Chifukwa Chimene Mboni za Yehova Zimakhalira Zodikira
“Dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.” —MATEYU 24:42.
1. Kodi chenjezo lakuti “dikirani” likuperekedwa kwa ndani?
KWA mtumiki wa Mulungu aliyense—kaya akhale wachichepere kapena wachikulire, kaya akhale wodzipatulira chatsopano kapena wa mbiri yaitali ya utumiki—Baibulo limachenjeza kuti: “Dikirani”! (Mateyu 24:42) Kodi nchifukwa ninji chimenechi chili chofunika?
2, 3. (a) Kodi ndi chizindikiro chotani chimene Yesu analongosola momvekera bwino, ndipo kodi kukwaniritsidwa kwa ulosi kwasonyezanji? (b) Kodi ndi mkhalidwe wotani wotchulidwa pa Mateyu 24:42 umene umaika pachiyeso chikhulupiriro chathu, ndipo umatero motani?
2 Chakumapeto kwa utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu ananeneratu za chizindikiro cha kukhalapo kwake kosaoneka ndi maso m’mphamvu ya Ufumu. (Mateyu, machaputala 24 ndi 25) Iye analongosola momvekera bwino nthaŵi imeneyo ya kukhalapo kwake kwaufumu—ndipo zochitika zokwaniritsa ulosi zimasonyeza kuti iye anaikidwa pa mpando wachifumu monga Mfumu kumwamba mu 1914. Iye anatchulanso chochitika chimene panthaŵiyo chikaika pachiyeso chikhulupiriro chathu. Zimenezi zinali ponena za nthaŵi pamene iye akachitapo kanthu monga Wakupha wowononga dongosolo loipa lilipoli mkati mwa chisautso chachikulu chimene Yesu anati: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.” Anali ndi zimenezo m’maganizo pamene anati: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.”—Mateyu 24:36, 42.
3 Kusadziŵa kwathu tsiku ndi nthaŵi pamene chisautso chachikulu chidzayamba kumafuna kuti ngati tidzinenera kukhala Akristu, tiyenera kukhala ndi moyo monga Akristu owona tsiku lililonse. Kodi njira imene mumagwiritsira ntchito moyo wanu idzakhala ndi chivomerezo cha Ambuye pamene chisautso chachikulu chifika? Kapena ngati imfa ndiyo iyamba kufika, kodi adzakukumbukirani monga munthu amene anatumikira Yehova mokhulupirika mpaka kumapeto a moyo wanu wa nthaŵi ino?—Mateyu 24:13; Chivumbulutso 2:10.
Ophunzira Oyambirira Analimbikira Kukhala Odikira
4. Kodi tingaphunzirenji pa chitsanzo cha Yesu cha kudikira kwauzimu?
4 Yesu Kristu iye mwini anapereka chitsanzo chabwino cha kudikira kwauzimu. Iye anapemphera kaŵirikaŵiri ndi mwaphamphu kwa Atate wake. (Luka 6:12; 22:42-44) Pamene anayang’anizana ndi ziyeso, anadalira kwambiri pa chitsogozo cha Malemba. (Mateyu 4:3-10; 26:52-54) Iye sanalole kuchenjenekedwa pantchito imene Yehova anamtuma. (Luka 4:40-44; Yohane 6:15) Kodi awo amene anadziona kukhala otsatira a Yesu anayenera kukhala odikira mofananamo?
5. (a) Kodi nchifukwa ninji kunali kovuta kwa atumwi a Yesu kusunga kukhazikika kwawo kwauzimu? (b) Kodi ndi chithandizo chanji chimene Yesu anapatsa atumwi ake pambuyo pachiukiriro chake?
5 Panthaŵi zina, ngakhale atumwi a Yesu anandenguma. Chifukwa cha changu chopambanitsa ndi malingaliro olakwika, iwo anakhala ogwiritsidwa mwala. (Luka 19:11; Machitidwe 1:6) Asanaphunzire kudalira pa Yehova mokwanira, ziyeso zadzidzidzi zinawasokoneza. Motero, pamene Yesu anamangidwa, atumwi ake anathaŵa. Pambuyo pake usiku womwewo, Petro, chifukwa cha mantha, anakana mobwerezabwereza ngakhale za kumdziŵa Kristu. Atumwiwo anali asanalabadire ndi mtima wonse uphungu wa Yesu wakuti: “Chenjerani ndi kupemphera.” (Mateyu 26:41, 55, 56, 69-75) Pambuyo pa kuukitsidwa kwake Yesu anagwiritsira ntchito Malemba kulimbitsa chikhulupiriro chawo. (Luka 24:44-48) Ndipo pamene kunaonekera kuti ena a iwo akanaika utumiki woikizidwa kwa iwo pamalo achiŵiri, Yesu anawalimbitsa kusumika maganizo awo pa ntchito yofunika kwambiri.—Yohane 21:15-17.
6. Kodi Yesu poyambirirapo anachenjeza ophunzira ake za misampha iŵiri iti?
6 Poyambirira, Yesu anali atachenjeza ophunzira ake kuti sanafunikire kukhala mbali ya dziko. (Yohane 15:19) Iye anali atawalangizanso kusachita umbuye pa wina ndi mnzake koma kutumikira pamodzi monga abale. (Mateyu 20:25-27; 23:8-12) Kodi iwo analabadira uphungu wake? Kodi iwo anaika patsogolo ntchito imene iye anali atawapatsa?
7, 8. (a) Kodi mbiri yopangidwa ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba imasonyeza motani kuti iwo analabadira chenjezo la Yesu? (b) Kodi nchifukwa ninji kudikira kwauzimu kopitirizabe kunali kofunika?
7 Kwa nthaŵi yonse imene atumwi anakhalapo, anatetezera mpingo. Mbiri yakale imachitira umboni kuti Akristu oyambirira sanadziloŵetse m’nkhani zandale za ufumu wa Roma ndi kuti analibe kagulu kolemekezeka ka atsogoleri achipembedzo. Mmalo mwake, iwo anali alengezi akhama a Ufumu wa Mulungu. Pofika kumapeto kwa zaka za zana loyamba, anali atachitira umboni kuzungulira mu ufumu wa Roma wonse, akumapanga ophunzira mu Asia, Ulaya, ndi North Africa.—Akolose 1:23.
8 Komabe, zokwaniritsidwa ndi kulalikira zimenezo sizinatanthauze kuti kudikira kwauzimu kunakhala kosafunikiranso. Kufika kwa Yesu konenedweratu kunali kudakali kutali mtsogolo. Ndipo pamene mpingo unaloŵa m’zaka za zana lachiŵiri C.E., panabuka mikhalidwe imene inaika pangozi uzimu wa Akristu. Motani?
Awo Amene Analeka Kukhala Odikira
9, 10. (a) Pambuyo pa kumwalira kwa atumwi onse, kodi ndi zochitika zotani zimene zinasonyeza kuti odzinenera kukhala Akristu sanali kudikira? (b) Kodi ndi malemba ati osonyezedwa m’ndime ino amene akanathandiza odzinenera kukhala Akristu kukhalabe olimba mwauzimu?
9 Ena amene anabwera mu mpingo anayamba kulongosola zikhulupiriro zawo m’mawu a nthanthi Zachigiriki, kotero kuti apangitse zimene analalikirazo kukhala zolandikira mosavuta kwa anthu a dziko. Pang’onopang’ono, ziphunzitso zachikunja, zonga ngati Utatu ndi kusafa kwa moyo kofalako, zinakhala mbali ya mtundu woipitsidwa wa Chikristu. Zimenezi zinachititsa kusiidwa kwa chiyembekezo cha zaka chikwi. Chifukwa ninji? Awo amene anatengera chikhulupiriro cha kusafa kwa moyo anaganiza kuti madalitso a ulamuliro wa Kristu onse akalandiridwa m’dziko lauzimu ndi moyo umene ukapulumuka thupi la munthu. Chotero sanaone kufunika kwa kudikira kaamba ka kukhalapo kwa Kristu m’mphamvu ya Ufumu.—Yerekezerani ndi Agalatiya 5:7-9; Akolose 2:8; 1 Atesalonika 5:21.
10 Mkhalidwe umenewu unakulitsidwa ndi zochitika zina. Ena amene anadzinenera kukhala oyang’anira Achikristu anayamba kugwiritsira ntchito mipingo yawo monga njira yopezera kutchuka. Iwo mwamachenjera anasonyeza malingaliro awoawo ndi ziphunzitso kukhala zofunika mofanana ndi Malemba kapena ngakhale kuwaposa. Pamene mpata unapezeka, tchalitchi champatuko chimenechi chinafikira pa kudzipereka kutumikira maubwino a boma landale.—Machitidwe 20:30; 2 Petro 2:1, 3.
Zotulukapo za Kudikira Kokulirapo
11, 12. Kodi nchifukwa ninji Kukonzanso Kwachiprotestanti sikunakhale chizindikiro cha kubweranso kwa kulambira kowona?
11 Pambuyo pa zaka mazana ambiri za nkhanza zochitidwa ndi Tchalitchi cha Roma Katolika, Ochirikiza Kukonzanso ena anatsutsa zimenezo m’zaka za zana la 16. Koma zimenezi sizinabwezeretse kulambira kowona. Kodi nchifukwa ninji sizinatero?
12 Ngakhale kuti magulu osiyanasiyana Achiprotestanti anagaluka ku ulamuliro wa Roma, iwo anatenga ziphunzitso zazikulu zambiri ndi machitachita ampatuko—kugaŵa pakati pa atsogoleri achipembedzo ndi anthu wamba, ndiponso chikhulupiriro cha Utatu, kusafa kwa moyo, ndi kuzunzidwa kwamuyaya pambuyo pa imfa. Ndiponso, mofanana ndi Tchalitchi cha Roma Katolika, iwo anapitiriza kukhala mbali ya dziko, akumagwirizana kwambiri ndi andale. Motero iwo ananyalanyaza ziyembekezo zilizonse za kubwera kwa Kristu monga Mfumu.
13. (a) Kodi nchiyani chimasonyeza kuti anthu ena anaonadi Mawu a Mulungu kukhala amtengo wapatali? (b) Mkati mwa zaka za zana la 19, kodi ndi chochitika chiti chimene chinakhala chapadera kwa ena odzinenera kukhala Akristu? (c) Kodi nchifukwa ninji ambiri anagwiritsidwa mwala?
13 Komabe, Yesu adaneneratu kuti pambuyo pa kumwalira kwa atumwi onse, oloŵa Ufumu enieni (omwe anawafanizira ndi tirigu) akapitiriza kukulira pamodzi ndi Akristu achiphamaso (kapena namsongole) kufikira nthaŵi ya kututa. (Mateyu 13:29, 30) Lerolino sitingathe kutchula motsimikizirika onsewo amene Ambuye anawaona kukhala tirigu. Koma nkofunika kudziŵa kuti mkati mwa zaka za mazana a 14, 15, ndi 16, panali amuna omwe anaika miyoyo yawo ndi ufulu wawo pangozi kuti alembe Baibulo m’chinenero cha anthu wamba. Ena sanangolandira Baibulo monga Mawu a Mulungu koma anakananso Utatu monga wotsutsa malemba. Ena anakana chikhulupiriro cha kusafa kwa moyo ndi kuzunzika kwa m’moto wahelo kukhala zosagwirizana konse ndi Mawu a Mulungu. Ndiponso, mkati mwa zaka za zana la 19, chifukwa cha kuphunzira Baibulo kowonjezereka, timagulu mu United States, Germany, England, ndi Russia tinayamba kusonyeza chikhutiro chakuti nthaŵi ya kubweranso kwa Kristu inali pafupi. Koma ziyembekezo zawo zambiri zinawagwiritsa mwala. Chifukwa ninji? Kwakukulukulu, chifukwa chinali chakuti iwo anadalira kwambiri pa anthu ndipo osati kwenikweni Malemba.
Mmene Iwoŵa Anatsimikizirira Kukhala Odikira
14. Longosolani njira imene C. T. Russell ndi anzake anagwiritsira ntchito kuphunzira Baibulo.
14 Ndiyeno, mu 1870, Charles Taze Russell ndi anzake ena anapanga kagulu kophunzira Baibulo mu Allegheny, Pennsylvania. Iwo sanali oyamba kuzindikira mfundo zambiri za chowonadi cha Baibulo zimene anazikhulupirira, koma pophunzira, anakhala ndi chizoloŵezi cha kupenda mosamalitsa malemba onse pafunso lopendedwa.a Cholinga chawo sichinali kupeza malemba ochirikizira malingaliro omwe anawakhulupirira kale, koma kuti atsimikizire kuti anafika pamfundo zimene zinagwirizana ndi kalikonse kamene Baibulo linanena pankhaniyo.
15. (a) Kodi nchiyani chimene enanso pambali pa Mbale Russell anazindikira? (b) Kodi nchiyani chimene chinasonyeza Ophunzira Baibulo kukhala osiyana ndi enaŵa?
15 Oŵerengeka ena, iwo asanatero, anali atazindikira kuti Kristu akabweranso mosaoneka ndi maso, monga mzimu. Ena anali ataona kuti cholinga cha kubweranso kwa Kristu, sichinali kudzatentha dziko lapansi ndi kufafaniza moyo wa anthu, koma, mmalo mwake, kudalitsa mabanja onse a padziko lapansi. Panali ngakhale oŵerengeka ena omwe anali atazindikira kuti chaka cha 1914 chikazindikiritsa mapeto a Nthaŵi za Akunja. Koma kwa Ophunzira Baibulo ogwirizana ndi Mbale Russell, izi sizinali mfundo za makambitsirano aumulungu chabe. Anazika miyoyo yawo pamfundo za chowonadi zimenezi ndipo anazifalitsa m’mitundu yonse pamlingo wosayerekezereka m’nyengo imeneyo.
16. M’chaka cha 1914, kodi nchifukwa ninji Mbale Russell analemba kuti: “Tili m’nyengo yachiyeso”?
16 Chikhalirechobe, iwo anafunikira kukhala odikira. Chifukwa ninji? Mwachitsanzo, ngakhale kuti anadziŵa kuti 1914 inasonyezedwa ndi ulosi wa Baibulo, iwo sanadziŵe motsimikizirika chimene chikachitika m’chaka chimenecho. Chimenechi chinawapatsa chiyeso. Mu The Watch Tower ya November 1, 1914, Mbale Russell analemba kuti: “Tiyeni tikumbukire kuti tili m’nyengo yachiyeso. . . . Ngati pali chifukwa chilichonse chimene chikachititsa aliyense kutaya chikhulupiriro mwa Ambuye ndi Chowonadi Chake ndi kuleka kudzimana kaamba ka Chifuniro cha Ambuye, pamenepo si kukonda Mulungu kochokera mu mtima kokha kumene kunasonkhezera chikondwerero mwa Ambuye, koma kanthu kena; mwinamwake chiyembekezo chakuti nthaŵiyo inali pafupi; kudziperekako kunali chabe kwa kanthaŵi.”
17. Kodi ndi motani mmene A. H. Macmillan, ndi ena ofanana naye, anasungira kukhazikika kwawo kwauzimu?
17 Ena anasiya utumiki wa Yehova kalelo. Koma A. H. Macmillan anali mmodzi wa awo amene sanatero. Zaka zochuluka pambuyo pake, iye anavomereza mowona mtima kuti: “Nthaŵi zina kuyembekezera kwathu deti lakutilakuti kunali kosagwirizana ndi zimene Malemba anapereka.” Kodi nchiyani chimene chinamthandiza kusunga kukhazikika kwauzimu? Iye anazindikira, monga momwe ananenera, kuti “pamene kuli kwakuti ziyembekezo zimenezo sizinakwaniritsidwe, zifuno za Mulungu sizinasinthe.” Anawonjezera kuti: “Ndinaphunzira kuti tiyenera kuvomereza zolakwa zathu ndi kupitirizabe kufufuza Mawu a Mulungu kuti tipeze chidziŵitso chowonjezereka.”b Modzichepetsa, Ophunzira Baibulo oyambirira amenewo analola Mawu a Mulungu kuwongolera malingaliro awo.—2 Timoteo 3:16, 17.
18. Kodi ndi motani mmene kudikira Kwachikristu kunapezera madalitso opita patsogolo m’nkhani ya kusakhala mbali ya dziko?
18 M’zaka zimene zinatsatirapo, kufunika kwawo kwa kukhala odikira sikunachepe. Ndithudi, iwo anadziŵa kuti Akristu sanafunikire kukhala mbali ya dziko. (Yohane 17:14; Yakobo 4:4) Mogwirizana ndi zimenezo, iwo sanagwirizane ndi Dziko Lachikristu m’kuvomereza Chigwirizano cha Mitundu monga chizindikiro chandale cha Ufumu wa Mulungu. Koma munali m’chaka cha 1939 pamene anazindikira bwino lomwe nkhani ya uchete Wachikristu.—Onani The Watchtower, November 1, 1939.
19. Kodi ndi mapindu otani a kuyang’anira mpingo amene apezedwa chifukwa chakuti gulu lakhalabe lodikira?
19 Iwo analibe kagulu ka atsogoleri achipembedzo, ngakhale kuti akulu ena osankhidwa analingalira kuti kulalikira mu mpingo ndiyo ntchito yokha imene iwo anayenera kuchita. Komabe, ndi chikhumbo chachikulu cha kugwirizana ndi Malemba, gululo linapendanso ntchito ya akulu mogwirizana ndi Malemba, akumatero mobwerezabwereza kupyolera mu Nsanja ya Olonda. Masinthidwe a m’gulu anapangidwa mogwirizana ndi zimene Malemba anasonyeza.
20-22. Kodi gulu lonse lakonzekeretsedwa mopita patsogolo motani kukwaniritsa ntchito yonenedweratu ya kulengeza Ufumu padziko lonse?
20 Gulu lonse linali kukonzekeretsedwa kukwaniritsa kotheratu ntchito imene Mawu a Mulungu anali atalongosola ponena za tsiku lathu. (Yesaya 61:1, 2) Kodi mbiri yabwino inafunikira kulalikidwa kumlingo wotani m’tsiku lathu? Yesu anati: “Uthenga wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Malinga ndi lingaliro laumunthu, ntchito imeneyo kaŵirikaŵiri yaoneka kukhala yosatheka.
21 Komabe, ndi chidaliro mwa Kristu monga Mutu wa mpingo, kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kapita patsogolo. (Mateyu 24:45) Mokhulupirika ndi molimba iwo asonyeza anthu a Yehova ntchito yofunikira kuchitidwa. Kuyambira mu 1919 kumkabe mtsogolo, chigogomezero chowonjezereka chinaikidwa pa utumiki wakumunda. Kwa ambiri, kunali kovuta kupita kunyumba ndi nyumba ndi kulankhula kwa anthu osawadziŵa. (Machitidwe 20:20) Koma nkhani zophunzira zonga zakuti “Odala Ali Opanda Mantha” (mu 1919) ndi “Khalani Olimba Mtima” (mu 1921) zinathandiza ena kuyamba ntchitoyo, ndi chidaliro mwa Yehova.
22 Pempholo, mu 1922, lakuti “lengezani, lengezani, lengezani, Mfumu ndi Ufumu wake” linapereka chisonkhezero chofunikira chosonyeza kufunika kwa ntchito imeneyi. Kuyambira mu 1927 kumka mtsogolo, akulu amene sanalandire thayo la Malemba limenelo anachotsedwa. Pafupifupi nthaŵi imeneyo, oimira oyendayenda a Sosaite, alaliki oyendayenda, anagaŵiridwa kukhala otsogoza utumiki achigawo, akumapereka malangizo achindunji kwa ofalitsa mu utumiki wakumunda. Si aliyense amene anakhoza kuchita upainiya, koma kumapeto a mlungu ambiri anali kuthera masiku athunthu mu utumiki, akumayamba mmamaŵa, ndi kupuma pang’ono chabe kuti adye sangweji yokha, ndiyeno kupitiriza utumikiwo mpaka madzulo kwambiri. Zimenezo zinali nthaŵi zofunika kwambiri za kupita patsogolo kwateokratiki, ndipo timapindula kwambiri mwa kupenda njira imene Yehova anali kutsogolerera anthu ake. Iye akupitirizabe kutero. Ndi dalitso lake, ntchito ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wokhazikitsidwa idzamalizidwa mwachipambano.
Kodi Inuyo Muli Wodikira?
23. Ponena za chikondi cha Chikristu ndi kulekana nalo dziko, kodi ndi motani mmene aliyense wa ife payekha angasonyezere kuti akukhala wodikira?
23 Kaamba kolabadira chilangizo cha Yehova, gulu lake likupitirizabe kutichenjeza ponena za machitachita ndi maganizo amene akatisonyeza kukhala mbali ya dziko, motero tikumaloŵa pangozi ya kupita nalo. (1 Yohane 2:17) Ifenso aliyense payekha, tifunikira kukhala odikira mwa kulabadira chitsogozo cha Yehova. Yehova akutipatsanso chilangizo ponena za kukhala ndi moyo ndi kugwira ntchito pamodzi. Gulu lake latithandiza kumvetsetsa zimene chikondi Chachikristu chimatanthauzadi. (1 Petro 4:7, 8) Kukhala kwathu odikira kumafuna kuti tiyeseyese mwakhama kugwiritsira ntchito uphungu umenewu, mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwaumunthu.
24, 25. Kodi ndi m’mbali zofunika ziti zimene tiyenera kukhala odikira, tili ndi chiyembekezo chotani?
24 Mosalekeza, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru watikumbutsa kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.” (Miyambo 3:5) “Pempherani kosaleka.” (1 Atesalonika 5:17) Talangizidwa kuphunzira kuzika zosankha zathu pa Mawu a Mulungu, kulola mawu ake kukhala ‘nyali ya kumapazi athu ndi kuunika pa njira yathu.’ (Salmo 119:105) Mwachikondi, talimbikitsidwa kuikabe patsogolo m’miyoyo yathu kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu, ntchito imene Yesu ananeneratu za m’tsiku lathu.—Mateyu 24:14.
25 Inde, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru alidi wodikira. Ifenso aliyense payekha, tifunikira kukhala odikira. Monga chotulukapo cha kuchita zimenezo, tiyeni tikapezeke pakati pa awo ovomerezedwa pamaso pa Mwana wa munthu pamene afika kudzapereka chiweruzo.—Mateyu 24:30; Luka 21:34-36.
[Mawu a M’munsi]
a Faith on the March, lolembedwa ndi A. H. Macmillan, Prentice-Hall, Inc., 1957, masamba 19-22.
b Onani The Watchtower, August 15, 1966, masamba 504-10.
Za Kupenda
◻ Monga momwe kwasonyezedwera pa Mateyu 24:42, kodi nchifukwa ninji tifunikira kukhala odikira?
◻ Kodi ndimotani mmene Yesu ndi otsatira ake a m’zaka za zana loyamba anakhalira odikira mwauzimu?
◻ Chiyambire mu 1870, kodi ndi zochitika zotani zimene zakhalapo chifukwa chakuti atumiki a Yehova apitirizabe kukhala odikira?
◻ Kodi nchiyani chimene chidzapereka umboni wakuti aliyense wa ife payekha akukhalabe wodikira?
[Zithunzi patsamba 23]
Yesu anakhala wotanganitsidwa m’ntchito yopatsidwa ndi Atate wake. Anapempheranso mwaphamphu
[Chithunzi patsamba 24]
Charles Taze Russell m’zaka zake zomalizira
[Chithunzi patsamba 25]
Alengezi a Ufumu ofika 4,700,000 ali okangalika padziko lonse lapansi