Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Oipa Adzakhalabe kwa Utali Wotani?
    Nsanja ya Olonda—2000 | February 1
    • 9 Habakuku akumvetsera mwachidwi mawu a Mulungu otsatira, omwe alembedwa pa Habakuku 1:6-11. Uwu ndi uthenga wa Yehova, ndipo palibe mulungu wonyenga kapena fano lililonse lopanda moyo lomwe lingalepheretse kukwaniritsidwa kwake. Uthengawo n’ngwakuti: “Pakuti taonani, ndiukitsa Akasidi, mtundu uja woŵaŵa ndi waliŵiro, wopitira pa chitando cha dziko lapansi, kuloŵa m’malo mosati mwawo, mukhale mwawomwawo. Ali oopsa, achititsa mantha, chiweruzo chawo ndi ukulu wawo zituluka kwa iwo eni. Akavalo awo aposa anyalugwe liŵiro lawo, aposa mimbulu ya madzulo ukali wawo, ndipo apakavalo awo atanda [“agugudaguguda pansi,” NW], inde apakavalo awo afumira kutali; auluka ngati chiwombankhanga chofulumira kudya. Adzera chiwawa onsewo; nkhope zawo zikhazikika zolunjika m’tsogolo [“zili ngati mphepo yakummaŵa,” NW]; asonkhanitsa andende ngati mchenga. Inde anyoza mafumu, aseka akalonga; aseka linga lililonse; popeza aunjika dothi, nalilanda. Pamenepo adzapitirira ngati mphepo, nadzalakwa ndi kupalamula, iye amene aiyesa mphamvu yake mulungu wake.”

  • Kodi Oipa Adzakhalabe kwa Utali Wotani?
    Nsanja ya Olonda—2000 | February 1
    • 12. Kodi Ababulo akuchitanji, ndipo kodi mdani woopsayu ‘akulakwa ndi kupalamula’ motani?

      12 Ankhondo a Akasidi akunyoza mafumu ndi kulalatira akalonga. Onseŵatu alibe mphamvu zowaletsera kufika. ‘Akuseka linga lililonse,’ pakuti mzinda uliwonse walinga ukulandidwa pamene Ababulo ‘akuunjika dothi’ mwa kukonza chimtumbira pamene akuukirirapo mzindawo. Panthaŵi yoikika ya Yehova, mdani woopsayu “adzapitirira ngati mphepo.” Poukira Yuda ndi Yerusalemu, ‘adzalakwa ndi kupalamula’ chifukwa chopweteka anthu a Mulungu. Atapambana mofulumira, kazembe wa Akasidi adzadzitama kuti: ‘Mphamvu imeneyi ndi ya mulungu wathu.’ Komatu iye sakudziŵa zenizeni!

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena