Kuchiritsa Anthu Mozizwitsa Kwayandikira
“ZOTERE sitinaziona ndi kale lonse.” Zinatero mboni zoona ndi maso pamene Yesu anachiritsa mozizwitsa munthu wodwala manjenje. (Marko 2:12) Ndipo Yesu anachiritsanso akhungu, osalankhula, ndi opunduka, ndipo otsatira ake nawo anatero. Kodi Yesu anachita zimenezo mwa mphamvu yanji? Nanga chikhulupiriro chinachitapo mbali yanji? Kodi zochitika za m’zaka za zana loyamba zimenezi zimatiuzanji ponena za kuchiritsa kozizwitsa lerolino?—Mateyu 15:30, 31.
“Chikhulupiriro Chako Chakupulumutsa Iwe”
Lerolino ochiritsa mwachikhulupiriro amakonda kutchula mawu a Yesu pouza mkazi wina yemwe anadwala kwa zaka 12 nthenda yokha mwazi yemwe anadza kwa iye kuti amchiritse namati: “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe.” (Luka 8:43-48) Kodi mawu a Yesu anatanthauza kuti mkaziyo anachira chifukwa cha chikhulupiriro chake? Kodi chimenecho chinali chitsanzo cha “kuchiritsa mwachikhulupiriro” monga mmene amachitira lerolino?
Tikaŵerenga nkhani ya Baibuloyo mosamalitsa, tiona kuti nthaŵi zambiri Yesu ndi ophunzira ake sanali kufuna konse kuti odwalawo aziyamba asonyeza chikhulupiriro chawo asanawachiritse. Mkazi yemwe tatchula poyambayo, popanda kunena chilichonse kwa Yesu, anadza mwakachetechete chakumbuyo nakhudza chovala chake ndipo “pomwepo nthenda yake inaleka.” Tsiku lina, Yesu anachiritsa munthu wina yemwe anali mmodzi wa amene anadzammanga. Anachiritsanso ngakhale munthu wina amene sanali kudziŵa nkomwe kuti Yesu anali yani.—Luka 22:50, 51; Yohane 5:5-9, 13; 9:24-34.
Nangano chikhulupiriro chinachitapo mbali yotani? Pamene Yesu ndi ophunzira ake anali m’dera la Turo ndi Sidoni, mkazi wina wa ku Kanani anadza nafuula nati: “Mundichitire ine chifundo Ambuye, mwana wa Davide; mwana wanga wamkazi wagwidwa koopsa ndi chiŵanda.” Talingalirani kusautsika mtima kwake pamene anachonderera kuti: “Ambuye, ndithangateni ine”! Atamva chifundo, Yesu anayankha kuti: “Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira.” Ndipo mwana wake anachira “nthaŵi yomweyo.” (Mateyu 15:21-28) Mwachionekere, chikhulupiriro anali nacho, komano ndani anali nacho? Taonani kuti pano Yesu anatamanda chikhulupiriro cha mayiyo, osati cha mwana wodwalayo iyayi. Ndipo kukhulupirira chiyani? Mwa kumtchula Yesu kuti “Ambuye, Mwana wa Davide,” mkaziyo anali kuvomereza poyera kuti Yesu anali Mesiya wolonjezedwayo. Sikunali chabe kukhulupirira Mulungu kapena kukhulupirira mphamvu ya wochiritsayo. Pamene Yesu anati “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe,” anatanthauza kuti popanda kukhulupirira kuti iye ndiye Mesiya, anthu odwala sakanadza kwa iye kudzachiritsidwa.
Pazitsanzo za m’Malemba zimenezi, tikuona kuti kuchiritsa kwa Yesu kunali kosiyana kwambiri ndi zimene timaona nthaŵi zonse kapena kumva akunena lerolino. Anthuwo sanatengekepo mtima—kufuula, kuimba, kulira, kukomoka, ndi zina zotero—ndipo ngakhale Yesu sanali kuchita kunyanyuka iyayi. Ndiponso, Yesu sanalephere konse kuchiritsa odwala nkumanamizira kuti iwo analibe chikhulupiriro kapena kuti sanalipire ndalama zokwanira.
Kuchiritsa mwa Mphamvu ya Mulungu
Kodi Yesu ndi ophunzira ake anachiritsa motani? “Mphamvu ya Ambuye inali ndi Iye yakuwachiritsa,” likuyankha choncho Baibulo. (Luka 5:17) Tsiku lina atachiritsa munthu, amatero Luka 9:43, “onse anadabwa pa ukulu wake wa Mulungu.” Moyenerera, Yesu sanadzitame kuti ndiye anali wochiritsa. Panthaŵi ina anamuuza munthu yemwe anamchotsera chiŵanda kuti: “Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo.”—Marko 5:19.
Popeza Yesu ndi atumwi ake anali kuchiritsa mwa mphamvu ya Mulungu, nkosavuta kuona chifukwa chake sikunali kofunika nthaŵi zonse kuti munthu wofuna kuchiritsidwayo akhale ndi chikhulupiriro. Komabe, wochiritsayo anafunikira kukhala ndi chikhulupiriro champhamvudi. Chotero, pamene otsatira a Yesu analephera kutulutsa chiŵanda champhamvu kwambiri, Yesu anawauza chifukwa chake: “Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching’ono.”—Mateyu 17:20.
Chifuno Chochiritsira Mozizwitsa
Ngakhale Yesu anachiritsa anthu ambiri mu utumiki wake wapadziko lapansi, kwenikweni iye sanali kuchita ‘utumiki wochiritsa.’ Kuchiritsa kwake kozizwitsa—kumene sanali kulipiritsa anthu kapena kupempha nako zopereka—kunali kwachiŵiri pa cholinga chake chachikulu cha ‘kulalikira uthenga wabwino wa ufumu.’ (Mateyu 9:35) Nkhaniyo imati panthaŵi ina “Iye anawalandira, nalankhula nawo za Ufumu wa Mulungu, nachiritsa amene anasoŵa kuchiritsidwa.” (Luka 9:11) M’Mauthenga Abwino, kaŵirikaŵiri Yesu amatchedwa “Mphunzitsi” koma osati “Wochiritsa.”
Nanga nchifukwa ninji Yesu anali kuchiritsa mozizwitsa? Kwenikweni anafuna kuti anthu azindikire kuti iye anali Mesiya wolonjezedwayo. Pamene Yohane Mbatizi anaponyedwa m’ndende mosayenera, anafuna kudziŵa ngati anali atakwaniritsa zimene Mulungu anali atamtuma kuti achite. Anatuma ophunzira ake kuti akamfunse Yesu kuti: “Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina?” Imvani zimene Yesu anawauza ophunzira a Yohane: “Mukani mubwezere mawu kwa Yohane zimene muzimva ndi kuziona: akhungu alandira kuona kwawo, ndi opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ndi ogontha akumva, ndi akufa aukitsidwa, ndi kwa aumphaŵi ulalikidwa uthenga wabwino.”—Mateyu 11:2-5.
Indedi, chokhacho choti Yesu sanangochiritsa mozizwitsa komanso anachita ntchito zina zozizwitsa zolembedwa m’Mauthenga Abwino zinamdziŵikitsa kuti ndiye anali “Wakudza,” Mesiya wolonjezedwayo. Panalibenso chifukwa choti aliyense ‘ayembekezere wina.’
Kuchiritsa Kozizwitsa Lerolino?
Kodi tsopano tiyenera kuyembekezera Mulungu kusonyeza mphamvu yake mwa kuchiritsa? Iyayi. Ndi ntchito zozizwitsa zimene anachita mwa mphamvu ya Mulungu, Yesu anachotseratu chikayikiro choti ndiye anali Mesiyayo amene Mulungu analonjeza kuti adzabwera. Ntchito zamphamvu za Yesu zalembedwa m’Baibulo kuti onse aŵerenge. Palibenso chifukwa choti Mulungu asonyeze mphamvu yake mwa kubwereza ntchito zoterozo kwa mbadwo uliwonse wa anthu.
Zofunikanso kudziŵa nzakuti kuchiritsa ndi ntchito zina zozizwitsa ngoŵerengeka basi amene anazikhulupirira. Ngakhale mboni zina zoona ndi maso zozizwitsa za Yesu sizinakhulupirire kuti Atate wake wakumwamba ndiye amene anali kumchirikiza. “Angakhale adachita zizindikiro zambiri zotere pamaso pawo iwo sanakhulupirira Iye.” (Yohane 12:37) Nchifukwa chake, pambuyo polongosola mphatso zozizwitsa zosiyanasiyana—kunenera, kulankhula m’malilime, machiritso, ndi zina zotero—zimene Mulungu anapatsa anthu osiyanasiyana mumpingo wachikristu m’zaka za zana loyamba, mtumwi Paulo anamuuzira kulemba kuti: “Kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe. Pakuti ife tidziŵa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera. Koma pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe.”—1 Akorinto 12:28-31; 13:8-10.
Nzoonadi, kukhulupirira Mulungu nkofunika kuti tikhale bwino. Komabe, kuzika chikhulupiriro cha munthuwe pa malonjezo onyenga a kuchiritsa kudzangokhala kogwiritsa mwala. Ndiponso, za nthaŵi ya mapeto, Yesu anachenjeza kuti: “Akristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe.” (Mateyu 24:24) Kuwonjezera pakusaona mtima ndi chinyengo, padzaonekeranso mphamvu yauchiŵanda. Chotero, zochitika zosafotokozeka siziyenera kutidabwitsa, ndipo zimenezo sindizo maziko a chikhulupiriro chenicheni mwa Mulungu.
Popeza kuti lerolino palibe aliyense amene amachiritsa monga mmene Yesu anachitira, kodi tilibe mwaŵi? Ayi. Ndithudi, awo amene Yesu anachiritsa anadzadwalanso potsirizira pake. Onse anakalamba nkufa. Mapindu ochiritsa amene analandira anali a kanthaŵi chabe. Komabe, kuchiritsa kozizwitsa kwa Yesu kuli ndi tanthauzo lokhalitsa chifukwa kunachitira chithunzi madalitso amtsogolo.
Chotero, pambuyo popenda Mawu a Mulungu, Baibulo, Alexandre ndi Benedita, omwe tatchula poyamba paja, samakhulupiriranso kuchiritsa mwachikhulupiriro kwamakono, ndi kwa amizimu. Komabe, iwo ngotsimikiza kuti kuchiritsa kozizwitsa sikuli zinthu zimene zinangochitika kale basi. Chifukwa ninji? Mofanana ndi anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi, iwo akuyembekeza madalitso a kuchiritsa mu Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 6:10.
Sikudzakhalanso Matenda ndi Imfa
Monga mmene taonera, cholinga chachikulu cha utumiki wa Yesu sichinali kuchiritsa odwala ndi kuchita zozizwitsa zina. M’malo mwake, anapanga kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kukhala ntchito yake yaikulu. (Mateyu 9:35; Luka 4:43; 8:1) Ufumu umenewo ndi umene Mulungu adzachiritsira anthu mozizwitsa ndi kuthetsera mavuto onse amene uchimo ndi kupanda ungwiro kwachitira banja la anthu. Kodi ndi liti ndipo adzazichita motani?
Poneneratu zamtsogolo, Kristu Yesu anapatsa mtumwi wake Yohane masomphenya olosera: “Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake.” (Chivumbulutso 12:10) Umboni wonse ukusonyeza kuti kuyambira 1914 wotsutsa Mulungu kwambiri, Satana, waponyedwa kudziko lapansi, ndipo Ufumuwo tsopano ukugwira ntchito ndipo uli weniweni! Yesu walongedwa kukhala Mfumu ya Ufumu Waumesiya ndipo tsopano ngwokonzekera kusintha zinthu kwambiri padziko lapansi.
Mtsogolomu posachedwapa, boma lakumwamba la Yesu lidzalamulira anthu atsopano olungama, omwe adzakhala “dziko latsopano.” (2 Petro 3:13) Kodi mikhalidwe idzakhala yotani panthaŵiyo? Nachi chithunzi chaulemerero: “Ndinaona m’mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m’mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka . . . Ndipo [Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:1, 4
Kodi mungayerekezere mmene moyo udzakhalira pamene anthu adzachiritsidwadi mozizwitsa? “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala mmenemo, adzakhululukidwa mphulupulu zawo.” Inde, Mulungu adzachita zimene ochiritsa mwachikhulupiriro sanathepo kuchita. ‘Adzameza imfa ku nthaŵi yonse.’ Ndithudi, “Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pankhope zonse.”—Yesaya 25:8; 33:24.
[Chithunzi patsamba 7]
Mu Ufumu wa Mulungu anthu adzachiritsidwa mozizwitsa