Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 8/1 tsamba 28-30
  • “Bwererani Kudza kwa Ine, Ndipo Ine Ndidzabwerera kwa Inu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Bwererani Kudza kwa Ine, Ndipo Ine Ndidzabwerera kwa Inu”
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zochita za Yehova Zachifundo
  • Mbuna Zobwevutsa
  • Kodi Mudzalabadira Chiitano cha Yehova?
  • Anathandizidwa Kubwerera
  • Kodi Munayamba Mwayanjanapo ndi Gulu la Yehova?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Athandizeni Kubwerera Mwamsanga
    Nsanja ya Olonda—2008
  • “Bwererani Kwa Ine”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Bwererani kwa ‘M’busa Wanu ndi Woyang’anira Moyo Wanu’
    Bwererani kwa Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 8/1 tsamba 28-30

“Bwererani Kudza kwa Ine, Ndipo Ine Ndidzabwerera kwa Inu”

BANJA lina linali kuchita masanje mwachimwemwe m’nkhalango. Ndiyeno, Peter, wamng’ono koposa pa onse, anasokera, pothamangitsa gologolo munsi mwa chitunda. Mwadzidzidzi, thambo linada bii, ndipo mvula inayamba kuvumba. Poyamba inali mvula yowaza, koma pang’ono ndi pang’ono inafikira kukhala pwatapwata. Mofulumira banjalo linatenga zinthu zawo ndi kuthaŵira kugalimoto lawo. Ndipo aliyense sanadziŵe kumene Peter anali.

Panthaŵiyo nkuti Peter akuyesayesa kubwerera kumene kunali banja. Kunali kovuta kuwona kutsogolo, ndipo njirayo pokwera chitunda inaterera ndi mvula. Mwadzidzidzi, nthaka inachita ngati kuti ikuzimiririka pansi pa mapazi ake pamene iye anagwera m’dzenje lakuya limene sanawone. Anayesa kutulukamo, koma m’mbali mwake munali moterera kwambiri.

Mvulayo inakokoloka kudzera pachitunda ndipo inadzadza dzenjelo ndi matope. Peter anali pangozi yeniyeni yakumira. Komabe atate ake anampeza namkokera kunja ndi chingwe. Pambuyo pake, Peter anakalipiridwa kwambiri chifukwa chosokera. Komano pokhala wokulungidwa m’mabulanjeti pamikono ya amake, kukalipiridwako kunali kosavuta kukulandira.

Chochitikachi chimachitira chitsanzo bwino lomwe zimene zimachitikira ena amene anali pakati pa anthu a Mulungu. Iwo agwera m’dzenje lakuya la dongosolo ili la zintu ndipo akuyesayesa mosaphula kanthu kutuluka ndi kubwerera m’ngaka ya gulu la Yehova. Nkosangalatsa chotani nanga kudziŵa kuti Yehova ngwachifundo ndipo ngwokonzekera ‘kutsitsa chingwe’ ndi kuwathandiza kubwereranso ku chisungiko!

Zochita za Yehova Zachifundo

Kalelo m’nthaŵi ya Israyeli, pamapeto akumanga kachisi, Solomo anapereka pemphero lotsegulira kachisiyo m’limene anachonderera Yehova kumvera mapembedzero olunjikitsidwa kukachisi. Kenako anati: “[Aisrayeli] akachimwira inu, popeza palibe munthu wosachimwa, ndipo mukakwiya nawo ndi kuwapereka kwa adani, . . . ndipo akakumbukira mitima yawo, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza inu m’dziko la iwo anawatenga ndende, . . . pamenepo mverani inu pemphero ndi pembedzero lawo m’mwamba mokhala inumo.”​—1 Mafumu 8:46-49.

Pempho la Solomo linayankhidwa nthaŵi zambiri m’mbiri ya Israyeli. Mobwerezabwereza, anthu a Mulungu anapambuka namsiya. Ndiyeno anazindikira mphulupulu zawo nabwerera, kumfunafuna. Ndipo Yehova anawakhululukira. (Deuteronomo 4:31; Yesaya 44:21, 22; 2 Akorinto 1:3; Yakobo 5:11) Kudzera mwa Malaki, Yehova anafotokoza mwachidule zaka chikwi za zochita zake ndi anthu Ake pamene Anati: “Kuyambira masiku a makolo anu mwapambuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa ine, ndipo ine ndidzabwerera kwa inu.”​—Malaki 3:7.

Mbuna Zobwevutsa

Monga momwe zinaliri kwa Aisrayeli, unyinji wa anthu a Mulungu lerolino amapambuka ndi kudzilekanitsa ndi gulu la Yehova. Chifukwa ninji? Ena amalondola zinthu zimene poyamba zimawonekera kukhala zosalakwa, mofanana ndi Peter wothamangitsa gologolo. Zimenezi ndizo zinachitikira Ada. Iye akusimba kuti: “Nthaŵi yamasana antchito tonsefe tinali ndi chizoloŵezi chopitira limodzi kukantini yapafupi kukadya chakudya chamasana. Choncho pamene anandiitanira kapu ya khofi titaŵeruka, ndinavomera mosavuta. Ndinalingalira kuti sindinali kugwiritsira ntchito nthaŵi imene ndinayenera kuithera pamisonkhano kapena muulaliki. Sindinazindikire kuti mwina kumeneku kukakhala kulephera kulabadira lamulo la pa 1 Akorinto 15:33.

“Posapita nthaŵi, ndinali kupita nawo kukakwera akavalo Loweruka lirilonse. Ndiyeno ndinayamba kupita nawo kuakanema ndi kunyumba za maseŵero. Zimenezo zinandipangitsa kuphonya misonkhano ina. Potsirizira pake, ndinaleka kupita kumisonkhano yonse ngakhale kukhala ndi phande m’ntchito yolalikira. Pamene ndinazindikira zimene zinali kuchitika, ndinali nditasiya kale kugwirizana ndi gulu.”

Nthaŵi zina chifukwa chingakhale tchimo lalikulu lobisika limene limachititsa munthuyo kulingalira kuti ngwosayenerera kutumikira Mulungu. (Salmo 32:3-5) Kapena munthuyo angakhumudwe ndi kanthu kena kamene kananenedwa kapena kuchitidwa ndi mabwenzi Achikristu, mosazindikira, monga momwe ananenera Solomo, kuti “palibe munthu wosachimwa.”​—1 Mafumu 8:46; Yakobo 3:2.

Ndiponso ena amalefulidwa atalandira chilango. (Ahebri 12:7, 11) Kukopeka ndi njira ya moyo yokondetsa zinthu zakuthupi kwachititsa ambiri kuleka kutumikira Mulungu. Kaŵirikaŵiri, pofunafuna chipambano chaudziko, iwo adzitanganitsa kwambiri ndi ntchito yakudziko kotero kuti miyoyo yawo yakhala yopanda mpata wotumikirira Mulungu. (Mateyu 13:4-9; 1 Timoteo 6:9, 10) Kodi mkhalidwe wa anthu otero ngwosatheka kuwongokera?

Kodi Mudzalabadira Chiitano cha Yehova?

Panthaŵi ina Yesu ananena kanthu kena kamene kanali kovuta kumvetsetsa, ndipo ena anakhumudwa. Cholembedwa chimati: “Ambiri a akuphunzira ake anabwerera m’mbuyo, ndipo sanayendayendanso ndi iye.” Koma sionse amene anakhumudwa. Cholembedwa cha Baibulocho chikupitiriza kuti: “Yesu anati kwa khumi ndi aŵiriwo, Nanga inunso mufuna kuchoka? Simoni Petro anamyankha iye, Ambuye, tidzamuka kwa yani? Inu muli nawo mawu a moyo wosatha.” (Yohane 6:66-68) Atumwi a Yesu mwanzeru anazindikira kuti kusiya Yesu kukatanthauza tsoka.

Ena amene amagwa amafikira pakunena zofananazo m’kupita kwa nthaŵi. Amadzazindikira kuti kusiya gulu la Mulungu kunali njira yaupandu ndi kuti kuli kokha kwa Yehova ndi Kristu kumene adzapeza mawu otsogolera kumoyo. Atangozindikira zimenezo, ayeneranso kuzindikira kuti sikuli m’mbuyo mwa alendo kudzipendanso, kupempha chikhululukiro kwa Yehova, ndi kubwerera kwa iye. Anali Yehova mwiniyo amene anapereka chiitano chakuti: “Bwererani kudza kwa ine, ndipo ine ndidzabwerera kwa inu.”​—Malaki 3:7.

Kunena zowona, kodi nkuti kumene Mkristu weniweni angapeze chimwemwe kusiyapo kutumikira Yehova? Ngati munthu abwevuka pambuyo pa kukhala chiŵalo cha gulu la Mulungu kwa nthaŵi yakutiyakuti, kodi nchiyani chimene chimyembekezera kunjako kudziko? Mofulumira adzazindikira kuti tsopano wakhala chiŵalo cha dziko limene likukhala lachiwawa mowonjezerekawonjezereka. Adzapeza kuti ngwoloŵetsedwa m’dongosolo la zinthu lodzala chinyengo, mabodza, ukatangale, ndi chisembwere, dziko laupandu ndi losakondweretsa longa dzenje lamatope limene linaika paupandu moyo wa Peter wachichepereyo. Pamene afika pakuzindikira nadziŵa kuti moyo wake wamuyaya uli paupandu, sayenera kutaya nthaŵi kufunafuna chithandizo chodziwonjolera kumkhalidwewo. Komatu kubwerera kungakhale kovuta.

Kodi inu munayesayesa kubwerera kwa Yehova koma munakupeza kukhala kovuta? Pamenepo dziŵani kuti mufunikira chithandizo. Ndipo tsimikizirani kuti abale anu ndi alongo m’gulu la Mulungu ngofunitsitsa kukuthandizani. Koma mudzafunikira kupanga kuyesayesa kuti musonyeze Yehova chikhumbo chanu. Ndinthaŵi ‘yakukumbukira mtima wanu’ ndi ‘kubwereradi kwa Yehova.’​—1 Mafumu 8:47.

Anathandizidwa Kubwerera

Ada akufotokoza zimene zinamthandiza kubwerera kwa Yehova kuti: “Pathaŵi yeniyeni yoyenerera, mlongo amene ankachititsa phunziro kwa ine anandiitanira kupita naye kumsonkhano wadera. Analidi wokoma mtima! Ndipo sananditonze mpang’ono pomwe! Iye anandisonyeza chikondi chachikulu. Panali patapita chaka kuyambira pamene ndinafika pamsokhano wanga womalizira, koma ndinali kumasinkhasinkha pakupanda pake kwa dziko ndi chenicheni chakuti, kumbuyo kwa zokopa zachiphamaso kunali chisoni chokhachokha, kugwiritsidwa mwala, ndi chisembwere. Choncho ndinasankha kupita kumsonkhano wadera. Nditaloŵa m’nyumba yamaseŵero kumene unachitikira, ndinapita kukakhala mumzera wa mipando womalizira ndi kudzibisa mumdima. Sindinafune abale kundiwona ndi kundifunsa mafunso.

“Komabe, programuyo inapereka uphungu umene ndinafunikira kwambiri. Pamene inatha, ndinali wofunitsitsa osati kokha kubwerera kwa anthu a Yehova komanso kudzipereka kwa iye ndi mtima wanga wonse. Abale anandilandira ndi manja aŵiri ndipo ‘mwana woloŵerera’ anabweranso.” (Luka 15:11-24) Zonsezo zinachitika kalekale, ndipo Ada tsopano wakhala muutumiki wanthaŵi yonse kwa zaka zoposa 25.

Nkhani ya munthu wina amene anasokera inakhala ndi zotulukapo zafanana zokondweretsa. Akulu ena anapatsa José uphungu umene unazikidwa kwambiri pamalingaliro awoawo mmalo mwa malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo. José, pokhala wolefulidwa maganizo ndi woipidwa, anakhala wosakangalika m’kupita kwa nthaŵi. Kwazaka zisanu ndi zitatu anali wolekanitsidwa ndi anthu a Mulungu, ndipo m’nthaŵi imeneyo anakwatira wosakhulupirira nakhala ndi ana amene mmodzi wa iwo anamlola kubatizidwa m’Tchalitchi cha Katolika.

Pomalizira pake, anathandizidwa pamene woyang’anira dera anakachita maulendo a ubusa pa iye nalimbikitsa akulu kuchita chimodzimodzi. Anabwezeretsedwa ndipo anakondwera kuwona mkazi wake akukhala ndi chikondwerero m’chowonadi. Pakali pano José akutumikira monga mkulu mumpingo. Monga momwe zokumana nazo ziŵirizi zikusonyezera, Yehova samamana madalitso anthu amene amalabadira chiitano chake chachikondi chakubwerera.

Komabe, kuti apeze madalitso otero, choyamba munthuyo ayenera kuyamikira chithandizo choperekedwa ndi kuchilabadira. M’mipingo yochuluka abale amakumbukira amene akhala osakangalika ndi kuwachezetsa nthaŵi ndi nthaŵi, kuyesa kuwathandiza. Kulabadira chithandizo chotero kumasonyeza chiyamikiro kaamba ka chifundo cha Yehova.​—Yakobo 5:19, 20.

Kunena zowona, ino ndiyo nthaŵi yakulabadira chiitano cha Yehova chakuti: “Bwererani kudza kwa ine.” (Malaki 3:7; Yesaya 1:18) Musazengereze. Zochitika zadziko zikuyenda mofulumira kwambiri. Malo okhala abwino koposa m’nthaŵi zowopsa zimene ziri patsogolopa ali m’kati mwa gulu la Yehova, losungika motetezeredwa ndi iye. Awo okha amene amabisala mwa Yehova ndiwo ali ndi chiyembekezo cholimba chakubisidwa kumkwiyo wake patsiku lalikulu laukali wake.​—Zefaniya 2:2, 3.

[Chithunzi patsamba 30]

Kodi mudzalabadira chiitano cha Yehova chakuti, “Bwererani kudza kwa ine”?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena