-
Madalitso a Yehova AlemeretsaNsanja ya Olonda—1992 | December 1
-
-
Kuweruzidwa ndi ‘Ambuye Wowona’
18. (a) Kodi Yehova akuchenjeza za kudza kwa yani? (b) Kodi ndiliti pamene kuzonda kachisi kunali kudzakhalako, kodi kunaphatikizapo yani, ndipo chotulukapo kwa Israyeli chinali chiyani?
18 Yehova kupyolera mwa Malaki anachenjezanso kuti akadza kudzaweruza anthu ake. “Tawonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye [wowona] amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; tawonani akudza.” (Malaki 3:1) Kodi kudza kukachisi kolonjezedwako kunachitika liti? Pa Mateyu 11:10, Yesu anagwira mawu ulosi wa Malaki wa mthenga amene akakonza njira naugwiritsira ntchito kwa Yohane Mbatizi. (Malaki 4:5; Mateyu 11:14) Chotero mu 29 C.E., nthaŵi ya chiweruzo inafika! Kodi ndani amene anali mthenga wachiŵiri, mthenga wa chipangano amene akatsagana ndi Yehova “Ambuye wowona,” kukachisi? Yesu iyemwiniyo, ndipo kaŵiri anadza kukachisi m’Yerusalemu nauyeretsa mwamphamvu, akumatulutsa osinthana ndalama osawona mtimawo. (Marko 11:15-17; Yohane 2:14-17) Ponena za nthaŵi ya m’zaka za zana loyamba imeneyi ya chiweruzo, Yehova mwaulosi akufunsa kuti: “Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka iye?” (Malaki 3:2) Kunena zowona, Israyeli sanaime. Anazondedwa, napezedwa kukhala wopereŵera, ndipo mu 33 C.E., ngakhale kuti anali mtundu wosankhidwa wa Yehova, iye anasadzidwa.—Mateyu 23:37-39.
19. Kodi ndimnjira yotani imene otsalira anabwerera kwa Yehova m’zaka za zana loyamba, ndipo kodi analandira dalitso lotani?
19 Komabe, Malaki analembanso kuti: “Ndipo [Yehova] adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golidi ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo.” (Malaki 3:3) Mogwirizana ndi zimenezi, ngakhale kuti ochulukitsitsa odzinenera kukhala otumikira Yehova m’zaka za zana loyamba anasadzidwa, ena anayengedwa nadza kwa Yehova, napereka nsembe zolandirika. Kodi anali ayani? Amene anali atalabadira Yesu, mthenga wa chipanganoyo. Pa Pentekoste wa 33 C.E., okwanira 120 a olabadira amenewa anasonkhana pamodzi m’chipinda chapamwamba m’Yerusalemu. Atalimbikitsidwa ndi mzimu woyera, anayamba kupereka zopereka m’chilungamo, ndipo ziŵerengero zawo zinakula mofulumira. Mwamsanga, anafalikira mu Ulamuliro wonse wa Roma. (Machitidwe 2:41; 4:4; 5:14) Chotero, otsalira anabwerera kwa Yehova.—Malaki 3:7.
20. Pamene Yerusalemu ndi kachisi zinawonongedwa, kodi nchiyani chimene chinachitikira Israyeli watsopano wa Mulungu?
20 Otsalira a Israyeli amenewa, amene anadzaphatikizapo Akunja omezanitsidwa, kunena kwake titero, patsinde la Israyeli, anali “Israyeli wa Mulungu” watsopano, mtundu wopangidwa ndi Akristu odzozedwa ndi mzimu. (Agalatiya 6:16; Aroma 11:17) Mu 70 C.E., “tsiku, lotentha ngati ng’anjo” linadzera Israyeli wakuthupi pamene Yerusalemu ndi kachisi wake zinawonongedwa ndi magulu ankhondo Achiroma. (Malaki 4:1; Luka 19:41-44) Kodi nchiyani chimene chinachitikira Israyeli wauzimu wa Mulungu? Yehova anasonyeza ‘chifundo pa iwo monga momwe munthu amasonyezera chifundo mwana wake womtumikira.’ (Malaki 3:17) Mpingo Wachikristu wodzozedwawo unalabadira chenjezo lolosera la Yesu. (Mateyu 24:15, 16) Anapulumuka, ndipo madalitso a Yehova anapitirizabe kuwalemeretsa mwauzimu.
21. Kodi ndimafunso otani amene atsalabe onena za Malaki 3:1 ndi 10?
21 Ndikulemekezedwa kwa Yehova kotani nanga! Komabe, kodi ndimotani nanga, mmene Malaki 3:1 akukwaniritsidwira lerolino? Ndipo kodi Mkristu ayenera kulabadira motani chilimbikitso cha Malaki 3:10 cha kubweretsa chakhumi chonse m’nkhokwe? Tidzakambitsirana zimenezi m’nkhani yotsatira.
-
-
“Mubwere Nalo Limodzi Limodzi Lonse la Khumi ku Nyumba Yosungiramo”Nsanja ya Olonda—1992 | December 1
-
-
1. (a) M’zaka za zana lachisanu B.C.E., kodi nchiitano chotani chimene Yehova anapereka kwa anthu ake? (b) M’zaka za zana loyamba C.E., kodi nchiyani chinali chotulukapo chakudza kwa Yehova kukachisi kudzapereka chiweruzo?
M’ZAKA za zana lachisanu B.C.E., Aisrayeli anali osakhulupirika kwa Yehova. Anali ataleka kupereka zakhumi ndipo anabweretsa zoŵeta zopuwala pakachisi monga nsembe. Komabe, Yehova analonjeza kuti ngati iwo akabweretsa zakhumi zonse m’nyumba yosungira, iye akatsanulira madalitso kufikira pakasoŵa malo owaikapo. (Malaki 3:8-10) Pafupifupi zaka 500 pambuyo pake, Yehova, moimiridwa ndi Yesu monga mthenga Wake wa chipangano, anadza kukachisi ku Yerusalemu kudzapereka chiweruzo. (Malaki 3:1) Israyeli monga mtundu anapezeka kukhala wopereŵera, koma aliyense wa amene anabwerera kwa Yehova anadalitsidwa molemerera. (Malaki 3:7) Anadzozedwa kukhala ana auzimu a Mulungu, chilengo chatsopano, “Israyeli wa Mulungu.”—Agalatiya 6:16; Aroma 3:25, 26.
2. Kodi ndiliti pamene Malaki 3:1-10 anali kudzakhala ndi kukwaniritsidwa kwachiŵiri, ndipo kodi tikupemphedwa kuchitanji mogwirizana ndi zimenezi?
2 Pafupifupi zaka 1,900 pambuyo pa zimenezi, mu 1914, Yesu anaikidwa pampando wachifumu monga Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu, ndipo mawu ouziridwa mwaumulungu pa Malaki 3:1-10 anali pafupi kukwaniritsidwa kachiŵiri. Mogwirizana ndi chochitika chochititsa nthumanzi chimenechi, Akristu lerolino akupemphedwa kubweretsa chakhumi chonse m’nyumba yosungiramo. Ngati titero, nafenso tidzalandira madalitso kufikira pakasoŵa malo owaikapo.
3. Kodi ndani amene anali mthenga wokonzekera njira pamaso pa Yehova (a) m’zaka za zana loyamba? (b) nkhondo yadziko yoyamba isanaulike?
3 Ponena za kudza kwake kukachisi, Yehova anati: “Tawonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga.” (Malaki 3:1) Monga kukwaniritsidwa kwa m’zaka za zana loyamba kwa zimenezi, Yohane Mbatizi anadza ku Israyeli akumalalikira za kulapa machimo. (Marko 1:2, 3) Kodi panali ntchito yokonzekera kudza kwachiŵiri kwa Yehova kukachisi wake? Inde. M’zaka makumi ambiri nkhondo yadziko yoyamba isanaulike, Ophunzira Baibulo anawonekera pankhope ya dziko lapansi akumaphunzitsa chiphunzitso choyera cha Baibulo ndi kuulula mabodza otonza Mulungu, onga chiphunzitso cha Utatu ndi cha helo wamoto. Anachenjezanso za kufika kwa mapeto a Nthaŵi za Akunja mu 1914. Ambiri analabadira mawu a onyamula kuunika kwa chowonadi amenewa.—Salmo 43:3; Mateyu 5:14, 16.
4. Kodi ndifunso lotani limene linafunikira kuyankhidwa m’tsiku la Ambuye?
4 Chaka cha 1914 chinayambitsa nyengo imene Baibulo limatcha “tsiku la Ambuye.” (Chivumbulutso 1:10) Zochitika zosaiŵalika zinali kudzachitika mkati mwa tsiku limenelo, kuphatikizapo kudziŵika kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi kuikidwa kwa ameneyo kukhala “woyang’anira zinthu [za Ambuye wake] zonse.” (Mateyu 24:45-47) Kalelo mu 1914, matchalitchi zikwi zambiri anadzinenera kukhala Achikristu. Kodi ndigulu liti limene likazindikiridwa ndi Mbuyeyo, Yesu Kristu, monga kapolo wake wokhulupirika ndi wanzeru? Funso limenelo linali kudzayankhidwa pamene Yehova akadza kukachisi.
Kudza Kukachisi Wauzimu
5, 6. (a) Kodi nkukachisi uti kumene Yehova anadza kudzapereka chiweruzo? (b) Kodi ndichiweruzo chotani chimene Chikristu Chadziko chinalandira kwa Yehova?
5 Komabe, kodi ndikukachisi uti, kumene anadza? Mwachiwonekere sanali kachisi wakuthupi m’Yerusalemu. Wotsiriza wa akachisi amenewo anawonongedwa kalelo mu 70 C.E. Komabe, Yehova ali naye, kachisi wokulirapo amene anaphiphiritsidwa ndi wa m’Yerusalemu. Paulo analankhula za kachisi wokulirapo ameneyu nasonyeza mmene aliridi wamkulu, malo ake opatulika akumakhala kumwamba ndipo bwalo lake pano padziko lapansi. (Ahebri 9:11, 12, 24; 10:19, 20) Kuli kukachisi wamkulu wauzimu ameneyu kumene Yehova anadza kudzachita ntchito yachiweruzo.—Yerekezerani ndi Chivumbulutso 11:1; 15:8.
6 Kodi zimenezi zinachitika liti? Malinga ndi umboni wotsimikizirika umene ulipo, munali mu 1918.a Kodi chotulukapo chinali chiyani? Ponena za Chikristu Chadziko, Yehova anawona kuti chinali gulu limene manja ake anakhathamira ndi mwazi, dongosolo lachipembedzo loluluzika limene linadziloŵetsa m’chigololo ndi dziko lino, lodzigwirizanitsa ndi olemera ndi kutsendereza osauka, lophunzitsa ziphunzitso zachikunja mmalo mwakuchita kulambira koyera. (Yakobo 1:27; 4:4) Kupyolera mwa Malaki, Yehova anali atachenjeza kuti: “Ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye.” (Malaki 3:5) Chikristu Chadziko chinali chitachita zonsezi ndi zina zoipirapo. Podzafika 1919 kunali kwachiwonekere kuti Yehova anali atachiweruzira chiwonongeko limodzi ndi mbali yonse yotsala ya Babulo Wamkulu, ulamuliro wa padziko lonse wa chipembedzo chonama. Kuyambira panthaŵiyo kumkabe mtsogolo, mfuu inamka kwa owona mtima yakuti: “Tulukani m’menemo, anthu anga.”—Chivumbulutso 18:1, 4.
-