Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 1/1 tsamba 12-22
  • Ulemerero Waukulu Kwambiri wa nyumba ya Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulemerero Waukulu Kwambiri wa nyumba ya Yehova
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Phoso” Lochuluka
  • Kututa Padziko Lonse
  • Kupitabe Patsogolo
  • Mauthenga Otsiriza a Hagai
  • Onse Alemekeze Yehova!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • “Ine Ndili Nanu”
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Manja Anu Alimbike
    Nsanja ya Olonda—2006
  • “Ndidzagwedeza Mitundu Yonse ya Anthu”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 1/1 tsamba 12-22

Ulemerero Waukulu Kwambiri wa nyumba ya Yehova

“Ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.” ​—HAGAI 2:7.

1. Kodi mzimu woyera ukugwirizana motani ndi chikhulupiriro ndi ntchito?

POLALIKIRA kunyumba ndi nyumba, mmodzi wa Mboni za Yehova anakumana ndi mkazi wa tchalitchi cha Pentecostal amene anati, ‘Ifeyo tili ndi mzimu woyera, koma inu ndinu mukugwira ntchito.’ Mwanzeru, anamfotokozera kuti munthu amene ali ndi mzimu woyera, mwachibadwa adzasonkhezeredwa kuchita ntchito ya Mulungu. Yakobo 2:17 amati: “Chikhulupiriro, chikapanda kukhala nazo ntchito, chikhala chakufa mkati mwakemo.” Mwa thandizo la mzimu wa Yehova, Mboni zake zakulitsa chikhulupiriro cholimba, ndipo iye ‘wadzaza nyumba yake ndi ulemerero’ mwa kuzipatsa ntchito zolungama​—makamaka ‘kulalikira uthenga uwu wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.’ Atachita ntchitoyi moti Yehova nkukhutira nayo, “pomwepo chidzafika chimaliziro.”​—Mateyu 24:14.

2. (a) Kodi kudziloŵetsa kwambiri m’ntchito ya Yehova kudzabweretsa dalitso lotani? (b) Nchifukwa ninji tiyenera kukondwera ndi kumene kukuoneka ngati ‘kuchedwa’?

2 Pamawu a Yesu ameneŵa, tikudziŵa kuti ntchito yathu lerolino iyenera kwenikweni kukhala ya kulalikira kwa ena za “uthenga wabwino waulemerero wa Mulungu wachimwemwe,” umene anatisungiza. (1 Timoteo 1:11, NW) Pamene tidziloŵetsa kwambiri mu utumiki wa Yehova mwachimwemwe, ndi pamenenso mapeto adzaoneka kuti akuyandikira mwamsanga kwambiri. Pa Habakuku 2:2, 3 timaŵerengapo mawu a Yehova akuti: “Lembera masomphenyawo, nuwachenutse pamagome, kuti awaŵerenge mofulumira. Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.” Inde, “masomphenyawo” adzafika ngakhale ‘atachedwa.’ M’chaka chino cha 83 cha ulamuliro wa Ufumu wa Yesu, ena angaganize kuti tsopano lino tili m’nyengo ya kuchedwa. Komabe, kodi sitiyenera kukondwera kuti mapeto sanafikebe? Monga chozizwitsa, m’zaka khumi zino za m’ma 1990 ziletso za kulalikira uthenga wabwino azichotsapo ku Eastern Europe, mbali za m’Afirika, ndi m’maiko ena. Kumene kukuoneka ngati ‘kuchedwa’ kumeneko kukulola kusonkhanitsa “nkhosa” zina zambiri m’magawo ameneŵa amene angotseguka kumene.​—Yohane 10:16.

3. Kodi nchifukwa ninji kumvetsa kwathu “mbadwo uno” kwatsopano kuyenera kutisonkhezera kuchita ntchito ya Mulungu mwachangu?

