arnold Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena