Funafunani Anthu a Mitima Yowongoka Kaamba ka Moyo Wosatha
“Anthu onse omwe anali ndi mitima yowongoka kaamba ka moyo wosatha anakhala akhulupiriri.”—MACHITIDWE 13:48, “NW.”
1. Ponena za mtima wa munthu, kodi Yehova ali ndi mphamvu yotani?
YEHOVA MULUNGU angadziŵe zimene ziri mumtima. Ichi chinamveketsedwa pamene mneneri Samueli ananka kukadzoza mwana wa Jese monga mfumu ya Israyeli. Pamene anawona Eliyabu, Samueli pomwepo ‘anati, Zowonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pake.’ Koma Yehova anati kwa Samueli: ‘Usayang’ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza ine ndinamkana iye; pakuti Yehova sawona monga awona munthu; pakuti munthu ayang’ana chowoneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.’ Mogwirizana ndi mfundozi, Samueli anatsogozedwa kudzoza Davide, amene anatsimikizira kukhala ‘wa pamtima pa Mulungu.’—1 Samueli 13:13, 14; 16:4-13.
2. Kodi nchiyani chomwe chimakhala choyala mizu mumtima wophiphiritsira wa munthu, ndipo chotero timaŵerenganji za ichi m’Malemba?
2 Munthu amawonetsa chizoloŵezi cha mkhalidwe wakutiwakuti. Amakhala ndi kaimidwe kamaganizo kakutikakuti komwe kamakhala koyala mizu mumtima wake wophiphiritsira. (Mateyu 12:34, 35; 15:18-20) Nchifukwa chake, timaŵerenga za munthu amene ‘mumtima mwake munali nkhondo.’ (Salmo 55:21) Tikuwuzidwanso kuti “mwamuna wamkwiyo aputa makangano.” Ndipo timaŵerenga kuti: ‘Woyanjana ndi ambiri angodziwononga; koma liripo bwenzi lipambana ndi mbale kuumirira.’ (Miyambo 18:24; 29:22) Mwachimwemwe, anthu ambiri amatsimikizira kukhala ngati Akunja ena m’Antiokeya wakale wa ku Pisidiya. Pamene anamva za makonzedwe a Yehova kaamba ka chipulumuko, “anayamba kukondwera nalemekeza mawu a Yehova, ndipo anthu onse amene anali ndi mitima yowongoka kaamba ka moyo wosatha anakhala akhulupiriri.”—Machitidwe 13:44-48, NW.
Akhulupiriri ‘Ngwoyera Mtima’
3, 4. (a) Kodi ndani omwe ali oyera mtima? (b) Kodi oyera mtimawo amamuwona Mulungu m’njira yotani?
3 Akhulupiriri amenewo mu Antiokeya anakhala Akristu obatizidwa, ndipo okhulupirika pakati pawo anakhoza kugwiritsira ntchito kwa iwo okha mawu awa a Yesu: “Achimwemwe ali oyera mtima, chifukwa adzawona Mulungu.” (Mateyu 5:8, NW) Koma kodi ndani omwe ali “oyera mtima”? Ndipo kodi ‘amamuwona bwanji Mulungu’?
4 Oyera mtima ngoyera mkati mwa thupi. Kwawo nkuyera kwa chiyamikiro, chikondi, zikhumbo, ndi zolinga. (1 Timoteo 1:5) Iwo amawona Mulungu tsopano lino m’lingaliro lakuti amamuwona iye akuchita mokomera osunga umphumphu. (Yerekezerani ndi Eksodo 33:20; Yobu 19:26; 42:5.) Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “kuwona” panopa limatanthauzanso “kuzindikira ndi maganizo, kuganizira, kudziŵa.” Popeza kuti Yesu anawunikira mwangwiro umunthu wa Mulungu, kukhala ndi chidziŵitso chaumunthu umenewo kumapezedwa ndi munthu “woyera mtima,” amene amasonyeza chikhulupiriro mwa Kristu ndi m’nsembe yake yotetezera uchimo, kupeza chikhululukiro cha machimo awo, ndipo ngokhoza kupereka kulambira kovomerezeka kwa Mulungu. (Yohane 14:7-9; Aefeso 1:7) Kwa odzozedwa, kuwona Mulungu kumafika pachimake ataukitsidwira kumwamba, komwe amamuwonadi Mulungu ndi Kristu. (2 Akorinto 1:21, 22; 1 Yohane 3:2) Koma kumuwona Mulungu kupyolera m’chidziŵitso cholongosoka ndi kulambira kowona nkothekera kwa onse omwe ali oyera mtima. (Salmo 24:3, 4; 1 Yohane 3:6; 3 Yohane 11) Iwo ngowongoka mtima kaamba ka moyo wosatha kumwamba kapena padziko lapansi la paradaiso.—Luka 23:43; 1 Akorinto 15:50-57; 1 Petro 1:3-5.
5. Kodi nkokha motani mmene munthu angakhalire wokhulupirira ndi kukhala mtsatiri wowona wa Yesu Kristu?
5 Anthu osawongoka mtima kaamba ka moyo wosatha sadzakhala akhulupiriri. Nkosatheka kwa iwo kusonyeza chikhulupiriro. (2 Atesalonika 3:2) Kuwonjezera apa, palibe munthu amene angakhale mtsatiri wowona wa Yesu Kristu kusiyapo ngati ali wophunzitsika ndi Yehova, amene amawona zimene ziri mumtima, namyandikitsa munthuyo. (Yohane 6:41-47) Ndithudi, polalikira kunyumba ndi nyumba, Mboni za Yehova sizimaweruziratu munthu aliyense. Iwo sangawone zomwe ziri mumtima mwake koma zomwe zidzatulukapo amazisiira kwa Mulungu.
6. (a) Kodi nchiyani chomwe chanenedwa ponena za kufikira kwa munthu mwini muuminisitala wa kunyumba ndi nyumba? (b) Kodi ndi makonzedwe otani omwe apangidwa kuthandiza Mboni za Yehova kupeza anthu owongoka mtima kaamba ka moyo wosatha?
6 Katswiri wina ananenapo molunjika motere: “[Paulo] anaphunzitsa chowonadi poyera ndi kunyumba ndi nyumba. Osati papulatifomu pokha, koma mofikira anthu amene anawalalikira za Kristu. Kaŵirikaŵiri kumfikira munthu mwaumwini kumakhala kophula kanthu kwambiri kuposa kachitidwe kapena njira ina iriyonse yofikira nayo anthu.” (August Van Ryn) Mabuku onga ngati Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki, Kukambitsirana za m’Malemba, ndi Utumiki Wathu Waufumu amathandiza Mboni za Yehova kupereka nkhani ndi kufikira anthu mwaumwini bwino kwambiri muutumiki wawo wakumunda. Zothandizanso, ndizitsanzo m’Misonkhano Yautumiki ndi uphungu wa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Awo opezeka pasukulu amalandira malangizo opindulitsa m’maluso a kulankhula onga ngati mawu oyamba abwino, kugwiritsira ntchito bwino Malemba, kukamba kotsatirika, chigomeko chokhutiritsa maganizo, kugwiritsira ntchito mafanizo, ndi mapeto ogwira mtima. Tiyeni tiwone mmene Baibulo limawonjezera malangizowa amene angapangitse anthu a Mulungu kukhala ogwira mtima kwambiri pamene akufunafuna anthu owongoka mtima kaamba ka moyo wosatha.
Mawu Oyamba Ogwira Mtima
7. Kodi mawu otsegulira a Ulaliki wa Yesu wa pa Phiri amaphunzitsanji ponena za mawu oyamba?
7 Kuchokera m’chitsanzo cha Yesu, anthu okonzekera kuchitira umboni wa kunyumba ndi nyumba angaphunzire kanthu kena ponena za mawu oyamba amene amadzutsa chikondwerero. Poyamba Ulaliki wake wa pa Phiri, iye anagwiritsira ntchito liwu lakuti “achimwemwe” nthaŵi zisanu n’zinayi. Mwachitsanzo, iye anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusowa kwawo kwauzimu, popeza kuti ufumu wakumwamba uli wawo. . . . Achimwemwe ali odekha mtima, popeza kuti adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:3-12, NW) Masentensiwo anali omveka ndi amyaa. Ndipo mawu oyambawo anadzutsadi chikondwerero ndipo anachititsa amvetseri ake kukhalamo ndi phande, pakuti kodi ndimunthu uti anthuni amene samafuna kukhala wachimwemwe?
8. Muuminisitala wakunyumba ndi nyumba, kodi ndimotani mmene nkhani yokambirana ingayambidwire?
8 Nkhani yokambirana yogwiritsiridwa ntchito muuminisitala wakunyumba ndi nyumba iyenera kuyambitsidwa m’njira yabwino, ndiyokondweretsa. Koma palibe munthu amene ayenera kugwiritsira ntchito mawu oyamba ozizwitsa, monga akuti, “Ndiri ndiuthenga kwa inu wochokera kunja kwa thambo.” Magwero a mbiri yabwino alidi kumwamba, komatu mawu oyamba oterowo angachititsenso mwininyumba kudabwa kaya Mboni ziyenera kulabadiridwa mosamalitsa kapena kuzifulatira mwamsanga.
Kulunjika Nawo Bwino Mawu a Mulungu
9. (a) Kodi malemba ayenera kutulutsidwa, kuŵerengedwa, ndi kugwiritsiridwa ntchito motani muuminisitala? (b) Kodi nchitsanzo chiti chimene chatchulidwa chosonyeza mmene Yesu anagwiritsira ntchito mafunso?
9 Muuminisitala wakumunda, mofanana ndi papulatifomu, malemba ayenera kutulutsidwa moyenerera, kuŵawerenga ndi chigogomezero chabwino, ndikugwiritsiridwa ntchito m’njira yomvekera, ndiyolongosoka. Mafunso omwe angapangitse mwininyumba kulingalira za mfundo za m’Malemba angakhalenso othandiza. Panonso, njira zogwiritsiridwa ndi Yesu ziri nawo malangizo. Pa chochitika china, munthu wophunzira kwambiri Chilamulo cha Mose anamfunsa kuti: ‘Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?’ Pomyankha Yesu anafunsa kuti: ‘M’chilamulo mulembedwa chiyani? Uwerenga bwanji?’ Mosakaikira, Yesu anadziŵa kuti iri ndilo funso limene munthuyo akadaliyankha. Iye anayankha molondola, naati: ‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwemwini.’ Ichi chinapangitsa Yesu kumuyamikira, ndipo kukambitsirana kowonjezereka kunatsatira.—Luka 10:25-37.
10. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukumbukiridwa ponena za nkhani yokambirana, ndipo kodi nchiyani chimene chiyenera kupeŵedwa pamene mukufunsa eninyumba mafunso?
10 Awo ochitira umboni kunyumba ndi nyumba ayenera kugogomezera mutu wa nkhani yokambirana nachimveketsa chifukwa choŵerengera malemba a Baibulo omwe amakulitsa nkhaniyo. Popeza kuti Mboni imayesera kufikira mtima wa mwininyumbayo, iyo iyenera kupeŵa kufunsa mafunso ochititsa manyazi. Pogwiritsira ntchito Mawu a Mulungu, ‘mawu athu nthaŵi zonse akhale m’chisomo, okoleretsedwa ndi mchere.’—Akolose 4:6.
11. Pogwiritsira ntchito Malemba kuwongolera malingaliro olakwika, kodi tiri ndi chitsanzo chotani ku chiyeso cha Yesu choperekedwa ndi Satana?
11 Makamaka pamaulendo obwereza mpomwe pangafunikire kuwongolera malingaliro olakwika mwa kusonyeza chimene Malemba kwenikweni amanena kapena kutanthauza. Yesu anachita chinthu chofanana ndi ichi podzudzula Satana, yemwe anati: ‘Ngati muli mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi [kuchokera pamalo osanja a kachisi, monga kudzipha kwenikweni]; pakuti kwalembedwa, kuti, Adzauza angelo ake za iwe, ndipo pa manja awo adzakunyamula iwe, ungagunde konse phazi lako pamwala.’ Salmo 91:11, 12, lomwe linagwidwa mawu ndi Satana, silimapereka chodzilungamitsira kwa munthu woikira dala moyo wake pachiswe, womwe uli mphatso yochokera kwa Mulungu. Pozindikira kuti kunali kolakwa kuyesa Yehova mwakuikira dala moyo wake pachiswe, Yesu anamuuza Satana kuti: ‘Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Yehova Mulungu wako.’ (Mateyu 4:5-7) Ndithudi, Satana samafunafuna chowonadi. Koma pamene anthu abwino atulutsa malingaliro olakwika amene angadodometse kupita kwawo patsogolo kwauzimu, minisitala wa Mawu a Mulungu ayenera kusonyeza mwaluso chimene Malemba amanenadi ndikutanthauza. Yonseyi ndimbali ya ‘kulunjika nawo bwino mawu a chowonadi’—limodzi la maphunziro ofunika ophunzitsidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki.—2 Timoteo 2:15.
Kukopa Kuli ndi Malo Ake
12, 13. Kodi nchifukwa ninji kuli kolunjika kugwiritsira ntchito kukopa muuminisitala?
12 Kukopa kuli ndi malo abwino muuminisitala Wachikristu. Mwachitsanzo, Paulo anasonkhezera wantchito mnzake Timoteo kukhalabe m’zinthu zimene anaziphunzira ndipo “anakopedwa kuzikhulupirira.” (2 Timoteo 3:14, NW) Mu Korinto, Paulo “anafotokozera m’sunagoge masabata onse, nakopa Ayuda ndi Ahelene.” (Machitidwe 18:1-4) Mu Efeso, iye ‘anatsutsana ndi kukopa kunena za ufumu wa Mulungu’ mwachipambano. (Machitidwe 19:8) Ndipo pamene anabindikiritsidwa m’Roma, mtumwiyo anaitanira anthu kwa iye napereka umboni, “ndi kuwakopa,” ndipo ena anakhala akhulupiriri.—Machitidwe 28:23, 24.
13 Ndithu, mosasamala kanthu za mmene Mboni ingakhalire yokopa, ndianthu owongoka mtima kaamba ka moyo wosatha okha amene adzakhala akhulupiriri. Zigomeko zokhutiritsa maganizo ndi kulongosola komvekera, kofotokozedwa mwaluso, kungaŵakope kukhulupirira. Koma kodi nchiyani chinanso chimene chingakhalenso chothandiza poŵakopa?
Khalani Otsatirika ndi Ogomeka
14. (a) Kodi kukamba kotsatirika, kogwirizana kumaphatikizanji? (b) Kodi chigomeko chokhutiritsa maganizo chimafunanji?
14 Limodzi la maluso a kulankhula ogogomezeredwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndilo kukamba kotsatirika, kogwirizana. Uku kumaphatikizapo kuika mfundo zazikulu zonse ndi nsonga zogwirizana nazo m’dongosolo labwino. Chofunikanso nchigomeko chokhutiritsa maganizo, chomwe chimafuna kuti muyale maziko abwino ndikupereka umboni womvekera. Chogwirizana ndi ichi ndicho kuthandiza omvetsera kulingalira mwa kuyala maziko ovomerezana, kutulutsa mfundo mokhutiritsa, ndikuzigwiritsira ntchito mogwira mtima. Panonso, Malemba amapereka zitsogozo.
15. (a) Kodi ndimotani mmene Paulo anasangalatsira omvetsera ndikuyala maziko okambirana pamene analankhula pa Phiri la Mars? (b) M’kulankhula kwa Paulo, kodi ndiumboni wotani umene tiri nawo wa kukamba kotsatirika, kogwirizana?
15 Maluso a kulankhula amenewa akumveka m’kukamba kotchuka kwa mtumwi Paulo pa Phiri la Mars mu Atene wakale. (Machitidwe 17:22-31) Mawu ake oyamba anakopa omvetsera ndipo anayala maziko ovomerezana, pakuti iye anati: “Amuna inu a Atene, m’zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.” Kwa iwo, mosakaikira uku kunamveka ngati kunali kuyamikiridwa. Potchula guwa lansembe loperekedwa ‘Kwa Mulungu Wosadziwika,’ Paulo anapitiriza ndi kukamba kwake kotsatirika, kogwirizana ndi chigomeko chokhutiritsa maganizo. Iye anasonya kuti Mulungu ameneyu amene iwo sanamdziŵa “analenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo.” Mosiyana ndi Athena kapena milungu ina Yachigiriki, ‘iye sakhala m’nyumba zakachisi zomangidwa ndi manja, satumikidwa ndi manja a anthu.’ Chotsatira mtumwiyo anasonyeza kuti Mulungu ameneyu ndiye anatipatsa moyo ndipo samatichititsa kumufunafuna mwakhungu. Pamenepo Paulo analingalira nawo kuti Mlengi wathu, amene analekerera nthaŵi za kusadziwa za kulambira mafano, ‘akulamulira anthu onse konsekonse atembenuke mtima.’ Kukamba kotsatirikaku kunatsogolera ku mfundo yakuti ‘Mulungu adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; amene anamuukitsa kwa akufa.’ Popeza kuti Paulo “analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa,” anthu a ku Atene amenewo anadziŵa kuti Woweruza ameneyu akakhala Yesu Kristu.—Machitidwe 17:18.
16. Kodi uminisitala wa munthuwe uyenera kuyambukiridwa motani ndi kulankhula kwa Paulo pa Phiri la Mars ndi kulangiza m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki?
16 Zowonadi, Paulo sankachitira umboni kunyumba ndi nyumba pa Phiri la Mars. Koma m’nkhani yake ndi malangizo operekedwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki, Mboni za Yehova zingaphunzire zinthu zambiri zimene zingazamitse maluso auminisitala wawo wakumunda. Inde, zonsezi zimathandiza kuŵachititsa kukhala aminisitala ogwira mtima kwenikweni, mongadi mmene kukamba kotsatirika ndi zigomeko zokhutiritsa maganizo za Paulo zinakopera anthu ena a ku Atene kukhala akhulupiriri.—Machitidwe 17:32-34.
Gwiritsirani Ntchito Mafanizo Ophunzitsa
17. Kodi ndi mafanizo amtundu wanji amene ayenera kugwiritsiridwa ntchito muuminisitala?
17 Sukulu Yautumiki Wateokratiki imathandizanso aminisitala a Mulungu kugwiritsira ntchito mafanizo abwino pochitira umboni kunyumba ndi nyumba ndi m’mbali zina zauminisitala wawo. Kuti mugogomezere mfundo zofunika, mafanizo opepuka omwe ngabwino ayenera kugwiritsiridwa ntchito. Mboni iyenera kuwatenga m’zinthu zozoloŵereka ndipo iyenera kukhala yosamala kupangitsa kugwiritsira ntchito kwake kukhala komvekera. Mafanizo a Yesu anafikiritsa zofunikira zonsezi.
18. Kodi ndimotani mmene Mateyu 13:45, 46 angatsimikizire kukhala wopindulitsa muuminisitala?
18 Mwachitsanzo, talingalirani mawu awa a Yesu: ‘Ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino: ndipo m’mene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.’ (Mateyu 13:45, 46) Ngale ndimiyala yamtengo wapatali yopezeka mkati mwazikamba za oyster ndi mtundu wina wankhono. Koma ndingale zakutizakuti zokha zimene ziri “zabwino.” Wamalondayo anali ndi kuzindikira kwabwino kofunikira kudziŵa phindu lakuya la ngale imodzi imeneyi ndipo anali wofunitsitsa kuwononga chinthu chirichonse kuti aipeze. Mwinamwake paulendo wobwereza kapena paphunziro la Baibulo lapanyumba, fanizoli lingagwiritsiridwe ntchito kusonyeza kuti munthu amene amayamikiradi Ufumu wa Mulungu adzachita mofanana ndi wamalonda uja. Munthu woteroyo adzaika Ufumu kukhala chinthu choyamba m’moyo wake, pozindikira kuti ngwoposa chinthu chirichonse chomwe angadzimane.
Malizani ndi Chisonkhezero
19. Muuminisitala wakunyumba ndi nyumba, kodi mapeto ayenera kumusonyezanji mwininyumba?
19 Mu Sukulu Yautumiki Wateokratiki, anthu a Mulungu amaphunziranso kuti mapeto ankhani kapena kukambitsirana ayenera kugwirizana mwathithithi ndi mutu wankhani ndipo ayenera kusonyeza omvetsera zomwe ayenera kuchita ndikuwalimbikitsa kuzichita. Muuminisitala wakunyumba ndi nyumba, mwininyumba ayenera kusonyezedwadi njira imene akuyembekezeredwa kuitenga, monga ngati kulandira bukhu la Baibulo kapena kuvomereza ulendo wobwereza.
20. Kodi nchitsanzo chabwino chotani cha mapeto osonkhezera chimene tikupeza pa Mateyu 7:24-27?
20 Mapeto a Ulaliki wa Yesu wa pa Phiri amapereka chitsanzo chabwino. Kupyolera m’fanizo losavuta kumva, Yesu anasonyeza kuti ikakhala njira yanzeru kulabadira mawu ake. Iye anamaliza motere: ‘Chifukwa chimenechi yense amene akamva mawu anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda panyumbayo; koma siinagwa; chifukwa inakhazikika pathanthwepo. Ndipo yense akamva mawu anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda panyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.’ (Mateyu 7:24-27) Ichi chikusonyeza bwino chotani nanga kuti aminisitala a Mulungu ayenera kuyesayesa kusonkhezera eninyumba!
21. Kodi kukambitsirana kwathu kwafotokoza chiyani mwafanizo, koma kodi nchiyani chimene chiyenera kuzindikiridwa?
21 Mfundo zomwe zatchulidwazo zikufotokoza mwafanizo mmene Sukulu Yautumiki Wateokratiki ingathandizire anthu ambiri kukhala alengezi oyeneretsedwa a Ufumu. Ndithudi, kukhala woyeneretsedwa mokwanira choyamba kumachokera kwa Mulungu. (2 Akorinto 3:4-6) Ndipo mosasamala kanthu zakuti minisitalayo ngwoyeneretsedwa motani, palibe munthu amene angakope anthu kukhala akhulupiriri kusiyapo atakokeredwa chifupi ndi Mulungu kupyolera mwa Kristu. (Yohane 14:6) Komabe, anthu a Mulungu ayeneradi kugwira mwaŵi wa makonzedwe onse auzimu opangidwa ndi Yehova pamene akufunafuna owongoka mtima kaamba ka moyo wosatha.
Kodi Mayankho Anu Ngotani?
◻ Kodi ndani omwe ali “oyera mtima,” ndipo kodi ‘amawona Mulungu’ motani?
◻ Kodi ndi mfundo ziti zimene ziyenera kulingaliridwa poyambitsa uthenga Waufumu m’ntchito ya kunyumba ndi nyumba?
◻ Kodi ndimotani mmene Mawu a Mulungu ayenera kulunjikitsidwa bwino muuminisitala?
◻ Kodi chidzathandiza nchiyani kupanga mafikiridwe a kukamba kotsatirika, kogomeka maganizo muutumiki wakumunda?
◻ Kodi nchiyani chimene chiyenera kukumbukiridwa ponena za mafanizo ogwiritsiridwa ntchito muuminisitala?
◻ Kodi nchiyani chimene chiyenera kukwaniritsidwa m’mapeto ogwiritsiridwa ntchito m’ntchito yochitira umboni?
[Chithunzi patsamba 16]
Yesu anati “oyera mtima” akatha ‘kuwona Mulungu.’ Kodi ichi chinatanthauzanji?
[Chithunzi patsamba 18]
Malemba ayenera kutulutsidwa moyenerera, kuwaŵerengedwa ndi chigogomezero chabwino, ndi kugwiritsiridwa ntchito mumkhalidwe womvekera, wolongosoka