Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 5/1 tsamba 15-21
  • Ntchito Zowonjezereka Mkati mwa Kukhalapo kwa Kristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ntchito Zowonjezereka Mkati mwa Kukhalapo kwa Kristu
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mathayo Owonjezereka
  • Kusonkhanitsa Nkhosa
  • Nzika za Ufumuwo
  • Kuthandiza Mfumuyo
  • Ntchito Zowonjezereka
  • “Kapolo” Amene Ali Wokhulupirika ndi Wanzeru
    Nsanja ya Olonda—2004
  • “Ndani Kwenikweni Amene Ali Kapolo Wokhulupirika ndi Wanzeru?”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Khalani Okhulupirika kwa Khristu ndi kwa Kapolo Wake
    Nsanja ya Olonda—2007
  • “Amatsatira Mwanawankhosa” Nthawi Zonse
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 5/1 tsamba 15-21

Ntchito Zowonjezereka Mkati mwa Kukhalapo kwa Kristu

“Pomwepo mfumuyo idzanena kwa iwo a ku dzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.”​—MATEYU 25:34.

1. Kodi ndimotani mmene pa·rou·siʹa ya Kristu yakhalira monga “masiku a Nowa”?

KUKHALAPO kwa Kristu​—ha, nchochitika choyembekezeredwa kwanthaŵi yaitali chotani nanga! Nthaŵi yonga “masiku a Nowa,” imene Yesu anakamba ponena za “chimaliziro cha dongosolo la zinthu,” inafika m’chaka cha 1914. (Mateyu 24:3, 37, NW) Koma kodi kukhalapo kwa Kristu, kapena pa·rou·siʹa, kukatanthauzanji kwa otsalira odzozedwa a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”? (Mateyu 24:45) Eya, kukatanthauza kuti iwo akakhala okangalika mowonjezereka monga onyamula kuunika! Zinthu zozizwitsa zinali kudzachitika! Ntchito yosonkhanitsa yoposa ndi kalelonse inali pafupi kuyambika.

2. Kodi ndikuyeretsa kotani kumene kwachitika kukwaniritsa Malaki 3:1-5?

2 Komabe, choyamba Akristu odzozedwa ameneŵa anafunikira kuyeretsedwa. Monga momwe Malaki 3:1-5 analoserera, Yehova Mulungu ndi “mthenga [wake] wa chipangano,” Yesu Kristu, anadza kudzayang’anira kachisi wauzimu m’ngululu ya 1918. Chiweruzo chinali kudzayambira pa “nyumba ya Mulungu.” (1 Petro 4:17) Malaki 3:3 ananeneratu kuti: “[Yehova] adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golidi ndi siliva.” Inali nyengo yakuyenga ndi kuyeretsa.

3. Kodi nchifukwa ninji kunali kofunika kuti pakhale kuyeretsa kwauzimu?

3 Atapyola chiweruzo chimenechi, chomwe chinafika pachimake mu 1918, otsalira a kagulu kakapolo anayeretsedwa ku chidetso cha kudziko ndi cha chipembedzo. Kodi nchifukwa ninji Yehova anawayeretsa? Chifukwa chakuti kachisi wake wauzimu analoŵetsedwamo. Ameneŵa ndiwo makonzedwe olambirira Yehova onga kachisi pamaziko a nsembe ya chiwombolo ya Yesu Kristu. Yehova anafuna kuti kachisi wake akhale woyera kotero kuti pamene olambira ochuluka okhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi abweretsedwa kumeneko, akapeze malo kumene uchifumu wake wachilengedwe chonse ukulemekezedwa, kumene dzina lake laumulungu likuyeretsedwa, ndi kumene malamulo ake olungama akutsatiridwa. Motero, iwo akazindikira Yehova ndi kugwirizana m’kudziŵitsa zifuno zake zazikulu.

Mathayo Owonjezereka

4, 5. (a) Kodi ndimotani mmene funso la Yesu Kristu limafunira kuti aliyense wa kagulu kakapolo achitepo kanthu lerolino? (b) Kodi mawu akuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi “banja lake” ayenera kumvedwa motani? (c) Kodi ndintchito yotani imene Yesu anapatsa kapoloyo?

4 Mu 1919 kagulu kakapolo koyeretsedwa kanakhoza kuyang’ana mtsogolo kuntchito yomakulakula nthaŵi zonse. Kalelo mu 1914, Yesu Kristu, Mbuye wawo, anapata Ufumu wakumwamba. Pamene anabwerera kwa apabanja ake kudzayang’anira “banja” lake, anali wovekedwa zovala zachifumu zaulemerero, zimene analibe pamene anali pano padziko lapansi. Kodi anadzapeza chiyani? Kodi kagulu kakapolo kanali kotanganidwa ndi kusamalira zinthu za Mbuye wake? Monga kwalembedwera pa Mateyu 24:45-47, Yesu anafunsa funso limene linafuna kuti wophunzira wodzozedwa aliyense apende kudzipereka kwake kwa Mesiya wa Yehova: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang’anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthaŵi yake? Wodala kapolo amene mbuye wake, pakufika, adzampeza iye alikuchita chotero. Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang’anira zinthu zake zonse.”

5 Mosakaikira, malongosoledwe a Yesu a kapolo wokhulupirika ameneyu samayenerera munthu mmodzi aliyense. Samaterodi, koma amalongosola mpingo wonse wa odzozedwa okhulupirika a Kristu, monga gulu. Banja ndiwo otsatira a Kristu odzozedwa aliyense pa yekha. Yesu anadziŵa kuti akawagula odzozedwa ameneŵa ndi mwazi wake, chotero moyenerera anawatcha onse pamodzi monga kapolo wake. Akorinto Woyamba amati ponena za iwo: “Munagulidwa [kunena onse pamodzi] ndi mtengo wake; musakhale akapolo a anthu.” Yesu anatuma kagulu kake kakapolo kuŵalitsa kuunika kwawo kuti akope ndi kupanga ophunzira ndi kudyetsa banja lake mopita patsogolo mwakuwapatsa chakudya chauzimu panthaŵi yake.

6. Kodi kapoloyo anafupidwa motani pambuyo pa kuyang’anira kwa Yesu?

6 Kuyambira panthaŵi imene kukhalapo kwa Kristu kunayamba mpaka 1918, kagulu kakapolo, mosasamala kanthu za chidani, chizunzo, ndipo ngakhale chisokonezo, kanayesayesa kupatsa banjalo chakudya cha panthaŵi yake. Izi nzimene Mbuyeyo anapeza pamene kuyang’anira kwake kunayamba. Ambuye Yesu anakondwera, ndipo mu 1919 analengeza kagulu kokhulupirika kakapoloko kukhala kodala. Kodi mphotho yosangalatsa ya kapoloyo ya kuchita zimene Mbuye wake anamuikira kuchita inali yotani? Kukwezedwa! Indedi, mathayo okulirapo anapatsidwa kwa iye m’kupititsa patsogolo zabwino za Mbuye wake. Eya, popeza kuti tsopano Mbuyeyo anali Mfumu yakumwamba, zinthu zake zapadziko lapansi zinakhala zamtengo wapatali koposerapo.

7, 8. (a) Kodi ‘zinthu zonse’ za Mbuye nchiyani? (b) Kodi nchiyani chimene chikufunikira kwa kapoloyo kuti ayang’anire zinthuzo?

7 Chotero, kodi “zinthu zake zonse” nchiyani? Izi ndizo chuma chake chonse chauzimu padziko lapansi chimene chakhala chuma cha Kristu malinga ndi ulamuliro wake monga Mfumu yakumwamba. Ndithudi zimenezi zinaphatikizapo ntchito yakupanga ophunzira a Kristu, okhala ndi mwaŵi waukulu wakukhala oimira a Ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwawo ku mitundu yonse ya dziko.