3 ‘Sadzazengereza,’ mneneriyo akutero. Yesu anati mbadwo woipa ulipowu sudzatha kuchoka kufikira “zinthu zonsezi zidzachitidwa.” (Mateyu 24:34) Kodi kumvetsa kwathu mawu akewa kwatsopano kukutanthauza kuti ntchito yathu ya kulalikira siyofulumira kwambiri?a Choonadi chikusonyeza kuti nzosiyana kwambiri ndi zimenezo! Mbadwowu umene tilimowu ukuloŵa mumkhalidwe wa kuipa ndi ukatangale wosafanana ndi wina uliwonse m’mbiri yonse yakale. (Yerekezerani ndi Machitidwe 2:40.) Tiyenera kuichita mwachangu ntchito yathu. (2 Timoteo 4:2) Maulosi onse onena za nthaŵi ya chisautso chachikulu amasonyeza kuti chidzafika mwadzidzidzi, pomwepo, mosadziŵika​—ngati mbala. (1 Atesalonika 5:1-4; Chivumbulutso 3:3; 16:15) “Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.” (Mateyu 24:44) Pamene mbadwo uwu wa anthu osadziŵa Mulungu uyandikira chiwonongeko, ndithudi sitiyenera kutaya chiyembekezo chathu cha moyo wamuyaya mwa kubwerera ku “kukunkhulira m’thope” la zochenjenetsa zadziko!​—2 Petro 2:22; 3:10; Luka 21:32-36.

4. Kodi ndi mikhalidwe yotani imene yachititsa kuwonjezera “zakudya panthaŵi yake,” ndipo chosoŵa chimenechi chakwaniritsidwa motani?

4 Mongadi mwa ulosi wa Yesu, mu 1914 kunali “zoŵaŵa zoyamba” pamene mtundu wa munthu unaloŵa mu “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” Zinthu zomvetsa chisoni, masoka, ndi kusayeruzika zakhala zikuwonjezeka mpaka m’tsiku lino. (Mateyu 24:3-8, 12) Nthaŵi imodzimodziyo, Yehova walangiza gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kuti lipereke “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake” ku banja la Ambuye wawo, Kristu. (Mateyu 24:45-47) Ili pampando wake wachifumu kumwamba, Mfumu Yaumesiya imeneyi tsopano ikutsogoza programu yabwino kwambiri yopereka chakudya padziko lonse lapansi.

“Phoso” Lochuluka

5. Kodi ‘chakudya’ chofunika kwambiri chikusamaliridwa motani?

5 Talingalirani za kukonza “phoso.” (Luka 12:42) Chakudya chachikulu pa zakudya za Akristu ndicho Mawu a Mulungu, Baibulo. Kuti aphunzitse Baibulo mogwira mtima, matembenuzidwe osavuta kuŵerenga ndipo olongosoka ndiwo ofunika kwambiri. M’zaka zonsezi chosoŵa chimenechi chakwaniritsidwa mowonjezereka, makamaka kuyambira mu 1950 pamene New World Translation of the Christian Greek Scriptures inatulutsidwa m’Chingelezi. Podzafika 1961 New World Translation ya Baibulo lonse inakhalapo, ndipo posapita nthaŵi makope a m’zinenero zina zazikulu anakhalaponso. Mavoliyumu 3 amene atulutsidwa m’chaka chautumiki cha 1996 apanga chiŵerengero chonse kukhala 27, mwa amene 14 ndi Baibulo lonse lathunthu. Kuti achite ntchito imeneyi ya Baibulo, ndi ya zothandizira kuphunzira Baibulo, Akristu odzipatulira 1,174 tsopano akugwira ntchito yanthaŵi zonse yotembenuza m’maiko 77.

6. Kodi Sosaite yakwaniritsa motani kufunika kwa zofalitsa za Baibulo?

6 Pochirikiza khamu limeneli la otembenuza, nthambi 24 za Watch Tower Society zosindikiza zakhala zikutulutsa zofalitsa zochuluka kwambiri nthaŵi zonse. Choncho, makina osindikiza aliŵiro kwambiri akuikidwabe m’nthambi zazikulu. Chiŵerengero cha magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! otulutsidwa chawonjezeka mwezi ndi mwezi, ndipo chafika pachiŵerengero chonse pamodzi cha makope 943,892,500, chiwonjezeko cha 13.4 peresenti m’chakachi. Chiŵerengero chonse cha ma Baibulo ndi mabuku a zikuto zolimba otulutsidwa m’maiko a United States, Brazil, Finland, Germany, Italy, Japan, Korea, ndi Mexico okha chawonjezeka ndi 40 peresenti kuchokera mu 1995 kufika pa makope 76,760,098 mu 1996. Nthambi zina zilinso ndi gawo lalikulu pa chiwonjezeko chonse chimenechi cha mabuku otulutsidwa.

7. Kodi ndi motani mmene lemba la Yesaya 54:2 lakhalira lofulumira kwambiri tsopano?

7 Mbali yaikulu ya kuwonjezera kumeneku yakhala yofunika m’ma 1990 chifukwa cha ziletso zochotsedwa pa Mboni za Yehova ku Eastern Europe ndi mu Afirika. M’malo ameneŵa muli njala yaikulu ya chakudya chauzimu. Choncho pempho likuperekedwa ndi changu chachikulu kuposa ndi kale lonse: “Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsalu za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.”​—Yesaya 54:2.

8. Kodi ndi kulabadira kwamataya kotani kumene kukuthandiza kupereka chichirikizo chandalama?

8 Choncho, kufutukula zambiri za nthambi 104 za Sosaite kwakhala kofunika. Chifukwa cha mavuto a zachuma m’magawo ochuluka otsegulidwa chatsopano, mbali yaikulu ya zotayika za kufutukuka kumeneku imakwaniritsidwa ndi zopereka za ntchito yapadziko lonse zochokera ku maiko olemera. Nkosangalatsa kuti mipingo ndi anthu paokha alabadira ndi mtima wonse, ndi mzimu wa Eksodo 35:21: “Ndipo anadza, aliyense wofulumidwa mtima, ndi yense mzimu wake wamfunitsa, nabwera nacho chopereka cha Yehova, cha kuntchito.” Tikugwiritsira ntchito mpatawu kuyamikira onse amene akhala ndi phande pakupatsa kwamataya kumeneku.​—2 Akorinto 9:11.

9. Kodi Aroma 10:13, 18 akukwaniritsidwa motani lerolino?

9 Mu 1996 zofalitsa za Watch Tower Society zalemekezadi dzina la Yehova ndi zifuno zake kumalekezero a dziko lapansi. Zangokhala monga momwe mtumwi Paulo ananeneratu. Pogwira mawu ulosi wa Yoweli ndi Salmo 19, iye analemba kuti: “Amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka. Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu, Liwu lawo linatulukira ku dziko lonse lapansi, ndi maneno awo ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.” (Aroma 10:13, 18) Choncho mwa kulitamanda kwambiri dzina lamtengo wapatali la Yehova, anthu ake achita mbali yaikulu podzaza nyumba yake yolambiriramo ndi ulemerero. Komabe, kodi chilengezo chimenechi chapambana motani makamaka mu 1996? Chonde onani tchati chotsatira pamasamba 18 mpaka 21.

Kututa Padziko Lonse

10. Kodi ndi zinthu zotani zapadera zimene mwaona pantchito ya anthu a Yehova, monga momwe yasonyezedwera mwachidule pa tchati pamasamba 18 mpaka 21?

10 Mawu a Yesu opezeka pa Luka 10:2 sanakhalepo atanthauzo kwambiri ngati tsopano: “Dzinthu dzichuluka, koma antchito achepa; potero pemphani Mwini dzinthu, kuti akankhe antchito kukututa kwake.” Kodi mwalabadira pempholo? Mamiliyoni ambiri kuzungulira dziko lonse lapansi atero. Zimenezi zikusonyezedwa ndi chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa Ufumu 5,413,769 amene anachitira lipoti utumiki wakumunda mu 1996. Ndiponso, abale ndi alongo atsopano 366,579 anabatizidwa. Mmene timazikondera “zofunika za amitundu onse” zimenezi, zimene tsopano zikukhala ndi phande ‘pakudzaza nyumba ya Yehova ndi ulemerero’!​—Hagai 2:7.

11. Kodi nchifukwa ninji tonsefe tili ndi chifukwa chokhalira achimwemwe kwambiri?

11 Mbiri ya kufutukuka m’minda yotseguka chatsopano njochititsa chidwi. Kodi enafe tikusirira awo amene tsopano ali ndi chiwonjezeko chimenecho? Ayi, ife tikukondwa limodzi nawo. Maiko onse anali ndi chiyambi chaching’ono. Mneneri Zekariya amene analiko m’nthaŵi ya Hagai, analemba kuti: “Wapeputsa tsiku la tinthu tating’ono ndani?” (Zekariya 4:10) Tili achimwemwe kwambiri kuti m’maiko amene ntchito ya umboni ili yokhazikika bwino, muli ofalitsa Ufumu miyandamiyanda tsopano, ndipo gawo limafoledwa kaŵirikaŵiri, ngakhale mlungu uliwonse m’mizinda yaikulu yambiri. Kodi tili ndi chifukwa chogwetsera manja pamene Yehova tsopano akupereka mpata wa chipulumutso m’madera amene kale analibe mpatawo? Kutalitali! “Munda ndiwo dziko lapansi,” Yesu anatero. (Mateyu 13:38) Tiyenera kupitirizabe kupereka umboni wosamalitsa, monga momwe ophunzira oyambirira anachitira umboni wosamalitsa pachimaliziro cha dongosolo la zinthu lachiyuda.​—Machitidwe 2:40; 10:42; 20:24; 28:23.

Kupitabe Patsogolo

12. Kodi tili ndi chisonkhezero chotani cha kuyenda ‘molunjika kutsogolo’? (Onaninso bokosi lakuti, “Kututa ‘Kuchokera ku Malekezero a Dziko Lapansi.’”)

12 Inde, tiyenera kuyendera limodzi ndi galeta lakumwamba laungelo la Yehova, tikumayenda ‘molunjika kutsogolo.’ (Ezekieli 1:12) Tikukumbukira mawu a Petro akuti: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Chitsanzo chabwino cha changu cha abale athu m’maiko osauka chitisonkhezeretu. Kumene kukuoneka ngati kuchedwa kwa Armagedo kukulola zikwi mazana kusonkhanitsidwa m’maiko ameneŵa limodzinso ndi anthu ambiri m’magawo ogwiridwamo ntchito bwino. Musakayikire konse: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza.” (Zefaniya 1:14) Ifenso tiyenera kufulumira kuchita umboni wosamalitsa wotsiriza!

13, 14. (a) Kodi tinganenenji pa kugaŵira zofalitsa mu 1996? (b) Kodi ndi makonzedwe apadera otani amene mipingo ingapange chaka chilichonse, ndipo mukulinganiza motani kuti mudzakhalemo ndi phande?

13 Ngakhale kuti tsatanetsatane wake sakuonekera patchati cha utumiki, kugaŵira ma Baibulo, mabuku, ndi magazini kwawonjezeka kwambiri m’chaka chathachi. Mwachitsanzo, magazini ogaŵiridwa padziko lonse anasonyeza chiwonjezeko cha 19 peresenti, chiŵerengero chonse cha makope 543,667,923 amene anagaŵiridwa. Magazini athu amagwira ntchito mu ulaliki uliwonse​—m’makwalala, m’mapaki, poima mabasi, m’zigawo za malonda. Malipoti akusonyeza kuti m’magawo ena amene kulalikira za Ufumu kumachitika kaŵirikaŵiri, akatswiri akondwera ndi mkhalidwe wa magazini athu ndipo akulandira maphunziro a Baibulo.

14 Chaka chilichonse m’mwezi wa April, mipingo nthaŵi zambiri imalinganiza ulaliki wapadera wa magazini, umene umakhala mkupiti wa tsiku lonse kukhomo ndi khomo ndi m’malo apoyera. Kodi mpingo wanu udzakhala ndi phande pazimenezi m’April 1997? Makope apadera a m’April a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! akonzedwa, ndipo kuwagaŵira panthaŵi imodzi dziko lonse lapansi kudzakhala kochititsa chidwi! Kuchisumbu cha Cyprus, mipingo, mwa kugwiritsira ntchito mawu akuti “fikirani aliyense yemwe mungathe ndi uthenga wa Ufumu,” inapitiriza mwezi uliwonse ndi ulaliki wa magazini wolinganizidwa umenewu, niifika pachiŵerengero chatsopano chapamwamba cha makope 275,359 ogaŵidwa chakacho, chiwonjezeko cha 54 peresenti.

Mauthenga Otsiriza a Hagai

15. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova anatumiza mauthenga enanso kupyolera mwa Hagai? (b) Uthenga wachitatu wa Hagai uyenera kutiphunzitsa chiyani?

15 Masiku 63 Hagai atapereka uthenga wake wachiŵiri, Yehova anamtumiza uthenga wachitatu umene tiyenera kuulabadira kwambiri lerolino. Hagai analankhula monga kuti panthaŵiyo Ayuda anali kuyala maziko a kachisi, amene kwenikweni anawayala zaka 17 zapitazo. Panonso Yehova anaona kuti kuyeretsa kunali kofunika. Ansembe ndi anthu anafooka, choncho sanali oyera pamaso pa Yehova. Kodi tinganene kuti ena a anthu a Yehova agwetsa manja awo lerolino, ngakhale kudziloŵetsa m’njira za dziko zolekerera ndi zokondetsa chuma? Ife tonse tisamalire mofulumira kulemekeza dzina la Yehova “kuyambira lero ndi mtsogolomo,” ndi chidaliro palonjezo lake lakuti: “Kuyambira lerolino ndidzakudalitsani.”​—Hagai 2:10-19; Ahebri 6:11, 12.

16. Kodi ndi ‘kugwedeza’ kotani kumene kuli pafupi kuchitika, ndipo nchiyani chidzatulukapo?

16 Patsiku limodzimodzilo, mawu a “Yehova wa makamu” anabwera kwa Hagai kachinayi ndi komaliza. Iye analongosola zimene zikuphatikizidwa pa ‘kugwedeza [Kwake] miyamba ndi dziko lapansi,’ nati: “Ndidzagubuduza mipando yachifumu ya maufumu, ndidzawononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magareta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wake.” (Hagai 2:6, 21, 22) Choncho ‘kugwedeza’ kudzafika pachimake pamene Yehova adzayeretseratu dziko lapansi pa Armagedo. Panthaŵiyo “zofunika za amitundu onse” zidzakhala zitafika, kudzapanga maziko a chitaganya cha anthu a m’dziko latsopano. Ndi zifukwa zabwino chotani nanga zosangalalira ndi kutamanda Yehova!​—Hagai 2:7; Chivumbulutso 19:6, 7; 21:1-4.

17. Kodi Yesu waikidwa motani monga “mphete yosindikizira”?

17 Potsiriza ulosi wake, Hagai akulemba kuti: “Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele . . . , ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu.” (Hagai 2:23) Kristu Yesu tsopano ndiye Mfumu Yaumesiya ndi Mkulu wa Ansembe wophiphiritsira wa Yehova, amene akuchitira pamodzi kumwamba ntchito imene Kazembe Zerubabele ndi Mkulu wa Ansembe Yoswa anali kuichita payekhapayekha m’Yerusalemu wapadziko lapansi. Monga mphete yosindikizira yalamulo padzanja lamanja la Yehova, Yesu ndiye wakhala “Eya” monga chiŵiya cha Yehova chokwaniritsira “malonjezano a Mulungu” ambiri. (2 Akorinto 1:20; Aefeso 3:10, 11; Chivumbulutso 19:10) Uthenga wonse waulosi wa Baibulo umagogomezera makonzedwe a Yehova a kuika Kristu monga Mfumu ndi Momboli wansembe.​—Yohane 18:37; 1 Petro 1:18, 19.

18. Kodi mawu omaliza a “Yehova wa makamu” adzakwaniritsidwa bwanji mwanjira yotsitsimula?

18 Ndithudi m’tsiku lathu lino, ulemerero waukulu kopambana umapezeka m’kachisi wowala wauzimu wa Yehova! Ndipo posachedwapa, Yehova atachotsapo dongosolo lonse la Satana, Hagai 2:9 adzakwaniritsidwanso mwanjira yosangalatsa: “M’malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.” Mtendere pomalizira pake!​—mtendere wokhalitsa ndipo wa padziko lonse, wotsimikizidwa ndi “mphete yosindikizira” ya Yehova, Kristu Yesu, “Kalonga wa Mtendere,” amene kwalembedwa ponena za iye kuti: “Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha . . . Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.” (Yesaya 9:6, 7) Ulemerero wa nyumba ya Yehova yolambiriramo udzaonekera mu ulamuliro wake wachilengedwe chonse wamtendere kwamuyaya. Tikhalebe m’nyumbayo!​—Salmo 27:4; 65:4; 84:10.

[Mawu a M’munsi]

a Onani “Opulumuka ku ‘Mbadwo Woipa’” ndi “Nthaŵi ya Kudikira” m’kope la Nsanja ya Olonda ya November 1, 1995.

Kodi Mungafotokoze?

◻ Kodi nyumba ya Yehova ‘ikudzazidwa motani ndi ulemerero’ lerolino?

◻ Kodi nchifukwa ninji kulalikira uthenga wabwino sikunakhalepo kofulumira kwambiri choncho?

◻ Kodi ndi chisonkhezero cha kulalikira mwachangu chotani chimene Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1996 likupereka?

◻ Kodi Kristu akutumikira motani monga “mphete yosindikizira” ya Yehova?

[Bokosi patsamba 15]

Kututa “Kuchokera ku Malekezero a Dziko Lapansi”

PA Yesaya 43:​6, timaŵerenga lamulo la Yehova kuti: “Usaletse; bwera nawo ana anga aamuna kuchokera kutali, ndi ana anga aakazi kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.” Lembali likukwaniritsidwa mwapadera ku Eastern Europe lerolino. Mwachitsanzo, tinene za dziko la Moldova limene kale linali lachikomyunizimu. Kumeneko kuli midzi imene theka la anthu ake tsopano ndi Mboni. Iwo ayenera kuyenda mitunda yaitali kuti akapeze gawo lolalikirako, koma akuyesayesa kuchita momwemo! Ofalitsa ambiri m’mipingo imeneyi ali mbadwa za makolo amene anawathamangitsira ku Siberia kuchiyambi cha ma 1950. Mabanja awo tsopano ali patsogolo kuchita ntchito yakututa. Pakati pa ofalitsa 12,565, pali 1,917 omwe abatizidwa chaka chathachi. Pakati pa mipingo imene iliko, 43 ili ndi ofalitsa pafupifupi 150 uliwonse, ndipo madera awonjezeka kuchokera pa anayi kufika pa asanu ndi atatu m’chaka chatsopano chautumiki.

Kuwonjezeka kwa ku Albania kulinso kwapadera. Kumeneko Mboni zokhulupirika zingapo zinapirira ulamuliro wopondereza wankhanza koposa kwa zaka ngati 50. Ambiri a iwo anaphedwa. Zimenezi zimatikumbutsa lonjezo la Yesu lakuti: “Usaope zimene uti udzamve kuŵaŵa; taona, Mdyerekezi adzaponya ena a inu m’nyumba yandende, kuti mukayesedwe . . . Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.” (Chivumbulutso 2:10; onaninso Yohane 5:​28, 29; 11:​24, 25.) Kodi tikuonanji tsopano ku Albania? Ndithudi kukwaniritsidwa kwenikweni kwa lonjezo la Yehova lopezeka pa Yesaya 60:22 lakuti: “Wamng’ono adzasanduka chikwi”! Mu 1990 wofalitsa mmodzi yekha ndiye anachitira lipoti utumiki ku Albania. Komabe, “antchito” owonjezereka ochokera ku Italy ndi maiko ena analabadira lamulo la Yesu lakuti: “Mukani, phunzitsani anthu . . . , ndi kuwabatiza.” (Mateyu 28:19; Luka 10:2) Podzafika nthaŵi ya Chikumbutso cha imfa ya Yesu mu 1996, ofalitsa 773 anali okangalika m’munda, ndipo ameneŵa anasonkhanitsa anthu 6,523 ku misokhano yawo ya Chikumbutso, kuŵirikiza chiŵerengero cha ofalitsa nthaŵi zoposa zisanu ndi zitatu! Madera akutali anachitira lipoti ziŵerengero zodabwitsa za opezekapo. Ngakhale kunalibe ofalitsa a kumaloko, mizinda ya Kukës ndi Divjakë inali ndi opezekapo 192 ndi 230. Krujë, amene ali ndi wofalitsa mmodzi yekha, anali ndi opezekapo 212. Ofalitsa 30 ku Korçë anachita lendi malo ena okhoza kuloŵetsa anthu 300. Chiŵerengero chimenecho chitadzaza nyumbayo, enanso 200 anabwezedwa popeza kunalibenso malo. Ndithudi uli munda wakucha!

Ku Romania kunabwera lipoti ili: “Pamene tinali kuchita ntchito ya kunyumba ndi nyumba, tinakumana ndi munthu amene anati ali mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo anali kukhala m’tauni ina yaing’ono imene, malinga ndi zimene tinali kudziŵa, munalibe Mboni. Anatiuza kuti kusiyapo iye kunali anthu enanso 15 amene kwa zaka zambiri akhala akuchita misonkhano pamasiku a Lachinayi ndi Sande ndi kuti anayamba kulalikira kunyumba ndi nyumba. Tsiku lotsatira tinapita ku tauni imeneyo. M’zipinda ziŵiri munali amuna, akazi, ndi ana 15 akutiyembekeza amene analandira mabuku 20 ndi magazini 20 atsopano. Tinawasonyeza mochitira maphunziro a Baibulo. Tinaimba nyimbo pamodzi ndi kuyankha mafunso awo ofunika koposa. Wotsogolera gululo anafotokoza kuti: ‘Masiku angapo apitawo, ndinapemphera kwa Yehova ndi misozi kuti atitumizire mbusa, ndipo pemphero langa layankhidwa.’ Tinakondwera kwabasi, ndipo pamene tinali kuchoka, monga mwana wamasiye amene pomalizira pake wapeza atate, iye anati: ‘Chonde musatiiŵale. Mukabwerenso kudzationa!’ Tinachita zimenezo, ndipo tsopano maphunziro a Baibulo asanu ndi aŵiri akuchitika m’tauniyo. M’magawo ambiri atsopano, ntchito imayamba bwino kwambiri ndi mabuku ofotokoza Baibulo, amene amawakonda kwambiri, ndipo zimenezi zikusonyeza kuti ntchitoyi ndi ya Mulungu.”

[Tchati patsamba 18-21]

LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 1996 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

“Zofunika za amitundu onse” zikusonkhanitsidwa m’Zisumbu za m’Nyanja (1), South America (2), Afirika (3), Asia (4), North America (5), ndi Ulaya (6)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena