-
Kodi Mudzakhumudwa N’kusiya Kutsatira Yesu?Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2021 | May
-
-
(3) YESU SANKACHITA NAWO MIYAMBO YAMBIRI YA CHIYUDA
Anthu ambiri anakana Yesu chifukwa’ anakana kuchita nawo miyambo ina. Kodi masiku ano zimenezi zingalepheretsenso bwanji ena kutsatira Yesu? (Onani ndime 13)d
13. Kodi n’chiyani chinalepheretsa anthu ambiri kutsatira Yesu?
13 Mu nthawi ya Yesu, ophunzira a Yohane M’batizi anadabwa kuti ophunzira a Yesu sankasala kudya. Koma Yesu anawauza kuti panalibe chifukwa choti azisalira kudya iye ali moyo. (Mat. 9:14-17) Ngakhale zinali choncho, Afarisi ndi anthu ena amene ankamutsutsa, anamudzudzula chifukwa choti sankachita nawo miyambo yawo. Iwo ankakwiya akaona kuti Yesu wachiritsa munthu patsiku la Sabata. (Maliko 3:1-6; Yoh. 9:16) Anthu amenewa ankanena kuti amasunga Sabata, koma sankaona vuto kuchita malonda m’kachisi. Ndipo anakwiya Yesu atawadzudzula chifukwa cha zimenezi. (Mat. 21:12, 13, 15) Ndiponso anthu amene Yesu anawalalikira m’sunagoge ku Nazareti, anakhumudwa chifukwa choti iye anawafotokozera nkhani za m’Malemba zimene zinasonyeza kuti iwo anali anthu odzikonda komanso opanda chikhulupiriro. (Luka 4:16, 25-30) Popeza Yesu ankachita zinthu zimene ambiri sankayembekezera, zimenezi zinawakhumudwitsa ndipo ambiri anasiya kumutsatira.—Mat. 11:16-19.
14. N’chifukwa chiyani Yesu ankadzudzula miyambo ya anthu yosemphana ndi Malemba?
14 Kodi Malemba amati chiyani? Kudzera mwa mneneri wake Yesaya, Yehova ananena kuti: “Anthu awa ayandikira kwa ine ndi pakamwa pawo pokha, ndipo andilemekeza ndi milomo yawo yokha koma mtima wawo auika kutali ndi ine, ndiponso amangophunzira malamulo a anthu n’kumaganiza kuti kuchita zimenezo ndiye kundiopa.” (Yes. 29:13) Yesu sanalakwitse kudzudzula miyambo ya anthu yomwe sinkagwirizana ndi Malemba. Anthu amene ankaona kuti kutsatira malamulo komanso miyambo ya anthu n’kofunika kwambiri kuposa kutsatira Malemba, anakana Yehova komanso Mesiya amene iye anamutuma.
-
-
Kodi Mudzakhumudwa N’kusiya Kutsatira Yesu?Nsanja ya Olonda (Yophunzira)—2021 | May
-
-
(4) YESU SANATHANDIZE ANTHU KUSINTHA ULAMULIRO
Anthu ambiri anakana Yesu chifukwa’ sankachita nawo zandale. Kodi masiku ano zimenezi zingalepheretsenso bwanji ena kutsatira Yesu? (Onani ndime 17)e
17. Kodi m’nthawi ya Yesu anthu ambiri ankayembekezera kuti Mesiya achita chiyani?
17 M’nthawi ya Yesu anthu ankafuna ulamuliro utasintha. Iwo ankayembekezera kuti Mesiya adzawapulumutsa ku ulamuliro wopondereza wa Aroma. Koma pamene ankafuna kumuveka Yesu ufumu, iye anakana. (Yoh. 6:14, 15) Anthu enanso kuphatikizapo ansembe, ankada nkhawa kuti Yesu akasintha zinthu pa nkhani ya ulamuliro akwiyitsa Aroma, ndipo izi zichititsa kuti awalande mphamvu zimene anawapatsa. Popeza ankada nkhawa ndi nkhani zandale, Ayuda ambiri anakana Yesu.
18. Kodi ndi maulosi ati okhudza Mesiya amene anthu ambiri ankanyalanyaza?
18 Kodi Malemba amati chiyani? Ngakhale kuti maulosi ambiri ananeneratu kuti Mesiya adzapambana pankhondo, panalinso maulosi ena amene anasonyeza kuti choyamba ankafunika kufa chifukwa cha machimo a anthu. (Yes. 53:9, 12) Ndiye n’chifukwa chiyani Ayudawo ankakhala ndi maganizo olakwika okhudza Mesiya? Anthu ambiri ankanyalanyaza maulosi amene sankanena zokhudza kuthetsa mavuto awo pa nthawiyo.—Yoh. 6:26, 27.
-