Kanani Zoyerekezera Zaudziko, Londolani Zenizeni Zaufumu
“Pamenepo, pitirizani, kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake, ndipo zinthu zina zonsezi zidzawonjezeredwa kwa inu.”—MATEYU 6:33, NW.
1. Kodi ndichenjezo lotani limene Mawu a Mulungu amapereka ponena za mtima wophiphiritsira, ndipo ndiiti imene iri imodzi ya njira zazikulu imene umatinyengeza nayo?
“TCHINJIRIZA mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Kodi nchifukwa ninji kunali kofunika kwa Mfumu yanzeruyo Solomo kupereka chenjezo limeneli? Chifukwa chakuti “mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika.” (Yeremiya 17:9) Imodzi ya njira zazikulu m’zimene mtima wathu wophiphiritsira ungatinyengere ndiyo mwa kutichititsa kudzikhutiritsa m’zoyerekezera zaudziko. Koma kodi zoyerekezerazo nchiyani? Izo ndizo malingaliro osatsimikizirika, kulota masana, kuyendayenda kwa maganizo osatanganitsidwa. Pamene kulota masana kumeneku kufikira kukhala zoyerekezera zaudziko, iko sikuli chabe kuwawanya nthaŵi komanso nkwaupandu. Chifukwa chake, tiyenera kuzikana kotheratu. Kwenikweni, ngati tida kusayeruzika monga momwe anachitira Yesu, tidzatchinjiriza mtima wathu pakudzikhutiritsa m’zoyerekezera zaudziko.—Ahebri 1:8, 9.
2. Kodi zoyerekezera zaudziko nchiyani, ndipo nchifukwa ninji tiyenera kuzikana?
2 Koma kodi zoyerekezera zaudziko nchiyani? Ndizo zoyerekezera zogwirizanitsidwa ndi dziko lino logona mumphamvu ya Satana. Ponena za ilo, mtumwi Yohane analemba kuti: “Chirichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.” (1 Yohane 2:16; 5:19) Kodi nchifukwa ninji Akristu ayenera kukana zoyerekezera zaudziko? Chifukwa chakuti zoyerekezera zotero zimasonkhezera zikhumbo zadyera m’maganizo ndi mumtima. Kulota masana za kuchita chimene chiri cholakwa kwenikweni kungakhale kuyeseza m’maganizo za chimene munthu adzachitadi. Wophunzirayo Yakobo akutichenjeza kuti: “Munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo, ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.”—Yakobo 1:14, 15.
Zitsanzo Zachenjezo
3. Kodi ndinkhani ya yani imene imapereka chitsanzo cha chenjezo chachikulu koposa cha kuvulaza kwa zoyerekezera zadyera?
3 Tiyeni tipende za zitsanzo zosonyeza chifukwa chake zoyerekezera zaudziko ziyenera kukanidwa. Nkhani ya Satana Mdyerekezi imapereka chitsanzo choyambirira koposa zonse cha upandu umene ungachitike m’kudzikhutiritsa m’zoyerekezera zadyera. Iye analola malingaliro akudzimva kukula mumtima mwake kufikira kumlingo wakuti anachitira nsanje malo apadera a Yehova monga Wolamulira wa Chilengedwe Chaponseponse ndipo anafuna kulambiridwa. (Luka 4:5-8) Kodi zinali zoyerekezera zosatsimikizirika? Ndithudi! Zimenezo zidzatsimikiziridwa popanda chikayikiro pamene Satana adzamangidwa kwa zaka chikwi ndipo makamaka pamene aponyedwa “m’nyanja ya moto,” imfa yachiŵiri.—Chivumbulutso 20:1-3, 10.
4. Kodi Satana ananyenga motani Hava?
4 Tiri ndi chitsanzo china cha chenjezo m’nkhani ya mkazi woyambayo, Hava. M’zoyesayesa za Satana kuti apeze chokhumba chakecho, ananyenga Hava mwa kuloŵetsa m’maganizo mwake kuyerekezera kwakuti ngati atadya chipatso choletsedwa, iye sakafa koma kuti akakhala wofanana ndi Mulungu, akumadziŵa chabwino ndi choipa. Kodi kuyerekezera kumeneku kunali kosatsimikizirika, dyera? Ndithudi, monga momwe tingawonere kuchokera m’chiweruzo chotsutsa cha Yehova kwa Hava ndi mwamuna wake, Adamu, pozenga mlandu. Monga chotulukapo, anatayikiridwa ndi kuyenera kwawo kwa kukhala ndi moyo m’Paradaiso kaamba ka iwo eni ndi kaamba ka mbadwa zawo zonse zopanda ungwirozo.—Genesis 3:1-19; Aroma 5:12.
5. Kodi chinagwetsa ana ena aungelo a Mulungu nchiyani, ndipo nchotulukapo chotani kwa iwo?
5 Tirinso ndi chitsanzo china cha chenjezo cha ana ena aamuna aungelo a Mulungu. (Genesis 6:1-4) Mmalo mwa kukhala okhutira ndi madalitso amene anali nawo kumwamba pamaso pa Yehova, iwo anayerekezera za akazi apadziko lapansi ndi mmene kukakhalira kokondweretsera kugona nawo. Chifukwa cha kuchitapo kathu pazoyerekezera zimenezi, angelo osamvera ameneŵa tsopano abindikiritsidwa Kumayenje a mdima wauzimu, akumayembekezera chiwonongeko chawo pamapeto a Ulamuliro Wazaka Chikwi wa Yesu Kristu.—2 Petro 2:4; Yuda 6; Chivumbulutso 20:10.
Kanani Zoyerekezera Zaudziko
6, 7. Kodi nchifukwa ninji zoyerekezera zaudziko ponena za chuma chakuthupi ziri zovulaza ndi zonyenga?
6 Tsopano tiyeni tilingalire chimodzi cha zoyerekezera zofala koposa ndi zaupandu zogwiritsiridwa ntchito ndi Satana. Kupyolera mwa mpangidwe uliwonse wa zofalitsira mawu, timayesedwa kuti tidzikhutiritse ndi zoyerekezera zaudziko. Kaŵirikaŵiri zimenezi zimachititsidwa ndi kukhumba chuma. Mwa izo zokha, palibe cholakwika ndi kukhala ndi chuma. Abrahamu wolambira Mulunguyo, Yobu, ndi Mfumu Davide anali olemera kwambiri, koma iwo sanakhumbe chuma chakuthupi. Zoyerekezera za kukondetsa zinthu zakuthupi zimasonkhezera anthu kugwira ntchito mwaukapolo kwazaka zambiri kuti apeze chuma. Zoyerekezera zotero zimawasonkhezeranso kuphatikizidwa m’mitundu yonse ya kutchova juga, monga ngati kubetcha ndi kugula matikiti a lotale. Tisakhaletu ndi lingaliro lirilonse lonyenga la chuma. Ngati tiganiza kuti chuma chakuthupi chidzapereka chisungiko, lingalirani za mwambi wotsimikizirika uwu: “Chuma sichidzathandiza tsiku lamkwiyo; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.” (Miyambo 11:4) Ndithudi, chuma chakuthupi chidzakhala chosathandiza populumuka “chisautso chachikulu.”—Mateyu 24:21, NW; Chivumbulutso 7:9, 14.
7 Chuma chakuthupi chingathe kutinyenga mosavuta. Ndicho chifukwa chake timauzidwa kuti: “Chuma cha wolemera ndicho mudzi wake wolimba; alingalira kuti ndicho khoma lalitali.” (Miyambo 18:11) Inde, ‘m’kuyerekezera kwake’ chabe, pakuti chuma chakuthupi chimapereka tchinjirizo lochepa m’kukwera mtengo kwa zinthu kosalamulirika, kunyonyotsoka kwa chuma, chipwirikiti cha ndale zadziko, kapena panthenda yosachiritsika. Yesu Kristu anachenjeza za kupusa kwa kuika chidaliro chathu m’chuma chakuthupi. (Luka 12:13-21) Tirinso ndi mawu a mtumwi Paulo achenjezo akuti: “Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.”—1 Timoteo 6:10.
8. Kodi zoyerekezera zaudziko zampangidwe wa zakugonana nzofala motani, ndipo ndimaupandu otani amene zimenezi zimachititsa?
8 Zoyerekezera zina zikuphatikizapo kugonana kopanda lamulo. Ukulu umene chibadwa cha anthu ochimwa umakonda kusumika pazoyerekezera zachisembwere ungathe kuwonedwa m’kutchuka kwa mawu onyansa amene amapezeka pamene muchitira telefoni nambala zina ndi kumvetsera mawu ena otukwana. Mu United States, malo ochitira telefoni kuti mupeze mawu achisembwere ndiwo bizinesi yachuma koposa. Ngati tikanati tilole maganizo athu kusumikidwa pakugonana kopanda lamulo, kodi sitikanakhala onyenga, ongowonekera kunja monga Akristu oyera? Ndipo kodi sipali upandu wakuti zoyerekezera zotero zingatsogolere kukuzoloŵerana kwa chisembwere? Zimenezi zachitika ndipo zachititsa ena kuchotsedwa mumpingo Wachikristu kaamba kakuchita dama kapena chigololo. Polingalira mawu a Yesu pa Mateyu 5:27, 28, kodi onse amene amaphatikizidwa mouma khosi m’zoyerekezera zotero sali ndi liwongo la kuchita chigololo m’mitima mwawo?
9. Kodi ndiuphungu wabwino kwambiri wotani umene Malemba ali nawo kutichenjeza pazoyerekezera zaudziko?
9 Kuti tilimbane ndi chikhoterero cha mitima yathu yauchimo cha kuphatikizidwa m’zoyerekezera zotero, tiyenera kukumbukira chenjezo la Paulo lakuti: “Palibe cholengedwa chosawonekera pamaso [pa Mulungu], koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa iye amene tichita naye.” (Ahebri 4:13) Nthaŵi zonse tiyenera kufuna kukhala ngati Mose, amene “anapirira molimbika, monga ngati kuwona Wosawonekayo.” (Ahebri 11:27) Inde, tiyenera kudzikumbutsabe kuti zoyerekezera zaudziko nzosakondweretsa kwa Yehova ndipo zingadzetse kokha chivulazo kwa ife eni. Tiyenera kudera nkhaŵa ndi kukulitsa zipatso zonse za mzimu wa Mulungu, makamaka kudziletsa, pakuti sitingathe kuzemba chenicheni chakuti ngati tifesa m’thupi, tidzatuta chivundi cha thupi.—Agalatiya 5:22, 23; 6:7, 8.
Zenizeni Zaufumu
10, 11. (a) Kodi ndimaumboni otani amene amapereka chigomeko chakuti Mlengi ali weniweni? (b) Kodi pali umboni wotani wakuti Baibulo liridi Mawu a Mulungu? (c) Kodi pali umboni wotani wakuti Mfumu ya Ufumu wa Mulungu iri yeniyeni?
10 Njira yabwino koposa yokanira zoyerekezera zaudziko ndiyo kupitirizabe kulondola zenizeni Zaufumu. Zenizeni Zaufumu zimene zimatulutsidwa ndi Mulungu ziri zosiyana kwambiri ndi zoyerekezera zaudziko. Kodi Mulungu ali weniweni? Palibe chikayikiro ponena za kukhalapo kwake. Chilengedwe chowoneka chimachitira umboni chowonadi chimenecho. (Aroma 1:20) Tikukumbutsidwa za zimene zinanenedwa zoposa zaka zana limodzi zapitazo m’bukhulo The Divine Plan of the Ages, lofalitsidwa ndi Watch Tower Society. Ilo linati: “Munthu amene angayang’ane m’mlengalenga ndi telesikopo, kapena ngakhale ndi diso lake lokha, ndi kuwona mmenemo ukulu wachilengedwe, kulinganizika kwake kwabwinoko, kukongola, dongosolo, kugwirizana ndi kusiyanasiyanako, ndipo komabe nakayikira ngati Mlengi wa zimenezi ali womposa iye ponse paŵiri munzeru ndi m’mphamvu, kapena amene mwinamwake angalingalire kwakamphindi kuti dongosolo lotero linachitika lokha, popanda Mlengi, munthuyo watayikiridwa kapena kunyalanyaza mphamvu ya kulingalira kotero kuti kumakhala koyenera kuti alingaliridwe ndi chimene Baibulo limatcha kuti, chitsiru (munthu amene amanyalanyaza kapena amene alibe nzeru).”—Salmo 14:1.
11 Timaphunzira zinthu zonse Zaufumu m’Bukhu Lopatulika. Kodi Baibulo liridi Mawu a Mulungu olembedwa? Ilo liridi lotero, monga momwe kungawonedwere m’kugwirizana kwake, kulondola kwake mwasayansi, ndi mphamvu yake ya kusintha miyoyo ya anthu ndipo makamaka mwa kukwaniritsidwa kwa maulosi ake.a Bwanji za Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu Kristu? Kodi iye anakhalakodi? Zolembedwa za Uthenga Wabwino ndi makalata ouziridwa ndi Mulungu a Malemba Achikristu Achigriki motsimikizirika ndi mosadodoma zimachitira umboni kuti Yesu Kristu anali munthu weniweni wa m’mbiri. Ponena za kuti Yesu anali wa m’mbiri, palinso umboni wa Talmud Yachiyuda, umene umamsonyeza kukhala munthu. Choteronso olemba mbiri Achiyuda ndi Achiroma a m’zaka za zana loyamba C.E.
12, 13. Kodi ndimaumboni otani amene amatsimikizira Ufumu wa Mulungu kuti uli weniweni?
12 Bwanji ponena za kuti Ufumu weniweniwo uli weniweni? Umanyalanyazidwa kwambiri ndi Chikristu Chadziko, monga momwe kukuwonedwera m’chidandaulo ichi chochitidwa ndi mwamuna wina wotchuka wa tchalitchi cha Presbyterian kuti: “Papitadi zoposa zaka makumi atatu kuyambira pamene ndinamvetsera kwa minisitala wina akumayesa kufotokozera anthu kuti Ufumu unali weniweni kwa iwo.” Chikhalirechobe, kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova mwa Ufumuwo ndiko mutu wankhani wa Mawu ake. Mulungu mwiniyo anapanga lonjezo loyamba la Ufumu, akumati: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Ufumuwo unachitiridwa chithunzithunzi ndi mtundu wa Israyeli, makamaka mkati mwa ulamuliro wa Mfumu Solomo. (Salmo 72) Ndiponso, Ufumu unali mutu wankhani wa kulalikira kwa Yesu. (Mateyu 4:17) Iye anausonyeza m’mafanizo ake ambiri, monga ngati a m’Mateyu chaputala 13. Yesu anatiuza kupempherera Ufumuwo ndi kupitirizabe kuufunafuna choyamba. (Mateyu 6:9, 10, 33) Kwenikweni, Ufumu wa Mulungu ukutchulidwa pafupifupi nthaŵi zokwanira 150 m’Malemba Achikristu Achigiriki.
13 Ufumuwo ndiwo boma lenileni, lokhala ndi mphamvu ndi ulamuliro, ndipo udzakwaniritsa zoyembekezeredwa zonse zoyenera. Uli ndi mpambo wa malamulo, wopezeka m’Baibulo. Ufumuwo wachititsa kale zinthu zambiri kukwaniritsidwa. Uli ndi nzika zokhulupirika—Mboni za Yehova zoposa 4,000,000. Zikulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu, m’maiko 211 mokwaniritsa Mateyu 24:14. Mkati mwa chaka chawo chautumiki cha 1991, izo zinathera maola 951,870,021 zikumalalikira uthenga wa Ufumu. Ntchito imeneyi ikutulutsa zipatso zodziŵika bwino, zokhalitsa pamene unyinji wa anthu uphunzira “chinenero choyera” cha chowonadi cha Baibulo.—Zefaniya 3:9, NW.
Kulondola Zenizeni Zaufumu
14. Kodi tingalimbikitse motani chiyamikiro chathu kuti Ufumuwo uli weniweni?
14 Nangano, kodi ndimotani mmene tingalondolere zenizeni Zaufumu? Chiyembekezo chathu chiyenera kuzikidwa kotheratu pachikhutiro champhamvu. Dziko latsopano la Mulungu lolonjezedwalo liyenera kukhala lenileni kwa ife. (2 Petro 3:13) Ndipo tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro m’lonjezo lakuti Mulungu ‘adzapukuta msozi uliwonse kuuchotsa pamaso [pathu], ndipo sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro kapena kulira kapena chowawitsa.’ (Chivumbulutso 21:4) Kodi tingatsimikizire motani kuti zimenezi sizoyerekezera? Zidzachitikadi m’nthaŵi yokwanira ya Mulungu, pakuti kuli kosatheka kwa iye kunama. (Tito 1:1, 2; Ahebri 6:18) Tifunikira kusinkhasinkha pamalonjezo amenewo. Kudziyerekeza ife eni tiri m’dziko latsopano la Mulungu ndi kusangalala ndi madalitso ake sindiko zoyerekezera zosatsimikizirika koma ndiko umboni wa chikhulupiriro. Monga momwe Paulo anachifotokozera kuti, “chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezereka, chiyesero cha zinthu [zenizeni, “NW”] zosapenyeka.” (Ahebri 11:1) Tiyeni tilimbikitse chikhulupiriro chathu mwa kudya pa Mawu a Mulungu mokhazikika ndi mabukhu Achikristu amene amatithandiza kuzindikira ndi kuwagwiritsira ntchito. Ndipo pamene tipereka nthaŵi yowonjezereka kuuza ena za Ufumuwo, mokonzekera ndi mwamwaŵi, ndipamenenso timalimbikitsa kwambiri chikhulupiriro chathu ndi kuŵalitsa chiyembekezo chathu mu uwo.
15. Kodi ndithayo lotani limene tiri nalo ponena za uminisitala Wachikristu?
15 Tifunikiranso kugwira ntchito mogwirizana ndi zenizeni Zaufumu mwa kuwongolera mkhalidwe wa uminisitala wathu. Popeza kuti padakali zambiri zoti zichitidwe, kodi tingachite zimenezi motani? (Mateyu 9:37, 38) Mawuwo ngowona akuti kuphunzira sikumalira kuti wakalamba. Mosasamala kanthu kuti takhala tiri ndi phande kwazaka zingati m’ntchito ya kuchitira umboni, tingathe kuwongolerabe. Mwa kukhala ogwira mtima mowonjezereka m’kugwiritsira ntchito Mawu a Mulungu, timakhala okhoza bwino kwambiri kuthandiza ena kumva liwu la Mfumuyo, Yesu Kristu. (Yerekezerani ndi Yohane 10:16.) Pamene tilingalira kuti zoikidwiratu zosatha za anthu zikuphatikizidwa, tiyenera kufuna kufola gawo lathu mosamalitsa kutsata kuti tiwapatse mwaŵi wobwerezedwabwerezedwa kusonyeza pamene aima, kaya monga “nkhosa” kapena monga “mbuzi.” (Mateyu 25:31-46) Zowonadi, zimenezo zimatanthauza kusunga zolembepo zosamalitsa za awo amene sali panyumba ndipo makamaka za awo amene ali okondwerera uthenga wa Ufumu.
Pitirizanibe Kulondola Ufumu
16. Kodi ndani amene apereka chitsanzo chabwino kwambiri m’kulondola zenizeni Zaufumu, ndipo kodi “aukwatula” motani Ufumuwo?
16 Kuyesayesa kwakhama kukufunika kuti tipitirizebe kulondola zenizeni Zaufumu. Kodi sitimalimbikitsidwa ndi chitsanzo chachangu cha Akristu odzozedwa otsalirawo? Iwo akhala akumalondola zenizeni Zaufumu kwa zaka makumi ambiri. Kulondola kumeneku kunafotokozedwa m’mawu a Yesu akutiwo: “Kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa kumwamba uli wokangamizidwa, ndipo okangamirawo aukwatula ndi mphamvu.” (Mateyu 11:12) Panopa lingalirolo silakuti adaniwo akulanda Ufumu. Mmalomwake, limeneli nlonena za ntchito ya awo okhala mumzera wa Ufumu. Katswiri wina wa Baibulo anati: “Zimenezi zikutanthauza kufunitsitsa, kukalimira kosaletseka ndi kumenyera nkhondo ufumu Waumesiya woyandikirawo.” Odzozedwawo achita zothekera zonse kupangitsa Ufumuwo kukhala wawo. Zoyesayesa zamphamvu zofananazo zikufunika kwa “nkhosa zina” kotero kuti ziyenerere kukhala nzika zadziko lapansi za Ufumu wakumwamba wa Mulungu.—Yohane 10:16.
17. Kodi nchiyani chimene chidzakhala mkhalidwe wa awo amene akulondola zoyerekezera zaudziko?
17 Ndithudi, tikukhala ndi moyo m’nyengo yapadera ya mwaŵiwo. Awo amene amalondola zoyerekezera zaudziko tsiku lina adzadzuka moyang’anizana ndi zenizeni zogwiritsa mwala. Mkhalidwe wawo ukufotokozedwa m’mawu aŵa: “Kudzafanana ndi munthu wanjala, pamene alota, ndipo, tawonani, akudya; koma auka, ndipo mkati mwake muli zii; kapena monga munthu waludzu pamene alota, ndipo, tawonani, akumwa; koma auka ndipo tawonani walefuka, ndipo mkati mwake muli gwa.” (Yesaya 29:8) Ntheradi, zoyerekezera zaudziko sizidzapangitsa konse aliyense kukhala wokhutira ndi wachimwemwe.
18. Popeza kuti Ufumuwo uli weniweni, kodi ndinjira yotani imene tiyenera kulondola, ndi chiyembekezo chotani?
18 Ufumu wa Yehova uli weniweni. Uli mkati mwa kulamulira, pamene kuli kwakuti dongosolo loipa lino la zinthu likuyang’anizana ndi chiwonongeko chotsimikizirika ndi chosatha. Chifukwa cha chimenecho, labadirani uphungu wa Paulo wakuti: “Tisagone monga otsalawo, komatu tidikire, ndipo tisaledzere.” (1 Atesalonika 5:6) Tisumiketu mitima yathu ndi maganizo pazenizeni Zaufumu ndipo motero kulandira madalitso osatha. Ndipo likhaletu dalitso lathu kumva Mfumu ya Ufumuwo ikumanena nafe: “Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pachikhazikiro chake cha dziko lapansi.”—Mateyu 25:34.
[Mawu a M’munsi]
a Wonani bukhulo Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi zoyerekezera zaudziko nchiyani, ndipo nchifukwa ninji tiyenera kuzipeŵa?
◻ Kodi ndizitsanzo zotani zimene zimasonyeza kupusa kwa kuphatikiza m’zoyerekezera zaudziko?
◻ Kodi ndimaumboni ati amene amatsimikizira kuti Mlengi, Mawu ake olembedwa, Yesu Kristu ndi Ufumu zirikodi?
◻ Kodi tingalimbikitse motani chikhulupiriro chathu m’zenizeni Zaufumuwo?
[Chithunzi patsamba 15]
Kaŵirikaŵiri zoyerekezera zaudziko zimachititsidwa ndi kukhumba chuma chakuthupi
[Chithunzi patsamba 16]
Kulalikira mbiri yabwino ndiko njira imodzi yolondolera zenizeni Zaufumu
[Chithunzi patsamba 17]
Kodi mukulondola zenizeni Zaufumu mwa kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama?