Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kubudula Ngala pa Sabata
MWAMSANGA Yesu ndi ophunzira ake akuchoka ku Yerusalemu kubwerera ku Galileya. Iri nyengo yamphakasa, ndipo m’munda muli ngala zatirigu pamapesi. Ophunzirawo ali ndi njala. Chotero iwo akubudula ngala zatirigu ndi kudya. Koma popeza kuti ndilo Sabata, zochita zawo zikuwonedwa.
Atsogoleri achipembedzo m’Yerusalemu angofunafuna kumene kupha Yesu kaamba ka zinenezo za kuswa Sabata. Tsopano, Afarisi akubweretsa chinenezo. “Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku lasabata,” iwo akuimba mlandu.
Afarisi akunena kuti kubudula ngala ndi kuzifukuta m’manja kuti adye ndiko kukolola ndi kupuntha. Koma kutanthauzira kwawo kwankhokera chimene kwenikweni chiri ntchito kwapangitsa Sabata kukhala lothodwetsa, pamene kuli kwakuti linafunikira kukhala nthawi yachisangalalo, ya kulimbikitsidwa mwauzimu. Chotero Yesu akutchula zitsanzo Zamalemba kusonyeza kuti Yehova Mulungu sanalinganize konse kugwira ntchito kopanikiza mosayenerera kotero m’Chilamulo Chake cha Sabata.
Pamene anali ndi njala, akutero Yesu, Davide ndi anthu ake anaima pa chihema nadya mitanda yamkate yowonetsa. Ngakhale kuli kwakuti mitandayo inali itachotsedwa kale pamaso pa Yehova ndi kulowedwa mmalo ndi yatsopano, iyo kwenikweni inasungidwira ansembe kuti adye. Chikhalirechobe, m’mikhalidweyo, Davide ndi anthu ake sanatsutsidwe chifukwa cha kuidya.
Popereka chitsanzo china, Yesu anati: “Simunawerenga kodi m’Chilamulo, kuti tsiku lasabata ansembe m’kachisi amaipitsa tsiku lasabata koma nakhala opanda tchimo?” Inde ngakhale pa Sabata ansembe amapitirizabe kupha nyama ndi ntchito ina pa kachisi pokonzekera nsembe zanyama! “Koma ndinena kwa inu,“ Yesu akutero, “wa kuposa kachisiyo ali pompano.”
Podzudzula Afarisiwo, Yesu akupitirizabe kuti: “Koma mukadadziwa nchiyani ichi, ndifuna chifundo, sinsembe ayi; simukadaweruza olakwa iwo osachimwa.” Ndiyeno akumaliza mwakumati: “Pakuti Mwana wa munthu ali mwini tsiku lasabata.” Kodi Yesu anatathauzanji mwakutero?
Yesu anali kusonya ku ulamuliro wake Waufumu wamtendere wa zaka chikwi. Kwazaka 6, 000 anthu avutika ndi ukapolo wothodwetsa kudzera mwa Satana Mdyerekezi, pamene chiwawa ndi nkhondo ziri zowanda. Kumbali ina, ulamuliro waukulu wasabata wa Kristu udzakhala nthawi ya mpumulo kuchokera kumavuto onse otero ndi chitsenderezo. Mateyu 12:1-8; Levitiko 24:5-9; 1 Samueli 21:1-6; Numeri 28:9; Hoseya 6:6.
◆ Kodi ndi chinenezo chotani chimene chinaperekedwa pa ophunzira a Yesu, ndipo kodi Yesu akuchiyankha motani?
◆ Kodi nkulephera kotani kwa Afarisi kumene Yesu akudziwikitsa?
◆ Kodi ndim’njira yotani mu imene Yesu ali “Mbuye wa sabata”?