Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 11/15 tsamba 28-31
  • Kodi Mukanamzindikira Mesiya?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mukanamzindikira Mesiya?
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Tifuna Kuona Chizindikiro”
  • “Okonda Ndalama”
  • “Kuwopa Ayuda”
  • Kodi Mumamzindikiradi Mesiya?
  • Mesiya Ndiye Njira ya Mulungu Yopulumutsira Anthu
    Nsanja ya Olonda—2009
  • N’chifukwa Chiyani Anakana Mesiya?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • “Tapeza Ife Mesiya”!
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 11/15 tsamba 28-31

Kodi Mukanamzindikira Mesiya?

YESU KRISTU anatha zaka zitatu ndi theka akulalikira Mawu a Mulungu pakati pa Aisrayeli. Koma podzafika nthaŵi pamene anatsiriza utumiki wake wa padziko lapansi, ochuluka a amene anali ndi moyo panthaŵiyo anali atamkana kuti sanali Mesiya, kapena “Wodzozedwa” wolonjezedwayo wa Mulungu. Chifukwa ninji?

Baibulo limatithandiza kudziŵa zifukwa zingapo zimene Ayuda a m’zaka za zana loyamba sanazindikirire Yesu kukhala Mesiya. Zitatu za zifukwa zimenezi zimachititsa ambiri kukana kuzindikira malo a Yesu lerolino monga Mfumu yolamulira Yaumesiya.

“Tifuna Kuona Chizindikiro”

Chifukwa chimodzi chimene Ayuda a m’zaka za zana loyamba sanazindikirire Mesiya chinali chakuti anakana kulandira zizindikiro za m’Malemba zosonyeza Umesiya wake. Nthaŵi ndi nthaŵi, anthu amene anali kumvetsera kwa Yesu anafuna kuti awasonyeze chizindikiro chopereka umboni wakuti anachokera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, Mateyu 12:38 amanena kuti ena a alembi ndi Afarisi anati: “Mphunzitsi, tifuna kuona chizindikiro cha inu.” Kodi Yesu anali asanawasonyeze kale zizindikiro? Ndithudi anali atatero.

Panthaŵiyo Yesu anali atachita kale zozizwitsa zambiri. Anali atasandutsa madzi kukhala vinyo, atachiritsa mnyamata amene anali kufuna kufa, atachiritsa apongozi a Petro odwala, atayeretsa mwamuna wakhate, atachititsa mwamuna wamanjenje kuyenda, atachiritsa mwamuna wina yemwe anali atadwala zaka 38, atabwezeretsa dzanja lopuwala la mwamuna wina, atachotsera anthu ambiri matenda awo oŵaŵa, atachiritsa kapolo wa mkulu wa asilikali, ataukitsa kwa akufa mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye, ndipo anali atachiritsa mwamuna wina wakhungu ndi wosalankhula. Zozizwitsa zimenezi zinachitikira m’Kana, Kapernao, Yerusalemu, ndi Naini. Ndiponso, mbiri ya zozizwitsa zimenezi inafala m’Yudeya monse ndi malo ozungulira.​—Yohane 2:1-12; 4:46-54; Mateyu 8:14-17; 8:1-4; 9:1-8; Yohane 5:1-9; Mateyu 12:9-14; Marko 3:7-12; Luka 7:1-10; 7:11-17; Mateyu 12:22.

Ndithudi, sipanali kupereŵera kwa zizindikiro zopereka umboni wakuti Yesu anali Mesiya. Ngakhale kuti anasonyeza zizindikiro zambiri kwa anthu, sanamkhulupirire. Awo amene anaona umboni wakuti Yesu anatumizidwa ndi Mulungu koma sanamzindikire kukhala Mesiya anali akhungu mwauzimu. Mitima yawo inali yolimba ndipo yosakhoza kuloŵa choonadi.​—Yohane 12:37-41.

Bwanji ponena za tsiku lathu? Anthu ena amanena kuti, “Ndimangokhulupirira zimene ndimaona ndi maso anga.” Koma kodi imeneyo ilidi njira yanzeru imene tingatenge? Ulosi wa Baibulo ukusonyeza kuti Yesu waikidwa kale kukhala Mfumu yakumwamba mu Ufumu Waumesiya. Popeza sakuoneka, tikufunikira chizindikiro chotithandiza kuzindikira ulamuliro wake, umene unasonyeza chiyambi cha masiku otsiriza a dongosolo loipali la zinthu. Kodi mumachidziŵa chizindikirocho?​—Mateyu 24:3.

Malinga ndi kunena kwa Baibulo, chiyambi cha ulamuliro wa Kristu monga Mfumu Yaumesiya chinali kudzasonyezedwa ndi nkhondo, zivomezi, njala, ndi miliri zimene sizinachitikepo. Mu “masiku otsiriza,” maunansi a anthu adzakhala adyera, aumbombo, ndipo osadziletsa. (2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:6, 7; Luka 21:10, 11) Kusiyapo umboni woŵerengera zaka, zochitika zosiyanasiyana zoposa 20 za masiku otsiriza zimasonyeza kuti chiyambi cha ulamuliro wa Mesiya chinali mu 1914.​—Onani Nsanja ya Olonda ya March 1, 1993, tsamba 5.

“Okonda Ndalama”

Kukonda chuma kunali chifukwa china chimene Ayuda anakanira Yesu monga Mesiya. Kuona chuma kukhala chofunika kwambiri kunaletsa ambiri kutsatira Yesu. Mwachitsanzo, Afarisi ankadziŵika kukhala “okonda ndalama.” (Luka 16:14) Talingalirani za chitsanzo cha wolamulira wachinyamata wina wachuma amene anafikira Yesu ndi kufunsa mmene akanapezera moyo wosatha. “Sunga malamulo,” Yesu anayankha motero. “Zonsezi ndinazisunga, ndisoŵanso chiyani?” mnyamatayo anafunsa motero, akumasonyeza kuti anazindikira kuti panali zambiri zofunika kuposa kusunga malamulo akutiakuti. “Kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphaŵi, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate,” Yesu anamuuza motero. Unali mwaŵi waukulu chotani nanga​—kukhala wophunzira wa Mesiya! Komabe wolamulirayo anachoka, ali wachisoni. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti chuma cha padziko lapansi chinali chofunika kwambiri kwa iye kuposa chuma cha kumwamba.​—Mateyu 19:16-22.

Mkhalidwewo sunasinthe. Kukhala wotsatira weniweni wa Mfumu Yaumesiya kumatanthauza kuika zinthu zauzimu patsogolo pa zina zilizonse, kuphatikizapo katundu wa padziko lapansi. Kwa alionse amene ali ndi malingaliro okonda chuma, kuchita zimenezi ndi vuto. Mwachitsanzo, amishonale aŵiri okwatirana kudziko lina la Kummaŵa analankhula ndi mkazi wina za Baibulo. Pokhulupirira kuti akanakonda kuphunzira zambiri ponena za Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, okwatiranawo anamgaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kodi anachitanji? “Kodi magaziniwa adzandithandiza kupanga ndalama zambiri?” anafunsa motero. Mkaziyo anali kufunitsitsa zinthu zakuthupi kuposa zinthu zauzimu.

Okwatirana amodzimodziwo anaphunzira Baibulo ndi mnyamata wina amene anayamba kufika pamisonkhano ku Nyumba ya Ufumu. “Ukutaya nthaŵi yako,” anamuuza motero makolo ake. “Uyenera kupeza ntchito yachiŵiri ya m’madzulo ndi kupeza ndalama zambiri.” Nzomvetsa chisoni chotani nanga pamene makolo alimbikitsa ana awo kuika zinthu zakuthupi patsogolo pa kuphunzira za Mfumu Yaumesiya! “Ndi chuma chake chonse wolamulira sangagule zaka zikwi khumi za moyo,” umatero mwambi wachitchaina.

Ambiri azindikira kuti kuphunzira za Mfumu Yaumesiya ndi kuitsatira sikumasiya mpata wa chikondi cha pandalama. Mboni ina ya Yehova imene inali ndi malonda akeake opanga ndalama zambiri, inati: “Kukhala ndi ndalama zambiri nkwabwino kwambiri koma nkosafunikira. Ndalama si zimene zimachititsa munthu kukhala wachimwemwe.” Tsopano mkaziyo ali chiŵalo cha banja la Beteli panthambi ina ya ku Ulaya ya Watch Tower Society.

“Kuwopa Ayuda”

Kuwopa anthu kunalinso chifukwa china chimene Ayuda sanalandirire Yesu monga Mesiya. Kuvomereza Umesiya wake poyera kukanaipitsa mbiri yawo. Kwa ena zimenezo zinali zovuta kwambiri. Talingalirani za Nikodemo, chiŵalo cha khoti lalikulu lachiyuda lotchedwa Sanhedrin. Atachita chidwi ndi zizindikiro ndi ziphunzitso za Yesu, anavomereza kuti: “Rabi, tidziŵa kuti inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye.” Komabe Nikodemo anapita kwa Yesu usiku, mwinamwake kuti apeŵe kudziŵidwa ndi Ayuda ena.​—Yohane 3:1, 2.

Kwa ambiri amene anamva Yesu akulankhula, chiyanjo cha anthu chinali chofunika kwambiri kuposa cha Mulungu. (Yohane 5:44) Pamene Yesu anali ku Yerusalemu kaamba ka Phwando la Misasa mu 32 C.E., ‘kunali kung’ung’udza kwambiri za iye m’makamu a anthu.’ Palibe amene analankhula za Yesu poyera “chifukwa cha kuwopa Ayuda.” (Yohane 7:10-13) Ngakhale makolo a mwamuna amene Yesu anamchiritsa khungu sanafune kuvomereza kuti chozizwitsacho chinachokera kwa woimira Mulungu. Iwonso “anawopa Ayuda.”​—Yohane 9:13-23.

Lerolino, ena amadziŵa kuti Yesu tsopano akulamulira monga Mfumu Yaumesiya kumwamba, koma amawopa kuvomereza zimenezo poyera. Kwa iwo kutaya malo awo nkovuta kwambiri. Mwachitsanzo, Mboni ya Yehova ina ku Germany inali ndi makambitsirano a m’Baibulo ndi mwamuna wina amene anavomereza kuti: “Zimene inu Mboni mumalalikira ponena za Baibulo nzoona. Koma ngati ndikhala Mboni lero, podzafika maŵa aliyense adzakhala atadziŵa za zimenezi. Kodi adzaganizanji kuntchito, anansi, ku kalabu limene ineyo ndi banja langa timapitako? Sindingazipirire zimenezo.”

Kodi nchiyani chimachititsa kuwopa anthu? Kunyada, kukonda kutchuka m’banja ndi pakati pa mabwenzi, kuwopa kutonzedwa ndi kusekedwa, nkhaŵa ya kukhala wosiyana ndi anthu ochuluka. Malingaliro ameneŵa amakhala chiyeso makamaka kwa awo amene amayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Mwachitsanzo, msungwana wina anachita chidwi kuphunzira za Paradaiso amene Ufumu Waumesiya udzakhazikitsa padziko lapansi mu ulamuliro wa Yesu Kristu. Koma anali kukonda kwambiri disco, ndipo kuwopa anthu kunamletsa kulankhula ndi ena za chiyembekezo chimenechi. Potsirizira pake, analimbika mtima ndi kulankhula momasuka za Baibulo. Mabwenzi ake a ku disco anamkana, koma mwamuna wake ndi makolo ake anasonyeza chidwi. Mkaziyo ndi amayi wake anabatizidwa m’kupita kwa nthaŵi, ndipo mwamuna wake ndi atate wake anayamba kuphunzira Baibulo. Anapeza mphotho yabwino chotani nanga chifukwa cha kugonjetsa kuwopa anthu!

Kodi Mumamzindikiradi Mesiya?

Pamene Yesu anali kufa pamtengo wozunzirapo, ena a ophunzira ake analipo. Anali atamzindikira kukhala Mesiya wonenedweratuyo. Panalinso olamulira achiyuda, amene tinganene kuti anali kufunabe chizindikiro. “Adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Kristu [kapena Mesiya] wa Mulungu, wosankhidwa wake.” (Luka 23:35) Kodi sakanaleka kufuna chizindikiro? Yesu anali atachita zozizwitsa zambirimbiri. Ndiponso, kubadwa kwake, utumiki wake, kuzengedwa mlandu kwake, kuphedwa, ndi kuukitsidwa kwake zinakwaniritsa Malemba Achihebri aulosi ambiri.​—Onani “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., masamba 343-4.

Odutsa pa malowo anamtonza Yesu, pokhala atakana umboni wa Umesiya. (Mateyu 27:39, 40) Mokondetsa chuma asilikali anagaŵana zovala za Yesu, akumachita maere pa malaya ake. (Yohane 19:23, 24) Ena analephera chifukwa cha kuwopa anthu. Mwachitsanzo, talingalirani za Yosefe wa ku Arimateya, chiŵalo cha Sanhedrin. Iye anali “wophunzira wa Yesu, koma mobisika, chifukwa cha kuwopa Ayuda.” Pambuyo pa imfa ya Mesiya, Yosefe ndi Nikodemo anasamalira thupi la Yesu. Chotero Yosefe anagonjetsa kuwopa anthu kwake.​—Yohane 19:38-40.

Ngati munali ndi moyo m’zaka za zana loyamba, kodi mukanamzindikira Yesu kukhala Mesiya? Kuchita motero kukanafuna kuti mulandire umboni wa m’Malemba, kukana malingaliro a kukonda chuma, ndi kusagonjera pa kuwopa anthu. M’masiku ano otsiriza, aliyense wa ife ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimamzindikira Yesu tsopano kukhala Mfumu yakumwamba Yaumesiya?’ Posachedwapa adzayamba kulamulira dziko lapansi. Zimenezo zitachitika, kodi mudzakhala pakati pa awo amene amazindikiradi Yesu Kristu kukhala Mesiya wolonjezedwayo?

[Zithunzi patsamba 28]

Musanyalanyaze umboni wakuti Yesu ndiye Mfumu Yaumesiya

[Chithunzi patsamba 31]

Kuphunzira za Mesiya nthaŵi zambiri kumafuna kugonjetsa mantha a zimene ena anganene

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena