Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Anthu Amene Akulalikira—Atumiki Anadzipereka Mofunitsitsa
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
    • Munthu wapeza chuma chobisika

      Akhristu amasangalala akapeza choonadi cha Ufumu ngati mmene anachitira munthu amene anapeza chuma chobisika uja (Onani ndime 20)

      20. Kodi fanizo la Yesu la chuma chobisika limasonyeza bwanji kuti otsatira ake adzamvera lamulo lakuti apitirize kufunafuna Ufumu choyamba?

      20 Yesu ankadziwa kuti otsatira ake adzamvera langizo lakuti apitirize kufunafuna Ufumu choyamba. Tiyeni tione zimene ananena m’fanizo la chuma chobisika. (Werengani Mateyu 13:44.) Pamene munthu wa m’fanizoli ankagwira ntchito m’munda, anapeza chuma chobisika ndipo nthawi yomweyo anazindikira kuti chinali chamtengo wapatali. Kodi anachita chiyani? Lembali limayankha kuti: “Chifukwa cha chimwemwe chimene anali nacho, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.” Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tikamvetsa mfundo zonena za Ufumu n’kuzindikira kuti n’zamtengo wapatali, tidzakhala okonzeka kusintha zinthu zina kuti tiyambe kuika zinthu za Ufumu pa malo oyamba m’moyo wathu.d

  • Anthu Amene Akulalikira—Atumiki Anadzipereka Mofunitsitsa
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
    • d Yesu ananena mfundo yofanana ndi imeneyi m’fanizo lake la wamalonda amene anapita kukafufuza ngale yamtengo wapatali. Wamalondayu atapeza ngaleyi anapita kukagulitsa zonse zimene anali nazo n’kukagula ngaleyo. (Mat. 13:45, 46) Mafanizo awiriwa akutiphunzitsa kuti tikhoza kuphunzira choonadi cha Ufumu m’njira zosiyanasiyana. Anthu ena amachita kufufuza choonadi pomwe ena amaphunzira mosachivutikira. Kaya tinaphunzira bwanji choonadi, koma tonse timasiya zinthu zina kuti tiike zinthu za Ufumu pamalo oyamba pa moyo wathu.

  • Anthu Amene Akulalikira—Atumiki Anadzipereka Mofunitsitsa
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulira
Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena