Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 1/1 tsamba 6-11
  • Onse Alemekeze Yehova!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Onse Alemekeze Yehova!
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Yehova wa Makamu” Alankhula
  • Kachisi Wauzimu Waulemerero
  • “Ine Ndili Nanu”
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Manja Anu Alimbike
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mfundo Zazikulu za M’mabuku a Hagai ndi Zekariya
    Nsanja ya Olonda—2007
  • “Ndidzagwedeza Mitundu Yonse ya Anthu”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 1/1 tsamba 6-11

Onse Alemekeze Yehova!

“Lemekezani inu Yehova kummaŵa.”​—YESAYA 24:15.

1. Kodi aneneri a Yehova ankaliona motani dzina lake, mosiyana ndi maganizo otani a m’Dziko Lachikristu lerolino?

YEHOVA​—dzina lomveka la Mulungu! Mmene aneneri okhulupirika akale anasangalalira kulankhula m’dzina limenelo! Mwa chisangalalo iwo analemekeza Ambuye wawo Mfumu, Yehova, amene dzina lake limamdziŵikitsa kuti ali Wachifuno Wamkulu. (Yesaya 40:5; Yeremiya 10:6, 10; Ezekieli 36:23) Ngakhale amene amatchedwa aneneri aang’ono ankalankhula kwambiri molemekeza Yehova. Mmodzi wa ameneŵa anali Hagai. M’buku la Hagai, la mavesi 38 okha, dzina la Mulungu amaligwiritsira ntchito nthaŵi 35. Ulosi umenewu umatha mphamvu yake pamene dzina lamtengo wapatali la Yehova alichotsamo ndi kuikamo dzina laulemu la “Ambuye,” monga momwe atumwi oposa a Dziko Lachikristu alitchulira m’matembenuzidwe awo a Baibulo.​—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 11:5.

2, 3. (a) Kodi ulosi wina wochititsa chidwi wonena za kubwezeretsa Israyeli unakwaniritsidwa motani? (b) Kodi otsalira achiyuda ndi atsamwali awo anali ndi chisangalalo chotani?

2 Pa Yesaya 12:2, akugwiritsira ntchito mitundu iŵiri ya dzinalo.a Mneneriyo akulengeza kuti: “Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini [“Ya Yehova,” NW] ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.” (Onaninso Yesaya 26:4, NW.) Chotero, zaka ngati 200 Israyeli asanamasuke ku ukapolo wa ku Babulo, Ya Yehova anali kuwatsimikiza mwa mneneri wake Yesaya kuti iye anali Mpulumutsi wawo wamphamvu. Ukapolowo unali kudzayamba mu 607 kufika mu 537 B.C.E. Yesaya analembanso kuti: “Ine ndine Yehova, amene ndipanga zinthu zonse, . . . ndi kunena za Koresi, Iye ndiye mbusa wanga, ndipo adzachita zofuna zanga zonse; ndi kunena za Yerusalemu, Adzamangidwa; ndi kwa Kachisi, Maziko ako adzaikidwa.” Kodi Koresi ameneyu anali yani? Ndithudi, anali Mfumu Koresi wa Perisiya, amene anagonjetsa Babulo mu 539 B.C.E.​—Yesaya 44:24, 28.

3 Mogwirizanadi ndi mawu a Yehova olembedwa ndi Yesaya, Koresi anapereka lamulo ili kwa Israyeli wokhala muukapolo: “Aliyense mwa inu a anthu ake onse, Mulungu wake akhale naye, akwere kumka ku Yerusalemu, ndiwo m’Yuda, nakaimange nyumba ya Yehova Mulungu wa Israyeli; Iye ndiye Mulungu wokhala m’Yerusalemu.” Otsalira achiyuda achimwemwe kwambiri limodzi ndi Anetini osakhala Aisrayeli ndi ana a akapolo a Solomo anabwerera ku Yerusalemu. Anafika panthaŵi yochita Phwando la Misasa mu 537 B.C.E. ndi kupereka nsembe kwa Yehova paguwa lake. Chaka chotsatira, m’mwezi wachiŵiri, iwo anayala maziko a kachisi wachiŵiri, pakati pa chimfuu chachikulu cha chikondwerero ndi chiyamiko kwa Yehova.​—Ezara 1:1-4; 2:1, 2, 43, 55; 3:1-6, 8, 10-13.

4. Kodi Yesaya chaputala 35 ndi 55 anachitikadi motani?

4 Ulosi wa Yehova wa kubwezeretsa unali kudzakwaniritsidwa mwaulemerero ku Israyeli: “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa. . . . Anthuwo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.” “Inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, . . . ndipo chidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati chizindikiro chosatha, chimene sichidzalikhidwa.”​—Yesaya 35:1, 2; 55:12, 13.

5. Kodi nchifukwa ninji chisangalalo cha Israyeli sichinakhalitse?

5 Komabe, chisangalalo chimenecho sichinakhalitse. Anthu oyandikana nawo anafuna kuti apange mgwirizano wa chikhulupiriro choloŵana pomanga kachisiyo. Poyamba Ayuda anakana, naati: “Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israyeli, monga mfumu Koresi mfumu ya Perisiya watilamulira.” Anansi amenewo tsopano anakhala adani aukali. “Anafooketsa manja a anthu Ayuda, nawavuta pomanga.” Iwo anawanenezanso kwa Aritasasta, wotenga malo a Koresi, amene analetsa kumanga kachisiyo. (Ezara 4:1-24) Ntchitoyo inaima kwa zaka 17. Mwachisoni, Ayuda panthaŵi imeneyo anakhala ndi moyo wokondetsa chuma.

“Yehova wa Makamu” Alankhula

6. (a) Kodi Yehova anachitaponji pa mkhalidwe wa mu Israyeli? (b) Kodi nchifukwa ninji limene lingakhale tanthauzo la dzina la Hagai lili loyenerera?

6 Ngakhale zitakhala choncho, Yehova anasonyeza ‘mphamvu yake’ pothandiza Israyeli mwa kutumiza aneneri ake, makamaka Hagai ndi Zekariya, kukagalamutsa Ayuda kuti asamalire mathayo awo. Dzina la Hagai nlogwirizana ndi phwando, popeza likuoneka kuti likutanthauza “Wobadwira pa Phwando.” Moyenerera, anayamba kulosera patsiku loyamba la mwezi wa Phwando la Misasa, nthaŵi imene Ayuda anafunikira ‘kukondwera monsemo.’ (Deuteronomo 16:15) Kupyolera mwa Hagai, Yehova anapereka mauthenga anayi m’masiku 112.​—Hagai 1:1; 2:1, 10, 20.

7. Kodi mawu oyamba a Hagai ayenera kutilimbikitsa motani?

7 Poyamba ulosi wake, Hagai anati: “Atero Yehova wa makamu.” (Hagai 1:2a) Kodi “makamu” amenewo angakhale yani? Ndiwo magulu a angelo a Yehova, amene nthaŵi zina m’Baibulo amatchedwa makamu ankhondo. (Yobu 1:6; 2:1; Salmo 103:20, 21; Mateyu 26:53) Kodi sizikutilimbikitsa lerolino kuti Ambuye Mfumu Yehova iyemwini akugwiritsira ntchito makamu akumwamba osagonjetseka ameneŵa kutsogolera ntchito yathu ya kubwezeretsa kulambira koona padziko lapansi?​—Yerekezerani ndi 2 Mafumu 6:15-17.

8. Kodi ndi malingaliro otani amene anayambukira Israyeli, ndipo ndi zotulukapo zotani?

8 Kodi uthenga woyamba wa Hagai unali kunenanji? Anthu anali kunena kuti: “Nthaŵi siinafike, nthaŵi yakumanga nyumba ya Yehova.” Kumanga kachisi, kumene kunaimira kubwezeretsedwa kwa kulambira Mulungu, sikunalinso ntchito yawo yoyamba. Iwo anayamba kudzimangira nyumba zapamwamba. Kukondetsa chuma kunapha changu chawo cha kulambira Yehova. Chifukwa cha zimenezo, anachotsapo dalitso lake. Minda yawo sinatulutsenso zakudya, ndipo anasoŵa zovala za m’nthaŵi yozizira kwambiri ya chisanu. Analibenso ndalama zokwanira, ndipo kunali monga ngati ankaika ndalama m’thumba lobooka.​—Hagai 1:2b-6.

9. Kodi ndi uphungu wamphamvu ndi womangirira wotani umene Yehova anapereka?

9 Kaŵiri konse, Yehova anapereka uphungu wamphamvuwu: “Mtima wanu usamalire njira zanu.” Mwachionekere, Zerubabele, kazembe wa Yerusalemu, ndi Yoswab mkulu wa ansembe analabadira nalimbikitsa anthu onse mwamphamvu kuti ‘amvere mawu a Yehova Mulungu wawo, ndi mawu a Hagai mneneri, monga Yehova Mulungu wawo adamtuma; ndipo anthu anaopa pamaso pa Yehova.’ Ndiponso, “Hagai mthenga wa Yehova muuthenga wa Yehova ananena ndi anthu, ndi kuti, Ine ndili nanu, ati Yehova.”​—Hagai 1:5, 7-14.

10. Kodi Yehova anagwiritsira ntchito motani mphamvu yake pothandiza Israyeli?

10 Mwinamwake achikulire m’Yerusalemu analingalira kuti ulemerero wa kachisi womangidwanso udzakhala ‘wachabe’ pouyerekezera ndi uja wa kachisi woyamba. Komabe, patapita masiku ngati 51, Yehova anatuma Hagai kulengeza uthenga wachiŵiri. Iye analengeza kuti: “Limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m’dziko, ati Yehova, ndi kuchita; pakuti Ine ndili pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu; . . . musamaopa inu.” Yehova, amene panthaŵi yake anali kudzagwiritsira ntchito mphamvu yake yonse ‘kugwedeza miyamba ndi dziko lapansi,’ anatsimikizira kuti chitsutso chonse, ngakhale chiletso cha mfumu, chachotsedwapo. M’zaka zisanu anatsiriza kumanga kachisi ndi chipambano chachikulu.​—Hagai 2:3-6.

11. Kodi Mulungu anadzaza motani kachisi wachiŵiri ndi ‘ulemerero woposapo’?

11 Ndiyeno lonjezo lochititsa chidwi linakwaniritsidwa: “Zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.” (Hagai 2:7) “Zofunika” zimenezo zinali anthu osakhala Aisrayeli amene anabwera kudzalambira pakachisiyo, pakuti kachisiyo anali kusonyeza ulemerero wa kukhalapo kwake kwauchifumu. Kodi kachisiyu womangidwanso angayerekezeredwe motani ndi uja womangidwa m’tsiku la Solomo? Mneneri wa Mulungu analengeza kuti: “Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu.” (Hagai 2:9) Pakukwaniritsidwa koyamba kwa ulosiwu, kachisi womangidwanso anakhalitsa kuposa nyumba yoyambayo. Anali akalipo pamene Mesiya anaoneka mu 29 C.E. Ndiponso, adani ake ampatuko asanamuphe mu 33 C.E., Mesiya iyemwini anabweretsa ulemerero pakachisiyo pamene analalikira choonadi mmenemo.

12. Kodi akachisi aŵiri oyambawo anali ndi ntchito yanji?

12 Kachisi woyamba ndi wachiŵiri m’Yerusalemu anali ndi ntchito yaikulu kwambiri monga mthunzi wa mbali zofunika za unsembe wa Mesiya nachititsa kulambira koyera kwa Yehova kukhalabe kwamoyo padziko lapansi kufikira Mesiya ataonekeradi.​—Ahebri 10:1.

Kachisi Wauzimu Waulemerero

13. (a) Kodi ndi zinthu zotani zokhudza kachisi wauzimu zimene zinachitika kuyambira mu 29 mpaka mu 33 C.E.? (b) Kodi nsembe ya dipo ya Yesu inachita mbali yofunika iti m’zochitikazi?

13 Kodi ulosi wa Hagai wa kubwezeretsa uli ndi tanthauzo lapadera m’nthaŵi yamtsogolo mwake? Ndithudi uli nalo! Kachisi womangidwanso wa ku Yerusalemu anakhala malo apakati a kulambira konse koona padziko lapansi. Koma anachitira chithunzi kachisi wauzimu waulemerero koposa. Ameneyu anayamba kugwira ntchito mu 29 C.E. pamene, paubatizo wa Yesu mumtsinje wa Yordano, Yehova anadzoza Yesu monga Mkulu wa Ansembe, mzimu woyera nutsika pa iye monga nkhunda. (Mateyu 3:16) Yesu atatsiriza utumiki wake wa padziko lapansi mwa imfa yansembe, anamuukitsira kumwamba, kochitidwa chithunzi ndi Malo Opatulikitsa a m’kachisi, ndipo kumeneko anapereka mtengo wa nsembe yake kwa Yehova. Umenewu unakhala dipo, nuphimba machimo a ophunzira ake, ndipo patsiku la Pentekoste wa 33 C.E., unatsegula njira yowadzozera kuti akhale ansembe aang’ono m’kachisi wauzimu wa Yehova. Utumiki wawo wokhulupirika kufikira imfa m’mabwalo a kachisi padziko lapansi unali kudzachititsa kuti mtsogolo mwake akaukire kumwamba, kukapitiriza ndi unsembe wawo.

14. (a) Kodi ndi chisangalalo chotani chimene mpingo wachikristu woyambirira unali nacho pantchito yawo yachangu? (b) Nchifukwa ninji kusangalala kumeneku sikunakhalitse?

14 Ayuda olapa zikwi zambiri​—ndipo pambuyo pake Akunja​—anabwera mumpingo wachikristu umenewo, nakhala ndi phande pa kulengeza uthenga wabwino wa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu ukudzawo padziko lapansi. Patapita zaka ngati 30, mtumwi Paulo ananena kuti uthenga wabwino unali utalalikidwa “cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.” (Akolose 1:23) Koma pambuyo pa imfa ya atumwi, mpatuko waukulu kwambiri unayamba, ndipo kuunika kwa choonadi kunayamba kuzima. Chikristu chenicheni chinaphimbidwa ndi mpatuko wa Dziko Lachikristu, wozikidwa pa ziphunzitso ndi mafilosofi achikunja.​—Machitidwe 20:29, 30.

15, 16. (a) Kodi mu 1914 ulosi unakwaniritsidwa motani? (b) Kodi ndi kusonkhanitsa kotani kumene kunayamba chakumapeto kwa zaka za zana la 19 ndi kuchiyambi cha zaka za zana la 20?

15 Zaka mazana ambiri zinapita. Ndiyeno cha m’ma 1870, gulu la Akristu oona mtima linayamba kuphunzira Baibulo mozama. Mwa kusanthula Malemba, anatha kusonyeza kuti mapeto a “nthaŵi zawo za anthu akunja” anali m’chaka cha 1914. Inali nthaŵiyo pamene “nthaŵi” zisanu ndi ziŵiri zophiphiritsira (zaka 2,520 za ulamuliro wonga chilombo wa munthu) zinatha pamene Kristu Yesu​—Iye amene ali “mwini chiweruzo,” adzakhazikidwa pa mpando wachifumu kumwamba monga Mfumu Yaumesiya ya dziko lapansi. (Luka 21:24; Danieli 4:25; Ezekieli 21:26, 27) Makamaka kuyambira mu 1919, Ophunzira Baibulo ameneŵa, lerolino odziŵika monga Mboni za Yehova, akhala akufalitsa mwamphamvu uthenga wabwino wa Ufumu ukudzawo padziko lonse lapansi. Munali mu 1919 pamene zikwi zingapo za iwowa zinayankha chiitano cha kuntchito choperekedwa pamsonkhano waukulu ku Cedar Point, Ohio, U.S.A. Chiŵerengero chawo chinakula mpaka m’chaka cha 1935 pamene 56,153 anachitira lipoti utumiki wakumunda. M’chakacho, 52,465 anadya zizindikiro za mkate ndi vinyo pa Chikumbutso cha pachaka cha imfa ya Yesu, kuphiphiritsira chiyembekezo chawo cha kukakhala ansembe ndi Kristu Yesu m’mbali yakumwamba ya kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. Iwo adzatumikiranso naye monga mafumu anzake mu Ufumu wake Waumesiya.​—Luka 22:29, 30; Aroma 8:15-17.

16 Komabe, Chivumbulutso 7:4-8 ndi 14:1-4 chimasonyeza kuti chiŵerengero chonse cha Akristu odzozedwa ameneŵa ndi 144,000 basi, ndipo ambiri a iwo anasonkhanitsidwa m’zaka za zana loyamba mpatuko waukulu usanayambe. Kuyambira kumapeto kwa zaka za zana la 19 ndi kufika m’zaka za zana la 20, Yehova wakhala akutsiriza kusonkhanitsa gulu limeneli la amene akuyeretsedwa ndi madzi a Mawu ake, kuyesedwa olungama mwa chikhulupiriro m’nsembe yoteteza ya Yesu, ndiyeno potsirizira pake kusindikizidwa chizindikiro monga Akristu odzozedwa opanga chiŵerengero chonse cha 144,000.

17. (a) Kodi ndi kusonkhanitsa kotani kumene kwachitika chiyambire m’ma 1930? (b) Nchifukwa ninji pano Yohane 3:30 ali wofunika? (Onaninso Luka 7:28.)

17 Nchiyani chidzatsatira chiŵerengero chonse cha odzozedwa chitasankhidwa? Mu 1935, pamsonkhano umene unasintha zinthu ku Washington, D.C., U.S.A., panadziŵika kuti “khamu lalikulu” la pa Chivumbulutso 7:9-17 linali gulu lodzadziŵika ‘atatha’ a 144,000 ndipo adzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi la paradaiso. Atamdziŵa bwino lomwe Yesu wodzozedwayo, Yohane Mbatizi, amene chiukiriro chake chidzakhala padziko lapansi monga mmodzi wa “nkhosa zina,” anati za Mesiya: “Iyeyo ayenera kukula koma ine ndichepe.” (Yohane 1:29; 3:30; 10:16; Mateyu 11:11) Ntchito ya Yohane Mbatizi yokonzera Mesiya ophunzira inali kutha pamene Yesu tsopano anayamba kusankha chiŵerengero chomawonjezereka cha amene adzakhala a 144,000. M’ma 1930 chosiyana ndi chimenecho chinachitika. Chiŵerengero chaching’ono cha a 144,000 ndiwo ‘anaitanidwa ndi kusankhidwa’ pamene kuli kwakuti chiŵerengero cha “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” chinayamba kukula kwambiri. Khamu lalikulu limeneli likupitirizabe kuwonjezeka pamene dongosolo loipa la dziko lili pafupi kutha pa Armagedo.​—Chivumbulutso 17:14b.

18. (a) Kodi nchifukwa ninji tingayembekezere mwachidaliro kuti “mamiliyoni okhala ndi moyo tsopano sadzafa konse”? (b) Nchifukwa ninji tiyenera kulabadira Hagai 2:4 mwachangu?

18 Kuchiyambi cha ma 1920, nkhani yapoyera imene inalengezedwa ndipo yoperekedwa ndi Mboni za Yehova inali ndi mutu wakuti “Mamiliyoni Okhala Ndi Moyo Tsopano Sadzafa Konse.” Mwinamwake mawuwa anasonyeza chiyembekezo chopambanitsa panthaŵiyo. Koma lerolino mawuwo tingawanene ndi chidaliro chonse. Zonse ziŵiri kuunika kowonjezereka pa ulosi wa Baibulo ndi kusokonezeka kwa dziko lino lomafa zimasonyezadi kuti mapeto a dongosolo la Satana ali pafupi kwenikweni! Lipoti la Chikumbutso la 1996 limasonyeza kuti 12,921,933 anapezekapo, mwa amene 8,757 okha (.068 peresenti) ndiwo anasonyeza chiyembekezo chawo chakumwamba mwa kudya zizindikiro. Kubwezeretsa kulambira koona kuli pafupi kufika kumapeto. Koma tisaleke kugwiritsa ntchitoyo. Inde, Hagai 2:4 amati: “Mulimbike inu nonse anthu a m’dziko, ati Yehova, ndi kuchita; pakuti Ine ndili pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu.” Tiyeni titsimikizire kuti kukondetsa chuma kapena zinthu zakudziko kwamtundu uliwonse sikudzafooketsa changu chathu cha ntchito ya Yehova!​—1 Yohane 2:15-17.

19. Kodi tingakhale ndi phande motani pakukwaniritsidwa kwa Hagai 2:6, 7?

19 Mwaŵi wathu wa kukhala ndi phande pakukwaniritsidwa kwamakono kwa Hagai 2:6, 7 uli wosangalatsa: “Atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthaŵi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe; ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu.” Umbombo, ukatangale ndi chidani nzofala kwambiri m’dziko lino la m’zaka za zana la 20. Lilidi m’masiku ake otsiriza, ndipo Yehova wayamba kale ‘kuligwedeza’ mwa kuchititsa Mboni zake ‘kulalikira tsiku lake lakubwezera.’ (Yesaya 61:2) Kugwedeza koyamba kumeneku kudzafika pachimake pachiwonongeko cha dziko lapansi pa Armagedo, koma nthaŵiyo isanafike, Yehova akusonkhanitsa “zofunika za amitundu onse”​—anthu ofatsa ndipo onga nkhosa a padziko lapansi​—kaamba ka utumiki wake. (Yohane 6:44) “Khamu lalikulu” limeneli tsopano ‘likutumikira’ m’mabwalo apadziko lapansi a nyumba yake yolambiriramo.​—Chivumbulutso 7:9, 15.

20. Kodi chuma chamtengo wapatali koposa chimapezeka kuti?

20 Utumiki m’kachisi wauzimu wa Yehova umadzetsa mapindu amtengo wapatali kwambiri kuposa chuma chilichonse chakuthupi. (Miyambo 2:1-6; 3:13, 14; Mateyu 6:19-21) Ndiponso, Hagai 2:9 amati: “Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m’malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu.” Kodi mawuwa amatanthauzanji kwa ife lerolino? Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza.

[Mawu a M’munsi]

a Mawu akuti “Ya Yehova” amagwiritsiridwa ntchito kaamba ka chigogomezero chapadera. Onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 1, tsamba 1248.

b Yesuwa m’Ezara ndi m’mabuku ena a Baibulo.

Mafunso Obwereramo

◻ Ponena za dzina la Yehova, kodi tiyenera kutsatira chitsanzo chiti cha aneneri?

◻ Kodi mauthenga amphamvu a Yehova kwa Israyeli wobwezeretsedwa amatipatsa chilimbikitso chotani?

◻ Kodi ndi kachisi wauzimu waulemerero uti amene akugwira ntchito lerolino?

◻ Kodi ndi kusonkhanitsa kotani kumene kwachitika motsatizana bwino m’zaka za zana la 19 ndi la 20, ndi chiyembekezo chachikulu chotani?

[Zithunzi patsamba 7]

Makamu akumwamba a Yehova amatsogolera ndi kuchirikiza Mboni zake padziko lapansi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena