Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 8/15 tsamba 8-9
  • Yesu Adzudzula Afarisi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Adzudzula Afarisi
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Yesu Adzudzula Afarisi
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Yesu Anadzudzula Afarisi
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yona Aphunzira za Chifundo cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Anaphunzira pa Zolakwa Zake
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 8/15 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Yesu Adzudzula Afarisi

NGATI NDI mphamvu ya Satana imene iye akutulutsira ziwanda, Yesu atsutsa, ndiye kuti Satana wagawanika. “Kaya anthu inu mupanga mtengo wokoma ndi chipatso chake chokoma,”iye akupitiriza, “kapena mupanga mtengo woipa ndi chipatso chake choipa; pakuti mtengo udziwika ndi chipatso chake.”

Chiri chopusa kuzenga mlandu kuti chipatso chabwino chakutulutsa ziwanda chinali chifukwa chakuti Yesu anali kutumikira Satana. Ngati chipatso chiri chabwino, mtengo sungakhale woipa. Ku mbali ina, chipatso choipa cha Afarisi cha chinenezo chabodza ndi chitsutso chopanda maziko motsutsana ndi Yesu chiri chitsimikiziro chakuti iwo eni ali oipa. “Akubadwa inu a njoka,” Yesu akulongosola, “mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti mkamwa mungolankhula mwa kusefukira kwake kwa mtima.”

Popeza mawu athu amaunikira mkhalidwe wa mitima yathu, zomwe timanena zimapereka maziko kaamba ka chiweruzo, “ndinena ndi inu,” anatero Yesu “kuti mawu onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mawu ako, ndipo ndi mawu ako omwe udzatsutsidwa.”

Mosasamala kathu za ntchito zamphamvu zonse za Yesu, alembi ndi Afarisi akufunsa: “Mphunzitsi, tifuna kuwona chizindikiro cha Inu.” Ngakhale kuti amuna awa a ku Yerusalemu angakhale asanawone mwaumwini zozizwitsa zake, pali chizindikiritso chaumboni wowona ndi maso ponena za iwo. Chotero Yesu akuuza atsogoleri a Chiyuda: “Akubadwa oipa achigololo afunafuna chizindikiro; ndipo sichidzapatsidwa kwa iwo chizindikiro, komatu chizindikiro cha Yona mneneri.”

Kulongosola zimene akutanthauza, Yesu akupitiriza: “Pakuti monga Yona anali m’mimba mwa chinsomba masiku atatu ndi usiku wake, chomwecho Mwana wa munthu adzakhala mu mtima mwa dziko lapansi masiku atatu ndi usiku wake.”Pambuyo pa kumezedwa ndi nsomba, Yona anatuluka monga ngati waukitsidwa, chotero Yesu akuneneratu kuti iye adzafa ndipo pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa wamoyo. Koma atsogoleri a Chiyuda, ngakhale pamene pambuyo pake Yesu anaukitsidwa, anakana “chizindikiro cha Yona.”

Chotero Yesu ananena kuti amuna a ku Nineve omwe anatembenuka mtima pakulalikira kwa Yona adzaukitsidwa pa chiweruzo kutsutsa Ayuda omwe anakana Yesu. Mofananamo, iye akusonyeza chofanana nacho cha Mfumu yaikazi ya ku Seba, yomwe inabwera kuchokera ku malekezero adziko kudzamva nzeru ya Solomo ndi kudabwitsidwa pa zimene anawona ndi kumva. “Ndipo onani!” Yesu akuzindikiritsa, “wakuposa Solomo ali pano.”

Yesu kenaka akupereka chisonyezero chamwamuna amene kuchokera mwa iye mizimu yoipa inatuluka. Mwamunayo, angakhale kuli tero, sadzaza nyumbayo ndi zinthu zabwino ndipo chotero akhala ogwidwa ndi mizimu ina isanu ndi iwiri yoipa koposa. “Kotero kudzakhalanso kwa obadwa oipa amakono,“ Yesu akutero. Mtundu wa Aisrayeli unayeretsedwa ndipo unakumana ndi maSinthidwe​- monga kuchoka kwa kanthawi ka mzimu wonyansa. Koma kukana kwamtunduwo kwa aneneri a Mulungu, kufikira mkuchotsa kwawo Kristu iye mwiniyo, kumavumbulutsa mkhalidwe wake woipa kukhala woipa koposa pachiyambi.

Pamene Yesu anali kulankhula, mayi wake ndi abale ake anafika ndi kukhala kumapeto kwa khamu. Chotero wina anati: “Tawonani, amayi wanu ndi abale anu aima pabwalo, nafuna kulankhula nanu.”

“Amayi wanga ndani, ndipo abale wanga ndi ayani?” Yesu anafunsa. Kutambalika dzanja lake pa ophunzira ake, iye anati: “Penyani amayi wanga ndi abale anga! Pakuti aliyense amene adzachita chifuniro cha Atate wanga wa kumwamba, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo wanga, ndi amayi wanga.” M’njira Yesu anasonyeza kuti mosasamala kanthu kuti ndi chikondi chotani chimene chimamangirira iye kwa anansi ake, chikondi poserapo chinali chiyanjo ndi ophunzira ake. Mateyu 12:33-50; Marko 3:31-35; Luka 8:19-21.

◆ Kodi ndimotani mmene Afarisi analepherera kupanga ponse pawiri mtengo wabwino ndi chipatso chabwino?

◆ Kodi nchiyani chimene china li “chizindikiro cha Yona,“ ndipo ndimotani mmene icho chinakanidwira?

◆ Ndimotani mmene mtundu wa Israyeli unaliri wofanana ndi munthu mwa amene mzimu wonyansa unatuluka?

◆ Ndimotani mmene Yesu anagogomezera chiyanjano chake ndi ophunzira ake?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena