-
‘Kupeza Ngale Imodzi ya Mtengo Wapatali’Nsanja ya Olonda—2005 | February 1
-
-
‘Kupeza Ngale Imodzi ya Mtengo Wapatali’
“Anthu akulimbikira kupeza mwayi wokalowa ufumu wa kumwamba, ndipo amene akulimbikira mwachamuna akuupeza.”—MATEYU 11:12, NW.
1, 2. (a) Kodi ndi mtima wosowa wotani umene Yesu anafotokoza m’limodzi la mafanizo ake a Ufumu? (b) Kodi Yesu anati chiyani m’fanizo la ngale ya mtengo wapatali?
KODI pali chinthu chimene mumachiona kuti ndi cha mtengo wapatali kwambiri, moti mungatayirepo zonse zimene muli nazo kuti chinthucho chikhale chanu? Anthu ena amanena kuti ndi odzipereka pa cholinga chawo, monga kupeza ndalama zambiri, kutchuka, kukhala ndi mphamvu zolamulira ena, kapena udindo wapamwamba. Ngakhale zili choncho, si kawirikawiri munthu kupeza chinthu chimene angalolere kutayirapo zonse zimene ali nazo. M’limodzi la mafanizo ake ogwira mtima a Ufumu wa Mulungu, Yesu Kristu ananenapo za munthu wa mtima wosowa ndi wosiririka woterewu.
2 Fanizo limeneli ndi limene Yesu anafotokozera ophunzira ake pamene anali paokha. Kawirikawiri limatchedwa kuti fanizo la ngale ya mtengo wapatali. Yesu anati: “Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wamalonda, wakufuna ngale zabwino: ndipo mmene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.” (Mateyu 13:36, 45, 46) Kodi Yesu anali kufuna kuti ophunzirawo aphunzirepo chiyani pa fanizolo? Ndipo ifeyo tingapindule motani ndi mawu a Yesu?
Mtengo Wapatali wa Ngale
3. N’chifukwa chiyani ngale zabwino zinali za mtengo wapatali kwambiri m’nthawi zakale?
3 Kuyambira nthawi zamakedzana, anthu akhala akuvala timiyala ta ngale monga zodzikongoletsera. Buku lina limanena kuti malinga ndi wolemba nkhani wa ku Roma, Pliny Wamkulu, ‘pa zinthu zonse za mtengo wapatali, panalibe choposa ngale.’ Mosiyana ndi golide, siliva, kapena miyala yambiri ya mtengo wapatali, ngale zimapangidwa ndi zinthu za moyo. Ambiri amadziwa kuti mitundu ina ya nkhono za m’nyanja ndi imene imapanga ngale. Chimene chimachitika n’chakuti, tinthu tina monga timiyala tikalowa m’chikamba chake, imatulutsa zinthu zamadzimadzi zimene zimakuta kamwalako. Ndiyeno kamwalako kamakhala ngale yosalala ndi yonyezimira. Kale, ngale zabwino kwambiri anali kuzipeza makamaka m’Nyanja Yofiira, m’nyanja ya Persian Gulf, ndi m’nyanja ya mchere ya Indian Ocean, kutali kwambiri ndi ku Israyeli. Mosakayikira, ndiye chifukwa chake Yesu ananena za “wamalonda [woyendayenda, NW], wakufuna ngale zabwino.” Kuti munthu apeze ngale za mtengo wapatalidi, ayenera kuyesetsa kwambiri.
4. Kodi phunziro lalikulu m’fanizo la Yesu la wamalonda n’chiyani?
4 Ngakhale kuti ngale zabwino zakhala zodula kuyambira kale, n’zoonekeratu kuti phunziro lalikulu m’fanizo la Yesu si kudula kwakeko ayi. M’fanizo limeneli, Yesu sanangoyerekezera Ufumu wa Mulungu ndi ngale ya mtengo wapatali. Mfundo yake yaikulu inali pa “munthu wamalonda, wakufuna ngale zabwino” ndiponso zimene munthuyo anachita atapeza ngaleyo. Mosiyana ndi mwinisitolo wamba, wamalonda a ngale anali kukhala katswiri wozindikira pa malondawo. Amati akaiyang’ana ngale ija, amatha kuona zina ndi zina zobisika zimene zikuchititsa ngaleyo kukhaladi yapadera. Ngale yeniyeni anali kuidziwa akangoiona, osapusitsika ndi ngale wamba kapena yachinyengo.
5, 6. (a) Kodi n’chiyani chochititsa chidwi kwambiri ndi wamalonda wa m’fanizo la Yesu? (b) Kodi fanizo la chuma chobisika likusonyeza chiyani chokhudza wamalonda a ngale?
5 Pali chinanso chochititsa chidwi ndi wamalonda ameneyu. Wamalonda wamba, mwina akanayamba waona kaye mtengo umene angakagulitsire ngaleyo, n’cholinga choti adziwe kuti angaigule ndalama zingati, kuti akakaigulitsa akapezepo phindu. Akanayambanso waona ngati pali anthu amene amafuna ngale yoteroyo, kuti isakamutengere nthawi kuigulitsa. M’mawu ena, chidwi chake chikanakhala pa kupezapo phindu mofulumira, osati kukhala ndi ngaleyo. Koma wamalonda wa m’fanizo la Yesu sanali wotero. Chidwi chake sichinali pa ndalama, kapena kupeza katundu wina wake monga phindu. M’malo mwake, analolera kugulitsa “zonse anali nazo,” mwina katundu wake yense, kuti agule chimene wakhala akuchifunafuna.
6 Kwa amalonda ambiri, zimene munthu ameneyu wa m’fanizo la Yesu anachita ndiko kufa mutu. Wamalonda wosamala sangaike dala ndalama zake pangozi mwa njira imeneyi. Koma wamalonda wa m’fanizo la Yesu anali wosiyana pa zinthu zimene amaziona kukhala zofunika. Iye sanali kufuna kusangalala ndi phindu la ndalama, koma kupeza chimwemwe ndiponso kukhala wokhutira pokhala ndi chinthu china cha mtengo wapatali koposa. Yesu anamveketsa mfundo imeneyi m’fanizo linanso lofanana ndi loyambali. Iye anati: “Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m’munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m’kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.” (Mateyu 13:44) Inde, chimwemwe chodza ndi kupeza chuma, kapena kuti chinthu cha mtengo wapatali n’kukhala nacho, chinali chokwanira kuchititsa munthuyo kugulitsa zonse zimene anali nazo. Kodi alipo anthu otero lerolino? Kodi pali chinthu cha mtengo wapatali chimene munthu angafune kutayirapo zonse zimene ali nazo?
Amene Anazindikira Mtengo Wake Wapatali
7. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali kumvetsadi mtengo wapatali wa Ufumu?
7 Mmene amafotokoza fanizo lake, Yesu anali kulankhula za “Ufumu wa Kumwamba.” Iyeyo anali kumvetsadi mtengo wapatali wa Ufumuwo. Nkhani zolembedwa m’Mauthenga Abwino zili ndi umboni wamphamvu wa mfundo imeneyi. Atabatizidwa m’chaka cha 29 C.E., Yesu “anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” Kwa zaka zitatu ndi theka, iye anaphunzitsa makamu a anthu za Ufumuwo. Anayendayenda m’dziko lonselo, “kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu.”—Mateyu 4:17; Luka 8:1.
8. Kodi Yesu anachitanji posonyeza zimene Ufumu udzachita?
8 Yesu anasonyezanso zimene Ufumu wa Mulungu udzachita mwa kuchita zozizwitsa zambiri m’dziko lonselo. Iye anachiritsa odwala, kupatsa anthu a njala chakudya, kuletsa namondwe, ngakhalenso kuukitsa akufa. (Mateyu 14:14-21; Marko 4:37-39; Luka 7:11-17) Pamapeto pake, anaonetsa umboni wakuti ndi wokhulupirika kwa Mulungu ndi Ufumu mwa kupereka moyo wake, kufera chikhulupiriro chake pa mtengo wozunzikirapo. Monga wamalonda uja anachitira, kupereka ndi mtima wonse zonse zimene anali nazo kuti agule “ngale imodzi ya mtengo wapatali,” Yesu anakhalira moyo Ufumu, ndipo anaferanso Ufumu.—Yohane 18:37.
9. Kodi ndi mtima wosowa wotani umene ophunzira oyambirira a Yesu anaonetsa?
9 Yesu sanaike moyo wake wokha pa Ufumu, koma anasonkhanitsanso kagulu ka otsatira ake. Amenewanso anali anthu omwe anamvetsadi mtengo wapatali wa Ufumu. Mmodzi wa amenewa anali Andreya, amene poyamba anali wophunzira wa Yohane Mbatizi. Atamva Yohane Mbatizi akuchitira umboni kuti Yesu ndiye “Mwanawankhosa wa Mulungu,” Andreya limodzi ndi wophunzira winanso wa Yohane Mbatizi, mwina mwake Yohane, nthawi yomweyo anayamba kutsatira Yesu nakhala okhulupirira. Yohane ameneyu anali mmodzi mwa ana a Zebedayo. Koma sizinathere pompo. Nthawi yomweyo, Andreya anapita kwa mbale wake Simoni ndi kumuuza kuti: “Tapeza ife Mesiya.” Posapita nthawi, Simoni (yemwe kenako anadziwika ndi dzina lakuti Kefa, kapena Petro) limodzi ndi Filipo ndi bwenzi lake Natanayeli anavomerezanso kuti Yesu ndiye Mesiya. Ndipotu Natanayeli anafika pouza Yesu kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israyeli.”—Yohane 1:35-49.
Analimbikitsidwa Kuchitapo Kanthu
10. Patapita nthawi kuchokera pamene anakumana koyamba, kodi ophunzira anatani Yesu atawapezanso n’kuwaitana?
10 Chimwemwe chimene Andreya, Petro, Yohane, ndi ena anali nacho atapeza Mesiya, n’chofanana ndi chimwemwe cha wamalonda uja atapeza ngale ya mtengo wapatali. Kodi iwo anatani kenako? Mauthenga Abwino sanena kuti anatani pambuyo pokumana ndi Yesu nthawi yoyamba imeneyi. Koma zikuonetsa kuti ambiri a iwo anabwerera ku ntchito zawo za masiku onse. Ndiyeno pambuyo pa miyezi isanu ndi umodzi, kapena pafupifupi chaka, Yesu anapezanso Andreya, Petro, Yohane, ndi Yakobo mbale wa Yohane ali pantchito yawo ya usodzi ku Nyanja ya Galileya.a Atawaona, Yesu anawauza kuti: “Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” Kodi iwo anatani? Nkhani yolembedwa ndi Mateyu imanena zimene Petro ndi Andreya anachita kuti: “Iwo anasiya pomwepo makokawo, nam’tsata iye.” Kunena za Yakobo ndi Yohane, timawerenga kuti: “Anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wawo, nam’tsata Iye.” Nkhani yolembedwa ndi Luka imawonjezapo mawu akuti iwo “anasiya zonse, nam’tsata Iye.”—Mateyu 4:18-22; Luka 5:1-11.
11. Kodi chifukwa chake chingakhale chiyani chimene ophunzira anavomerera kuitana kwa Yesu mosazengereza?
11 Kodi ophunzira anachita zinthu mopupuluma pamene anavomera kuitana kwa Yesu? Kutalitali! Ngakhale kuti atakumana ndi Yesu kwa nthawi yoyamba iwo anabwerera ku ntchito yawo ya usodzi, n’zosakayikitsa kuti zimene anaona ndi kumva patsikulo zinawakhudza mtima kwambiri. Nthawi yokwanira pafupifupi chaka imene inadutsa, iyenera kuti inawapatsa mpata wonse wosinkhasinkha pa zimene anaona ndi kumva. Tsopano inali nthawi yoti asankhe chochita. Kodi iwo akanakhala ngati wamalonda uja amene mtima wake unasangalala kwambiri atapeza ngale ya mtengo wapatali, moti malinga ndi kunena kwa Yesu, “anapita [‘ndipo mwamsanga,’ NW]” anachita zonse zotheka kuti agule ngaleyo? Inde. Zimene anaona ndi kumva zinawakhudza mtima. Anaona kuti nthawi yafika yoti achitepo kanthu. Ndiye chifukwa chake, monga nkhaniyo ikunenera, mosazengereza anasiya zonse n’kukhala otsatira a Yesu.
12, 13. (a) Kodi ambiri amene anamva Yesu akulankhula anatani? (b) Kodi Yesu anati chiyani za ophunzira ake okhulupirika, ndipo mawu akewo amatanthauzanji?
12 Anthu okhulupirika amenewa anali osiyana kwambiri ndi ena amene anatchulidwa pambuyo pake m’nkhani za m’Mauthenga Abwino. Panali ambiri amene Yesu anawachiritsa kapena kuwapatsa chakudya koma amene anangopitiriza zochita zawo za masiku onse. (Luka 17:17, 18; Yohane 6:26) Ena anachita kukana ndithu, Yesu atawaitana kuti akhale otsatira ake. (Luka 9:59-62) Mosiyana kwambiri ndi amenewa, Yesu anadzanena za okhulupirika kuti: “Koma kuyambira m’masiku a Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu akulimbikira kupeza mwayi wokalowa ufumu wa kumwamba, ndipo amene akulimbikira mwachamuna akuupeza.”—Mateyu 11:12, NW.
13 ‘Kulimbikira.’ Kodi mawu amenewa akutanthauzanji? Pofotokoza mawu achigiriki amene m’Baibulo la Chichewa anawatembenuza kuti ‘kulimbikira,’ buku la Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words limati: “Mawuwa amatanthauza kuyesetsa mwamphamvu.” Ndiponso, pothirira ndemanga vesili, katswiri wa Baibulo Heinrich Meyer anati: “Mawuwa akufotokoza kuyesetsa mwamphamvu pofuna kupeza ufumu wa Mesiya umene ukubwera . . . Munthuyo ali ndi chidwi chachikulu kwambiri ndiponso champhamvu zedi, moti sakungokhalanso phee n’kumauyembekeza.” Mofanana ndi wamalonda a ngale uja, anthu ochepa amenewa anazindikira mofulumira chinthu cha mtengo wapatali, ndipo ndi mtima wonse anasiya zonse zimene anali nazo kuti achite ntchito ya Ufumu.—Mateyu 19:27, 28; Afilipi 3:8.
Enanso Anayamba Kufunafuna Ufumuwo
14. Kodi Yesu anawakonzekeretsa motani atumwi kuchita ntchito yolalikira za Ufumu, ndipo panali zotsatira zotani?
14 Popitiriza utumiki wake, Yesu anaphunzitsa ndi kuthandiza anthu ena kuti akalamire Ufumu. Anayamba ndi kusankha anthu 12 mwa ophunzira ake n’kuwatcha atumwi, kapena kuti otumizidwa ndi iye. Amenewa, Yesu anawapatsa malangizo atsatanetsatane onena mmene adzachitire utumiki wawo komanso machenjezo a zopinga ndi zovuta zimene adzakumane nazo. (Mateyu 10:1-42; Luka 6:12-16) Pazaka ngati ziwiri zotsatira, iwo anatsagana ndi Yesu pa maulendo ake olalikira m’dziko lonselo, ndipo anali paubwenzi wolimba ndi iye. Iwo anamva zonena zake, anaona ntchito zake zamphamvu ndi chitsanzo chake. (Mateyu 13:16, 17) Mosakayikira, zonsezi zinawakhudza mtima kwambiri, moti mofanana ndi wamalonda uja, iwo anali achangu pantchito ya Ufumu, ndipo anachita ntchitoyo ndi mtima wonse.
15. Kodi Yesu anati chifukwa chenicheni cha kusangalala kwa otsatira ake chinali chiyani?
15 Kuwonjezera pa atumwi 12, Yesu “anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo alionse kumene ati afikeko mwini.” Amenewanso anawauza za ziyeso ndi zovuta zimene adzakumane nazo. Anawalangizanso kuuza anthu kuti: “Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu.” (Luka 10:1-12) Anthu 70 amenewa anabwerako akusangalala kwambiri, nauza Yesu kuti: “Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m’dzina lanu.” Koma Yesu anawauza kuti m’tsogolo, iwo adzasangalala kuposa pamenepo chifukwa cha changu chawo pantchito ya Ufumu. Ayenera kuti anadabwa kumva zimenezo. Powauza, Yesu anati: “Musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti mayina anu alembedwa m’Mwamba.”—Luka 10:17, 20.
16, 17. (a) Kodi Yesu anawauzanji atumwi ake okhulupirika pamene anali nawo usiku womaliza? (b) Kodi mawu a Yesu anapatsa atumwi chimwemwe ndi chitsimikizo chotani?
16 Pomalizira, pa Nisani 14, 33 C.E., usiku womaliza ndi atumwi, Yesu anayambitsa mwambo umene pambuyo pake unatchedwa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Analamula atumwiwo kuti azichita mwambo umenewo. Usiku umenewo, Yesu anauza atumwi 11 otsalawo kuti: “Inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga; ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.”—Luka 22:19, 20, 28-30.
17 Atumwi atamva mawu amenewa kwa Yesu, ayenera kuti anadzazidwa ndi chimwemwe chachikulu m’mitima yawo. Iwo anali kupatsidwa chiyembekezo chodzakhala ndi ulemerero ndiponso mwayi wapamwamba kuposa wina uliwonse umene munthu angakhale nawo. (Mateyu 7:13, 14; 1 Petro 2:9) Mofanana ndi wamalonda uja, iwo anali atasiya zambiri kuti atsatire Yesu pantchito ya Ufumu. Tsopano anawatsimikizira kuti kudzipereka kwawo kumene anali atachita sikunapite pachabe.
18. Kupatulapo atumwi 11, enanso ndani amene anali kudzapindula ndi Ufumu?
18 Amene anali kudzapindula ndi Ufumuwo si atumwi okhawo amene anali ndi Yesu usiku umenewo. Chifuniro cha Yehova chinali kulowetsa anthu okwanira 144,000 m’pangano la Ufumu, kuti akakhale olamulira anzake a Yesu Kristu mu Ufumu wa ulemerero wa kumwamba. Kuwonjezera apo, mtumwi Yohane anaona m’masomphenya “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, . . . akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, . . . nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” Amenewa ndi nzika za Ufumu za pa dziko lapansi.b—Chivumbulutso 7:9, 10; 14:1, 4.
19, 20. (a) Kodi anthu a mitundu yonse ali ndi mwayi wotani? (b) Tiyankha funso loti bwanji m’nkhani yotsatira?
19 Yesu atatsala pang’ono kukwera kumwamba, analamula otsatira ake okhulupirika kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 28:19, 20) Chotero, anthu a mitundu yonse anali kudzakhala ophunzira a Yesu Kristu. Amenewanso anali oti adzaika mtima wawo pa Ufumu, monga anachitira wamalonda uja atapeza ngale yabwino. Cholinga chawo ndicho kulandira mphoto ya kumwamba kapena ya pa dziko lapansi.
20 Mawu a Yesu anasonyeza kuti ntchito yopanga ophunzira idzapitirizabe mpaka “chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.” Chotero, kodi m’masiku athu ano, alipobe anthu ofanana ndi wamalonda a ngale uja, omwe ndi okonzeka kupereka zonse ali nazo kuti apeze Ufumu wa Mulungu? Funso limeneli tiliyankha m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Yohane, mwana wa Zebedayo, ayenera kuti analondola Yesu atakumana koyamba, ndipo anaona zina zimene Yesu anachita. Mwina ndi zimene zinachititsa Yohane kulemba zinthuzo mogwira mtima kwambiri mu Uthenga wake Wabwino. (Yohane, machaputala 2-5) Koma anadzabwererabe ku ntchito yake ya usodzi kwa nthawi ndithu Yesu asanamuitanenso.
b Kuti mudziwe zambiri pa mfundoyi, onani mutu 10 m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
-
-
Kufunafuna ‘Ngale ya Mtengo Wapatali’ LerolinoNsanja ya Olonda—2005 | February 1
-
-
Kufunafuna ‘Ngale ya Mtengo Wapatali’ Lerolino
“Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu.”—MATEYU 24:14.
1, 2. (a) Kodi Ayuda m’nthawi ya Yesu anali kuuona bwanji Ufumu wa Mulungu? (b) Kodi Yesu anatani kuti athandize anthu kumvetsa za Ufumuwo, ndipo panali zotsatira zotani?
PANTHAWI imene Yesu anabwera pa dziko lapansi, Ufumu wa Mulungu unali nkhani yaikulu kwambiri pakati pa Ayuda. (Mateyu 3:1, 2; 4:23-25; Yohane 1:49) Koma poyamba, ambiri mwa iwo sanali kuzindikira bwino lomwe ukulu ndi mphamvu ya Ufumuwo. Sanalinso kudziwa kuti udzakhala boma la kumwamba. (Yohane 3:1-5) Ngakhale ena amene anakhala otsatira a Yesu sanali kudziwa bwinobwino kuti Ufumu wa Mulungu n’chiyani, kapena zimene ayenera kuchita kuti alandire dalitso lokhala olamulira anzake a Kristu.—Mateyu 20:20-22; Luka 19:11; Machitidwe 1:6.
2 M’kupita kwa nthawi, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake zinthu zambiri moleza mtima, kuphatikizapo fanizo la ngale ya mtengo wapatali, limene takambirana m’nkhani yoyamba. Fanizolo linali lowasonyeza kufunika koyesetsa mwamphamvu pofunafuna Ufumu wa kumwambawo. (Mateyu 6:33; 13:45, 46; Luka 13:23, 24) Mfundo imeneyi iyenera kuti inawakhudza mtima kwambiri, chifukwa mosataya nthawi anayamba kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu mosatopa ndiponso molimba mtima kumalekezero a dziko lapansi. Buku la Machitidwe lili ndi umboni wokwanira wa mfundo imeneyi.—Machitidwe 1:8; Akolose 1:23.
3. Kunena za m’nthawi yathu ino, kodi Yesu anati chiyani za Ufumu?
3 Ndiyeno bwanji za lerolino? Anthu mamiliyoni ambiri akuuzidwa za madalitso a paradaiso wa pa dziko lapansi lolamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu. Mu ulosi wake waukuluwo wonena za “mathedwe a nthawi ya pansi pano,” Yesu ananena mosapita m’mbali kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:3, 14; Marko 13:10) Anafotokozanso kuti ntchito yaikulu imeneyi iyenerabe kuchitidwa ngakhale padzakhale zopinga ndi zovuta zazikulu, kuphatikizapo chizunzo chimene. Koma anatitsimikizira kuti: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:9-13) Zonsezi n’zofuna kudzimana ndi kudzipereka kumene wamalonda wa m’fanizo la Yesu anaonetsa. Kodi lerolino alipo anthu amene amasonyeza chikhulupiriro ndi changu choterocho pofunafuna Ufumu?
Kupeza Choonadi Kumadzetsa Chimwemwe
4. Kodi choonadi cha Ufumu chikuwakhudza motani anthu lerolino?
4 Wamalonda wa m’fanizo la Yesu anasangalala kwambiri atapeza ngale imene anaizindikira kuti ndi “ya mtengo wapatali.” Chimwemwe chimenecho chinam’limbitsa mtima kuchita zonse zotheka kuti agule ngaleyo. (Ahebri 12:1) Lerolinonso, choonadi chonena za Mulungu ndi Ufumu wake chimakopa anthu ndi kuwalimbitsa mtima kuchita zonse zotheka kuti apeze Ufumuwo. Izi zikutikumbutsa mawu a Mbale A. H. Macmillan, onena za mmene anayesetsera kudziwa Mulungu ndi cholinga Chake polenga anthu. Analemba mawuwo m’buku lakuti Faith on the March. Anati: “Zimene ndapezazi, anthu ambiri chaka ndi chaka akuzipezanso. Anthu amenewa ali ngati inuyo ndi ine, chifukwa ndi osiyanasiyana, ochokera m’mitundu yonse, m’mafuko onse, ndipo ndi amisinkhu yonse. Choonadi sichiona nkhope. Chimakopa munthu aliyense, kaya akhale wa mtundu wotani.”
5. Kodi lipoti la chaka cha utumiki cha 2004 likusonyeza zinthu zotani zolimbikitsa?
5 Mawu amenewa ndi oona, chifukwa chaka ndi chaka anthu oona mtima masauzande ambiri amalimbikitsidwa ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kuti apereke moyo wawo kwa Yehova ndi kuchita chifuniro chake. Ndi zimene zinachitikanso m’chaka chautumiki cha 2004, chomwe chinayamba mu September 2003 mpaka mu August 2004. Pa miyezi 12 imeneyo, anthu 262,416 anaonetsa poyera kuti adzipereka kwa Yehova pobatizidwa m’madzi. Izi zinachitika m’mayiko 235. M’mayikowo, Mboni za Yehova zikuchititsa maphunziro a Baibulo a panyumba okwana 6,085,387 mlungu uliwonse. Akutero kuti athandize anthu osiyanasiyana, ochokera m’mitundu yambiri, mafuko, ndi zinenero kuphunzira choonadi cha m’Mawu a Mulungu.—Chivumbulutso 7:9.
6. Kodi n’chiyani chachititsa kuwonjezeka pa zaka zonsezi?
6 Kodi zonsezi zinatheka bwanji? Sitingakayikire kuti Yehova ndiye amakokera anthu amenewa ofuna choonadi kwa iye. (Yohane 6:65; Machitidwe 13:48) Koma sitinganyalanyaze awo amene adzikhutula pantchito ya Ufumu mosadzikonda ndiponso mwa kuyesetsa osatopa. Pamene anali ndi zaka 79 zakubadwa, Mbale Macmillan analemba kuti: “Kuchokera pamene ndinaphunzira kwa nthawi yoyamba za malonjezo operekedwa kwa mtundu wa anthu umene ukudwala ndi kufawu, chiyembekezo changa pa zimene uthenga wa m’Baibulo umasonyeza sichinachepe. Nditangophunzira za malonjezowo, ndinatsimikiza mtima kufufuza zowonjezeka zimene Baibulo limaphunzitsa. Cholinga chinali chakuti ndikathandizenso ena ofanana ndi ine, amene akufunitsitsa kudziwa za Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova, ndi zolinga zake zabwino zokhudza mtundu wa anthu.”
7. Ndi chitsanzo chotani chimene chikusonyeza bwino lomwe chimwemwe ndi changu chimene anthu opeza choonadi cha m’Baibulo amakhala nacho?
7 Kufunitsitsa komweko tikukuonanso pakati pa atumiki a Yehova lerolino. Chitsanzo ndi Daniela wochokera ku Vienna, m’dziko la Austria. Iye anati: “Kuyambira ndili mwana, Mulungu anali bwenzi langa la pamtima. N’chifukwa chake ndinali kufunitsitsa kudziwa dzina lake, chifukwa kwa ineyo, kungom’tchula kuti ‘Mulungu’ zinali kumveka ngati ndi wakutali kwambiri woti sangakhale bwenzi langa. Koma sindinalidziwe mpaka pamene ndinali ndi zaka 17 zakubadwa, pamene a Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwathu. Iwo anandifotokozera zonse zokhudza Mulungu zimene ndinali kufuna kudziwa. Ndinasangalala kwambiri kupeza choonadi pamapeto pake, moti ndinayamba kulalikira kwa wina aliyense.” Posakhalitsa, chifukwa cha changu chake, anzake ku sukulu anayamba kum’seka. Koma Daniela anati: “Kwa ine zinali ngati kuona ulosi wa m’Baibulo ukukwaniritsidwa, chifukwa ndinali nditaphunzira kuti Yesu ananena kuti otsatira ake adzadedwa ndi kuzunzidwa chifukwa cha dzina lake. Ndinakondwera kwambiri ndipo ndinadabwa kuona zikuchitikadi.” Posapita nthawi, Daniela anapereka moyo wake kwa Yehova, ndipo anabatizidwa. Kenako, anayamba kuchita zinthu zom’thandiza kuti afike pa cholinga chake chokhala mmishonale. Atakwatiwa, Daniela, limodzi ndi mwamuna wake, Helmut, anayamba kulalikira kwa anthu ochokera ku Africa, ku China, ku Philippines, ndi ku India omwe anali mu mzinda wa Vienna. Daniela ndi Helmut tsopano ndi amishonale kum’mwera koma chakumadzulo kwa Africa.
Saleka
8. Kodi ochuluka asonyeza chikondi chawo pa Mulungu ndi kukhulupirika ku Ufumu wake m’njira yokhutiritsa yotani?
8 Ndithudi, umishonale ndi imodzi mwa njira zimene anthu a Yehova lerolino amasonyezera chikondi chawo kwa Mulungu ndiponso kukhulupirika ku Ufumu wake. Mofanana ndi wamalonda woyendayenda wa m’fanizo la Yesu, amene amalowa utumiki umenewu amakhala ofunitsitsa kupita kutali kwambiri chifukwa cha Ufumu wa Mulungu. Koma amishonale amenewa sayenda ulendowo kuti akapeze uthenga wabwino wa Ufumu ayi. Iwo amapititsa uthengawo kwa anthu okhala kumadera akutali kwambiri, kuwaphunzitsa ndi kuwathandiza kukhala ophunzira a Yesu Kristu. (Mateyu 28:19, 20) M’mayiko ambiri, iwo amapirira mavuto adzaoneni. Koma amapeza mphoto yaikulu pa kupirira kwawo.
9, 10. Kodi amishonale akuona zosangalatsa zotani m’mayiko ngati Central African Republic?
9 Chitsanzo chimodzi ndi dziko la Central African Republic. Chaka chatha, anthu 16,184 anasonkhana pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu, pamene m’dzikolo muli ofalitsa Ufumu 2,426 okha. Popeza kuti madera ambiri m’dziko limenelo kulibe magetsi, anthu pochita ntchito zawo za pakhomo zatsiku ndi tsiku amakhala panja, pansi pa mtengo. Ndiye amishonale nawonso amachita ntchito yawo m’njira yomweyo, kuchititsa maphunziro a Baibulo atakhala pa mthunzi, pansi pa mtengo wogudira bwino. Panjapo pamakhala powala bwino ndipo pamakhala kamphepo kayaziyazi. Koma si zokhazo. Anthu m’dzikolo amakonda kwambiri Baibulo, ndipo amatha kucheza nkhani zokhudza Mulungu paliponse, mmene anthu amachezera za mpira ndi zanyengo. Chotero, odutsa chapafupi amaona phunziro la Baibulo limene likuchitika ndipo amangopatuka n’kukhala nawo pa phunzirolo.
10 N’zimene zinachitika mmishonale wina akuchititsa phunziro la Baibulo panja pa nyumba ina. Mnyamata amene anali kukhala tsidya lina la msewu anafika pomwe panali mmishonale uja, n’kumuuza kuti mmishonaleyo afikenso ku nyumba kwa mnyamatayo kudzaphunzira naye Baibulo, chifukwa palibe anam’fikira. Mmishonaleyo analola, ndipo mnyamatayo akupita patsogolo kwambiri. M’dziko limenelo, apolisi kawirikawiri amaimitsa a Mboni pa msewu, osati kuti awapatse chisamani kapena kuti awalipiritse pa mlandu winawake, koma kuti awapemphe magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kapena kuti awathokoze chifukwa cha nkhani ina ya m’magazini amenewa imene inawasangalatsa kwambiri.
11. Mosasamala za mayesero, kodi amishonale amene atumikira kwa nthawi yaitali amamva bwanji za utumiki wawo?
11 Ochuluka amene anayamba umishonale zaka 40 kapena 50 zapitazo akutumikirabe mokhulupirika. Alitu chitsanzo chabwino zedi kwa tonsefe cha chikhulupiriro ndi kulimbikira. Pa zaka 42 zapitazi, mbale wina ndi mkazi wake achita umishonale m’mayiko atatu. Mbaleyo anati: “Takumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, tinalimbana ndi malungo zaka 35. Koma sitinalingalirepo kuti tinalakwitsa kukhala amishonale.” Mkazi wake anawonjezapo kuti: “Nthawi zonse pamakhala zinthu zambiri zimene timaziyamikira. Utumiki wa kumunda umadzetsa chimwemwe chachikulu, ndipo kuyambitsa maphunziro a Baibulo n’kosavuta. Ukamaona ophunzira akufika pamisonkhano, n’kumadziwana nawo bwino, nthawi zonse misonkhano imakhala ngati macheza a pabanja.”
Amaona Zonse Kukhala Zosapindulitsa
12. Kodi munthu amaonetsa motani kuti amayamikiradi mtengo wapatali wa Ufumu?
12 Wa malonda uja atapeza ngale ya mtengo wapatali, “anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.” (Mateyu 13:46) Mtima umenewu wololera kusiya zimene zimaonedwa kukhala za mtengo wapatali, ndiwo uli ndi anthu amene amayamikiradi mtengo wapatali wa Ufumu. Monga mmodzi mwa amene adzalandira ulemerero wa Ufumu pamodzi ndi Kristu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadziwonjezere Kristu.”—Afilipi 3:8.
13. Kodi munthu wina ku Czech Republic anaonetsa motani chikondi chake pa Ufumu?
13 Mofananamo, ambiri lerolino ndi ofunitsitsa kusintha zinthu zikuluzikulu m’moyo wawo kuti apeze madalitso a Ufumu. Mwachitsanzo, mu October 2003, ku dziko la Czech Republic, mwamuna wina wa zaka 60 zakubadwa, yemwe ndi mphunzitsi wamkulu pa sukulu, anapeza buku lothandiza kuphunzira Baibulo lotchedwa Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Ataliwerenga, nthawi yomweyo anapempha a Mboni za Yehova a kuderalo kuti azikam’phunzitsa Baibulo. Anapita patsogolo mwauzimu, ndipo posapita nthawi, anayamba kupezeka pa misonkhano yonse. Nangano bwanji za maganizo ake ofuna kudzapikisana nawo pa chisankho cha meya, kenako cha aphungu? Anasankha kulowa mpikisano wina, mpikisano wothamangira moyo wosatha, monga wolengeza Ufumu. Iye anati: “Ndinagawira mabuku ophunzitsa Baibulo ochuluka kwa ana a sukulu pa sukulu yathu.” Anaonetsa kuti wadzipereka kwa Yehova pobatizidwa m’madzi pa msonkhano wachigawo mu July 2004.
14. (a) Kodi uthenga wabwino wa Ufumu walimbitsa mtima anthu ambirimbiri kuchita chiyani? (b) Kodi aliyense wa ife angadzifunse mafunso otani ofuna kuganizapo kwambiri?
14 Enanso ambirimbiri achita zofananazo atamva uthenga wabwino wa Ufumu. Iwo atuluka m’dziko loipali, avula umunthu wawo wakale, asiyana ndi mabwenzi awo akale, ndi kusiyanso zotanganitsa za dziko. (Yohane 15:19; Aefeso 4:22-24; Yakobo 4:4; 1 Yohane 2:15-17) N’chifukwa chiyani amatero? Amatero chifukwa amaona madalitso a Ufumu wa Mulungu kukhala apamwamba kuposa china chilichonse chimene angapeze m’dongosolo lino la zinthu. Kodi inunso mumaona uthenga wabwino wa Ufumu mofananamo? Kodi wakulimbitsani mtima kusintha zina ndi zina kuti moyo wanu, zolinga zanu, ndi zinthu zimene mumaona kukhala zofunika zikhale zogwirizana ndi zimene Yehova amafuna? Mukatero, mudzalandira madalitso ochuluka, lerolino ndi m’tsogolo momwe.
Ntchito Yotuta Yafika Pachimake
15. Kodi ulosi unati anthu a Mulungu adzachita zotani m’masiku otsiriza?
15 Wamasalmo analemba kuti: “Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu.” Odziperekawo akuphatikizapo “mame a ubwana,” kapena kuti anyamata ochuluka ngati mame. Palinso “khamu lalikuku” la ‘akazi olalikira uthengawo.’ (Salmo 68:11; 110:3) Kodi pakhala zotsatira zotani masiku otsiriza ano chifukwa cha khama ndi kudzipereka kwa anthu a Yehova, amuna ndi akazi, ana ndi achikulire?
16. Perekani chitsanzo cha mmene atumiki a Mulungu akuyesetsera kuthandiza ena kuphunzira za Ufumu.
16 Mpainiya wina, kapena kuti wolengeza Ufumu nthawi zonse, ku India anali ndi nkhawa poganiza mmene anthu ogontha oposa mamiliyoni awiri m’dzikolo angathandizidwire kudziwa za Ufumu. (Yesaya 35:5) Anaganiza zochita kosi ya chinenero cha manja mu mzinda wa Bangalore. Ali ku kosiko, mlongoyu anauza ogontha ambiri za chiyembekezo cha Ufumu, ndipo anayambitsa magulu ophunzira Baibulo. Pambuyo pa milungu yochepa chabe, anthu oposa 12 anayamba kufika pamisonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Kenako, ali pa phwando la ukwati, mpainiyayu anakumana ndi mnyamata wina wogontha wochokera ku mzinda wa Calcutta. Ameneyu anali ndi mafunso ambiri ndipo anasonyeza chidwi chofuna kudziwa zambiri za Yehova. Koma panali vuto. Mnyamatayo anafunikira kubwerera ku Calcutta, ulendo wa makilomita 1,600, kuti akayambe maphunziro a ku koleji. Koma kumeneko kunalibe Mboni zodziwa chinenero cha manja. Atalimbikira kukambirana ndi bambo ake, anamulola kuimba sukulu yakeyo mu mzinda wa Bangalore m’malo mwake, n’cholinga choti apitirize kuphunzira Baibulo. Iye anapita patsogolo mwauzimu, ndipo patatha pafupifupi chaka chimodzi, anapereka moyo wake kwa Yehova. Kenako, iyeyo anaphunzitsa Baibulo anthu ogontha angapo, kuphatikizapo mnyamata amene anali bwenzi lake la paubwana. Ofesi ya nthambi ku India tsopano ikukonza zoti apainiya aphunzire chinenero cha manja kuti azithandiza anthu ogontha.
17. Fotokozani chimene mwaona kukhala cholimbikitsa kwambiri pa lipoti la chaka chautumiki cha 2004, pa masamba 19 mpaka 22.
17 Pa masamba 19 mpaka 22 a magazini ino, pali lipoti losonyeza ntchito imene Mboni za Yehova zagwira m’munda, m’chaka chautumiki cha 2004 padziko lonse lapansi. Liwerengeni mofatsa kuti mudzionere nokha umboni wakuti anthu a Yehova padziko lonse lapansi aikadi maganizo awo onse pa ‘ngale ya mtengo wapatali’ lerolino.
Pitirizani ‘Kufunafuna Ufumu Choyamba’
18. N’chiyani chimene Yesu sananene m’fanizo lake la wamalonda a ngale, ndipo sananenerenji?
18 Tiyeni tibwererenso ku fanizo la Yesu la wamalonda uja. Tikuona kuti Yesu sananene kalikonse kokhudza mmene wamalondayo anali kupezera zofunika pa moyo, atagulitsa zonse zimene anali nazo. Pachifukwa chimenechi, ena angafunse kuti: ‘Tsono wamalondayu akanapeza bwanji chakudya, zovala, ndi pogona, alibe kena kalikonse? Ngale ya mtengo wapatali imeneyo inalinso ndi phindu lanji?’ Amenewo angaoneke ngati mafunso anzeru malinga ndi kaganizidwe ka munthu. Koma kodi Yesu sanalimbikitse ophunzira ake kuti: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu”? (Mateyu 6:31-33) Mfundo yaikulu ya fanizo limeneli ndiyo kufunika kosonyeza kudzipereka ndi mtima wonse kwa Mulungu, ndi kuchita changu pantchito ya Ufumu. Kodi pali phunziro kwa ife?
19. Kodi tingaphunzire mfundo yanji yaikulu pa fanizo la Yesu la ngale ya mtengo wapatali?
19 Kaya tangophunzira kumene za uthenga wabwino kapena takhala tikugwira ntchito ya Ufumu ndi kuuza ena za madalitso ake kwa nthawi yaitali, tiyenera kupitirizabe kuika chidwi chathu chonse pa Ufumuwo. Tili m’nthawi zovuta, koma tili ndi zifukwa zabwino zokhulupirira kuti chimene tikuchigwirira ntchito ndi chinthu chenicheni ndipo sitingachiyerekeze ndi china chilichonse. Chili ngati ngale imene wamalonda uja anapeza. Zimene zikuchitika m’dziko ndiponso maulosi a m’Baibulo amene akwaniritsidwa ndizo umboni wotsimikizika wakuti tikukhala ‘m’mathedwe a nthawi ya pansi pano.’ (Mateyu 24:3) Mofanana ndi wamalonda uja, tiyeni tisonyeze changu chochokera pansi pa mtima, pogwira ntchito ya Ufumu wa Mulungu. Ndiponso, tisangalale ndi mwayi umenewu wolengeza uthenga wabwino.—Salmo 9:1, 2.
-