Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mankhwala Omwe Angathandize Kuthetsa Nkhaŵa
    Nsanja ya Olonda—2001 | December 15
    • Kugwira Ntchito Mutasenza Goli

      9, 10. Kodi kale goli linali chizindikiro cha chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani Yesu anapempha anthu kuti asenze goli lake?

      9 Kodi munaona kuti pa Mateyu 11:28, 29 paja Yesu anati: “Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine”? Kalelo, munthu wamba mwina amamva ngati ankagwira ntchito atasenza goli. Kuyambira kale, goli linali chizindikiro cha ukapolo. (Genesis 27:40; Levitiko 26:13; Deuteronomo 28:48) Anthu ambiri amene anali kugwira ntchito masana amene Yesu ankakumana nawo, anali kugwira ntchito atasenzadi goli pamapeŵa awo, kunyamula katundu wolemera. Goli linkakhala labwino losavulaza pakhosi ndi paphewa kapena linkasupula malinga ndi mmene analikonzera. Popeza Yesu anali kalipentala, ayenera kuti ankapanga magoli, ndipo ankadziŵa mmene angapangire goli “lofewa.” Mwina anali kulikuta ndi chikopa kapena nsalu pamalo amene linkakhudza khosi ndi phewa kuti likhale lofeŵa.

      10 Pamene Yesu ananena kuti, “Senzani goli langa,” ayenera kuti anali kudzifanizira ndi munthu amene ankapanga magoli abwino amene anali ‘ofeŵa’ pakhosi ndi pamapewa a munthu wogwira ntchito. Motero, Yesu anawonjezera kuti: “Katundu wanga ali wopepuka.” Zimenezi zikusonyeza kuti golilo linali labwino kuligwiritsa ntchito ndipo ntchito yake sinali ya ukapolo. N’zoona kuti Yesu popempha anthu amene anali kumumvera kuti asenze goli lake sanali kupereka mpumulo wa msangamsanga wa mavuto onse amene analipo nthaŵi imeneyo. Komabe, mfundo zatsopano zimene iye anawauza zikanawapumulitsa ku mavuto ena. Kusintha mmene anali kukhalira pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku ndi mmene anali kuchitira zinthu zikanawapumulitsanso. Chofunika kwambiri chinali chakuti chiyembekezo choŵala ndi cholimba chikanawathandiza kusakhala ndi nkhaŵa zambiri pamoyo wawo.

      Inunso Mutha Kupeza Mpumulo

      11. N’chifukwa chiyani Yesu sanali kutanthauza kungosinthanitsa magoli chabe?

      11 Onani kuti Yesu sanali kunena kuti anthu asinthanitse magoli. Ufumu wa Roma ukanapitirizabe kulamulira m’dzikolo monga mmene maboma lerolino akulamulirabe m’mayiko mmene Akristu amakhala. Anthu akanapitirizabe kukhoma msonkho wachiroma wa m’zaka za zana loyamba. Matenda ndi mavuto a zachuma akanakhalapobe. Anthu akanavutikabe ndi kupanda ungwiro ndi uchimo. Komabe, akanapeza mpumulo ngati akanatsatira zimene Yesu anali kuphunzitsa monga mmenenso ifeyo tingaupezere lerolino.

      12, 13. Kodi Yesu anatsindika kuti n’chiyani chimene chingabweretse mpumulo, ndipo ena anachita motani atamva zimenezo?

      12 Tanthauzo lalikulu la fanizo la Yesu la goli linaonekera bwino pa nkhani yopanga ophunzira. Mosakayika, ntchito yaikulu ya Yesu inali yophunzitsa anthu ndipo anatsindika kwambiri pa Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 4:23) Motero, pamene ananena kuti, “ Senzani goli langa,” zimenezo mosakayika zikanaphatikizapo kumutsanzira kuchita ntchito yomweyo. Nkhani ya m’Mauthenga Abwino imasonyeza kuti Yesu analimbikitsa anthu oona mtima kusiya ntchito yawo, yomwe ndi nkhani yaikulu m’miyoyo ya anthu ambiri. Kumbukirani mmene anaitanira Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane. Iye anati: “Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.” (Marko 1:16-20) Yesu anawasonyeza asodzi amenewo mmene akanakhalira okhutira ngati akanachita ntchito imene iye anali kuiika patsogolo m’moyo wake, kwinaku akuwatsogolera ndi kuwathandiza pochita zimenezo.

      13 Ena mwa Ayuda amene anali kumva, anamvetsa zimene anali kuphunzitsa ndipo anazigwiritsa ntchito. Tayesani kuona m’maganizo mwanu zimene zinachitika m’mphepete mwa nyanja pamene tikuŵerenga pa Luka 5:1-11. Asodzi anayi anali atagwira ntchito zolimba usiku wonse koma osapeza kanthu. Ndiyeno mwadzidzidzi makoka awo anadzaza nsomba. Zimenezi sizinangochitika mwamwayi. Yesu ndi amene anachititsa. Pamene anayang’ana ku gombe, anaona khwimbi la anthu amene anachita chidwi kwambiri ndi zimene Yesu anali kuphunzitsa. Zimenezi zinathandiza kuona chifukwa chake Yesu anawauza asodzi anayiwo kuti: ‘Kuyambira tsopano mudzakhala asodzi a anthu.’ Kodi asodziwo anachita chiyani atamva zimenezi? “Mmene iwo anakocheza ngalaŵa zawo pamtunda, anasiya zonse, nam’tsata Iye.”

      14. (a) Kodi tingapeze bwanji mpumulo lerolino? (b) Kodi ndi uthenga wabwino wotsitsimula uti umene Yesu analengeza?

      14 Inunso mungachite chimodzimodzi. Ntchito yophunzitsa anthu choonadi cha Baibulo ikupitirizabe. Mboni za Yehova pafupifupi mamiliyoni asanu ndi limodzi zavomera pempho la Yesu lakuti ‘asenze goli lake.’ Iwo ndi “asodzi a anthu.” (Mateyu 4:19) Ena amagwira ntchitoyi nthaŵi zonse ndipo ena amaigwira mmene angathere pa nthaŵi zosiyanasiyana. Onse amapeza kuti ndi ntchito yotsitsimula, ndipo motero sakhala ndi nkhaŵa zambiri pa moyo wawo. Imaphatikizapo kuchita zimene iwo amakonda, kuuza ena uthenga wabwino​—“uthenga wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 4:23) Nthaŵi zonse zimasangalatsa kulankhula za uthenga wabwino koma makamaka uthenga wabwino wa Ufumuwu. Baibulo lili ndi nkhani zofunika kwambiri zimene tingakhutiritse nazo anthu kuti atha kuchepetsa nkhaŵa pa moyo wawo.​—2 Timoteo 3:16, 17.

      15. Kodi mungapindule motani ndi zimene Yesu anaphunzitsa za mmene tingakhalire?

      15 Ngakhale anthu amene angoyamba kumene kuphunzira za Ufumu wa Mulungu apindula ku mlingo wina wake ndi zimene Yesu anaphunzitsa za mmene angakhalire. Ambiri anganene moona mtima kuti zimene Yesu anaphunzitsa zawatsitsimula ndipo zawathandiza kusinthiratu moyo wawo. Mutha kutsimikiza nokha zimenezi mwa kupenda mfundo zina za mmene mungakhalire zimene zili m’nkhani zosimba moyo wa Yesu ndi utumiki wake, makamaka Mauthenga Abwino amene analemba Mateyu, Marko, ndi Luka.

      Mmene Tingapezere Mpumulo

      16, 17. (a) Kodi ziphunzitso zazikulu za Yesu mungazipeze kuti? (b) Kodi n’chiyani chimafunika kuti tipeze mpumulo pogwiritsa ntchito zimene Yesu anaphunzitsa?

      16 Yesu m’ngululu ya 31 C.E., anaphunzitsa chiphunzitso chomwe mpaka lero n’chodziŵika kwambiri padziko lonse. Nthaŵi zambiri chimatchedwa Ulaliki wa pa Phiri. Chiphunzitsochi chili pa Mateyu machaputala 5 mpaka 7 ndi Luka chaputala 6, ndipo chikufotokoza mwachidule ziphunzitso zake zambiri. Mungapeze zina zimene Yesu anaphunzitsa m’mbali zina za Mauthenga Abwino. Mfundo zambiri zimene ananena n’zosavuta kuzimvetsa, ngakhale kuti mwina kungakhale kovuta kuzigwiritsa ntchito munthu payekha. Bwanji osaŵerenga machaputala amenewo mosamalitsa ndiponso mukumasinkhasinkha? Mphamvu ya mfundo zake ilimbikitsetu maganizo ndi mtima wanu.

      17 N’zachidziŵikire kuti zimene Yesu anaphunzitsa tingaziike m’magulu osiyanasiyana. Tiyeni tiike m’gulu limodzi ziphunzitso zake zazikulu kuti tikhale ndi chiphunzitso chimodzi tsiku lililonse la mwezi, tili n’cholinga chozigwiritsa ntchito pa moyo wathu. Motani? Eya, musangoziyang’ana mfundozo mwa patalipatali. Kumbukirani wolamulira wolemera amene anafunsa Yesu Kristu kuti: “Ndizichita chiyani, kuti ndiloŵe moyo wosatha?” Yesu atabwereza zofunika zazikulu za Chilamulo cha Mulungu, munthuyo anati anali kuzisunga zonsezi. Komabe, anazindikira kuti anafunika kuchita zambiri. Yesu anam’pempha kuchita zowonjezereka kuti agwiritse ntchito mfundo zachikhalidwe za Mulungu m’njira zothandiza kuti akhale wophunzira wachangu. Mwachionekere, munthuyu sanali wokonzeka kuchita zambiri. (Luka 18:18-23) Choncho, munthu amene lerolino akufuna kuphunzira zimene Yesu anaphunzitsa, afunika kukumbukira kuti pali kusiyana pakati pa kuvomereza zimene Yesu anaphunzitsa ndi kuzitsatira kuti zichepetse nkhaŵa.

      18. Perekani chitsanzo cha mmene mungagwiritsire ntchito mopindulitsa bokosi limene lili m’nkhani ino.

      18 Poyamba kupenda ndi kugwiritsa ntchito zimene Yesu anaphunzitsa, taonani mfundo yoyamba m’bokosi limene lili m’nkhani ino. Mfundo yoyambayi yachokera pa Mateyu 5:3-9. Inde, tonsefe tingatenge nthaŵi ndithu kusinkhasinkha malangizo abwino amene ali m’mavesi ameneŵa. Komabe, kuwatenga mavesi onsewo pamodzi, kodi munganene kuti akufotokoza chiyani za mtima wa munthu? Ngati mukufunadi kugonjetsa nkhaŵa zopitirira muyeso m’moyo wanu, kodi n’chiyani chingakuthandizeni? Kodi moyo wanu ungasinthe motani ngati muika mtima kwambiri pa zinthu zauzimu ndi kumaganiza zimenezo nthaŵi zonse? Kodi pali zinthu zina m’moyo wanu zimene mufunika kuchepetsa kuti muike mtima kwambiri pa zinthu zauzimu? Ngati mungatero, zidzawonjezera chimwemwe chanu pakalipano.

      19. Kodi mungatani kuti mupeze nzeru ndi kumvetsa kowonjezereka?

      19 Pali zinanso zimene mungachite. Bwanji osakambirana mavesi amenewo ndi mtumiki wina wa Mulungu, mwina mwamuna kapena mkazi wanu, wachibale, kapena mnzanu? (Miyambo 18:24; 20:5) Kumbukirani kuti wolamulira wolemera uja anafunsa munthu wina​—Yesu​—za nkhani ngati imeneyi. Zimene anamuyankha zikanakulitsa chiyembekezo chake chokhudza chimwemwe ndi moyo wautali. Wolambira mnzanu amene mungakambirane naye mavesiŵa safanana ndi Yesu. Komabe, kukambirana zimene Yesu anaphunzitsa kukupindulitsani nonsenu. Tayesani kuchita zimenezo mwamsanga.

      20, 21. Kodi mungatsatire ndondomeko yotani kuti muphunzire zimene Yesu anaphunzitsa, ndipo mungaone bwanji kuti mukupita patsogolo?

      20 Tayang’ananinso m’bokosilo lakuti “Ziphunzitso Zokuthandizani.” Ziphunzitsozi aziika m’magulu motero kuti tsiku lililonse pali chiphunzitso chimodzi choti mupende. Choyamba mungaŵerenge zimene Yesu ananena m’mavesi amene tasonyeza. Ndiyeno ganizirani mawu akewo. Sinkhasinkhani mmene mungawagwiritsire ntchito pa moyo wanu. Ngati mukuona kuti mukuchita kale zimenezo, sinkhasinkhani kuti muone zina zimene mungachite kuti muzitsatira chiphunzitso cha Mulungu chimenecho nthaŵi zonse. Yesani kugwiritsa ntchito chiphunzitso chimenecho patsikulo. Ngati simunamvetse chiphunzitsocho kapena mmene mungachigwiritsire ntchito, chibwerezeni tsiku lotsatira. Komabe, kumbukirani kuti simufunika kuchita kukwanitsa bwinobwino chiphunzitso chilichonse musanayambe kupenda chiphunzitso china. Tsiku lotsatira, mungapende chiphunzitso china. Pakutha pa mlungu, mungabwereremo ndi kuona ngati mwakwanitsa kutsatira ziphunzitso za Yesu zinayi kapena zisanu. Mlungu wotsatira wonjezerani, tsiku ndi tsiku. Ngati muona kuti penapake mwalephera kugwiritsa ntchito chiphunzitso china, musagwe mphwayi. Zimenezo zingachitikire Mkristu aliyense. (2 Mbiri 6:36; Salmo 130:3; Mlaliki 7:20; Yakobo 3:8) Pitirizani kugwiritsa ntchito ziphunzitsozo mlungu wachitatu ndi wachinayi.

      21 Pakutha pa mwezi kapena kuposerapo, mungakhale mutapenda mfundo zonse 31. Kaya mudzakhala mutapenda zonse kapena ayi, kodi zotsatira zake zidzakhala zotani? Kodi simudzakhala wachimwemweko, mwinanso kuchepetsa nkhaŵa? Ngakhale mutasintha pang’ono chabe, mosakayika mudzaona kuti mwachepetsako nkhaŵa, kapena muzitha kuthana nazo bwinoko, ndipo mudzakhala ndi njira yopitirizira. Musaiŵale kuti pali mfundo zina zabwino kwambiri zimene Yesu anaphunzitsa zimene sizili mu mndandandawo. Bwanji osafufuza zina mwa mfundo zimenezi ndi kuyesa kuzigwiritsa ntchito?​—Afilipi 3:16.

      22. Kodi n’chiyani chingachitike ngati titatsatira zimene Yesu anaphunzitsa, koma ndi mbali inanso iti imene tifunika kuiphunzira?

      22 Mutha kuona kuti goli la Yesu n’lofeŵadi ngakhale kuti lili ndi kulemera kwake. Katundu wa zimene anaphunzitsa ndi kukhala wophunzira ali wopepuka. Mtumwi Yohane, mnzake wapamtima wa Yesu, atadzionera yekha kwa zaka zoposa 60, anavomereza kuti: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Inunso mungakhale ndi chidaliro ngati chimenechi. Mukagwiritsa ntchito zimene Yesu anaphunzitsa mudzapeza kuti zinthu zimene zikudetsa nkhaŵa anthu ambiri lerolino sizidzakudetsani nkhaŵa kwambiri monga mmene ena akuchitira. Mudzaona kuti mwapeza mpumulo waukulu ndithu. (Salmo 34:8) Komabe, pali mbali ina ya goli lofeŵa la Yesu imene mufunika kuiphunzira. Yesu ananenanso kuti anali “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.” Kodi zimenezo zikugwirizana motani ndi kuphunzira kwathu kwa Yesu ndi kumutsanzira? M’nkhani yotsatirayi, tipenda zimenezi.​—Mateyu 11:29.

  • “Phunzirani kwa Ine”
    Nsanja ya Olonda—2001 | December 15
    • “Phunzirani kwa Ine”

      “Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.”​—MATEYU 11:29.

      1. N’chifukwa chiyani kuphunzira kwa Yesu kungakhale kosangalatsa ndiponso kopindulitsa?

      YESU KRISTU nthaŵi zonse ankaganiza, kuphunzitsa ndi kuchita zinthu moyenera. Nthaŵi imene anakhala padziko lapansi inali yaifupi. Komabe anali ndi ntchito yopindulitsa ndiponso yokhutiritsa, ndipo anali wachimwemwe nthaŵi zonse. Anasonkhanitsa ophunzira ndipo anawaphunzitsa mmene angalambirire Mulungu, kukonda anthu, ndi kugonjetsa dziko lapansi. (Yohane 16:33) Anawathandiza kukhala ndi chiyembekezo ndipo “[a]naonetsera poyera moyo ndi chosavunda mwa Uthenga Wabwino.” (2 Timoteo 1:10) Ngati inunso ndinu wophunzira wake, kodi mukuganiza kuti kukhala wophunzira kumatanthauzanji? Mwa kupenda zimene Yesu ananena zokhudza ophunzira, tingaphunzire mmene tingapindulire. Zimenezo zimafuna kutsatira maganizo ake ndi kugwiritsa ntchito mfundo zina zazikulu zachikhalidwe.​—Mateyu 10:24, 25; Luka 14:26, 27; Yohane 8:31, 32; 13:35; 15:8.

