Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Maulosi Onena za Mesiya Amatsimikizira Kuti Yesu Analidi Mesiya?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    • b Dzina lakuti Emanueli ndi la Chiheberi ndipo limatanthauza kuti “Mulungu Ali Nafe.” Dzinali limafotokoza bwino za udindo wa Yesu monga Mesiya. Kubwera kwake padzikoli komanso zimene anachita, zinasonyeza kuti Mulungu ali kumbali ya anthu omwe amamulambira.​—Luka 2:27-32; 7:12-16.

  • Kodi Baibulo Limaphunzitsa Zotani Zokhudza Mariya Virigo?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    • Polosera mmene zidzakhalire kuti Mesiya aonekere padzikoli, Yesaya analemba kuti: “Tamverani mtsikana adzatenga pakati ndipo adzabereka mwana wamwamuna.” (Yesaya 7:14) Mothandizidwa ndi mzimu woyera, Mateyu anafotokoza kuti ulosi wa Yesaya unkanena za Mariya amene anali ndi pakati pa Yesu. Mateyu atafotokoza kuti Mariya anali ndi pakati mothandizidwa ndi mzimu woyera, ananenanso kuti: “Zonsezi zinachitika kuti zimene Yehova ananena kudzera mwa mneneri wake zikwaniritsidwe. Iye anati: “Tamverani namwalia adzatenga pakati ndipo adzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo adzam’patsa dzina lakuti Emanueli,” lotanthauza “Mulungu Ali Nafe,” likamasuliridwa.”—​Mateyu 1:​22, 23.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena