Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kusangalala mwa Mulungu wa Chipulumutso Chathu
    Nsanja ya Olonda—2000 | February 1
    • 18. Ngakhale kuli kwakuti Habakuku anayembekezera mavuto, kodi anali ndi malingaliro otani?

      18 Nthaŵi zonse nkhondo imabweretsa mavuto, ngakhalenso kwa amene pomalizira pake amapambana. Chakudya chingathe. Katundu angawonongeke. Moyo wa anthu ungakhale wovuta kwambiri. Ngati zimenezi zitatichitikira, kodi tidzatani? Malingaliro a Habakuku anali chitsanzo chabwino, pakuti iye anati: “Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m’minda m’mosapatsa chakudya; ndi zoŵeta zachotsedwa kukhola, palibenso ng’ombe m’makola mwawo; koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa.” (Habakuku 3:17, 18) Moyenerera Habakuku anayembekezera mavuto, mwinamwake njala. Koma iye sanaleke kusangalala mwa Yehova, mwa amene anapeza chipulumutso.

  • Kusangalala mwa Mulungu wa Chipulumutso Chathu
    Nsanja ya Olonda—2000 | February 1
    • 20. Mosasamala kanthu za mavuto a kanthaŵi kochepaŵa, kodi tiyenera kutsimikiza mtima kuchita chiyani?

      20 Ngakhale tikumane ndi mavuto alionse a kanthaŵi kochepa, sitidzataya chikhulupiriro m’mphamvu yopulumutsa ya Yehova. Abale ndi alongo athu ochuluka mu Afirika, Eastern Europe, ndi malo enanso akukumana ndi mavuto adzaoneni, koma akupitirizabe ‘kukondwera mwa Yehova.’ Mofanana ndi iwowo, tisaleketu kuchita zofananazo. Kumbukirani kuti Ambuye Mfumu Yehova ali Gwero lathu la “mphamvu.” (Habakuku 3:19) Sadzalephera kutithandiza. Armagedo ikubweradi, ndipo tili otsimikizira kuti dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu lidzatsatiradi. (2 Petro 3:13) Ndiyeno, “dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziŵitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi aphimba pansi pa nyanja.” (Habakuku 2:14) Mpaka nthaŵi yosangalatsa imeneyo, tiyeni titsanzire chitsanzo chabwino cha Habakuku. Tiyeni tisekere mwa Mulungu wa chipulumutso chathu’ nthaŵi zonse.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena