Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 6/15 tsamba 24-27
  • Kusamalira Banja—Kodi Kumafutukuka Kufika ku Utali Wotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusamalira Banja—Kodi Kumafutukuka Kufika ku Utali Wotani?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Makolo ndi Ana
  • “Kubwezera”
  • Kupereka Chiyani? Liti?
  • Pewani Kulingalira Kodzilungamitsa
  • Kumachita Chimene Chiri Chabwino kwa Onse
  • Kuphunzira Kupembedza Mulungu Kulinga kwa Makolo Okalamba
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kulemekeza Makolo Athu Okalamba
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Kodi Nchifukwa Ninji Agogo Ŵathu Anadzakhala Nafe?
    Galamukani!—1992
  • Makolo, Pezerani A M’banja Lanu Zosowa Zawo
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 6/15 tsamba 24-27

Kusamalira Banja​—Kodi Kumafutukuka Kufika ku Utali Wotani?

“MWAMBO wa Chiafrica umandiuza ine kuti ndiri msungi wa abale anga,” anatero wolemba wa ku Nigeria S. A. Jegede. “Mwambo wa Chiafrica umaitanira kaamba ka ulemu ndi kusamalira makolo a munthuwe.” Inde, mu Africa ndi mbali zina za dziko lapansi, kuthandiza ziwalo za banja iri njira ya moyo.

Kaŵirikaŵiri, ngakhale kuli tero, “banja”limalingaliridwa kuphatikizapo azakhali, amalume, asuwani, mfumakazi, ndi aphwathu​—ngakhale anthu omwe ali kokha ochokera m’mudzi umodzi! Koma pamene mabanja a Chiafrica achoka mbali zakumidzi kupita kuntchito mu mzinda, ziwalo zabanja lofutukuka zimenezo zimakhala magwero enieni a mavuto. Mabanja osamutsidwa kaŵirikaŵiri amadzipeza iwo eni ogwidwa ndi achibale osakhala a mimba imodzi akuwafunsa ndalama kapena malo ogona. Chifukwa cha zifunsiro zapadera za moyo wa mu mzinda, ngakhale kuli tero, kuthandiza achibale osakhala a mimba imodzi kapena anthu ochokera m’mudzi umodzi kaŵirikaŵiri kumakhala kovuta, ngati kuli kosatheka nkomwe.

Baibulo limati: “Ndithudi ngati aliyense samapezera zosowa za awo amene ali ake ake ndipo makamaka awo amene ali ziwalo za banja lake, iye wakana chikhulupiriro ndipo ali woipa kwambiri koposa munthu wopanda chikhulupiriro.” (1 Timoteo 5:8, NW) Ndi kuutali wotani, ngakhale kuli tero, kumene prinsipulo la kusamalira banja limafutukuka? Kodi Mkristu ali pansi pa chitsenderezo chakupereka kaamba ka ziwalo zabanja lofutukulidwa mu mikhalidwe yonse? Kapena kodi icho chiri monga mmene wolemba wa Chinigeria wogwidwa mawu pamwambapo akunenera: “Kugwiritsira ntchito kolakwika kwa kachitidwe ka zinthu ka banja lofutukulidwa kulibe malo mu mwambo wa Chiafrica kapena mu Baibulo”?

Makolo ndi Ana

Njira ya kachitidwe ka zinthu ya banja lofutukulidwa inalipo mu nthawi za Baibulo. Komabe, mkupatsa thayo Mkristu la “kumapezera zowosa za awo amene ali ake ake,” palibe pena pali ponse mu Baibulo pamene pamasonyeza kuti ichi moyenerera chimaphatikiza anansi onse ndi ena onse. mnjira ya kachitidwe ka zinthu ya banja lofutukulidwa.

Baibulo mwachindunji limagogomezera za mathayo a makolo kulinga kwa ana. Ponena za kuthandiza kwake ndi mpingo, mtumwi Paulo analemba: “Pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amayi, koma atate ndi amayi kuunjikira ana.” (2 Akorinto 12:14) H. B. Clark, wolamulira wotchuka wa lamulo, anachitira ndemanga: “Thayo lachibadwa ndi loyenera limakhala pa atate kuchirikiza mwana wake.” Monga mutu wabanja wosankhidwa ndi Mulungu, atate ali ndi thayo loyambirira la kukhala wopezera zosowa za banja. Kawirikawiri mkazi amathandiza mwa kusamalira kaamba ka nyumba moyenerera, kuwononga mwanzeru, ngakhale kugwira ntchito kunja kwa nyumba pamene mikhalidwe ilamulira icho.​—Yerekezani ndi Miyambo 31: 10-31.

Dziwani, ngakhale kuli tero, kuti makolo akulimbikitsidwa kuchita zochulukira koposa ndi kungopeza ndalama. Iwo akufulumizidwa “kuunjikira” ndalama zina m’malo mwa ana awo. Makolo amene amatsatira uphungu wanzeru umenewu kawirikawiri amakhoza kuthandiza ana awo ngakhale pamene iwo akula ndi kuchoka panyumba. Mwapadera ichi chiri choyenera pamene ana alondola utumiki wanthawi zonse Wachikristu ndipo mwa kamodzikamodzi amafuna thandizo landalama kuti akhalebe mu utumiki umenewo. Palibe kutchulidwa kulikonse kwakuti makolo ayenera “kuunjikira” kaamba ka ziwalo zosawerengeka zabanja lofutukulidwa.

“Kubwezera”

Chisamaliro chachikondi chimenechi kumbali ya makolo sichiyenera kusafupidwa. Mtumwi Paulo ananena pa 1 Timoteo 5:4: “Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.” Chirikizo loterolo la kholo lokalamba kapena gogo mwachiwonekere lingagwirizane ndi lamulo la Baibulo la kulemekeza makolo.​—Aefeso 6:2; Eksodo 20:12.

Kachiwirinso, dziwani kuti Paulo mwachiwonekere sanaike thayo pa anansi osakhala amimba imodzi kusamalira kaamba ka akazi amasiye oterowo. Kubwerera mu nthawi imeneyo, panthawi imene panalibe mnansi yemwe anali pafupi kusamalira mkazi wamasiye Wachikristu wokhala ndi cholembera cha utumiki wokhulupirika, mpingo unayenera kusenza thayo la kuchirikiza iye.​—1 Timoteo 5:3, 9, 10.

Thayo la Chikristu lakupezera “awo amene ali ake ake” chotero mwachidziwikire limaphatikiza, mnzanu wa muukwati ndi ana, makolo ndi agogo. Thayo lamtundu umenewu limapezeka ngakhale pamene anthu okudalirani oterowo sali okhulupirira kapena ali opunduka mwakuthupi mwanjira ina yake. Ilo limapitirira kuutali womwe oterewa angakhalire ndi moyo. Ndipo ngati wina ali wokwatira, ilo lingaphatikizeponso kuthandiza mnzake wa muukwati kulemekeza makolo ake. Mavuto aakulu am’banja nthawi zina amabuka pamene prinsipulo limeneli lachitiridwa mphwayi kapena kunyozeredwa.

Kupereka Chiyani? Liti?

Mosasamala kanthu za chimenechi, makolo sayenera kumaliza kuti iwo angamalize ndalama zawo zonse mu chikhulupiriro chakuti iwo, panthawi iriyonse, angalamulire chirikizo lakuthupi kuchokera kwa ana awo. Sichikutanthauzanso kuti iwo angapange zifunsiro zopanda pake kaamba ka chisamaliro kuchokera kwa mbadwa zawo, zomwe kawirikawiri zimakhala ndi mabanja awo awo kwa amene thayo lawo loyambirira limaperekedwa. Kayang’anidwe kotereka kali m’chigwirizano ndi mawu a Paulo: “Pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amayi, koma atate ndi amayi kuunjikira ana.”​—2 Akorinto 12:14.

Mu zochitika za zinthu za chibadwa, makolo angakhale okhoza kupeza nyumba yawo, katundu wawo ndi magwero awo a ndalama (kuphatikizapo malipiro akuleka kugwira ntchito a kampani kapena a boma) omwe angachirikize iwo mu zaka zawo za ukalamba. “Ndalama zichirikiza,” ndipo mwa ‘kuunjikira’ kaamba ka iwo eni mwanzeru, makolo kawirikawiri angapewe kuika thayo lalikulu landalama kapena maganizo pa ana awo panthawi yamtsogolo m’moyo.​—Mlaliki 7:12.

Mawu a Solomo pa Mlaliki 9:11, ngakhale kuli tero, amatikumbutsa ife kuti ngakhale makonzedwe amene ali ndi maziko abwino koposa angayambukiridwe ndi “[nthawi ndi zotulukapo zosayembekezeredwa NW]” Chotero, bwanji ngati, mosasamala kanthu za kukonzekera kosamalitsa, njira yachichirikizo ya awiri okwatira ilephera kapena ifunikira kuwonjezera? Ana awo owopa Mulungu mwachibadwa adzafulumizidwa kuwathandiza iwo m’njira ina yoyenerera. Ichi chingatanthauze kupereka thandizo la ndalama, kuwaitana makolo kudzakhala nawo kapena pafupi nawo, kapena, ngati chiri choyenera, kukonzekera kaamba ka chisamaliro cha malo apadera. Indetu makolo achikulire kapena agogo mwachidziwikire ayenera kukhala anzeru, osati kuyembekezera mbadwa zawo kuwapezera njira ya moyo yapamwamba, popeza uphungu wa Baibulo umati: “Koma pokhala nazo zakudya ndi zofunda, zimenezi zitikwanire.”​—1 Timoteo 6:8.

Mu mbali zambiri, maprogramu a boma a chisungiko cha mayanjano, ndalama zopatsidwa pamene mwaleka ntchito, mapindu aukalamba, ndi zosunga zaumwini zingapereke chinjirizo lokwanira, koma losapambanitsa, kwa makolo okalamba kapena agogo. Chirichanzeru kupeza ndi zoperekedwa ziti zomwe ziripo kwa awo amene ali oziyenera.​—Aroma13:6.

Pewani Kulingalira Kodzilungamitsa

Yesu analanga alembi ndi Afarisi chifukwa iwo ananena kwa makolo osowa: “Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu.” (Mateyu 15:5) Mtsiku la Yesu, Ayuda opembedza anali kuika pambali ndalama kapena chuma kaamba ka kugawira ku kachisi. Afarisi anali kunyengezera kawonedwe kakuti pamene katundu anaperekedwa, katundu woteroyo pansi pa mikhalidwe iriyonse sakanagwiritsidwa ntchito kaamba ka cholinga china​—kuphatikizapo kusamalira kaamba ka makolo okalamba.

Kristu anadzudzula kulingalira Kodzilungamitsa kumeneku kukhala kosagwirizana ndi mzimu wa Lamulo la Mulungu. Mkawonedwe kake, kulemekeza makolo a munthuwe kunatenga malo oyambirira kuposa lamulo lopangidwa ndi anthu. Mofananamo lerolino, Akristu ena apereka miyoyo yawo ku utumiki, mwinamwake kutumikira monga amishonale, apainiya, kapena oyang’anira oyendayenda. Pamene anamva kuti makolo awo anali osowa, iwo ayesetsa kwambiri kupeza njira zakusamalira makolo awo pamene akupitirizabe mu mtundu wawo wautumiki. Koma pamene makonzedwe oterowo mnjira iriyonse alephera kugwira ntchito, iwo sanapereke chifukwa kuti mwawi wawo wautumiki unali wopambana koposa kulemekeza makolo awo. Oterowo ayenera kuyamikiridwa kaamba ka kupanga masinthidwe mu miyoyo yawo​—kawirikawiri pa kudzipereka kwa Umwini kokulira​—kotero kuti afikiritse mathayo awo abanja.

Kumachita Chimene Chiri Chabwino kwa Onse

Ngakhale kuti Baibulo limakakamiza Akristu kusamalira kaamba ka zosowa za ziwalo zabanja lawo, ichi sichimaletsa kusonyeza chikondi moyenerera kwa ziwalo zabanja lofutukulidwa. Panthawi zina azakhali ena, asuweni, kapena aphwathu amawoneka monga ziwalo zenizeni zabanja! Baibulo limatilimbikitsa ife “kuchita chimene chiri chabwino kwa onse.” (Agalatiya 6:10) Ngati Mkristu ali ndi njira za kuthandizira oterowo, mwachiwonekere iye sakafunikira ‘kutsekereza chifundo chake.’ Indedi, iye angadzimve kukhala moyenera wokakamizidwa kuthandiza.​—1 Yohane 3:17.

Mosasamala kanthu za chimenecho, thayo loyambirira la Mkristu liri kulinga kwa ziwalo zenizeni zabanja lake—mnzake wa muukwati, ana, makolo, ndi agogo. Iye chotero adzapereka lingaliro losamalitsa asanatenge thayo lomwe lidzavulaza iwo​—mwachuma, mwa maganizo, kapena mwauzimu.

Chenjezo la Baibulo pa kusamalira banja liri chotero lokoma mtima ndi lanzeru. Kugwiritsira ntchito ilo kungapumulitse Mkristu ku kudera nkhawa kochuluka kosayenera, ndipo lingamuthandize iye kukhazikitsa zoyambirira zake. Zonsezi ziri ku chilemekezo cha Yehova, “Atate amene kuchokera kwa iye pfuko lonse la m’mwamba ndi padziko alitcha dzina.”​—Aefeso 3:14, 15.

[Chithunzi patsamba 25]

Makolo Achikristu ali ndi thayo loyamba kulinga kwa ana awo enieni

[Chithunzi patsamba 26]

Mathayo a Mkristu angafutukukire kwa makolo okalamba ndi ana ake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena