-
Yehova—Gwero la Chilungamo ChenicheniNsanja ya Olonda—1998 | August 1
-
-
11. (a) Kodi nchifukwa ninji Afarisi anafunsa Yesu za kuchiritsa pa Sabata? (b) Kodi yankho la Yesu linavumbulanji?
11 Pamene anali kuchita utumiki ku Galileya m’ngululu ya m’chaka cha 31 C.E., Yesu anaona mwamuna wina wadzanja lopuwala m’sunagoge. Popeza kuti panali pa Sabata, Afarisi anafunsa Yesu kuti: “Nkuloleka kodi kuchiritsa tsiku la Sabata?” M’malo modera nkhaŵa za mavuto a mwamuna wovutikayu, cholinga chawo chinali kupeza chifukwa choimbira mlandu Yesuyo, monga momwe funso lawo linasonyezera. Ndiye chifukwa chake Yesu anachita chisoni ndi kuuma kwa mitima yawo! Kenako iye anafunsanso Afarisiwo mosapita m’mbali funso lofanana kuti: “Kodi nkuloledwa dzuŵa la Sabata kuchita zabwino?” Popeza kuti iwo sanayankhe, Yesu anadziyankhira funso lake mwa kuwafunsa ngati sangapulumutse nkhosa imene yagwera m’dzenje pa Sabata.b “Nanga kuposa kwake kwa munthu ndi nkhosa nkotani!” Yesu anatero, atafotokoza mfundo zosatsutsika. “Chifukwa cha ichi nkuloleka [kapena kuti, nkolondola] kuchita zabwino tsiku la Sabata,” iye anatero. Chilungamo cha Mulungu sichiyenera kutsekerezedwa ndi miyambo ya anthu. Atafotokoza bwino mfundo imeneyo, Yesu anachiritsa dzanja la mwamunayo.—Mateyu 12:9-13; Marko 3:1-5.
-
-
Yehova—Gwero la Chilungamo ChenicheniNsanja ya Olonda—1998 | August 1
-
-
b Chitsanzo cha Yesu chinali choyenerera chifukwa chakuti chilamulo chapakamwa cha Ayuda chinkawavomereza kuthandiza nyama yomwe yaloŵa m’vuto pa Sabata. Nthaŵi zinanso zingapo, panali mikangano pankhani imodzimodziyi, yakuti kaya kunali kololeka kuchiritsa pa Sabata.—Luka 13:10-17; 14:1-6; Yohane 9:13-16.
-