Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mafanizo Ofotokoza za Ufumu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
    • Munthu wapeza chuma chomwe chinabisidwa m’munda
      Wamalonda woyendayenda wapeza ngale yamtengo wapatali

      Kenako Yesu anauza ophunzira ake mafanizo ena atatu. Fanizo loyamba linali lakuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika m’munda, chimene munthu anachipeza n’kuchibisa. Chifukwa cha chimwemwe chimene anali nacho, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.”—Mateyu 13:44.

  • Mafanizo Ofotokoza za Ufumu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
    • Pogwiritsa ntchito mafanizo awiriwa, Yesu anasonyeza kuti munthu amalolera kukhala wopanda zinthu zina kuti apeze chinthu chofunika kwambiri. Mwachitsanzo, wamalonda uja analolera kugulitsa “zinthu zonse zimene anali nazo” n’cholinga choti akagule ngale imodzi imene inali ya mtengo wapatali kwambiri. Ophunzira a Yesu ayenera kuti anamvetsa bwino fanizo la ngale. Komanso wamalonda amene anapeza chuma chobisika m’munda, ‘anagulitsa zinthu zonse’ kuti agule mundawo. M’mafanizo awiri onsewa, anthuwo anapeza chinthu chamtengo wapatali chomwe atachipeza anafunika kuchiteteza. Nayenso munthu amene akufuna kupeza zosowa zake zauzimu, amalolera kusiya zinthu zina kuti apeze zinthu zauzimu zomwe ndi zamtengo wapatali. (Mateyu 5:3) Anthu ena amene ankamvetsera Yesu akufotokoza mafanizowa anali atasonyeza kale kuti anali okonzeka kuchita zambiri n’cholinga choti aphunzire zinthu zauzimu komanso kuti akhale otsatira okhulupirika a Yesu.—Mateyu 4:19, 20; 19:27.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena