Kodi Khoka ndi Nsomba Zimatanthauzanji kwa Inu?
‘Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziŵa zinsinsi za ufumu wa kumwamba.’—MATEYU 13:11.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji tingakhale okondweretsedwa ndi mafanizo a Yesu?
KODI mumakonda kudziŵa chinsinsi kapena kumasulira mwambi? Bwanji ngati kutero kukakuthandizani kuwona mbali yanu bwino lomwe m’nchifuno cha Mulungu? Mwachimwemwe, mungathe kupeza mwaŵi wotero wa chidziŵitso kudzera m’fanizo limene Yesu anapereka. Linadabwitsa ambiri amene analimva ndipo ladabwitsa ambiri chiyambire, koma inu mungalimvetse.
2 Onani zimene Yesu ananena pa Mateyu chaputala 13 ponena za kugwiritsira kwake mafanizo. Ophunzira ake adafunsa kuti: “Chifukwa chanji muphiphiritsira iwo m’mafanizo?” (Mateyu 13:10) Inde, kodi nchifukwa ninji Yesu anagwiritsira ntchito mafanizo amene anthu ambiri sanamvetsetse? Iye anayankha pa mavesi 11 kufikira ku 13: ‘Chifukwa kwapatsidwa kwa inu kudziŵa zinsinsi za ufumu wa kumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo. Pakuti yense amene ali nazo, kudzapatsidwa kwa iye, ndimo adzakhala nazo zochuluka; koma yense amene alibe, chingakhale chomwe ali nacho chidzachotsedwa kwa iye. Chifukwa chake ndiphiphiritsira iwo m’mafanizo; chifukwa kuti akuwona samawona, ndi akumva samamva, kapena samadziŵitsa.’
3. Kodi kumvetsa mafanizo a Yesu kungatipindulitse motani?
3 Ndiyeno Yesu anagwiritsira ntchito Yesaya 6:9, 10, amene anafotokoza za anthu amene adali ogontha ndi akhungu mwauzimu. Komabe, ife sitiyenera kukhala otero. Ngati timvetsetsa ndi kuchitapo kanthu pamafanizo ake, tingakhale achimwemwe kwambiri—tsopano ndi mtsogolo mosatha. Yesu akutitsimikizira mwaubwenzi kuti: “Maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva.” (Mateyu 13:16) Chitsimikiziro chimenecho chikuphatikizapo mafanizo onse a Yesu, komano tiyeni tisumike maganizo pafanizo lalifupi la khoka, lolembedwa pa Mateyu 13:47-50.
Fanizo Lokhala ndi Tanthauzo Lozama
4. Kodi Yesu anasimbanji mwafanizo, monga momwe kwalembedwera pa Mateyu 13:47-50?
4 “Ndiponso, ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi khoka loponyedwa m’nyanja, ndi kusonkhanitsa pamodzi za mitundu yonse; limene podzala, analivuulira pamtunda; ndipo m’mene anakhala pansi, anazisonkhanitsa zabwino m’zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo. Padzatero pa chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino, nadzawataya m’ng’anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”
5. Kodi ndimafunso otani amene amabuka ponena za tanthauzo la fanizo la khoka?
5 Mwinamwake munawonapo anthu akusodza ndi khoka, kaya pa kanema kapena pa wailesi yakanema, chotero fanizo la Yesu nlosavuta kuliwona m’maganizo. Koma bwanji ponena za tsatanetsatane ndi tanthauzo lake? Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti fanizoli limanena za “ufumu wa kumwamba.” Komabe, ndithudi iye sanatanthauze kuti ‘mitundu yonse’ ya anthu, abwino ndi osayenerera, kapena oipa, adzakhala mu Ufumuwo. Ndiponso, kodi ndani amene akusodza? Kodi kusodzaku ndi kulekanitsa kunachitika m’tsiku la Yesu, kapena kodi nkwa nthaŵi yokha, ‘mapeto a dongosolo la zinthu’? Kodi inu mukudziwona m’fanizo limeneli? Kodi mungapeŵe motani kukhala pakati pa awo amene amalira ndi kukukuta mano?
6. (a) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala okondweretsedwa kwambiri m’kumvetsetsa fanizo la khoka? (b) Kodi nchiyani chingathandize kulimvetsetsa?
6 Mafunso ameneŵa akusonyeza kuti fanizo limeneli siliri lokhweka konse. Komabe, musaiŵale kuti: “Maso anu ali odala, chifukwa apenya, ndi makutu anu chifukwa amva.” Tiyeni tiwone ngati tingafufuze tanthauzo lake kotero kuti makutu athu asakhale osamva ndi maso athu osawona tanthauzo lake. Kwenikweni, tiri nayo kale mfungulo yofunika yopezera tanthauzo lake. Nkhani yapitayi yatiuza za Yesu akumaitana asodzi a ku Galileya kusiya ntchito yawoyo ndi kuloŵa ntchito yauzimu monga “asodzi a anthu.” (Marko 1:17) Iye anawauza kuti: ‘Kuyambira tsopano mudzakhala asodzi a anthu.’—Luka 5:10.
7. Kodi Yesu anali kuchitira fanizo chiyani pamene analankhula za nsomba?
7 Mogwirizana ndi zimenezo, nsomba za m’fanizo lino zimaimira anthu. Chifukwa chake, pamene vesi 49 limalankhula za kulekanitsa oipa kwa olungama, limasonya, osati kwa zolengedwa za m’nyanja zolungama kapena zoipa, koma anthu olungama kapena oipa. Mofananamo, vesi 50 siliyenera kutipangitsa kulingalira za nyama za m’nyanja zimene zimalira kapena kukukuta mano awo. Ayi. Fanizoli likunena za kusonkhanitsidwa kwa anthu ndi kulekanitsidwa kwawo kotsatirapo, kumene kuli nkhani yaikulu kwambiri, monga momwe zotulukapo zake zimasonyezera.
8. (a) Kodi tingaphunzire chiyani pachotulukapo cha nsomba zosayenera? (b) Polingalira za zimene zinanenedwa ponena za nsomba zosayenera, kodi tingatsimikizirenji ponena za Ufumu?
8 Onani kuti nsomba zosayenera, ndiko kuti oipa, adzaponyedwa m’ng’anjo yamoto, kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. Kwinakwake, Yesu anagwirizanitsa kulira koteroko ndi kukukuta mano kukhala kunja kwa Ufumu. (Mateyu 8:12; 13:41, 42) Pa Mateyu 5:22 ndi 18:9, anatchuladi ‘Gehena wamoto,’ kusonyeza chiwonongeko chosatha. Kodi zimenezo sizimasonyeza mmene kuliri kofunika kupeza tanthauzo la fanizo limeneli ndi kuchitapo kanthu moyenera? Tonsefe tidziŵa kuti mu Ufumu wa Mulungu mulibe kapena simudzakhala oipa. Chifukwa chake, pamene Yesu ananena kuti “ufumu wa kumwamba uli wofanana ndi khoka,” ayenera kukhala anatanthauza kuti mogwirizana ndi Ufumu wa Mulungu, muli mbali yofanana ndi khoka loponyedwa kuti ligwire nsomba za mitundumitundu.
9. Kodi angelo akuphatikizidwa motani m’fanizo la khoka?
9 Khoka limenelo litaponyedwa ndipo nsomba zitagwidwa, pakakhala ntchito yolekanitsa. Kodi ndani amene Yesu anati anaphatikizidwa? Mateyu 13:49 amasonyeza asodzi olekanitsa ameneŵa monga angelo. Chotero Yesu akutiuza za uyang’aniro wa angelo pachiŵiya cha padziko lapansi chimene chikugwiritsidwa ntchito kudziŵikitsa anthu—ena abwino ndi oyenerera Ufumu wa kumwamba, ena osayenerera chiitano chimenecho.
Kusodza—Liti?
10. Kodi ndimwanjira yakulingalira kotani kumene tingatsimikiziritse kuti kusodzako kunafutukulidwira kunyengo yaitali yanthaŵi?
10 Mawu apambuyo ndi apatsogolo pa lembalo amatithandiza kudziŵa pamene zimenezi zikugwira ntchito. Mwamsanga izi zisanachitike, Yesu anapereka fanizo lonena za kufesa mbewu yabwino, komano namsongole anafesedwanso m’mundamo, amene amaphiphiritsira dziko. Iye anafotokoza pa Mateyu 13:38 kuti mbewu yabwino inaimira “ana a ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo.” Zimenezi zinakulira limodzi kwa zaka mazana ambiri, kufikira kututa m’nthaŵi ya mapeto a dongosolo la zinthu. Pamenepo namsongole analekanitsidwa ndipo pambuyo pake kutenthedwa. Poyerekezera ndi fanizo la khoka, tikuwona kuti kuloŵetsa zolengedwa m’khoka kunali kudzatenga nyengo yaitali yanthaŵi.—Mateyu 13:36-43.
11. Kodi ntchito yakusodza kwa mitundu yonse inayamba motani m’zaka za zana loyamba?
11 Malinga ndi fanizo la Yesu, nsombazo zikasonkhanitsidwa mosasankha, ndiko kuti, khokalo linakola ponse paŵiri nsomba zabwino ndi nsomba zosayenera. Pamene atumwiwo anali moyo, angelo otsogoza ntchito yosodza anagwiritsira ntchito gulu Lachikristu la Mulungu kugwira “nsomba” zomwe zinakhala Akristu odzozedwa. Munganene kuti Pentekoste wa 33 C.E. asanafike, kusodza anthu kwa Yesu kunakola pafupifupi ophunzira 120. (Machitidwe 1:15) Koma pamene mpingo wa Akristu odzozedwa unakhazikitsidwa, kusodza kochitidwa ndi chiŵiya cha khoka kunayamba, ndipo nsomba zikwi zambiri zabwino zinagwidwa. Kuyambira 36 C.E. kusodzako kunafalikira m’madzi amitundu yonse, pamene Akunja analoŵetsedwa m’Chikristu ndipo anakhala ziŵalo za mpingo wodzozedwa wa Kristu.—Machitidwe 10:1, 2, 23-48.
12. Kodi nchiyani chinayambika pambuyo pa imfa ya atumwi?
12 Zaka mazana ambiri pambuyo pakuchoka kwa atumwi padziko lapansi, Akristu ena oyesayesa kupeza ndi kugwiritsira chowonadi cha Mulungu anapitiriza kukhalako. Ndipo ena a iwo anayanjidwa ndi Mulungu, ndipo iye anawadzoza ndi mzimu woyera. Chikhalirechobe, imfa ya atumwi inachotsa chisonkhezero choletsa, ikumaloleza mpatuko wofalikirawo kuyambika. (2 Atesalonika 2:7, 8) Gululo linakula mwakuti linadzinenera mosayenerera kukhala mpingo wa Mulungu. Linadzinenera monyenga kukhala mtundu wopatulika wodzozedwa ndi mzimu wa Mulungu kudzalamulira ndi Yesu.
13. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti Chikristu Chadziko chinali ndi mbali m’ntchito ya khoka?
13 Kodi muganiza kuti Akristu odzinenera osakhulupirikawo anali ndi mbali iriyonse m’fanizo la khoka? Eya, pali chifukwa cha kuyankhira kuti inde, anaterodi. Khoka lophiphiritsiralo linaphatikizapo Chikristu Chadziko. Zowona, kwa zaka zambiri Tchalitchi Chachikatolika chinayesa kuletsa anthu wamba kukhala nalo Baibulo. Komabe, mkupita kwa zaka mazana ambiri ziŵalo za Chikristu Chadziko zinachita mbali yaikulu kutembenuza, kukopa, ndi kufalitsa Mawu a Mulungu. Pambuyo pake matchalitchi anapanga kapena anachirikiza magulu otetezera Baibulo, amene anamasulira Baibulo m’zinenero zakumidzi. Iwo anatumizanso amishonale amene anali madokotala ndi aphunzitsi, amene anagwira ntchito yopanga Akristu m’dzina lokha. Izi zinasonkhanitsa ziŵerengero zazikulu za nsomba zosayenerera, zimene Mulungu sanavomereze. Koma zinayesa kuchititsa mamiliyoni osakhala Akristu kuwona Baibulo ndi mpangidwe wa Chikristu, ngakhale kuti unali woipa.
14. Kodi ntchito ina ya matchalitchi a Chikristu Chadziko inathandizira motani kusodza nsomba zabwino?
14 Panthaŵi yonseyi, okhulupirika omwazikanawo omamatira ku Mawu a Mulungu anagwira ntchito zolimba monga momwe anathera. Panthaŵi iriyonse, iwo anakhalapo monga mpingo wowona wa odzozedwa a Mulungu padziko lapansi. Ndipo tingatsimikizire kuti nawonso anali kusodza nsomba, kapena anthu, amene unyinji wawo Mulungu akawawona kukhala abwino ndi kuwadzoza ndi mzimu wake. (Aroma 8:14-17) Odzinenera kukhala Akristu abwinowa anali okhoza kudzetsa chowonadi cha Baibulo kwa ambiri amene anakhala Akristu m’dzina lokha kapena amene anapeza chidziŵitso chochepekera cha Baibulo m’Malemba otembenuzidwa m’zinenero zawo ndi magulu ochirikiza Baibulo a Chikristu Chadziko. Zowonadi, kusonkhanitsidwa kwa nsomba zabwino kukupitirizabe, ngakhale kuti zambiri zimene zinali kusonkhanitsidwa ndi Chikristu Chadziko zosayenerera zinali m’lingaliro la Mulungu.
15. Mwachindunji, kodi nchiyani chimene chikuimiridwa ndi khoka la fanizolo?
15 Chotero khoka limaphiphiritsira chiŵiya chapadziko lapansi chimene chimadzinenera kukhala mpingo wa Mulungu chimene chimasonkhanitsa nsomba. Chimaphatikizapo ponse paŵiri Chikristu Chadziko ndi mpingo wa Akristu odzozedwa, apambuyowa akumapitirizabe kusonkhanitsa nsomba zabwino, pansi pa chitsogozo chosawoneka cha angelo, mogwirizana ndi Mateyu 13:49.
Nthaŵi Yathu Iri Yapadera
16, 17. Kodi nchifukwa ninji nthaŵi imene tikukhalamo iri yofunika m’kukwaniritsidwa kwa fanizo la Yesu la khoka?
16 Tsopano tiyeni tilingalire za mbali ya nthaŵi. Kwa zaka mazana ambiri chiŵiya cha khokalo chinasonkhanitsa nsomba zabwino ndiponso zambiri zosayenera, kapena oipa. Ndiyeno nthaŵi inadza pamene angelo anaphatikizidwa m’kuchita ntchito yofunika ya kulekanitsa. Liti? Eya, vesi 49 (NW) limanena bwino lomwe kuti muli mkati mwa “mapeto a dongosolo la zinthu.” Izi zimagwirizana ndi zimene Yesu ananena m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi: “Koma pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pachimpando cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.”—Mateyu 25:31, 32.
17 Chifukwa chake, mogwirizana ndi Mateyu 13:47-50, ntchito yolekanitsa yofunikayo yotsogozedwa ndi angelo yakhala ikuchitika chiyambire pamene “mapeto a dongosolo la zinthu” anayamba mu 1914. Izi zinali zowonekera makamaka pambuyo pa 1919, pamene otsalira a odzozedwa anamasulidwa muukapolo wakanthaŵi, kapena undende, ndi kukhala chiŵiya chogwira mtima mowonjezereka cha kumaliza ntchito yosodza.
18. Kodi ndimotani mmene nsomba zabwino zasonkhanitsidwira m’zotengera?
18 Kodi nchiyani chimene chinali kudzachitikira nsomba zabwino zolekanitsidwazo? Vesi 48 limanena kuti asodzi olekanitsa aungelowo “anazisonkhanitsa [nsomba] zabwino m’zotengera, koma zoipa anazitaya kuthengo.” Zotengerazo ndizo ziŵiya zotetezerera m’zimene nsomba zabwino zimaikidwa. Kodi zimenezi zachitika m’nthaŵi yathu? Ndithudi. Pamene nsomba zabwino zophiphiritsira zagwidwa zamoyo, zasonkhanitsidwira m’mipingo ya Akristu owona. Mipingo yonga zotengera imeneyi yathandizira kuwatchinjiriza ndi kuwasunga kaamba ka utumiki wa Mulungu, kodi simukuvomereza? Chikhalirechobe, wina angaganize kuti, ‘Zonsezi nzabwino, koma kodi ziri ndi chiyani ndi moyo wanga watsopano ndi mtsogolo mwanga?’
19, 20. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika lerolino kumvetsetsa tanthauzo lenileni la fanizoli? (b) Kodi ndintchito yakusodza yofunika kwambiri yotani imene yakhala ikuchitidwa chiyambire 1919?
19 Kuchitidwa kwa zinthu zimene zinafotokozedwa mwafanizo pano sikunali kolekezera m’zaka za mazana apakati pa nthaŵi ya atumwi ndi 1914. Mkati mwa nyengo imeneyo, chiŵiya cha khoka chinafikira pakusonkhanitsa ponse paŵiri odzinenera monyenga kuti ndi Akristu ndi odzinenera mowona. Inde, chinali kusonkhanitsa ponse paŵiri nsomba zosayenera ndi zabwino. Ndiponso, ntchito yolekanitsayo yochitidwa ndi angelo sinathe kumbuyoko cha ku ma 1919. Ndithudi ayi. M’mbali zina fanizo limeneli la khoka limafikira kunthaŵi yathu yeniyeniyo. Tikuphatikizidwamo ndipo motero mtsogolo mwathunso. Kuli kofunika kwa ife kumvetsetsa mmene ndi chifukwa chake zimenezo ziri choncho ngati tifuna kuti mawu awa agwire ntchito pa ife: “Maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva” ndi kuzindikira.—Mateyu 13:16.
20 Mwachiwonekere mumadziŵa kuti pambuyo pa 1919 otsalira odzozedwa anatanganitsidwa m’ntchito yolalikira mogwirizana ndi angelo, amene anapitirizabe kugwiritsira ntchito khoka lophiphiritsira kukokera nsombazo pagombe, kuti zilekanitsidwe zabwino ndi zosayenera. Ziŵerengero zochokera nthaŵi imeneyo zimasonyeza kuti kugwidwa kwa nsomba zabwino za odzozedwa ndi mzimu wa Mulungu kunapitirizabe pamene otsirizira a 144,000 anasonkhanitsidwa ndi khoka lophiphiritsira. (Chivumbulutso 7:1-4) Koma podzafika chapakati pa ma 1930, kusonkhanitsidwa kwa nsomba zabwino zokadzozedwa ndi mzimu woyera kwakukulukulu kunatha. Kodi pamenepo mpingo wa otsalira odzozedwa unafunikira kutaya khoka, kunena kwake titero, ndi kungokhala manja lende, kudikirira mphotho yawo yakumwamba? Kutalitali!
Mbali Yanu m’Kusodzako
21. Kodi nkusodza kwina kotani kumene kwachitika m’nthaŵi yathu? (Luka 23:43)
21 Fanizo la Yesu la khoka linasumikidwa pansomba zabwino zimene zikapatsidwa mphotho ya kupeza malo mu Ufumu wa kumwamba. Komabe, kuwonjezera pa fanizo limenelo, pali kusodza kwina kophiphiritsira kochitika pamlingo waukulu, monga momwedi kunafotokozedwera m’nkhani yapitayo. Kusodza kumeneku, sindiko kwa nsomba zabwino za odzozedwa za m’fanizo la Yesu, koma kwa nsomba zophiphiritsiridwa kukhala zikugwidwa zamoyo ndi kupatsidwa chiyembekezo chodabwitsa cha moyo padziko lapansi la paradaiso.—Chivumbulutso 7:9, 10; yerekezerani ndi Mateyu 25:31-46.
22. Kodi nchotulukapo chabwino chotani chimene tingakhale nacho, ndipo kodi chosiyana nacho nchotani?
22 Ngati inu muli ndi chiyembekezo chimenecho, pamenepo mungathe kukondwera kuti Yehova walola ntchito yopulumutsa miyoyo ya kusodza kupitirizabe kufikira tsopano. Izi zakutheketsani kukhala ndi chiyembekezo chodabwitsa. Chiyembekezo? Inde, limenelo ndilo liwu loyenerera kuligwiritsira ntchito, popeza kuti zotulukapo zidzadalira pakukhulupirika kwathu kopitirizabe kwa Uyo amene akutsogoza zoyesayesa za kusodza kopitirizako. (Zefaniya 2:3) Kumbukirani fanizolo kuti sinsomba zonse zogwidwa ndi khoka zimene zimakhala ndi chotulukapo chabwino. Yesu ananena kuti zosayenera, kapena oipa, adzalekanitsidwa kwa olungama. Ndi chotulukapo chotani? Pa Mateyu 13:50, Yesu anafotokoza chotulukapo chowopsa cha nsomba zosayenera, kapena zoipa. Zimenezi zidzaponyedwa m’ng’anjo yamoto, kutanthauza chiwonongeko chosatha.—Chivumbulutso 21:8.
23. Kodi nchiyani chimene chimapangitsa ntchito yosodza lerolino kukhala yofunika kwambiri?
23 Nsomba zabwino zodzozedwa, kudzanso nsomba zophiphiritsira zimene zingakhale ndi moyo kosatha padziko lapansi, ziri ndi chiyembekezo cha ulemerero. Pamenepotu, ndi chifukwa chabwino, angelo akutsimikizira kuti tsopano lino ntchito yosodza yachipambano ikuchitika kuzungulira padziko lonse. Ndipo ndinsomba zochuluka chotani nanga zimene zikugwidwa! Mukakhala wolondola kunena kuti m’lingaliro lapadera, kuli kugwira kozizwitsa kofanana ndi kuja kwa nsomba zenizeni kumene atumwi anali nako pamene anaponya makoka awo atalamulidwa ndi Yesu.
24. Kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita ponena za kusodza kwauzimu?
24 Kodi inuyo mumakhala ndi phande lokulirapo monga momwe mungathere m’ntchito yopulumutsa moyo ya kusodza kwauzimu imeneyi? Mosasamala kanthu za ukulu wa phande lomwe takhala nalo kufikira tsopano lino, aliyense wa ife angalimbikitsidwe mwa kuyang’ana pazimene zikukwaniritsidwa padziko lonse m’ntchito yaikulu yosodza ndi yopulumutsa moyo imene ikuchitidwa tsopano. Kutero kuyenera kutisonkhezera kukhaladi achangu chokulirapo m’kuponya makoka kuti tisodze m’masiku apatsogolopa!—Yerekezerani ndi Mateyu 13:23; 1 Atesalonika 4:1.
Kodi Mukuzikumbukira Mfundo Izi?
◻ Kodi nchiyani chimene chikuimiridwa ndi mitundu iŵiri ya nsomba m’fanizo la Yesu?
◻ Kodi ndim’lingaliro lotani limene matchalitchi a Chikristu Chadziko aphatikizidwira m’ntchito ya khoka?
◻ Kodi nchifukwa ninji kusodza kumene kukuchitika m’nthaŵi yathu kuli kofunika kwambiri?
◻ Kodi fanizo la khoka liyenera kusonkhezera aliyense wa ife kudzipenda motani?
[Chithunzi patsamba 18]
Ntchito yosodza yachitika m’Nyanja ya Galileya kwa zaka mazana ambiri
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.