      2, 3. (a) Kodi kukhala wophunzira wa Yesu n’kutani? (b) N’chifukwa chiyani n’kofunika kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine wophunzira wa ndani?’

      2 M’Malemba Achigiriki Achikristu, liwu limene analimasulira kuti “wophunzira” limatanthauza munthu amene amaika maganizo ake pa chinachake, kapena munthu amene amaphunzira. Liwu longa limenelo lili mu lemba limene latsogolera nkhani ino la Mateyu 11:29 limene likuti: ‘Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.’ Inde, wophunzira ndi munthu amene akuphunzira chinachake. Nthaŵi zambiri, Mauthenga Abwino amagwiritsa ntchito liwu lakuti “wophunzira” kunena za otsatira apamtima a Yesu amene ankayenda naye limodzi polalikira ndiponso amene anali kuwalangiza. Ena ayenera kuti anangovomereza zimene Yesu ankaphunzitsa, ndipo mwina ankachita zimenezo mwam’seri. (Luka 6:17; Yohane 19:38) Olemba Mauthenga Abwino ananenanso za “ophunzira a Yohane [Mbatizi], ndi ophunzira a Afarisi.” (Marko 2:18) Popeza Yesu anachenjeza om’tsatira kuti ‘apeŵe chiphunzitso cha Afarisi,’ tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndine wophunzira wa ndani?’​—Mateyu 16:12.

      3 Ngati ndife ophunzira a Yesu ndipo ngati taphunzira kwa iye, ndiye kuti ena ayenera kuona kuti timawatsitsimula mwauzimu tikakhala nawo. Aone kuti tsopano ndife ofatsa ndi odzichepetsa mtima. Ngati tili ndi udindo woyang’anira anthu ena kuntchito, kapena ngati ndife kholo, kapenanso ngati tili ndi udindo wosamala nkhosa mumpingo wachikristu, kodi amene tikuwayang’anirawo amaona kuti tikuwachitira zinthu monga mmene Yesu ankachitira ndi anthu amene anali kuwayang’anira?

      Mmene Yesu Ankachitira ndi Anthu

      4, 5. (a) N’chifukwa chiyani n’kosavuta kudziŵa mmene Yesu anachitira ndi anthu amene anali kuvutika? (b) Kodi n’chiyani chinachitika pamene Yesu anali kudya m’nyumba ya Mfarisi?

      4 Tifunika kudziŵa mmene Yesu ankachitira ndi anthu, makamaka amene anali ndi mavuto aakulu. Zimenezo n’zosavuta kuziphunzira chifukwa Baibulo lili ndi nkhani zambiri zosimba mmene Yesu ankachitira ndi anthu omwe anali kuvutika. Tiyeni tionenso mmene atsogoleri achipembedzo, makamaka Afarisi, ankachitira ndi anthu amene analinso ndi mavuto ngati omwewo. Kusiyana kwa Yesu ndi Afarisi kutitsegula m’maso.

      5 M’chaka cha 31 C.E., pamene Yesu anali kulalikira m’Galileya, “mmodzi wa Afarisi anamuitana [Yesu] kuti akadye naye.” Yesu anavomera. “Ndipo analoŵa m’nyumba ya Mfarisi, naseama pachakudya. Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene anali m’mudzimo; ndipo pakudziŵa kuti Yesu analikuseama pachakudya m’nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino, naimirira kumbuyo, pa mapazi ake, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsompsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino.”​—Luka 7:36-38.

      6. N’chifukwa chiti chimene chiyenera kuti chinam’pangitsa mkazi yemwe anali “wochimwa” kupezeka kunyumba ya Mfarisi?

      6 Kodi mungayerekezere m’maganizo zimenezo? Buku lina la maumboni limati: “Mkaziyu (v.37) anapezerapo mwayi pa miyambo imene inalipo yomwe inkaloleza anthu osoŵa kupita nawo ku phwando ngati limeneli kuti akatole nawo makombo.” Zimenezi zingafotokoze chifukwa chake ena ankatha kuloŵa asanaitanidwe pa phwandolo. Ayenera kuti analipo ena amene ankafuna kukatola makombo phwando likatha. Komabe, khalidwe la mkaziyu linali lachilendo. Iye sanaime kaye kuti adikire mpaka phwandolo lithe. Anali ndi mbiri yoipa monga “wochimwa” amene anali kudziŵika kwambiri motero kuti Yesu anati ankadziŵa kuti “machimo ake, [anali] ambiri.”​—Luka 7:47.

      7, 8. (a) Kodi tikanatani ngati zimene zili pa Luka 7:36-38 zikanatichitikira ifeyo? (b) Kodi Simoni anachita bwanji?

      7 Tayerekezani kuti inuyo munalipo nthaŵi imeneyo ndipo munali Yesu. Kodi mukanatani? Kodi mukanaipidwa poona mkaziyu akufika kwa inu? Kodi zimene zinachitikazi zikanakukhudzani bwanji? (Luka 7:45) Kodi zikanakunyansani?

      8 Ngati mukanakhala mmodzi mwa alendo amene anaitanidwa, kodi mukanaganiza monga mmene anachitira Simoni, Mfarisi uja? “Koma Mfarisi, amene adamuitana [Yesu], pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo wom’khudza Iye, chifukwa ali wochimwa.” (Luka 7:39) Mosiyana ndi Mfarisiyu, Yesu anali munthu wachifundo chachikulu. Anadziŵa vuto la mkaziyo ndipo anazindikira kuvutika kwake maganizo. Malemba sakutifotokozera kuti mkaziyo anatani kuti akhale wochimwa. Ngati analidi hule, ndiye kuti mwachionekere amuna a m’mudzimo omwe anali Ayuda odzipatulira, sanamuthandize.

      9. Kodi Yesu anachita motani, ndipo zotsatira zake ziyenera kuti zinali zotani?

      9 Koma Yesu anafuna kumuthandiza mkaziyo. Anamuuza kuti: “Machimo ako akhululukidwa.” Ndiyeno anapitiriza kuti: “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.” (Luka 7:48-50) Nkhaniyo imathera pamenepa. Munthu wina anganene kuti Yesu sanamuthandize kwambiri mkaziyo. Komatu, anamuuza kuti azipita atam’patsa madalitso. Kodi mukuganiza kuti mwina anayambiranso kuchita khalidwe lake lomvetsa chisoni lija? Ngakhale kuti sitinganene motsimikiza, taonani zimene Luka kenako ananena. Anasimba kuti Yesu anayendayenda “kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu.” Luka ananenanso kuti “akazi ena” anali ndi Yesu ndi ophunzira ake ndipo “anawatumikira ndi chuma chawo [akaziwo].” N’zotheka kuti mkazi wolapa ndi woyamikira ameneyo anali nawo m’gululo. Ayenera kuti anayamba kuchita zimene zimasangalatsa Mulungu ali ndi chikumbumtima choyera, cholinga chatsopano m’moyo wake ndi kukonda kwambiri Mulungu.​—Luka 8:1-3.

      Kusiyana kwa Yesu ndi Afarisi

      10. N’chifukwa chiyani kuli kopindulitsa kupenda nkhani ya Yesu ndi mkazi amene anakumana naye kunyumba ya Simoni?

      10 Kodi tingaphunzire chiyani pa nkhani yomveka bwino imeneyi? Kodi siinatikhudze mtima? Tayerekezerani kuti munalimo m’nyumba ya Simoni. Kodi mukanamva bwanji? Kodi mukanachita monga mmene anachitira Yesu, kapena pang’ono pokha mukanaganiza monga Mfarisi amene anaitana Yesu uja? Yesu anali Mwana wa Mulungu, motero sitingaganize ndi kuchita mofanana ndendende ndi mmene iye anachitira. Komabe, sitingafune kukhala ngati Simoni, Mfarisi uja. Ndi ochepa okha amene angakonde kukhala ngati Afarisi.

      11. N’chifukwa chiyani sitingafune kufanana ndi Afarisi?

      11 Poona maumboni a m’Baibulo ndiponso a m’mabuku omwe si ofotokoza za Baibulo, tinganene kuti Afarisi ankadziona ngati apamwamba monga osamalira nkhani za kupita patsogolo kwa anthu onse ndiponso ubwino wa mtunduwo. Sanali kukhutira kuti Chilamulo cha Mulungu chinali chomveka bwino ndiponso chosavuta kumvetsa. Ankati akaona ngati Chilamulo sichinafotokoze mwachindunji, ankawonjezera tanthauzo lawolawo ku Chilamulocho kuti asapereke mpata woti munthu agwiritse ntchito chikumbumtima. Atsogoleri a chipembedzo ameneŵa ankayesetsa kupanga malamulo a makhalidwe pa nkhani iliyonse ngakhale zazing’ono kwambiri.a

      12. Kodi Afarisi ankadziona ngati anali anthu otani?

      12 Josephus, wolemba mbiri wachiyuda wa m’zaka za zana loyamba, anati Afarisi ankadziona kuti ndi anthu okoma mtima, ofatsa, opanda tsankhu ndiponso oyenerera ntchito yawo. Mosakayika, Afarisi ena anayesera kukhaladi otero. Mwina mungakumbukire Nikodemo. (Yohane 3:1, 2; 7:50, 51) M’kupita kwa nthaŵi, ena mwa iwo anayamba kutsatira njira yachikristu. (Machitidwe 15:5) Mtumwi wachikristu Paulo analemba za Ayuda ena, monga Afarisi kuti: “Ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziŵitso.” (Aroma 10:2) Komabe, Mauthenga Abwino amafotokoza khalidwe la Afarisi malinga ndi mmene anthu wamba anali kuwaonera. Anali onyada, amwano, odziona ngati olungama, opezera zifukwa anzawo, oweruza ndi opeputsa anthu ena.

      Maganizo a Yesu

      13. Kodi Yesu anati Afarisi anali otani?

      13 Yesu anawanena alembi ndi Afarisi kuti anali achinyengo. “Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pamapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chawo.” Inde, katunduyo analidi wolemera, ndipo goli limene anasenzetsa anthu linali loŵaŵa. Yesu anapitiriza kunena kuti alembi ndi Afarisi anali “opusa.” Wopusa ndi munthu wosafunika pakati pa anthu. Yesu anatinso alembi ndi Afarisi anali “atsogoleri akhungu” ndipo anati ‘anasiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro.’ Ndani angafune kuti Yesu azimuona ngati Mfarisi?​—Mateyu 23:1-4, 16, 17, 23.

      14, 15. (a) Kodi mmene Yesu anachitira ndi Mateyu Levi zikuvumbula chiyani za khalidwe la Afarisi? (b) Kodi ndi phunziro lofunika liti limene tingatenge pa nkhani imeneyi?

      14 Pafupifupi munthu aliyense amene amaŵerenga Mauthenga Abwino angaone khalidwe loipa la Afarisi ambiri. Yesu ataitana Mateyu Levi, wokhometsa msonkho, kuti akhale wophunzira, Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu lomulandira. Nkhaniyo imati: “Ndipo Afarisi ndi alembi awo anang’ung’udza kwa ophunzira ake, nanena kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa? Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, . . . Sindinadza Ine kuitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.”​—Luka 5:27-32.

      15 Levi mwiniyo anazindikira kanthu kena kamene Yesu ananena tsiku limenelo. Yesu anati: “Koma mukani muphunzire n’chiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ayi.” (Mateyu 9:13) Ngakhale Afarisi ankanena kuti anali kukhulupirira zimene aneneri a Chihebri analemba, sankavomereza mawu ameneŵa amene ali pa Hoseya 6:6. Iwo anali kuonetsetsa kuti ngati kuli kuchimwa, asachimwe chifukwa choti alephera kumvera mwambo koma chifukwa choti sanasonyeze chifundo. Tingadzifunse kuti, ‘Kodi ndili ndi mbiri ya kuumirira malamulo ena ake, monga okhudza kuti munthu payekha aganize kapena nkhani zoti munthu asankhe zochita yekha? Kapena kodi ena choyamba akangondiona amaganizira zoti ndine wachifundo ndiponso wokoma mtima kwambiri?’

      16. Kodi Afarisi anali ndi khalidwe lotani ndipo tingatani kuti tisafanane nawo?

      16 Afarisi ankadzudzula nthaŵi zonse ngakhale pa nkhani zing’onozing’ono. Iwo ankafufuza zolakwa zilizonse kaya zikhale kuti munthuyo walakwadi kapena akungomuganizira. Amawachititsa anthu kukhala tcheru nthaŵi zonse ndi kuwakumbutsa zolakwa zawo. Afarisi anali kudzitama pa kupereka chakhumi cha timbewu tating’ono kwambiri monga timbewu tonunkhira, katsabola ndi chitowe. Ankadzionetsera monga anthu opembedza kwambiri mwa kavalidwe kawo ndipo ankatsogolera mtunduwo. Ndithudi, kuti titsanzire chitsanzo cha Yesu, tiyenera kupeŵa khalidwe lokonda kufufuza ndi kunena zolakwa za ena nthaŵi zonse.

      Kodi Yesu Ankatani Pakakhala Mavuto?

      17-19. (a) Fotokozani mmene Yesu anachitira pa chochitika china chovuta chimene chikanatha kukhala ndi zotsatirapo zoopsa. (b) Kodi n’chiyani chinachititsa nkhaniyi kukhala yodetsa nkhaŵa ndiponso yosasangalatsa? (c) Mukanakhala kuti munalipo pamene mkaziyu ankafika kwa Yesu, kodi mukanatani?

      17 Mmene Yesu ankachitira pakakhala mavuto zinali zosiyana kwambiri ndi mmene ankachitira Afarisi. Taganizani mmene Yesu anachitira pa nkhani ina imene ikanakhala yoopsa kwambiri. Nkhani yake ndi ya mkazi wina amene anali ndi nthenda ya kukha mwazi kwa zaka 12. Mutha kuŵerenga nkhaniyo pa Luka 8:42-48.

      18 M’buku la Marko nkhaniyi imati mkaziyo “anachita mantha, ndi kunthunthumira.” (Marko 5:33) Anachita zimenezi chifukwa chiyani? Mosakayika, anatero chifukwa chakuti ankadziŵa kuti waswa Lamulo la Mulungu. Malinga ndi Levitiko 15:25-28, mkazi amene anali kukha mwazi kosakhala kwachibadwa anali wodetsedwa mpaka kukha mwaziko kutatha n’kuwonjezeraponso mlungu umodzi. Chinthu chilichonse ndiponso munthu aliyense amene iye anamukhudza anali wodetsedwa. Kuti akafike pamene panali Yesu, mkaziyu anavutika kuti adutse m’chikhamu cha anthu. Tikamaganiza za nkhani imeneyi pambuyo pa zaka 2,000, timamumvera chisoni mkaziyu chifukwa cha kuvutika kwake.

      19 Mukanakhala kuti munalipo nthaŵi imeneyo, kodi mukanaiona bwanji nkhaniyi? Mukanati chiyani? Onani kuti Yesu anamuthandiza mkaziyu mokoma mtima, mwachikondi ndiponso momuganizira, osatchula n’komwe vuto lililonse limene mkaziyu ayenera kuti analiyambitsa.​—Marko 5:34.

      20. Kukanakhala kuti Akristu anafunika kutsatira lamulo la pa Levitiko 15:25-28, kodi tikanakumana ndi vuto lotani?

      20 Kodi tingaphunzire kenakake pa chochitika chimenechi? Tiyerekeze kuti ndinu mkulu mu mpingo wachikristu lerolino. Ndipo tiyerekezenso kuti Akristu anafunika kutsatira lamulo la pa Levitiko 15:25-28 ndi kutinso mkazi wachikristu waswa lamulo limenelo, mtima wake suli m’malo ndipo akusoŵa thandizo. Kodi mukanatani? Kodi mukanamuchititsa manyazi mwa kum’dzudzula pa gulu? Mwina mukuti: “Ayi ndithu. Sindikanachita zimenezo! Potsatira chitsanzo cha Yesu, ndikanayesetsa kumukomera mtima, kum’sonyeza chikondi ndi kumuganizira.” Mwanena bwinotu pamenepo. Komabe, nkhani yagona pa kuchitadi zimenezo, kutsanzira zimene Yesu anachita.

      21. Kodi Yesu anaphunzitsa anthu chiyani za Chilamulo?

      21 Kwenikweni, anthu anaona kuti Yesu anawapatsa mpumulo, kuwatsitsimula mwauzimu ndi kuwalimbikitsa. Pamene Chilamulo cha Mulungu chinanena mwatchutchutchu, chinkatanthauzadi zimenezo. Ngati sichinafotokoze mwatchutchutchu, anthu akanagwiritsa ntchito chikumbumtima chawo ndipo akanasonyeza kukonda kwawo Mulungu pa zimene akanasankha kuchita. Chilamulo chinkapereka mpata wochitsatira mogwirizana ndi kusintha kwa zinthu. (Marko 2:27, 28) Mulungu ankakonda anthu ake, kuwachitira zabwino, ndipo ankafunitsitsa kuwasonyeza chifundo akalakwitsa. Yesu anachitanso chimodzimodzi.​—Yohane 14:9.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena