-
Kusangalala mwa Mulungu wa Chipulumutso ChathuNsanja ya Olonda—2000 | February 1
-
-
14-16. Malinga ndi Habakuku 3:14, 15, kodi n’chiyani chomwe chidzachitikire anthu a Yehova komanso adani awo?
14 Pa Armagedo, awo amene akuyesa kuwononga “odzozedwa” a Yehova adzasokonezedwa maganizo. Malinga ndi Habakuku 3:14, 15, mneneriyu akulankhula ndi Mulungu kuti: “Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kavumvulu kundimwaza; kukondwerera kwawo kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika. Munaponda panyanja ndi akavalo anu, madzi amphamvu anaunjikana mulu.”
-
-
Kusangalala mwa Mulungu wa Chipulumutso ChathuNsanja ya Olonda—2000 | February 1
-
-
16 Komanso pali zambiri zomwe zidzachitika. Yehova adzagwiritsa ntchito magulu auzimu, amphamvu zoposa za anthu kumalizitsa kuwononga adani akewo. Ndi “akavalo” a ankhondo ake a kumwamba otsogozedwa ndi Yesu Kristu, iye adzapitabe patsogolo mwachipambano kudutsa “panyanja” ndi ‘pamadzi amphamvu ounjikana mulu,’ ndiko kuti, chiŵerengero chomawonjezereka cha anthu achidani. (Chivumbulutso 19:11-21) Ndiyeno oipa adzachotsedwa padziko lapansi. Mphamvu za Mulungu ndi chilungamo chake zidzasonyezedwatu mwamphamvu kwambiri!
-