8 Kukwezedwa koteroko kopatsidwa uyang’aniro pa zinthu zonse za Mbuye kunafuna kuti kagulu kakapoloko kapereke nthaŵi ndi chisamaliro chowonjezereka kuchita ntchito ya Ufumu, inde, ndi kuwonjezera ziŵiya zogwirira ntchitoyo. Tsopano kanali ndi munda waukulu kwambiri wogwiriramo ntchito​—dziko lonse lokhalamo anthu.

Kusonkhanitsa Nkhosa

9. Kodi nchiyani chakhala chotulukapo cha kuwonjezereka kwa ntchito za kapoloyo?

9 Motero, momvera, kagulu kakapolo wokhulupirika ndi wanzeru ka Kristu kanawonjezera ntchito zake. Chotulukapo? Omalizira odzozedwa a 144,000 anasonkhanitsidwa. Ndiyeno masomphenya a Yohane monga kwalembedwa pa Chivumbulutso 7:9-17 anakhala chenicheni chothutsa mtima ndi chosangalatsa. Makamaka kuyambira 1935 kagulu kakapolo kasangalala ndi kuchitira umboni kukwaniritsidwa kopitirizabe kwa masomphenya ameneŵa. Kuchokera kumbali zonse zadziko lapansi, “khamu lalikulu” la mamiliyoni tsopano akuloŵa m’maunyinji awo m’mabwalo a kachisi wauzimu wa Yehova monga olambira ake. Mngelo wa Yehova anauza Yohane kuti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga khamu lalikulu limeneli. Zimenezo zikutanthauza kuti palibe malire oikidwa pa chiŵerengero cha anthu amene kagulu kakapolo kadzabweretsa m’kachisi wauzimu wa Yehova. Malinga ngati khomo lili lotseguka, ntchito yowasonkhanitsa idzapitiriza.

10. Kodi kapolo akuchita ntchito yachikondi yotani lerolino?

10 Kagulu kakapolo wokhulupirika kali ndi thayo lalikulu lakusamalira chiŵerengero chomawonjezerekabe cha “nkhosa zina,” podziŵa kuti onga nkhosa ameneŵa ochokera m’mitundu yonse ali okondeka kwambiri kwa Mbuyeyo, Yesu. Kwenikwenidi, iwo ali nkhosa zake. (Yohane 10:16; Machitidwe 20:28; 1 Petro 5:2-4) Chotero pokhala ndi chikondi pa Mbuyeyo ndi nkhosazo, kagulu kakapolo kamasamalira mwachisangalalo zosoŵa zauzimu za khamu lalikulu.

11-13. Kodi prezidenti wa Watch Tower Society wapanthaŵiyo anapereka ndemanga yoyenera yotani ponena za ntchito ya kapolo?

11 Inde, mbali yaikulu ya ntchito yakapoloyo yakunyamula kuunika imaloŵetsamo kusonkhanitsa nzika zapadziko lapansi zimenezi za Ufumu wa Mulungu. Ponena za ntchito zowonjezereka nthaŵi zonse za kapolo wokhulupirika, F. W. Franz, prezidenti wa Watch Tower Society wapanthaŵiyo, ananena zotsatirazi imfa yake itayandikira mu December 1992:

12 “Yesu Kristu wagwiritsira ntchito gululi modabwitsa kwambiri nthaŵi zonse, malinga ndi zimene ndawona m’moyo wanga pazaka 99. Sali munthu wamba amene akutsogolera gululi, koma ayenera kukhala Ambuye Yesu Kristu. Popeza kuti lagwira ntchito zazikulu ndi zodabwitsa kuposa zimene tinalingalira. Lerolino tili ndi gulu limene lakula kuzungulira dziko lonse. Likugwira ntchito m’Chigawo Chadziko Chakumpoto ndi m’Chigawo Chadziko Chakum’mwera, Kum’maŵa ndi Kumadzulo. Munthu mmodzi yekha ndiye akakhoza kutheketsa chiwonjezeko chochititsa chidwi chimenechi​—Mwana wa Mulungu, amene akuyang’anira kagulu kakapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Iye wakhala akuchita mathayo ake bwino lomwe, ndipo nzimene zatheketsa chiwonjezeko chachikuluchi chimene tawona.

13 “Ntchitoyo siikuchitidwa ndi munthu mmodzi. Tili ndi gulu limene lili lateokratiki, ndipo limagwira ntchito mwanjira yateokratiki, mwanjira yotsogozedwa ndi Mulungu. Palibe munthu, osati ngakhale amene anayambitsa Watch Tower Bible and Tract Society, akhoza kudzinenera kapena ena kunena kuti ndiye wachititsa zimene zakwaniritsidwa padziko lonse lapansi. Zilidi chozizwitsa.” Kodi onsewo amene ali a khamu lalikulu sakuvomereza ndi mtima wonse mawu amenewo a malemu Mbale Franz? Indedi, iwo alidi oyamikira koposa ntchito zowonjezereka za kapolo wokhulupirika.

Nzika za Ufumuwo

14, 15. (a) Kodi Yesu anachitira fanizo chiyani m’fanizo la matalente (Mateyu 25:14-30)? (b) Moyenerera, kodi chikutsatira nchiyani m’Mateyu chaputala 25?

14 M’Mateyu chaputala 25, fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi limalongosola ntchito yaikulu imeneyi yosonkhanitsa nzika zapadziko lapansi za Ufumu wa Mulungu. M’fanizo losimbidwa poyamba pake, lija la matalente, Yesu akuchitira fanizo kuti ophunzira odzozedwa amene akuyembekezera kudzalamulira naye mu Ufumu wake wakumwamba ayenera kugwira ntchito kuti awonjezere zinthu zake zapadziko lapansi. Chotero moyenerera, m’fanizo lotsatira, Yesu akutchula zofunikira kwa awo ofuna kukhala nzika za Ufumu wake wakumwamba.

15 Tamverani mawu ake pa Mateyu 25:31-33: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere.”

16. Kodi mitundu ikusonkhanitsidwa motani ndipo anthu akulekanitsidwa motani?

16 Yesu anafika muulemerero wake mu 1914. Kuyamba uchamuna wake, iye, pamodzi ndi angelo ake onse, anaukira ndi kupitikitsa adani ake auchiŵanda kumwamba. Zimene zikutsatira m’fanizo lake zimatithandiza kuzindikira kuti kukhala pansi kwa Yesu pachimpando chaulemerero kumatanthauza kukhala pamalo a chiweruzo mkati mwa kukhalapo kwake. Kusonkhanitsidwa kwa mitundu yonse pamaso pake kumatanthauza kuti Yesu akuchita ndi amitundu monga oyembekezeredwa kukhala nkhosa zake, kunena m’mawu ophiphiritsira. Ndigulu lokhalamo nkhosa ndi mbuzi. Pamene kuli kwakuti kungatenge maola okha a tsiku kulekanitsa nkhosa ndi mbuzi m’gulu lenileni, kulekanitsa kwa padziko lonse kwa anthu okhala ndi ufulu wakusankha kumatenga nthaŵi yaitali kuposapo. Chifukwa nchakuti kulekanitsako kumadalira pa njira ya munthu aliyense payekha yakachitidwe ka zinthu.

17. Kodi nchifukwa ninji mkhalidwe lerolino uli wowopsa kwa anthu onse?

17 M’fanizolo, Mfumu Mbusayo akuika onga nkhosa kudzanja lake lamanja ndi onga mbuzi kumanzere kwake. Mbali ya kulamanja ndiyo chiweruzo chokhala ndi chotulukapo chabwino​—moyo wosatha. Mbali yakumanzere imatanthauza chiweruzo choipa​—chiwonongeko chamuyaya. Chigamulo cha Mfumu pankhaniyo chili ndi zotulukapo zochititsa mantha.

18. Kodi nchifukwa ninji kusawoneka kwa Mfumuyo sikuli chodzikhululukira kwa aliyense?

18 Kusawoneka kwa Mwana wa munthu wolamulirayo mkati mwa kukhalapo kwake, kapena pa·rou·siʹa, sikumapereka chodzikhulukira kwa aliyense. Onga nkhosa owonjezerekawonjezereka lerolino akugwirizana ndi kagulu kakapolo m’kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu padziko lonse, akumaŵalitsa kuunika kwawo. Ndithudi, kuchitira umboni kwawo kwafikira ngondya zakutali za dziko lapansi.​—Mateyu 24:14.

19. Kodi ndimikhalidwe yotani ya kagulu kankhosa imene yachitiridwa fanizo m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi?

19 Kodi nchifukwa ninji Mfumu Mbusayo akufupa akagulu ka nkhosa ndi mtsogolo modalitsika? Chifukwa cha chichilikizo chawo cha mtima wonse pa ntchito yakulalikira Ufumu ndi kukoma mtima kumene amakusonyeza kwa abale ake odzozedwa, zimene Yesu akuwona kukhala zikuchitidwa kwa iyemwini. Chifukwa chake, Mwana wa munthu wachifumuyo akuti kwa iwo: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.”​—Mateyu 25:34; 28:19, 20.

Kuthandiza Mfumuyo

20, 21. Kodi nkhosa zimapereka umboni wotani wakuti zili kumbali ya Ufumuwo?

20 Onani kuti pamene Mfumu iitana nkhosa zimenezi kulandira malo apadziko lapansi a Ufumu wa Mulungu, iwo akudabwa. Aifunsa kuti: ‘Ambuye, kodi tinakuchitirani liti zinthu zonsezi?’ Iyo iyankha kuti: “Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang’onong’ono awa, munandichitira ichi ine.” (Mateyu 25:40) Pamene Yesu anawonekera kwa Mariya wa Magadala patsiku limene anaukitsidwa, ananena za abale ake auzimu pamene anati kwa iye: “Pita kwa abale anga.” (Yohane 20:17) M’nthaŵi yakukhalapo kwake kosawoneka, Yesu ali ndi otsalira a abale ake auzimu a 144,000 oŵerengeka okha okhalabe ndi moyo padziko lapansi.

21 Popeza kuti Yesu sakuwoneka kumwambako, anthu onga nkhosa amamchitira zinthu zachikondi zimenezi kokha mwanjira yosakhala yachindunji. Iwo amamuwona pampando wake wachifumu kokha ndi maso awo achikhulupiriro. Yesu amayamikira zoyesayesa zonse zimene amachita kuthandiza abale ake auzimu, amene adzakhala oloŵa nyumba anzake akumwamba. Zimene zimachitidwa kwa abale ake akuziwona kukhala zikuchitidwa kwa iye mwiniyo. Onga nkhosawo modzifunira amachita zabwino kwa abale a Kristu chifukwa chakuti amadziŵa kuti iwo alidi abale ake. Amazindikira kuti abale auzimu a Kristu ali oimira a Ufumu wa Yehova, ndipo amafuna kupereka umboni wamphamvu wakuti akugwirizana nawo pakuchilikiza Ufumuwo.

22. Kodi kagulu kankhosa kakupatsidwa mphotho yanji? (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 7:14-17.)

22 Yehova anawoneratu kuti kagulu ka onga nkhosa kameneka kakakhalapo mkati mwa nthaŵi ino ya kukhalapo kwa Mwana wake, ndipo iye wawasungira mphotho yabwino koposa! Khamu lalikulu lidzalandira madalitso a mtendere pompano padziko lapansi mkati mwa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kosangalatsa kwa Mfumu ya Yehova, Yesu Kristu.

23. Kodi ndimwanjira yotani imene nkhosa zimathandizira abale a Mfumuyo modziŵa bwino?

23 Pamene tipenda maulosi a Baibulo amene akukwaniritsidwa panthaŵi ya kukhalapo kwa Kristu, ndiponso ndi fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi, kodi tikuwona chiyani? Izi: Kuchitira zabwino mosadziŵa ndi mwamwaŵi aliyense wa abale auzimu a Mfumuyo sikumene kumachititsa munthu kukhala nkhosa yokhala ndi kaimidwe kolungama pamaso pa Mulungu ndi Mfumu yake. Awo a kagulu kankhosa amadziŵa zimene amachita, ngakhale kuti samawona Mfumu yolamulirayo ndi maso awo akuthupi. Amayesayesa kuthandiza abale a Mfumu amenewo osati mwanjira yakuthupi yokha komanso mwanjira yauzimu. Motani? Mwakuwathandiza m’ntchito yolalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndi mwakuchititsa maphunziro Abaibulo kuti apange ophunzira a Kristu. Motero, lerolino pali olengeza Ufumu wa Mulungu onyamula kuunika oposa mamiliyoni anayi.

Ntchito Zowonjezereka

24. Kodi ndintchito zachikondi zotani zimene zachititsa kagulu kakapolo kukhala anthu achimwemwe koposa padziko lapansi lerolino?

24 Nayi ndandanda ya zina za ntchito zabwino zochuluka za kagulu kakapolo wokhulupirika. Yoyamba, kagulu kakapolo kaikidwa kuyang’anira zinthu zonse za Mbuye​—zabwino za Ufumu wake zapadziko lapansi​—ndipo zinthuzi zikuwonjezerekabe. Yachiŵiri, kagulu kameneko kakudyetsa chakudya chauzimu osati banja lokha la odzozedwa komanso khamu lalikulu lomakulakulabe la nkhosa zina. Yachitatu, kagulu kakapolo kakutsogolera m’kuŵalitsa kuunika kwa Ufumu. Yachinayi, kuwonjezereka koposa kwa ntchito zake kuli m’ntchito yakusonkhanitsa khamu lalikulu la nkhosa zina, kuziloŵetsa m’kachisi wauzimu wa Yehova. Yachisanu, kagulu kakapoloko, ndi chichilikizo cha mtima wonse cha onga nkhosa, kakufutukula nthambi kuzungulira dziko lonse lapansi kuphatikizapo ndi kumalikulu mu United States kaamba ka kuyendetsa bwino ntchito. Ntchito zachikondi zoterozo zachititsa kagulu kakapolo kukhala anthu achimwemwe koposa padziko lapansi lerolino, ndipo achititsa mamiliyoni a anthu ena kukhalanso achimwemwe. Onsewa akupereka chithokozo kwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu, amene atsogolera ntchito zowonjezereka za kapolo wanzeruyo!

25. Kodi nkhosazo zingapitirize motani kuchilikiza kagulu kakapolo, ndipo ndi chiyembekezo chotani?

25 Kagulu kakapolo tsopano kakugwira ntchito zolimba kuposa ndi kalelonse m’mathayo ake opatsidwa ndi Mulungu. Nthaŵi yatha kale kuti “chisautso chachikulu” chiulike! (Mateyu 24:21) Nkofunika chotani nanga kuti awa amene ali nkhosa za Mulungu akhalebe kulamanja ku chiyanjo cha Mfumu Mbusayo! Pamenepo, tonsefe tipitirizetu kuchilikiza mwachangu kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Kuchita zenizeni ndiko kokha kumene posachedwapa kudzatheketsa onga nkhosawo kumva mawu osangalatsawo akuti: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.”

Kodi Mungayankhe?

◻ Kodi nkuweruza koyamba kotani kumene kunatsatira kukhala pampando wachifumu kwa Mfumuyo?

◻ Kodi ndimotani mmene lemba la Mateyu 24:45-47 linalili ndi kukwaniritsidwa kwamakono?

◻ Ponena za ntchito zowonjezereka, kodi kagulu kakapolo ndi khamu lalikulu ali oyamikira koposa kaamba ka chiyani?

◻ Kodi lemba la Mateyu 25:34-40 likukwaniritsidwa motani mkati mwa pa·rou·siʹa?

[Chithunzi patsamba 16]

Mbuye akuikizira zinthu zake zonse kwa kapolo wokhulupirika

[Chithunzi patsamba 18]

Yesu wakhala pampando wake wachifumu kuti aweruze mtundu wa anthu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena