PHUNZIRO 36
Kutambasula Mutu wa Nkhani
OKAMBA nkhani ozoloŵera amadziŵa phindu lokhala ndi mutu wa nkhani. Pamene akonzekera nkhani, mutu wa nkhani umawathandiza kuika maganizo pa mfundo zapadera ndi kuzilingalira mozama. Zimenezo zimawathandiza kusatchula chisawawa mfundo zosiyanasiyana, koma kufotokoza mfundozo m’njira yopindulitsa omvera. Pamene agwirizanitsa mfundo yaikulu iliyonse ndi mutuwo, ndi kuumveketsa bwino, omvera amathandizidwa kukumbukira mfundozo ndi kumvetsa phindu lake.
Ngakhale tinganene kuti mutu wanu ndiyo nkhani imene mukuilankhula, nkhani zanu zikhoza kumakhala zogwira mtima kwambiri ngati mungamaone mutu kukhala mfundo yapadera imene mutambasulire nkhani yanu. Ufumu, Baibulo, ndi kuuka kwa akufa, ndi nkhani chabe zopanda mitu. Nkhani zimenezi mukhoza kuzipatsa mitu yosiyanasiyana. Nazi zitsanzo zina: “Ufumu, Boma Lenileni,” “Ufumu wa Mulungu Udzasintha Dziko Lapansi Kukhala Paradaiso,” “Baibulo ndi Mawu Ouziridwa ndi Mulungu,” “Baibulo ndi Chithandizo Chenicheni M’masiku Athu Ano,” “Kuuka kwa Akufa Kumapereka Chiyembekezo kwa Olira,” ndi “Chiyembekezo cha Akufa Chimatithandiza Kukhalabe Olimba Pozunzidwa.” Mitu yonseyi imafuna kuitambasula m’njira zosiyanasiyana.
Mogwirizana ndi mutu waukulu wa Baibulo, ulaliki wa Yesu Kristu pamene anali pa dziko lapansi unaunika mutu wakuti: “Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mat. 4:17) Kodi mutu umenewo anautambasula motani? Ufumuwo akuutchula koposa ka 110 m’nkhani zinayi za Uthenga Wabwino. Koma Yesu samangobwereza chabe mawu akuti “ufumu.” Mwa zimene anaphunzitsa ndi zozizwitsa zimene anachita, Yesu anasonyeza bwino lomwe kuti iye mwiniyo, amene analipo panthaŵiyo, anali Mwana wa Mulungu, Mesiyayo, amene Yehova akam’patsa Ufumuwo. Yesu anasonyezanso kuti njira inatsegulidwa kupyolera mwa iye kuti ena akaloŵe naye Ufumuwo. Anasonyeza makhalidwe oyenera anthu odzapatsidwa mwayi umenewo. Mwa zimene anaphunzitsa ndi ntchito zamphamvu zimene anachita, anaonetsa bwino lomwe zimene Ufumu wa Mulungu udzachitira anthu. Anatchulanso kuti kutulutsa kwake ziŵanda mwa mzimu wa Mulungu unali umboni wakuti ‘Ufumu wa Mulungu unafikira’ omvera akewo. (Luka 11:20) Ndi Ufumuwo umene Yesu anatumiza otsatira ake kuti akauchitire umboni.—Mat. 10:7; 24:14.
Kusankha Mutu Woyenera. Sikuti mufunikira kutambasula mutu pamlingo umene Baibulo limachitira ayi, koma kukhala ndi mutu woyenera n’kofunika kwambiri.
Ngati mutuwo ndi woti musankhe nokha, choyamba ganizirani cholinga cha nkhani yanu. Ndiyeno pamene musankha mfundo zazikulu za nkhani yanu, onetsetsani kuti zikugwirizanadi ndi mutu umene mwasankha.
Ngati mutu ulipo kale, sinkhasinkhani mosamala muone kuti mutuwo ukufuna kuti mfundo zanu muzitambasule m’njira yotani. Mungafunikire kuganizira mozama kuti muzindikire phindu lake ndi mfundo zake za mutuwo. Ngati mufunika kusankha mfundo zotambasulira mutu umene ulipo kalewo, sankhani mosamala kuti mutuwo ukaonekere bwino. Koma ngati mfundozo zilipo kale, mufunikirabe kuona mmene mungazifotokozere mogwirizana ndi mutuwo. Ganiziraninso chifukwa chake nkhaniyo ili yofunika kwa omvera anu ndi cholinga chanu poikamba. Zimenezi zidzakuthandizani kudziŵa mfundo zofunika kutsindika poikamba.
Mmene Mungaunikire Mutuwo. Pofuna kuunika bwino mutuwo, muyenera kuyala maziko ake posankha mfundo zanu komanso pozisanja. Ngati mugwiritsa ntchito mfundo zogwirizana ndi mutu wanu zokha ndi kutsatira malangizo okonzera autilaini yabwino, mutu wanuwo udzaunikika mosavuta.
Kubwereza mawu kungathandizenso kumveketsa bwino mutu wa nkhani. Poimba nyimbo, timatchula mutu wake mobwerezabwereza. Mutuwo sitimautchula ndi mawu amodzimodzi nthaŵi zonse ayi. Nthaŵi zina timatchula mawu aŵiri kapena atatu a mutuwo, nthaŵi zina timatchula ganizo la mutuwo m’mawu ena, mpaka mutuwo umamveka m’nyimbo yonse. Ndi mmene ziyenera kukhalira ndi mutu wa nkhani. Kubwereza mawu ofunika a mutu kuli ngati kumatchula mutu wa nyimbo poimba. Kugwiritsa ntchito mawu ena ofanana tanthauzo ndi mawuwo kapena kutchula ganizo la mutuwo m’njira zosiyanasiyana kumathandiza kuunika. Kugwiritsa ntchito njira zimenezo kudzapangitsa mutuwo kukhala mfundo yaikulu imene omvera anu azikaikumbukira.
Njira zimenezi zimathandiza pokonza nkhani za papulatifomu, komanso pokambirana ndi anthu mu utumiki wa kumunda. Nkhani yaifupi imene mungakambirane imakumbukika mosavuta ngati mutu wake mwaumveketsa bwino. Ngati mutu wa nkhani waunikidwa bwino pa phunziro la Baibulo, mfundo zake zimakumbukika bwino. Khama limene mungachite posankha mutu ndi poutambasula bwino lingathandize kwambiri kuti mukhale wodziŵa kulankhula bwino Mawu a Mulungu ndi kuwaphunzitsa mogwira mtima.