Kodi Mungalipire Zingati pa Chinthuchi?
KODI mumadziŵa chinthu chilichonse chamtengo kwambiri chimene mungakhale wofunitsitsa kupereka chilichonse chimene muli nacho kuti mukhale nacho? Yesu anachita zimenezo, ndipo analankhula za icho kwa otsatira ake.
Iye anati: “Ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi munthu wa malonda, wakufuna ngale zabwino: ndipo mmene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.”—Mateyu 13:45, 46.
Munthu wamalonda ameneyo anali wofunitsitsa kulepa zonse kotero kuti agule “ngale” imeneyo, Ufumu wa Mulungu. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti palibe chinthu china m’dzikoli chimene chingafanane nawo. Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto amene munthu walephera kuwathetsa, monga ngati nkhondo, njala, upandu, ndi kutsendereza. (Salmo 72:4-8, 13, 14) Pansi pa Ufumuwo, ngakhale uchimo, matenda, ndi imfa sizidzakhalako. (Chivumbulutso 21:4, 5) Nkosadabwitsa kuti pempho lachiŵiri la Pemphero la Ambuye (“Atate Wathu”) limati, “Ufumu wanu udze”!—Mateyu 6:9, 10.
Kodi mungalipirenji kuti mugaŵanemo m’madalitso a Ufumuwo? Kwenikwenidi, madalitsowo ngaulere. Koma kuti musangalale nawo, mufunikira kudziŵa chimene Ufumuwo uli, kukhulupirira kuti ulidi weniweni, ndi kuupatsa malo oyamba m’moyo wanu. Kodi mungachite zimenezo? M’Baibulo muli chidziŵitso chimene chidzakuthandizani. Bwanji osalola Mboni za Yehova kukuthandizani kuphunzira za Ufumu wa Mulungu ndi kupeza mmene ungakupindulitsireni ngakhale tsopano lino.