Maphunziro Kuchokera m’Malemba: Obadiya 1-21
Machenjezo Aumulungu Amene Amakuyambukirani
“IYE wokhudza inu, akhudza mwana wa m’diso [langa].” (Zekariya 2:8) Mawu atsoka amenewo amaima monga uthenga wachenjezo kwa aliyense: Yehova akuzindikira mmene mitundu imachitira ndi anthu ake. Ngakhale ndi tero, kodi nchiyani chomwe chikuchitika, ku mtundu umene ukungopita monyalanyaza pamaso pa chenjezo laumulungu loterolo ndipo movulaza kugwira anthu a Mulungu? Bukhu lalifupi koposa la Malemba Achihebri, Obadiya, likuyankha.
Tsoka kaamba ka Edomu
Palibe aliyense amene angapulumuke chiweruzo cha Yehova. Ulosi wa Obadiya, woperekedwa chifupifupi 607 B.C.E., unaneneratu za kuthamangitsidwa kwa Aedomu kuchoka m’dziko lawo mosasamala kanthu za malo awo owoneka kukhala achisungiko okwezeka “pakati pa nyenyezi.” Ndipo ngakhale kuti moyo waumunthu wa wolemba Baibulo ameneyu sunavumbulidwe, iye akukhalira moyo ku tanthauzo la dzina lake, “Mtumiki wa Yehova.” Motani? Mwa kulengeza chiweruzo chosakaza. Pamene Edomu akugwa, iye adzalandidwa kotheratu ndi mabwenzi amene ali m’pangano ndi iye. Osati ngakhale anzeru kapena amphamvu ake akapulumuka.—1-9.
Mulungu abweretsa tsoka pa awo a liwongo la chiwawa molimbana ndi anthu ake. Kodi nchiyani chimene chiri chifukwa kaamba ka tsoka la Aedomu? Machitidwe obwerezedwabwerezedwa achiwawa molimbana ndi ana amuna a Yakobo, abale awo. Monga mbadwa za Esau, Aedomu anali pa ubale kwa Aisrayeli. Komabe, iwo akupatsidwa mlandu wa kulanda fuko lawo, kusangalala mwankhalwe pa kugwa kwa Yerusalemu, ndi kufikitsa chimenechi pachimake mwa kupereka opulumuka kwa mdani. Chotero, Edomu wasindikiza kugwa kwake.—10-16.
Nyumba ya Yakobo Ibwezeretsedwa
Malonjezo a Yehova ali odalirika nthaŵi zonse. M’tsiku la Obadiya, Yehova anatsimikizira kuti anthu Ake akatenganso dziko lawo ndi kuwonjezeka. Israyeli sadzagawikananso. Nyumba ya Yakobo, ufumu wa mafuko aŵiri wa Yuda, idzagwirizanitsidwanso ndi nyumba ya Yosefe, ufumu wa kumpoto wa mafuko khumi, m’kusakaza Edomu monga moto umadya udzu ndi kudzaza gawo la Edomu. Akumaliza pa liwu la chilimbikitso, Obadiya akulengeza kuti Aisrayeli otengedwanso adzalambira Mulungu wawo mogwirizana ndi kukhala anthu ake. Ndithudi, ufumu udzakhala wa Yehova.—17-21.
Phunziro kaamba ka lerolino: Machenjezo onyalanyazidwa amabala chipatso chovulaza. Chotero, chenjezo lamphamvu la Obadiya kwa Edomu liyenera kumvekanso m’makutu a otsutsa Mulungu a lerolino: Aja amene akulimbana motsutsana ndi Yehova ndi anthu ake adzadulidwa kosatha.
Maphunziro Kuchokera m’Malemba: Yona 1:1-4:11
PEWANI tsoka! Landirani chifundo! Motani? Mwa kulabadira phunziro la nkhani yowona imene iri ya zaka zoposa 2,800—bukhu la Yona. Lolembedwa chifupifupi 844 B.C.E. ndi mneneri Yona wa ku Galileya, ilo liri lodzazidwa ndi chidziŵitso chauzimu.
Yona Athaŵa
Tiyenera kukhulupirira Yehova kuti atichirikize mu utumiki wake. Ngakhale kuli tero, Yona akuthaŵa ntchito yopatsidwa ndi Mulungu m’malo modalira pa Yehova kum’chirikiza iye. Zowona, yake sinali mbali yopepuka. Iye mopanda manyazi anayenera kuchenjeza Nineve woipa za tsoka laumulungu. Koma Yona akupita njira ina, kukwera chombo kupita ku Tarisi, tsopano Spain. Pa njira, namondwe achititsa mantha kwenikweni kotero kuti chipulumuko kaamba ka chombocho ndi okweramo chinawoneka kukhala chosatheka. Yona akuwulula, amarinyero akumponya iye m’madzi, ndipo nyanjayo ikhala bata. Chinsomba chachikulu chimeza mneneriyo.—1:1-17.
Atumiki a Mulungu angakhale a chidaliro kuti iye adzayankha mapemphero awo. Mkati mwa chinsombacho, Yona akulira kwa Yehova kaamba ka thandizo, mwa pemphero akuyamika Mulungu kaamba ka chipulumutso kuchokera ku manda a madzi, ndipo akulonjeza kulabadira chimene wawinda. M’kupita kwa nthaŵi, iye akusanzidwira kumtunda.—2:1-10.
Yona Apita ku Nineve
Musathaŵi konse ntchito yochokera kwa Yehova. Mwachiwonekere ataphunzira phunziro limeneli, mneneriyo amene kwa nthaŵi ina anali wozengereza alalikira mu “mzinda waukulu.” Yona akulengeza chenjezo lopepuka koma lolunjika: “Atsala masiku makumi anayi ndipo Nineve adzapasuka.” M’kusintha kozizwitsa kwa zinthu, anthu a ku Nineve akulapa ndipo akupeŵa tsoka.—3:1-10.
Munthu sangaikire malire chifundo cha Mulungu. Mkwiyo wa Yona ukula chifukwa chakuti Nineve wasungidwa. Koma mwanjira ya chomera, Yehova aphunzitsa Yona kuti Iye adzasonyeza chifundo mogwirizana ndi chisangalalo chabwino cha mwini Wake.—4:1-11.
Phunziro kaamba ka lerolino: Tsoka lingapewedwe mwa kulabadira ulosi waumulungu! Tsanzirani anthu a ku Nineve. Modzichepetsa mvetserani kwa Yesu Kristu, mneneri wokulira koposa Yona.—Luka 11:32.
[Bokosi patsamba 30]
MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA
○ 7—Mu nthaŵi za Baibulo, “kudya chakudya” pamodzi ndi munthu wina kunali kwenikweni pangano la unansi. Nchopyoza chotani nanga! Ababulo, “akupangana nawo” ndi Aedomu, akatsimikizira kukhala owawononga. Mowonadi, Ababulo a tsiku la Nebukadinezara analola Edomu kutengamo mbali m’kufunkha Yuda pambuyo pa kukhalitsidwa bwinja kwa Yerusalemu. Koma mfumu ya Babulo ya pambuyo pake Nabonidus kamodzi ndipo kwa nthaŵi zonse inathetsa zikhumbo za Edomu za chuma ndi malonda.
○ 10—Edomu anaweruzidwa “nawonongeka ku nthaŵi yonse” chifukwa cha udani wake wowononga ndi kusoweka kwa chikondi cha chibadwa kolimba kaamba ka mtundu wake wachibale, “ana a Yuda.” (Vesi 12) Kuzimitsidwa kwa mtundu koteroko kunatanthauza kuti ufumu wa Edomu ndi boma limodzinso ndi anthu pamalo a dziko odziŵika ukazimiririka pa nkhope ya dziko lapansi. Lerolino, palibe anthu ozindikirika a mtundu wa Edomu; iwo “akhala monga ngati sanalipo.”—Vesi 16.
[Bokosi patsamba 31]
MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA
○ 1:17—Chifukwa cha mutu wake waukulu ndi mmero, nsomba yotchedwa sperm whale iri yokhoza kumeza munthu. Ngakhale kuti nsomba zotchedwa whale sizipezeka kaŵirikaŵiri mu Mediterranean, anthu akupha nsomba za whale pa nthaŵi ina anakhala pa Yopa. Nsomba yodziŵika kutsatira zombo mu Mediterranean ndi kudya chirichonse choponyedwa m’madzi ikutchedwa great white shark. Nayonso iri yokhoza kumeza munthu wathunthu. Mu nkhani ya Yona, ngakhale kuli tero, Mulungu anagwiritsira ntchito “chinsomba chachikulu,” mwinamwake cholengedwa chosadziŵika ku sayansi yamakono.
○ 2:1, 2—Yona motsimikizirika analibe mikhalidwe yabwino kaamba ka kupanga ndakatulo pamene anali “m’mimba ya nsombayo.” Koma iye pambuyo pake analemba chokumana nacho chake. Kuchokera pansi pa mtima wake panatuluka mawu omveketsa aja opezeka mu Masalmo olongosola malingaliro ake.—Yerekezani 2:2 ndi Salmo 120:1 ndiponso 130:1; 2:5 ndi Salmo 69:1.
○ 3:3—Ukulu wa Nineve sunayerekezedwe mopambanitsa. Ngakhale kuti malinga owuzungulira anali kokha chifupifupi makilomita 13 m’kuzungulira, dzina la mzindawo mwachiwonekere linaphatikizapo mizinda yaing’ono, imene mwinamwake inakuta utali wa ulendo wa makilomita 42.
○ 3:10—Liwu la Chihebri lolembedwa monga “analeka choipa” limatanthauza “kusintha malingaliro a munthu kulinga ku kachitidwe kakale (kapena kofunidwa).” Chotero, Yehova ‘angaleke choipa’ kapena kusintha malingaliro ake ponena za kubweretsa chilango pa anthu olakwa pamene iwo alapa mowonadi.