Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 7/1 tsamba 30-31
  • Ambuye Wowona Adza Kaamba ka Chiweruzo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ambuye Wowona Adza Kaamba ka Chiweruzo
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kunyoza Dzina la Mulungu
  • Chiweruzo ndi Kuyenga
  • Tsiku la Yehova Likubwera!
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Malaki
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Nthawi ya Kuyesedwa ndi Kusefedwa
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Ndani Adzapulumuka Tsiku la Yehova?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • “Madalitso Oti Mudzasowa Powalandirira”
    Muzikumbukira Tsiku la Yehova Nthawi Zonse
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 7/1 tsamba 30-31

Maphunziro Kuchokera ku Malemba: Malaki 1:1–4:6

Ambuye Wowona Adza Kaamba ka Chiweruzo

“KUTUMIKIRA Mulungu nkwachabe.” (Malaki 3:14) Kukaikira kotero kunanenedwa ndi anthu a Mulungu enieni pamene Malaki analosera m’zana lachisanu B.C.E. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti mu Yuda munali mikhalidwe yochititsa chisoni, makamaka pakati pa ansembe. Phindu ladyera linali cholinga chawo choyambirira. Mu mkhalidwe wachindunji ndi wokakamiza, Malaki anavumbula atsogoleri achipembedzo achinyengo amenewo ndi kuchenjeza kuti Ambuye wowona anali kubwera kaamba ka chiweruzo.​—Malaki 1:6-8; 2:6-9; 3:1.

Ulosi wa Malaki uli ndi kukwaniritsidwa m’tsiku lathu lenileni. Chotero, timachita bwino kulingalira maphunziro omwe uli nawo.

Kunyoza Dzina la Mulungu

Yehova amayembekezera anthu ake kumpatsa iye zabwino zawo zoposa. Mulungu choyamba akulongosola chikondi chake kaamba ka anthu ake. Mosasamala kanthu za icho, ansembe akunyoza dzina lake mwa kulandira kuchokera kwa anthu nyama zakhungu, zodwala, ndi zolemala kaamba ka nsembe. Yehova alibe chisangalalo mwa ansembe odzitumikira eni okha kapena m’zopereka zotsika za manja awo. Koma mosasamala kanthu za chimene iwo akuchita, “dzina [la Yehova lidzakhala] lowopsya pakati pa amitundu.”​—1:1-14.

Awo omwe ali aphunzitsi ali ndi thayo lalikulu. (Yakobo 3:1) Ansembe “anakhumudwitsa ambiri m’chilamulo.” Tero motani? Mwa kulephera kulangiza anthu mu lamulo la Mulungu ndipo mwa kusonyeza tsankho. Yehova ali moyenerera wokwiya ndi iwo, “pakuti milomo ya wansembe iyenera kusunga chidziŵitso, ndi anthu ayenera kufunafuna chilamulo pakamwa pake.”​—2:1-9.

Yehova samawona mopepuka awo osasonyeza ulemu kaamba ka kakonzedwe ka ukwati. Mosiyana ndi lamulo la Mulungu, amuna a ku Yuda adzitengera akazi achilendo. (Deuteronomo 7:3, 4) Iwo achita mwachinyengo ndi akazi a uchichepere wawo mwa kuwasudzula iwo. Yehova “adana nako kulekana,” Malaki akuchenjeza tero.​—2:10-17.

Chiweruzo ndi Kuyenga

Yehova samalekerera kosatha kuchita choipa. “Ambuye [wowona]” adzadza ku kachisiyo, wotsagana ndi “mthenga wachipangano.” Iye adzayenga ndi kuyeretsa ana a Levi. Yehova adzakhala mboni yofulumira kutsutsa obwebweta, achigololo, olumbira monama, onyenga, ndi opondereza.​—3:1-5.

Awo okana kupereka nsembe kwa Yehova akudzisautsa iwo eni. Yehova ali wosasintha. Ngati anthu osokera abwerera kwa iye, iye mwachifundo adzabwerera kwa iwo. Iwo akhala akulanda Mulungu mwa kusapereka zachikhumi ndi zopereka. Koma ngati iwo apereka za magawo khumi, Yehova amalonjeza mdalitso “wakuti adzasoweka malo a kuwulandira.” Iwo adzakhala ndi zipatso zosalephera.​—3:6-12.

Maso a Yehova ali pa anthu ake. Mulungu ali ndi mlandu ndi awo amene alankhula mawu oipa motsutsana ndi iye. Mosiyana, iye amapereka chisamaliro chapafupi kwa awo omuwopa iye. “Bukhu la chikumbutso” lidzalembedwa kaamba ka “[awo o]kumbukira dzina lake.” Anthu ake adzawona kusiyana pakati pa olungama ndi oipa.​—3:13-18.

Tsiku la Yehova Likubwera!

Tsiku la Yehova lidzatanthauza chiwonongeko chotheratu kaamba ka oipa. Tsiku la Yehova likubwera, ndipo oipa adzadyedwa monga udzu m’ng’anjo yotentha. Iwo adzalikwiridwa, osasiya ‘muzu kapena nthambi.’ Ponena za awo owopa dzina la Yehova, iwo adzasangalala ndi madalitso ochiritsa a “dzuŵa la chilungamo.” Lisanabwere tsiku lowopsa limeneli, Yehova adzatumiza mneneri Eliya kuchita ntchito yobwezeretsa.​—4:1-6.

Maphunziro kaamba ka lerolino: Pamene chikubwera ku kulambira, Yehova amafuna kuti anthu ake ampatse iye zabwino zawo zoposa. (Yerekezani ndi Mateyu 22:37, 38.) Aphunzitsi a Mawu a Mulungu ali ndi thayo la kulangiza moyenera ndi kutsogoza ena m’kulambira kowona. Timachita bwino kukumbukira kuti maso a Mulungu wa chilungamo ali pa awo omwe alephera kusonyeza ulemu woyenera kaamba ka ukwati ndi awo odzilowetsa m’kuchita choipa. Tiyeni modzichepetsa tigonjere ku kachitidwe koyenga ndi kuyeretsa ka Ambuye wowona pamene tikuyembekezera mofunitsitsa “kudza kwa tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova”!

[Bokosi patsamba 30]

MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA

○ 1:10​—Ansembe odzikonda, olakalaka ndalama anali kutumikira kaamba ka phindu laumwini. Iwo anafunsa malipiro kaamba ka ntchito zopepuka kwambiri za m’kachisi, zonga ngati kutseka zitseko kapena kuyatsa moto wa pa guwa. Nchosadabwitsa kuti Yehova ‘sanalandire zopereka zochokera m’manja awo’!

○ 1:13​—Ansembe opanda chikhulupirirowo anafikira pa kuwona nsembe kukhala mwambo wotopetsa, mtolo. Iwo ananyodola, kapena kunyoza, zinthu zopatulika za Yehova. Sitifunikira konse kulola “milomo yathu ngati ng’ombe” kuperekedwa monga kachitidwe wamba!​—Hoseya 14:2; Ahebri 13:15.

○ 2:13​—Amuna ambiri a Chiyuda anali kusudzula akazi a uchichepere wawo, mwinamwake kuti akwatire akazi akunja achichepere. Guwa la Yehova linaphimbidwa ndi misozi​—mwachiwonekere ija ya akazi okanidwa omwe anabwera ku malo oyera kutsanula chisoni chawo pamaso pa Mulungu.​—Malaki 2:11, 14, 16.

○ 3:1​—“Ambuye [wowona]” ali Yehova Mulungu, ndipo “mthenga wa chipangano” ali Yesu Kristu. Kukwaniritsidwa koyambirira kwa ulosiwo kunachitika pamene Yesu anayeretsa kachisi. (Marko 11:15-17) Ichi chinali zaka zitatu ndi theka pambuyo pa kudzozedwa monga Mfumu Yolinganizidwa. Mofananamo, zaka zitatu ndi theka pambuyo pa kuikidwa kwa Yesu monga Mfumu mu ngululu ya 1914, iye anatsagana ndi Yehova ku kachisi wauzimu ndi kupeza anthu a Mulungu ofunikira kuyengedwa ndi kuyeretsedwa.

○ 3:2, 3​—Njira yakale yoyengera inatenga nthaŵi. Chotero, woyengayo kaŵirikaŵiri “akakhala pansi,” akudikira kufikira chitsulo chosungunukacho chinawoneka monga kalilole woyeretsedwa bwino koposa ndipo iye ankakhoza kuwona chithunzi chake mwa icho. Mofananamo, Yehova wapitirizabe kuyenga anthu ake lerolino, kuchotsa ziphunzitso zodetsedwa ndi machitachita. Ichi chawathandiza iwo kusonyeza molongosoka kwakukulu chithunzi chake.​—Aefeso 5:1.

○ 4:2​—Aka kali kalongosoledwe ka madalitso a mtsogolo omwe adzasangalalidwa ndi awo owopa dzina la Mulungu. Iwo ali ndi chiyembekezo cha kusangalala m’kuwunikira kwa dzuŵa la chiyanjo cha Mulungu pamene zovutitsa zakuthupi, maganizo, ndi malingaliro zomwe zakantha banja la munthu zakhala zitachiritsidwa.​—Chibvumbulutso 21:3, 4.

○ 4:5​—Mneneri Eliya anakhala ndi moyo zaka 500 ulosi umenewu usanaperekedwe. M’zana loyamba C.E., Yesu Kristu anazindikira Yohane Mbatizi monga mzake wonenedweratu wa Eliya. (Mateyu 11:12-14; Marko 9:11-13) Ngakhale kuli tero, “Eliya” anafunikira kukhala woyambirira wa “tsiku la Yehova,” kusonyeza kukwaniritsidwa kowonjezereka m’nthaŵi ino ya “kukhalapo” kwa Kristu.​—2 Atesalonika 2:1, 2.

[Chithunzi patsamba 31]

Mkati mwa utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu anayeretsa kachisi. Mu 1918 iye anatsagana ndi Yehova ku kachisi wauzimu kukayeretsa anthu a Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena