Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lff phunziro 36
  • Muzichita Zinthu Zonse Moona Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzichita Zinthu Zonse Moona Mtima
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • FUFUZANI MOZAMA
  • ZOMWE TAPHUNZIRA
  • ONANI ZINANSO
  • Muzichita Zinthu Zonse Mwachilungamo
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Chitani Zinthu Zonse Moona Mtima
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kuona Mtima N’kopindulitsa
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Kodi Ubwino Wopewa Chinyengo Ndi Wotani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff phunziro 36
Phunziro 36. Munthu akusainira chikalata chinachake.

PHUNZIRO 36

Muzichita Zinthu Zonse Moona Mtima

Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa

Aliyense amafuna kukhala ndi anzake amene amachita zinthu moona mtima. Nayenso Yehova amafuna kuti anzake azichita zinthu moona mtima. Koma kuchita zimenezi si kophweka chifukwa tikukhala m’dziko limene anthu ambiri sachita zinthu moona mtima. Ndiye kodi timapindula bwanji chifukwa chochita zinthu zonse moona mtima?

1. N’chifukwa chiyani kuchita zinthu moona mtima n’kofunika kwambiri?

Tikamachita zinthu moona mtima timasonyeza kuti timakonda ndi kulemekeza Yehova. Taganizirani izi: Yehova amadziwa chilichonse chomwe tikuganiza komanso zimene tikuchita. (Aheberi 4:13) Iye amaona tikamachita zinthu moona mtima ndipo amayamikira kwambiri. Mawu ake amanena kuti: “Munthu wochita zachiphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.”​—Miyambo 3:32.

2. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timachita zinthu moona mtima?

Yehova amafuna kuti ‘tizilankhula zoona zokhazokha.’ (Zekariya 8:16, 17) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Timayesetsa kupewa kunena bodza tikamalankhulana ndi anthu am’banja lathu, ogwira nawo ntchito, abale ndi alongo mumpingo kapenanso akuluakulu a boma. Anthu oona mtima sabera anthu ena kapena kuwapusitsa. (Werengani Miyambo 24:28 ndi Aefeso 4:28.) Komanso anthu oona mtima sazemba misonkho. (Aroma 13:5-7) Choncho, tiyenera kuyesetsa “kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheberi 13:18.

3. Kodi timapindula bwanji tikamachita zinthu moona mtima?

Tikamachita zinthu moona mtima nthawi zonse, anthu amayamba kutikhulupirira. Zimenezi zimathandizanso kuti anthu onse azisangalala mumpingo ngati mmene zimakhalira m’banja. Komanso timakhala ndi chikumbumtima choyera. Tikamachita zinthu moona mtima ‘timakometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu.’ Anthu amene satumikira Mulungu akamationa tikuchita zinthu moona mtima angakopeke n’kuyamba kuphunzira zokhudza Yehova.​—Tito 2:10.

FUFUZANI MOZAMA

Onani mmene kuchita zinthu moona mtima kumasangalatsira Yehova komanso mmene kungathandizire kuti zinthu zizikuyenderani bwino. Onaninso zimene mungachite kuti muzichita zinthu moona mtima nthawi zonse.

4. Timasangalatsa Yehova tikamachita zinthu moona mtima

Werengani Salimo 44:21 ndi Malaki 3:​16, kenako mukambirane mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti si nzeru kukhulupirira kuti tingamubisire zinazake Yehova?

  • Kodi mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji tikasankha kunena zoona ngakhale pa nthawi imene kunena zoona kungakhale kovuta?

Mwana akulankhula ndi bambo ake omwe agwada. Juwisi wataikira mbali ina ya desiki n’kugwera pansi.

Ana akamanena zoona amasangalatsa makolo awo. Ifenso tikamanena zoona Yehova amasangalala

5. Muzichita zinthu moona mtima nthawi zonse

Anthu ambiri amaganiza kuti n’zosatheka kumachita zinthu moona mtima nthawi zonse. Koma onani chifukwa chake tiyenera kumachita zinthu moona mtima nthawi zonse. Onerani VIDIYO.

VIDIYO: Zimene Zimatithandiza Kukhala Osangalala​—Chikumbumtima Chabwino (2:​32)

Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Zimene Zimatithandiza Kukhala Osangalala​​—Chikumbumtima Chabwino.’ Ben ndi abwana ake akugwirana chanza pambuyo powauza moona mtima kuti wawononga mashini odula kwambiri.

Werengani Aheberi 13:​18, kenako mukambirane mmene tingachitire zinthu moona mtima . . .

  • ndi anthu am’banja lathu.

  • kuntchito kapena kusukulu.

  • pa zochitika zina.

6. Zinthu zimatiyendera bwino tikamachita zinthu moona mtima

Nthawi zina tikamachita zinthu moona mtima tikhoza kukumana ndi mavuto. Komabe, pamapeto pake timapeza madalitso. Werengani Salimo 34:12-16, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi kuchita zinthu moona mtima kungakuthandizeni bwanji?

A. Mwamuna ndi mkazi wake akucheza kwinaku akumwa khofi. B. Makaniko ali mu galaja ndipo abwana ake akumuyamikira. C. Munthu ali mugalimoto ndipo akuonetsa apolisi chiphaso chake.
  1. Amuna ndi akazi okwatirana akamachita zinthu moona mtima amakhala ndi banja losangalala

  2. Mabwana amakhulupirira kwambiri antchito amene amachita zinthu moona mtima

  3. Nzika zimene zimachita zinthu moona mtima zimakhala ndi mbiri yabwino kwa akuluakulu a boma

ZIMENE ENA AMANENA: “Mabodza ena ndi ang’onoang’ono ndiye sakhala odetsa nkhawa kwenikweni.”

  • N’chifukwa chiyani mumakhulupirira kuti Yehova amadana ndi mabodza alionse?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Yehova amafuna kuti anzake azichita zinthu zonse moona mtima.

Kubwereza

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife oona mtima?

  • N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti si nzeru kukhulupirira kuti tingamubisire zinazake Yehova?

  • N’chifukwa chiyani mukufuna kumachita zinthu moona mtima nthawi zonse?

Zolinga

ONANI ZINANSO

Kodi makolo angaphunzitse bwanji ana awo kuti azichita zinthu moona mtima?

Uzinena Zoona (1:44)

Kodi kuchita zomwe talonjeza kuli ndi ubwino wotani?

Anthu Omwe Amachita Zimene Alonjeza Amadalitsidwa (9:09)

Onani ngati m’pofunika kumaperekabe misonkho ngakhale itamagwiritsidwa ntchito molakwika.

“Kodi Muyenera Kukhoma Misonkho?” (Nsanja ya Olonda, September 1, 2011)

N’chiyani chinathandiza munthu yemwe ankachita zachinyengo kuti ayambe kuchita zinthu moona mtima?

“Ndinaphunzira Kuti Yehova Ndi Wachifundo Komanso Amakhululuka” (Nsanja ya Olonda, May 1, 2015)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena