Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Yesu—Maziko a Kusagwirizana
NTHAWl PANG’ONO pambuyo pa kusangalatsidwa ku nyumba ya Simoni, Yesu akuyamba ulendo wake wachiwiri wa kulalikira ku Galileya. Pa ulendo wake womalizira wa ku gawolo, iye anali limodzi ndi ophunzira ake oyambirira, Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane. Koma tsopano atumwi 12 akupita naye, limodzinso ndi akazi ena. Awa akuphatikizapo Mariya wa Magdala, Suzana, ndi Johana, amene mwamuna wake ndi nduna ya Mfumu Herode.
Pamene kayendedwe ka uminisitala wa Yesu kakupita patsogolo, chimodzimodzinso kusagwirizana m’chigwirizano ndi ntchito yake. Munthu wogwidwa ndi ziwanda, yemwe alinso wakhungu ndipo wosakhoza kulankhula, akubweretsedwa kwa Yesu. Pamene Yesu amchiritsa iye, kotero kuti iye ali womasuka ku kulamuliridwa ndi ziwanda ndipo angathe ponse pawiri kulankhula ndi kupenya, makamu onse a anthu anazizwa. Iwo anayamba kunena kuti: “Uyu si mwana wa Davide kodi?”
Khamu linasonkhana mu unyinji waukulu kuzungulira nyumba imene Yesu ali kukhala kotero kuti iye ndi ophunzira ake sakanatha ngakhale kudya chakudya. Pambali pa awo omwe akulingalira kuti mwinamwake iye ali “Mwana wa Davide” wolonjezedwa, pali alembi ndi Afarisi omwe abwera kuchokera ku Yerusalemu kudzamuchititsa manyazi iye. Pamene abale ake a Yesu amva ponena za phokoso lomwe liri kukambidwa ponena za Yesu, iwo akubwera kudzamugwira iye. Chifukwa ninji?
Chabwino, abale ake enieni a Yesu sanakhulupirirebe kuti iye ali Mwana wa Mulungu. Ndiponso, phokoso launyinji ndi ndewu imene iye wapangitsa siiri kwenikwenidi mkhalidwe wa Yesu yemwe iwo anamudziwa pamene anali kukula ku Nazarete. Chotero iwo akukhulupirira kuti pali chinachake cholakwika kwambiri ndi maganizo a Yesu. “lye wachita misala,” iwo akumaliza motero, ndipo iwo akufuna kumugwira iye ndi kumuchotsa iye kuchokera kumeneko.
Koma chitsimikiziro chiri chomveka kuti Yesu wachiritsa munthu wogwidwa ndi ziwanda. Alembi ndi Afarisi akudziwa kuti sangakane chenicheni cha chimenechi, limodzinso ndi zozizwitsa zina za Yesu. Chotero kuti amuchititse Yesu manyazi iwo akuuza anthu: “Uyu amatulutsa ziwanda kokha ndi mphamvu yake ya Beelzebule, mkulu wa ziwanda.”
Kudziwa malingaliro awo, Yesu akuitana alembi ndi Afarisi kwa iye ndi kunena kuti: “Ufumu uli wonse wogawanika pa wokha sukhalira kupasuka, ndi mudzi uli wonse kapena banja logawanika pa lokha silidzakhala. [Mu njira yofananayo NW], ngati Satana amatulutsa Satana, iye wagawanika payekha; ndipo udzakhala bwanji ufumu wake?”
Iri nzeru yosakaza chotani nanga! Popeza Afarisi akunena kuti anthu a mu mathayo awo anatulutsa ziwanda, Yesu akuwafunsanso kuti: “Ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya Beelzebule, ana anu amazitulutsa ndi mphamvu ya yani?” M’mawu ena, mulandu wawo motsutsana ndi Yesu mu njira yofananayo ungagwiritsiridwe ntchito kwa iwo monga momwe akupangira kwa iye. Yesu kenaka akuchenjeza: “Koma ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu yake ya mzimu wa Mulungu, pomwepo Ufumu wa Mulungu unafika pa inu.”
Kuchitira chitsanzo kuti kutulutsa kwake kwa ziwanda chiri chitsimikiziro champhamvu yake kuposa ya Satana, Yesu akuti: “Kapena akhoza bwanji munthu kulowa m’banja la munthu wolimba, ndi kufunkha akatundu ake, ngati iye sayamba kumanga munthu wolimbayo? Ndipo pamenepo adzafunkha za m’banja lake, lye amwazamwaza.” Afarisi mwachiwonekere ali otsutsana ndi Yesu, kuchitira chitsanzo iwo eni kuti ali athenga a Satana. Iwo akumwazamwaza Aisrayeli kuchokera kwa iye.
Mofananamo, Yesu akuchenjeza otsutsaa usatana amenewa kuti: “Chamwano cha pa mzimu woyera sichidzakhululukidwa.” lye akulongosola: “Amene ali yense anganenere Mwana wa munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene ali yense anganenere mzimu woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi ino kapena irinkudzayo.” Alembi amenewo ndi Afarisi apanga chimo lalikulu losakhululukidwa mwa moipidwa kupereka kwa Satana chomwe mwachidziwikire chiri chopangidwa mozizwitsa ndi kugwira ntchito kwa mzimu woyera wa Mulungu. Mateyu 12:22-32; Marko 3:19-30; Yohane 7:5.
◆ Kodi ndimotani mmene ulendo wachiwiri wa Yesu wa ku Galileya uli wosiyana ndi woyambirira?
◆ Kodi nchifukwa ninji abale ake a Yesu akuyesa kumugwira iye?
◆ Kodi ndimotani mmene Afarisi akuyesa kuchititsa manyazi zozizwitsa za Yesu, ndipo kodi ndimotani mmene Yesu akutsutsira iwo?
◆ Kodi Afarisi amenewo achimwira chiyani, ndipo ndi chifukwa ninji?