Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo
    Nsanja ya Olonda—2009 | April 1
    • Yona anamva chisoni ndi kuuma kwa msatsi womwe unamera mu usiku umodzi wokha. Koma Mulungu anafotokoza kuti ndi iye amene anachititsa msatsiwu kumera ndiponso kukula, osati Yonayo. Pomalizira pake Mulungu anamuuza kuti: “Sindiyenera Ine kodi kuchitira chifundo Nineve mudzi waukulu uwu; mmene muli anthu oposa zikwi zana limodzi mphambu zikwi makumi awiri osadziwa kusiyanitsa pakati pa dzanja lawo lamanja ndi lamanzere, ndi zoweta zambiri zomwe?”​—Yona 4:10, 11.e

      Kodi mukuona kufunika kwa zimene Yehova anachita kuti aphunzitse Yona? Yona si amene anameretsa kapena kukulitsa msatsi uja. Yehova ndi amene anapatsa moyo anthu a ku Nineve ndipo ankawasamalira ngati mmene amasamalirira zolengedwa zake zonse padzikoli. Nanga n’chifukwa chiyani Yona ankaona kuti msatsi uja unali wofunika kwambiri kuposa anthu 120, 000 pamodzi ndi zoweta zawo zomwe? Kodi sichinali chifukwa choti iye ankaganiza modzikonda? Ndipotu iye ankadandaula chifukwa choti msatsi umene unkam’patsa mthunzi unali utauma. Kwenikweni Yona anakwiya chifukwa choti anali wodzikonda ndiponso sankafuna kuti anthu azimuona ngati mneneri wabodza.

      Limenelitu ndi phunziro labwino kwambiri. Koma mwina mungadzifunse kuti: Kodi Yona anaphunzirapodi kanthu pa zimenezi? Buku la m’Baibulo limene iye analemba limamaliza ndi funso limene Yehova anamufunsa koma silinayankhidwe. Anthu ena otsutsa amanena kuti Yona sanayankhe chilichonse. Koma zoona zake n’zakuti yankho lilipo ndipo yankho limenelo ndi buku la Yonali. Tikutero chifukwa timadziwa kuti Yona ndi amene analemba bukuli lomwe lili ndi dzina lake. Ndiyeno yerekezerani kuti mukuona mneneriyu yemwe poyamba anali wouma mtima, wosafuna kumvera Mulungu komanso wopanda chifundo, akulemba zonse zimene zinachitika pa ulendo wake wa ku Nineve. Panthawiyi Yona anali atasintha ndipo ayenera kuti anali wachikulire, wanzeru komanso wodzichepetsa. N’zoonekeratu kuti Yona anaphunzirapo kanthu pa malangizo anzeru amene Yehova anam’patsa. Anaphunziranso kufunika kochitira anthu ena chifundo. Kodi nafenso pamenepa sitikuphunzira kufunika kochitira ena chifundo?

  • Anaphunzira Kufunika Kochitira Ena Chifundo
    Nsanja ya Olonda—2009 | April 1
    • d Pa lembali, mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “msatsi” amatanthauza zomera zoyanga zimene zimabala zikho.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena