Mutu 6
Kuulula Chinsinsi Chopatulika
1. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikaganizira masomphenya ochititsa mantha amene ali pa Chivumbulutso 1:10-17?
MTUMWI Yohane anaona masomphenya ochititsa mantha kwambiri a Yesu ali mu ulemerero wake. Sitikukayika kuti nafenso tikanaona nawo masomphenyawo, tikanachita mantha chifukwa cha kuwala kwake kwa ulemerero ndipo tikanagwa pansi monga mmene Yohane anachitira. (Chivumbulutso 1:10-17) Masomphenya odabwitsa ouziridwa amenewa, anasungidwa kuti atilimbikitse kutumikira Mulungu mwakhama masiku ano. Mofanana ndi Yohane, tiyenera kukhala odzichepetsa ndi kuyamikira kwambiri zimene masomphenyawo akutanthauza. Choncho, tonsefe tiyenera kupereka ulemu waukulu kwa Yesu, yemwe anaikidwa kukhala Mfumu, Mkulu wa Ansembe ndiponso Woweruza.—Afilipi 2:5-11.
“Woyamba ndi Wotsiriza”
2. (a) Kodi Yesu anadzitchula dzina la udindo liti? (b) Kodi Yehova ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Ine ndine woyamba ndi womaliza”? (c) Kodi dzina la udindo la Yesu lakuti “Woyamba ndi Wotsiriza” likusonyeza chiyani?
2 Komabe tiyenera kusonyeza mantha aulemu osati ngati kuopa chinthu chinachake choopsa. Mtumwi Yohane ananena mawu osonyeza kuti analimbikitsidwa ndi Yesu. Iye anati: “Ndipo anandigwira ndi dzanja lake lamanja ndi kundiuza kuti: ‘Usachite mantha. Ine ndine Woyamba ndi Wotsiriza, ndiponso wamoyo.’” (Chivumbulutso 1:17b, 18a) Palemba la Yesaya 44:6, Yehova anafotokoza moyenerera za udindo wake kuti iye ndi Mulungu wamphamvuyonse. Iye anati: “Ine ndine woyamba ndi womaliza, ndipo palibenso Mulungu kupatulapo ine.”a Pamene Yesu ananena kuti iye ndi “Woyamba ndi Wotsiriza,” sankatanthauza kuti iye ndi wofanana ndi Yehova, yemwe ndi Mlengi Wamkulu. Iye ankangogwiritsa ntchito dzina la udindo loyenerera limene Mulungu anamupatsa. Palemba la Yesaya, Yehova ankafotokoza za udindo wake wapadera monga Mulungu woona. Iye ndi Mulungu wamuyaya ndipo palibenso Mulungu wina wofanana naye. (1 Timoteyo 1:17) Palemba la Chivumbulutso, Yesu akunena za dzina la udindo limene Mulungu anamupatsa, chifukwa cha kuukitsidwa kwake kwapadera.
3. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu anali “Woyamba ndi Wotsiriza”? (b) Kodi mfundo yakuti Yesu ali ndi “makiyi a imfa ndi a Manda” ikutanthauza chiyani?
3 Yesu anali munthu “Woyamba” kuukitsidwa ndi moyo wauzimu umene sungafe. (Akolose 1:18) Komanso iye ndi “Wotsiriza” kuukitsidwa ndi Yehova mwachindunji mwanjira imeneyi. Motero, iye anakhala “wamoyo” ndipo adzakhala “ndi moyo kwamuyaya.” Panopa, iye akusangalala ndi moyo umene sungafe ngati mmene alili Atate ake, amene amatchedwa “Mulungu wamoyo.” (Chivumbulutso 7:2; Salimo 42:2) Koma kwa anthu ena onse, Yesu ndiye “kuuka ndi moyo.” (Yohane 11:25) Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, Yesu anauza Yohane kuti: “Ndinali wakufa, koma taona, ndili ndi moyo kwamuyaya, ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi a Manda.” (Chivumbulutso 1:18b) Yehova wapatsa Yesu udindo woukitsa anthu akufa. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti ali ndi makiyi otsegulira zipata za Manda.—Yerekezerani ndi Mateyu 16:18.
4. Kodi Yesu analamula Yohane kachiwiri kuti achite chiyani, ndipo ndani angapindule ndi zimene anamuuzazo?
4 Kenako Yesu analamula Yohane kachiwiri kuti alembe masomphenyawo. Iye anamuuza kuti: “Lemba zimene waona, zimene zikuchitika panopa, ndi zimene zidzachitike pambuyo pa zimenezi.” (Chivumbulutso 1:19) Kodi ndi zinthu zina ziti zosangalatsa zimene Yohane anauzidwa kuti alembe n’cholinga choti zitipindulitse?
Nyenyezi Ndiponso Zoikapo Nyale
5. Kodi Yesu anati “nyenyezi 7” ndi “zoikapo nyale 7” zikutanthauza chiyani?
5 Yohane anaona Yesu ataimirira pakati pa zoikapo nyale 7 zagolide ndipo m’dzanja lake lamanja munali nyenyezi 7. (Chivumbulutso 1:12, 13, 16) Tsopano Yesu anafotokoza kuti: “Koma za chinsinsi chopatulika cha nyenyezi 7, zimene waona m’dzanja langa lamanja, ndi za chinsinsi cha zoikapo nyale 7 zagolide, tanthauzo lake ndi ili: Nyenyezi 7, zikuimira angelo a mipingo 7, ndipo zoikapo nyale 7, zikuimira mipingo 7.”—Chivumbulutso 1:20.
6. Kodi nyenyezi 7 zikuimira chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani uthengawu ukupita kwa nyenyezi zimenezi?
6 “Nyenyezi” zikuimira “angelo a mipingo 7.” M’buku la Chivumbulutso, nyenyezi nthawi zina zimaimira angelo enieni, komabe Yesu sakanagwiritsa ntchito munthu kulemba uthenga wopita kwa angelo. Choncho, “nyenyezi” zimenezi ziyenera kuti zikuimira oyang’anira kapena kuti akulu a m’mipingo amene ali ngati opereka uthenga a Yesu.b Uthengawo ukupita kwa nyenyezi, kapena kuti akulu, chifukwa choti ali ndi udindo woyang’anira nkhosa za Yehova.—Machitidwe 20:28.
7. (a) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti mawu a Yesu opita kwa mngelo mmodzi yekha pampingo uliwonse, sakutanthauza kuti mpingo uliwonse unali ndi mkulu mmodzi yekha basi? (b) Kodi tingati nyenyezi 7 zimene zili m’dzanja lamanja la Yesu zikuimira ndani?
7 Popeza kuti Yesu analankhula ndi “mngelo” mmodzi yekha pampingo uliwonse, kodi zimenezi zikutanthauza kuti mpingo uliwonse unali ndi mkulu mmodzi basi? Ayi, chifukwa ngakhale m’nthawi ya Paulo, mpingo wa ku Efeso unali ndi akulu angapo osati mmodzi yekha. (Chivumbulutso 2:1; Machitidwe 20:17) Choncho, m’nthawi ya Yohane, pamene mauthenga anatumizidwa kwa nyenyezi 7 kuti akawawerenge m’mipingo (kuphatikizapo wa ku Efeso), nyenyezizo ziyenera kuti zinkaimira akulu onse amene ankatumikira m’mabungwe a akulu mumpingo wa Yehova wa Akhristu odzozedwa. Masiku anonso, oyang’anira amawerengera mipingo makalata amene alandira kuchokera ku Bungwe Lolamulira. M’bungweli muli oyang’anira odzozedwa omwe amatumikira Mulungu motsogoleredwa ndi Yesu. Bungwe la akulu pampingo uliwonse liyenera kuonetsetsa kuti mpingo ukutsatira malangizo onse ochokera kwa Yesu. Ndipotu malangizowo amakhala othandiza kwa anthu onse mumpingo osati kwa akulu okha.—Onani Chivumbulutso 2:11a.
8. Kodi mfundo yakuti akulu ali m’dzanja lamanja la Yesu ikutanthauza chiyani?
8 Popeza Yesu ndi Mutu wa mpingo, m’pomveka kuti akulu akutchulidwa kuti ali m’dzanja lake lamanja. Zimenezi zikutanthauza kuti iye amawatsogolera ndi kuwapatsa malangizo. (Akolose 1:18) Iye ndi M’busa Wamkulu, ndipo akulu ndi abusa aang’ono.—1 Petulo 5:2-4.
9. (a) Kodi zoikapo nyale 7 zikuimira chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani zoikapo nyalezo zili chizindikiro choyenerera? (b) Kodi mtumwi Yohane ayenera kuti anakumbukira chiyani ataona masomphenya amenewa?
9 Zoikapo nyale 7 zikuimira mipingo 7 imene Yohane anailembera uthenga wa m’buku la Chivumbulutso. Mipingoyi inali ya ku Efeso, Simuna, Pegamo, Tiyatira, Sade, Filadefiya, ndi Laodikaya. N’chifukwa chiyani zoikapo nyale zikuimira mipingo? Chifukwa choti Akhristu, kaya mpingo wonse kapena aliyense payekha, amayenera ‘kuonetsa kuwala kwawo pamaso pa anthu’ m’dziko la mdimali. (Mateyu 5:14-16) Komanso, zoikapo nyale zinali zina mwa zinthu zimene zinali m’kachisi wa Solomo. Yohane atamva kuti mipingo ikutchedwa zoikapo nyale, ayenera kuti anakumbukira kuti mpingo uliwonse wa Akhristu odzozedwa ukuimira “kachisi wa Mulungu,” malo amene mzimu wa Mulungu umakhala. (1 Akorinto 3:16) Ndiponso mofanana ndi mmene zinthu zinkakhalira pakachisi wa Ayuda, anthu amene ali mumpingo wa Akhristu odzozedwa amatumikira ngati “ansembe achifumu” m’kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. M’kachisi wakumwamba ameneyu, Yesu ndi Mkulu wa Ansembe ndipo Yehova amakhala m’Malo Oyera Koposa.—1 Petulo 2:4, 5, 9; Aheberi 3:1; 6:20; 9:9-14, 24.
Mpatuko Waukulu
10. N’chiyani chimene chinachitikira ulamuliro wachiyuda pamodzi ndi anthu ake osalapa mu 70 C.E.?
10 Pamene Yohane ankalemba buku la Chivumbulutso, Chikhristu chinali chitakhalapo kwa zaka zoposa 60. Kwa zaka 40 zoyambirira, anthu a m’chipembedzo chachiyuda ankatsutsa kwambiri Akhristu. Koma kenako mu 70 C.E., ulamuliro wachiyuda unathetsedwa ndipo Ayuda osalapa anabalalikira m’mayiko ena. Iwo analibenso dziko lawolawo. Ayuda ena anawonongedwa pamodzi ndi kachisi wa ku Yerusalemu, amene ankamuona ngati mulungu wawo.
11. N’chifukwa chiyani zinali zoyenera kuti M’busa Wamkulu achenjeze mipingo za zinthu zimene zinali zitayamba kuchitika?
11 Pamenepa n’kuti mtumwi Paulo ataneneratu kuti pakati pa Akhristu odzozedwa padzayamba mpatuko ndipo mauthenga a Yesu akusonyeza kuti pa nthawi ya ukalamba wa Yohane, mpatuko umenewu unali utayamba kale. Yohane anali womaliza pa anthu amene ankalepheretsa Satana pa ntchito yake yofuna kusocheretsa mbewu yonse ya mkazi. (2 Atesalonika 2:3-12; 2 Petulo 2:1-3; 2 Yohane 7-11) Motero, imeneyi inali nthawi yoyenerera kuti M’busa Wamkulu wa Yehova atumize uthenga kwa akulu a m’mipingo, kuwachenjeza za zinthu zimene zinali zitayamba kuchitika ndiponso kulimbikitsa anthu oona mtima kuti akhale olimba pochita chilungamo.
12. (a) Kodi mpatuko unafalikira mpaka pati Yohane atamwalira? (b) Kodi Matchalitchi Achikhristu anayamba bwanji?
12 Sitikudziwa kuti mipingo inachita chiyani itamva mfundo za m’mauthenga amene Yesu anatumiza mu 96 C.E. Koma zimene tikudziwa n’zakuti mpatuko unafalikira mofulumira kwambiri Yohane atamwalira. Anthu amene ankadzitchula kuti ndi “Akhristu” anasiya kugwiritsira ntchito dzina lakuti Yehova ndipo analichotsa m’Mabaibulo awo n’kuikamo “Ambuye” kapena “Mulungu.” Ndipo pofika m’zaka za m’ma 300 C.E., chiphunzitso chabodza choti pali milungu itatu mwa mulungu mmodzi chinali chitakhazikika m’mipingo. M’nthawi yomweyi mipingo inayamba kukhulupirira kuti pali chinthu china chimene chimakhalabe ndi moyo munthu akamwalira. Kenako, mfumu yachiroma Constantine inavomereza kuti chipembedzo chachikhristu chikhale chipembedzo chaboma ndipo zimenezi zinachititsa kuti Matchalitchi Achikhristu akhale onyenga. Kwa zaka 1,000, atsogoleri andale ankakhalanso atsogoleri a Tchalitchi, choncho zinali zosavuta kuti Matchalitchi Achikhristu amenewa akhale osiyana ndi Chikhristu choyambirira. Mafuko osiyanasiyana anasintha pang’ono zikhulupiriro zawo zachikunja kuti zigwirizane ndi Chikhristu chimenechi. Atsogoleri ambiri a Matchalitchi Achikhristu analinso atsogoleri andale ankhanza ndipo aliyense wokana kutsatira ziphunzitso zawo za mpatuko ankamupha.
13. Ngakhale kuti Yesu anachenjeza za mpatuko, n’chiyani chimene Akhristu ampatuko akhala akuchita?
13 Akhristu a mpatuko ananyalanyaza mawu onse a Yesu opita kumipingo 7. Yesu analimbikitsa Akhristu a ku Efeso kuti ayesetse kukhalanso ndi chikondi chimene anali nacho poyamba. (Chivumbulutso 2:4) Ngakhale zinali choncho, anthu a m’Matchalitchi Achikhristu sankagwirizana komanso sankakonda Yehova. Zimenezi zinawachititsa kuti aziphana koopsa pa nkhondo ndiponso azizunzana mwankhanza kwambiri. (1 Yohane 4:20) Yesu anachenjeza anthu a mumpingo wa ku Pegamo kuti apewe chiphunzitso cha mpatuko. Komabe, magulu ampatuko anayamba kuonekera ngakhale m’zaka za m’ma 100 C.E., ndipo masiku ano Matchalitchi Achikhristu, komanso magulu ampatuko, alipo ambirimbiri ndipo amangokhalira kukangana.—Chivumbulutso 2:15.
14. (a) Ngakhale kuti Yesu anachenjeza kuti tipewe kufa mwauzimu, kodi anthu amene amati ndi Akhristu amachita zotani? (b) Kodi anthu amene amati ndi Akhristu amasonyeza bwanji kuti alephera kutsatira chenjezo la Yesu loti apewe kulambira mafano ndiponso kuchita chiwerewere?
14 Yesu anauza anthu a mumpingo wa ku Sade kuti anali akufa mwauzimu. (Chivumbulutso 3:1) Mofanana ndi Akhristu a ku Sade, anthu amene ankati ndi Akhristu, anasiya mofulumira ntchito zachikhristu. Ndipo ntchito yofunika kwambiri yolalikira anaisiya m’manja mwa atsogoleri achipembedzo ochepa okha amene ankalipidwa. Yesu anachenjeza anthu a mumpingo wa ku Tiyatira kuti asiye kulambira mafano ndiponso kuchita dama. (Chivumbulutso 2:20) Koma Matchalitchi Achikhristu anayamba kuvomereza kulambira mafano, komanso anayamba kulimbikitsa mtundu wina wobisika wolambira mafano, womwe ndi kukonda kwambiri dziko lako ndiponso kukonda chuma. Ndipo ngakhale kuti nthawi zina amalalikira kuti chiwerewere n’choipa, iwo akhala akulekerera khalidwe limeneli.
15. Tikaona mawu a Yesu opita kumipingo 7, kodi n’zoonekeratu kuti Matchalitchi Achikhristu alephera kutani, nanga atsogoleri a Matchalitchiwa asonyeza kuti ndi ndani?
15 Choncho tikaona mawu a Yesu opita kumipingo 7, n’zoonekeratu kuti anthu a m’Matchalitchi Achikhristu onse alephera kukhala apadera kwa Yehova. N’zoonadi, atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu asonyeza kuti iwo ndi mbali yaikulu ya mbewu ya Satana. Ponena za atsogoleri amenewa kuti ndi ‘osamvera malamulo,’ mtumwi Paulo ananeneratu kuti ‘kukhalapo kwawo kukutheka mwa mphamvu za Satana. Adzachita ntchito iliyonse yamphamvu ndi zizindikiro zabodza ndi zodabwitsa, ndi kusalungama ndi chinyengo chilichonse.’—2 Atesalonika 2:9, 10.
16. (a) Kodi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu anasonyeza mwapadera kuti amadana ndi ndani? (b) Kodi n’chiyani chimene chinachitika m’Matchalitchi Achikhristu m’zaka za m’ma 500 C.E. mpaka m’ma 1500 C.E.? (c) Kodi zinthu zinasintha m’Matchalitchi Achikhristu anthu ena atachoka m’tchalitchi cha Katolika n’kuyambitsa zipembedzo zina?
16 Ngakhale kuti atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu, omwenso ndi atsogoleri andale, ankati ndi abusa a nkhosa za Mulungu, iwo ankadana kwambiri ndi aliyense amene ankayesetsa kulimbikitsa anthu kuti aziwerenga Baibulo kapena aliyense amene ankaulula zochita zawo zosagwirizana ndi Malemba. Mwachitsanzo, John Hus ndiponso munthu wina amene anamasulira Baibulo, dzina lake William Tyndale, anazunzidwa kwambiri mpaka kuphedwa. Pa nthawi imene kunali mdima waukulu wauzimu, m’zaka za m’ma 500 C.E. mpaka m’ma 1500 C.E., ulamuliro woipa unafika pachimake chifukwa khoti lakafukufuku la Akatolika linkachitira anthu nkhanza kwambiri. Aliyense amene sankagwirizana ndi ziphunzitso kapena ulamuliro wa tchalitchi ankamupha mwankhanza. Ndipo anthu ambirimbiri amene iwo ankawaona kuti ndi ogalukira ankawapha mozunza kapena kuwaotcha atawamangirira pamtengo. Choncho, cholinga cha Satana chinali chakuti awononge mwamsanga mbewu iliyonse yoona ya gulu la Mulungu limene lili ngati mkazi. Anthu atayamba kuchoka m’tchalitchi cha Katolika n’kuyambitsa zipembedzo zina (kuyambira m’chaka cha 1517), zipembedzo zoyamba kumenezo nazonso zinasonyeza khalidwe lofanana ndi la Akatolika. Anthu a m’zipembedzozi nawonso anakhala ndi mlandu wamagazi chifukwa ankapha aliyense amene ankayesetsa kukhala wokhulupirika kwa Mulungu ndi kwa Khristu. N’zoonadi, “magazi a oyera” anakhetsedwa kwambiri padziko lapansi.—Chivumbulutso 16:6; Yerekezerani ndi Mateyu 23:33-36.
Mbewu Inapirira
17. (a) Kodi Yesu ananeneratu za chiyani mufanizo lake la tirigu ndi namsongole? (b) Kodi chinachitika n’chiyani mu 1918, ndipo ndani anakanidwa, nanga ndani amene anaikidwa pa udindo?
17 Mufanizo lake la tirigu ndi namsongole, Yesu ananeneratu za nthawi ya mdima wauzimu umene udzakhalapo pa nthawi imene atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu azidzalamulira anthu. Komabe, pa zaka zonse zimene mpatuko wakhalapo, pakhala pakupezeka Akhristu osiyanasiyana oona ndiponso odzozedwa, ndipo Akhristu amenewa ali ngati tirigu. (Mateyu 13:24-29, 36-43) Choncho, pamene tsiku la Ambuye linayamba mu October 1914, Akhristu oona analipobe padziko lapansi. (Chivumbulutso 1:10) Zikuoneka kuti patatha zaka zitatu ndi hafu, Yehova anabwera kukachisi wake wauzimu mu 1918 kudzapereka chiweruzo. Pa nthawiyi, iye anali ndi Yesu, amene anali ngati “mthenga [wake] wa pangano.” (Malaki 3:1; Mateyu 13:47-50) Imeneyi inali nthawi yoti tsopano Mbuye akane Akhristu onse onyenga ndi kuika ‘kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kuti aziyang’anira zinthu zake zonse.’—Mateyu 7:22, 23; 24:45-47.
18. Kodi ndi “ola” liti limene linafika mu 1914, ndipo nthawi imeneyi inali yoti kapolo achite chiyani?
18 Imeneyi inalinso nthawi yoti kapolo ameneyu atsatire kwambiri zinthu zimene zinalembedwa m’mauthenga a Yesu opita kumipingo 7, monga mmene taonera kale. Mwachitsanzo, Yesu anatchula za kubwera kwake kudzaweruza mipingo, ndipo chiweruzo chimenechi chinayamba mu 1918. (Chivumbulutso 2:5, 16, 22, 23; 3:3) Iye ananena zoti adzateteza mpingo wa ku Filadefiya “pa ola la kuyesedwa, limene likubwera padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 3:10, 11) “Ola la kuyesedwa” limeneli linafika pamene tsiku la Ambuye linayamba m’chaka cha 1914, ndipo Akhristu anayesedwa kuti adziwike ngati anali okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu umene unali utangokhazikitsidwa kumene.—Yerekezerani ndi Mateyu 24:3, 9-13.
19. (a) Kodi mipingo 7 ikuimira chiyani masiku ano? (b) Kodi ndi gulu lalikulu liti limene likugwirizana ndi Akhristu odzozedwa, ndipo n’chifukwa chiyani malangizo a Yesu akukhudzanso anthu a m’gulu limeneli? (c) Kodi mauthenga a Yesu opita ku mipingo 7 ya m’nthawi ya atumwi tiyenera kuwaona bwanji?
19 Pa chifukwa chimenechi, mawu a Yesu opita kumipingo akugwira ntchito kwambiri kuyambira mu 1914. Zimenezi zikutanthauza kuti mipingo 7, ikuimira mipingo yonse ya Akhristu odzozedwa m’tsiku la Ambuye. Komanso, m’zaka 50 zapitazi kapena kuposerapo, pakhala gulu lalikulu la Akhristu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi. Gulu limeneli likugwirizana ndi Akhristu odzozedwa amene ankachitiridwa chithunzi ndi Yohane. Mmene zinthu zinalili m’mipingo 7 imene Yesu anaiyendera zikufanana ndi mmene zinthu zililinso m’mipingo masiku ano. Ndipo malangizo amene Yesu Khristu, yemwe ali mu ulemerero wake, anapereka kumipingoyo, akugwiranso ntchito mofanana kwa gulu la Akhristu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi. Zili choncho chifukwa chakuti atumiki onse a Yehova amayendera mfundo zofanana pa nkhani ya chilungamo ndiponso kukhulupirika. (Ekisodo 12:49; Akolose 3:11) Choncho, mauthenga a Yesu opita kumipingo 7 ya ku Asia Minor m’nthawi ya atumwi sikuti angokhala mbiri yochititsa chidwi basi. Kumvera kapena kusamvera malangizo amene ali m’mauthengawa ndi nkhani ya moyo kapena imfa kwa aliyense wa ife. Motero, tiyeni tiyesetse mwakhama kumvera mawu a Yesu.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “Ine ndine woyamba ndi womaliza” pa Yesaya 44:6, amasonyeza kuti Yehova yekha ndiye Mulungu. Ndipo mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “Ine ndine woyamba ndi wotsiriza” pa Chivumbulutso 1:17, amasonyeza udindo umene Yesu ali nawo.
b Mawu achigiriki akuti agʹge·los (amene amatchulidwa kuti “anʹge·los”) amatanthauza “mthenga” kapena “mngelo.” Palemba la Malaki 2:7, wansembe wachilevi akutchulidwa kuti “mthenga” (m’Chiheberi, mal·’akhʹ).
[Bokosi patsamba 32]
Nthawi Yoyesedwa Ndiponso Yoweruzidwa
Yesu anabatizidwa mumtsinje wa Yorodano ndi kudzozedwa cha mu October, m’chaka cha 29 C.E., kuti adzakhale Mfumu. Patapita zaka zitatu ndi hafu, mu 33 C.E., anabwera kukachisi wa ku Yerusalemu, ndipo anathamangitsa anthu amene anasandutsa kachisiyo phanga la achifwamba. Zimenezi zikuoneka kuti zikugwirizana ndi zaka zitatu ndi hafu zimene Yesu anakhala kumwamba ataikidwa pampando monga mfumu mu October 1914, mpaka nthawi imene anabwera kudzayendera anthu onse amene ankati ndi Akhristu. Pa nthawiyi m’pamene anayamba kupereka chiweruzo panyumba ya Mulungu. (Mateyu 21:12, 13; 1 Petulo 4:17) Kumayambiriro kwa chaka cha 1918, anthu anayamba kutsutsa kwambiri ntchito ya anthu a Yehova yokhudzana ndi Ufumu. Imeneyi inali nthawi yoyesedwa padziko lonse lapansi ndipo anthu amantha anapetedwa ndi kuponyedwa kunja. Mu May 1918, atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu anachititsa kuti akuluakulu a bungwe la Watch Tower Society amangidwe, koma patatha miyezi 9, anamasulidwa. Kenako milandu yonse imene ankawanamizira inathetsedwa. Kuyambira mu 1919 gulu la anthu a Mulungu, lomwe linali litayesedwa ndi kuyengedwa, linapita patsogolo mwachangu polengeza kuti Ufumu wa Yehova, umene wolamulira wake ndi Khristu Yesu, ndi umene udzathetse mavuto onse a anthu.—Malaki 3:1-3.
Pamene Yesu anayamba kuyendera mpingo mu 1918, atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu mosakayikira zinthu sizinawayendere bwino. Kuwonjezera pa kuzunza anthu a Mulungu, iwo anali ndi mlandu waukulu wamagazi chifukwa chothandiza mayiko amene ankamenyana pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse. (Chivumbulutso 18:21, 24) Atsogoleri azipembedzo amenewo anayamba kudalira bungwe la anthu la League of Nations kuti ndi limene lingathetse mavuto a anthu. Pofika m’chaka cha 1919, Mulungu anali atakaniratu zipembedzo zonyenga zonse pamodzi, kuphatikizapo Matchalitchi Achikhristu.
[Mapu patsamba 28, 29]
(Onani m’buku lenileni kuti mumvetse izi)
EFESO
SIMUNA
PEGAMO
TIYATIRA
SADE
FILADEFIYA
LAODIKAYA
[Zithunzi patsamba 31]
Matchalitchi Achikhristu ali ndi mlandu waukulu wamagazi chifukwa chozunza ndi kupha anthu amene ankamasulira Baibulo, kuliwerenga ngakhalenso kupezeka nalo