Kutumikira Monga Asodzi a Anthu
“Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.”—LUKA 5:10.
1, 2. (a) Kodi kusodza kwachita mbali yotani m’mbiri ya anthu? (b) Kodi ndimtundu watsopano wakusodza wotani umene unayamba pafupifupi zaka 2,000 zapitazo?
KWA zaka zikwi zambiri, anthu asodza nsomba kaamba ka chakudya m’nyanja zamchere zadziko lapansi, nyanja zina zazikulu, ndi m’mitsinje. Mu Igupto wakale, nsomba zochokera mu Nile zinali mbali yofunika ya chakudya. Pamene madzi a Nile anasandulizidwa mwazi m’tsiku la Mose, Aigupto anavutika osati ndi kupereŵera kwa madzi kokha kumene kunachitika komanso chifukwa chakuti nsomba zinafa, kupangitsa vuto la kupeza chakudya. Pambuyo pake, pa Sinayi, pamene Yehova anapatsa Israyeli Chilamulo, anawauza kuti nsomba zakutizakuti zikadyedwa koma zina zinali zodetsedwa, zosayenera kudya. Izi zinasonyeza kuti Aisrayeli akadya nsomba pamene akafika ku Dziko Lolonjezedwa, chotero ena a iwo akakhala asodzi.—Eksodo 7:20, 21; Levitiko 11:9-12.
2 Komabe, pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, anthu anaphunzira mtundu wina wa kusodza. Umene unali kusodza kwauzimu kumene kukapindulitsa osati asodzi okha komanso nsombazo! Mtundu wa kusodza umenewu ukuchitikabe lerolino, kupindulitsa anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse.
‘Kusodza Anthu Amoyo’
3, 4. Kodi ndiasodzi aŵiri ati amene anasonyeza chikondwerero chachikulu mwa Yesu Kristu?
3 M’chaka cha 29 C.E., Yesu, Amene akayambitsa mpangidwe watsopano umenewu wa kusodza, anabatizidwa mumtsinje wa Yordano ndi Yohane Mbatizi. Masabata angapo pambuyo pake, Yohane anasonyeza Yesu kwa aŵiri a ophunzira ake naati: “Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!” Mmodzi wa ophunzira ameneŵa, amene dzina lake anali Andreya, mwamsanga anauza mbale wake Simoni Petro kuti: “Tapeza ife Mesiya”! Mokondweretsa, onse aŵiri Andreya ndi Simoni anali asodzi.—Yohane 1:35, 36, 40, 41; Mateyu 4:18.
4 Patapita nthaŵi, Yesu anali kulalikira kumakamu m’mphepete mwa Nyanja ya Galileya, osati kutali ndi kumene Petro ndi Andreya ankakhala. Anali kuuza anthuwo kuti: “Tembenukani mitima, pakuti ufumu wakumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:13, 17) Tingathe kuyerekezera kuti Petro ndi Andreya anali ofunitsitsa kumva uthenga wake. Mwachiwonekere, iwo sanazindikire kuti Yesu anali pafupi kunena kanthu kena kwa iwo komwe kakasintha miyoyo yawo kosatha. Ndiponso, zimene Yesu anali kudzanena ndi kuchita pamaso pawo ziri ndi tanthauzo lofunika kwa tonsefe lerolino.
5. Kodi msodzi Petro anali wokhoza motani kutumikira Yesu?
5 Timaŵerenga kuti: “Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mawu a Mulungu, iye analikuimirira m’mbali mwa nyanja ya Genesarete; ndipo anawona ngalaŵa ziŵiri zinakhala m’mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adatuluka mmenemo, nalikutsuka makoka awo.” (Luka 5:1, 2) Kalelo, amuna ogwira ntchito yausodzi kaŵirikaŵiri ankagwira ntchito usiku, ndipo amuna ameneŵa anali kutsuka makoka awo pambuyo pa usiku wa kusodza. Yesu anasankha kugwiritsira ntchito imodzi ya ngalaŵa zawo kuti alalikire mogwira mtima kwambiri kukhamulo. “Ndipo iye analoŵa m’ngalaŵa imodzi, ndiyo yake ya Simoni, nampempha iye akankhe pang’ono. Ndipo anakhala pansi mmenemo, naphunzitsa m’ngalaŵa makamuwo a anthu.”—Luka 5:3.
6, 7. Kodi ndichozizwitsa chotani chokhudza kusodza chimene Yesu anachita, chikutsogolera ku ndemanga yotani yonena za kusodza?
6 Tawonani kuti Yesu anali kulingalira za kanthu kena kuposa kuphunzitsa makamuwo: “Ndipo pamene iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwakuya, nimuponye makoka anu kukasodza.” Kumbukirani kuti, asodzi ameneŵa anali atagwira kale ntchito usiku wonse. Koma Petro akuyankha kuti: “Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pamawu anu ndidzaponya makoka.” Kodi nchiyani chinachitika pamene anachita zimenezi? “Anazinga unyinji waukulu wa nsomba; ndipo makoka awo analinkung’ambika; ndipo anakodola anzawo a m’ngalaŵa inayo, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza ngalaŵa zonse ziŵiri, motero kuti zinalinkumira.”—Luka 5:4-7.
7 Yesu anali atachita chozizwitsa. Mbali imeneyo ya nyanja inalibe nsomba usiku wonse; tsopano inali yodzala ndi nsomba. Chozizwitsa chimenechi chinayambukira Petro mwamphamvu. “Simoni Petro, pamene anawona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa. Pakuti chizizwo chidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pakusodzako kwa nsomba zimene anazikola; ndipo chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, amene anali anzake a Simoni.” Yesu anatonthoza Petro ndipo pamenepo ananena mawu amene analikudzasintha moyo wa Petro. “Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.”—Luka 5:8-10.
Asodzi a Anthu
8. Kodi ndimotani mmene asodzi anayi analabadirira ku chiitano cha ‘kusodza anthu amoyo’?
8 Motero Yesu anayerekezera anthu ndi nsomba, ndipo anaitana msodzi wodzichepetsa ameneyu kuleka ntchito yake yakuthupi kuti akachite kusodza kokulirapo kwambiri—kusodza anthu amoyo. Petro, ndi mbale wake Andreya, anavomereza chiitanocho. “Iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata iye.” (Mateyu 4:18-20) Kenako Yesu anaitana Yakobo ndi Yohane, amene anali m’ngalaŵa yawo, kumasoka makoka awo. Anaitana ameneŵa kuti nawonso akhale asodzi a anthu. Kodi iwo analabadira motani? “Ndipo anasiya pomwepo ngalaŵayo ndi atate wawo, namtsata iye.” (Mateyu 4:21, 22) Yesu anali wa luso monga msodzi wa anthu. Pachochitikachi iye anasodza anthu anayi amoyo.
9, 10. Kodi Petro ndi mabwenzi ake anasonyeza chikhulupiriro chotani, ndipo kodi anaphunzitsidwa motani kusodza kwauzimu?
9 Katswiri wosodza amapeza ndalama mwakugulitsa nsomba zake, koma msodzi wauzimu sangachite zimenezo. Chifukwa chake, ophunzira ameneŵa anasonyeza chikhulupiriro chachikulu pamene anasiya zonse kutsata Yesu. Komabe, iwo sanakaikire kuti kusodza kwawo kwauzimu kukakhala kwachipambano. Yesu anali wokhoza kupangitsa madzi opanda kanthu kudzala ndi nsomba zenizeni. Mofananamo, poponya makoka awo m’madzi a mtundu wa Israyeli, ophunzirawo akanakhala otsimikizira kuti, ndi chithandizo cha Mulungu, akagwira anthu amoyo. Ntchito yakusodza kwauzimu imene inayamba kalelo ikupitirizabe, ndipo Yehova akuperekabe zotuta zambiri.
10 Kwa zaka zoposa ziŵiri, ophunzirawo anaphunzitsidwa ndi Yesu kusodza anthu. Panthaŵi ina, anawapatsa malangizo olondola ndi kuwatumiza patsogolo pake kukalalikira. (Mateyu 10:1-7; Luka 10:1-11) Pamene Yesu anaperekedwa ndi kuphedwa, ophunzirawo anachita kakasi. Koma kodi imfa ya Yesu inatanthauza kulekeka kwa kusodza anthu? Zochitika zotsatira zinapereka yankho.
Kusodza m’Nyanja ya Anthu
11, 12. Pambuyo pa chiukiriro chake, kodi Yesu anachita chozizwitsa chotani chokhudza kusodza?
11 Mwamsanga pambuyo pa imfa ya Yesu kunja kwa Yerusalemu ndi kuuka kwake, ophunzirawo anabwerera ku Galileya. Panthaŵi ina asanu ndi aŵiri a iwo anali pamodzi pafupi ndi Nyanja ya Galileya. Petro ananena kuti anali kupita kukasodza, ndipo enawo anagwirizana naye. Mwachizoloŵezi, anakasodza usiku. Kwenikweni, anaponya makoka awo m’nyanja usiku wonse osagwira chirichonse. Ndiyeno, mbandakucha, munthu wina wowonedwa woimilira kugombe anawaitana nati: “Ananu, muli nako kanthu kakudya kodi?” Ophunzirawo anayankha kuti: “Iyayi.” Chotero woima pangombeyo anawauza kuti: “Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja ya ngalaŵa, ndipo mudzapeza. Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka chifukwa cha kuchuluka nsomba.”—Yohane 21:5, 6.
12 Nchokumana nacho chochititsa chidwi chotani nanga! Mosakaikira, ophunzirawo anakumbukira chozizwitsa choyambirira chokhudza kusodza, ndipo mmodzi wa iwo anazindikira munthu wokhala pagombeyo. “Pamenepo wophunzira uja amene Yesu anamkonda ananena kwa Petro, Ndiye Ambuye. Simoni Petro pakumva kuti ndiye Ambuye, anadziveka malaya a pathupi, pakuti anali wamaliseche, nadziponya yekha m’nyanja. Koma akuphunzira ena anadza m’kangalaŵa, pakuti sanali kutali ndi mtunda, koma monga mikono mazana aŵiri.”—Yohane 21:7, 8.
13. Pambuyo pa kukwera kumwamba kwa Yesu, kodi ndiprogramu yakusodza yapadziko lonse yotani imene inayamba?
13 Kodi chozizwitsa chimenechi chinasonyezanji? Kuti ntchito ya kusodza anthu inali isanathe. Chenicheni chimenechi chinagogomezeredwa pamene Yesu anapitiriza kuuza Petro katatu—ndipo kudzera mwa iye ophunzira onsewo—kudyetsa nkhosa za Yesu. (Yohane 21:15-17) Inde, programu yakudyetsa kwauzimu inali patsogolo. Imfa yake isanachitike, iye adalosera kuti: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa padziko lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kumitundu yonse.” (Mateyu 24:14, NW) Tsopano inali nthaŵi yakuti kukwaniritsidwa kwa m’zaka za zana loyamba kwa ulosi umenewo kuyambe. Ophunzira ake anali pafupi kuponya makoka awo m’nyanja ya anthu, ndipo makokawo sakatuluka opanda kanthu.—Mateyu 28:19, 20.
14. Kodi kusodza kwa otsatira a Yesu kunadalitsidwa motani m’zakazo Yerusalemu asanawonongedwe?
14 Asanakwere kumwamba kumpando wachifumu wa Atate wake, Yesu anati kwa otsatira ake: ‘Mudzalandira mphamvu, mzimu woyera utadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.’ (Machitidwe 1:8) Pamene mzimu woyera unatsanulidwa pa ophunzirawo pa Pentekoste wa 33 C.E., ntchito yaikulu yakusodza kwauzimu m’mitundu yonse inayamba. Pa Pentekoste pokha, anthu zikwi zitatu anasodzedwa amoyo, ndipo mwamsanga pambuyo pake ‘chiŵerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.’ (Machitidwe 2:41; 4:4) Chiwonjezeko chinapitirizabe. Cholembedwacho chimatiuza kuti: ‘Anawonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi.’ (Machitidwe 5:14) Mwamsanga, Asamariya analabadira mbiri yabwino, ndipo mwamsanga pambuyo pake anateronso Akunja osadulidwa. (Machitidwe 8:4-8; 10:24, 44-48) Zaka zokwanira 27 pambuyo pa Pentekoste, mtumwi Paulo analembera Akristu ku Kolose kuti mbiri yabwino inali ‘italalikidwa m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.’ (Akolose 1:23) Mwachiwonekere, ophunzira a Yesu anasodza kutali m’madzi a Galileya. Iwo anaponya makoka awo pakati pa Ayuda omwazikana mu Ulamuliro wa Roma, limodzinso ndi m’madera osatsimikizirika a anthu osakhala Ayuda. Ndipo makoka awo anatuluka ali odzaza. Kaamba ka zosoŵa za Akristu a m’zaka za zana loyamba, ulosi wa Yesu wa pa Mateyu 24:14 unakwaniritsidwa Yerusalemu asanawonongedwe mu 70 C.E.
Kusodza Anthu mu “Tsiku la Ambuye”
15. M’bukhu la Chivumbulutso, kodi ndintchito yowonjezereka yosodza yotani yomwe inaloseredwa, ndipo kodi ndiliti pamene ikachitika?
15 Komabe, zambiri zinali kutsogolo. Pafupi ndi mapeto a zaka za zana loyamba, Yehova anapatsa mtumwi womalizira, Yohane, chivumbulutso cha zinthu zimene zinali kudzachitika mkati mwa “tsiku la Ambuye.” (Chivumbulutso 1:1, 10) Mbali imodzi yapadera inali kulalikira mbiri yabwino padziko lonse. Timaŵerenga kuti: “Ndinawona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, ali ndi [mbiri yabwino yosatha kuti ailalikire, NW] kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.” (Chivumbulutso 14:6) Mwachitsogozo cha angelo, atumiki a Mulungu akalalikira mbiri yabwino padziko lonse lokhalidwa ndi anthu, osati mu Ulamuliro wa Roma mokha. Ntchito yapadziko lonse ya kusodza anthu inayenera kuchitika, ndipo tsiku lathu tawona kukwaniritsidwa kwa masomphenya amenewo.
16, 17. Kodi ntchito yakusodza kwauzimu kwapambuyo pake inayamba liti, ndipo kodi Yehova waidalitsa motani?
16 Kodi ndimotani mmene kusodza kwakhalira m’zaka za zana lino la 20? Poyamba, asodziwo anali oŵerengeka. Nkhondo Yadziko ya I itatha, panali alaliki okangalika ambiri yabwino pafupifupi zikwi zinayi zokha, amuna ndi akazi achangu amene anali kwakukulukulu odzozedwa. Iwo anaponya makoka awo kulikonse kumene Yehova anatsegula njira, ndipo anthu ambiri anasodzedwa amoyo. Pambuyo pa nkhondo yadziko yachiŵiri, Yehova anatsegula madzi atsopano osodzamo. Amishonale amene analoŵa Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower anapititsa patsogolo ntchito m’maiko ambiri. Maiko onga Japani, Italiya, ndi Spanya, amene anawonekera kukhala osabala zipatso, potsirizita pake anatulutsa anthu ambiri. Posachedwapa tamvanso mmene kusodza kwakhalira kwachipambano Kum’maŵa kwa Yuropu.
17 Lerolino, m’maiko ambiri makoka ali pafupi kung’ambika. Kututa kwakukulu kwa miyoyo kwachititsa kulinganiza mipingo ndi madera atsopano kukhala kofunika. Kuti amenewa asamaliridwe, Nyumba Zaufumu ndi Nyumba Zamsonkhano Wadera Zatsopano zimamangidwa nthaŵi zonse. Akulu ndi atumiki otumikira owonjezereka akufunikira kusamalira chiwonjezekocho. Ntchito yaikulu inayambidwa ndi okhulupirika amenewo kalelo mu 1919. Mwalingaliro lenileni, Yesaya 60:22 wakwaniritsidwa. ‘Wamng’ono wakhala chikwi,’ monga momwe asodzi zikwi zinayi amenewo afikira kukhala oposa mamiliyoni anayi lerolino. Ndipo mapeto sanafikebe.
18. Kodi tingatsanzire motani chitsanzo chabwino kwambiri cha asodzi auzimu a anthu a m’zaka za zana loyamba?
18 Kodi zonsezi zikutanthauzanji kwa ife aliyense payekha? Lembalo linena kuti pamene Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane anaitanidwa kukhala asodzi a anthu, “iwo . . . anasiya zonse namtsata [Yesu].” (Luka 5:11) Nchitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga cha chikhulupiriro ndi kudzipereka! Kodi ife tingakulitse mzimu umodzimodziwo wakudzimana, ndi changu chofananacho cha kutumikira Yehova mosasamala kanthu ndi zimene zingakugwereni? Mamiliyoni ayankha kuti angatero. M’zaka za zana loyamba, ophunzira anasodza anthu kulikonse kumene Yehova analola. Kaya kunali pakati pa Ayuda kapena Akunja, iwo anasodza mosasankha. Tiyeni nafenso tilalikire kwa aliyense mosazengereza ndi mopanda tsankho.
19. Kodi tiyenera kuchitanji ngati dera limene tikusodzako likuwonekera kukhala losaphula kanthu?
19 Komabe, bwanji ngati gawo lanu panthaŵi ino likuwonekera kukhala losabala zipatso? Musalefulidwe. Kumbukirani, Yesu anadzaza makoka a ophunzira pambuyo pakusodza usiku wonse mosaphula kanthu. Zofananazo zingachitike mwanjira yauzimu. Mwachitsanzo, mu Ireland, Mboni zokhulupirika zinagwira ntchito kwa zaka zambiri nzotulukapo zochepa. Komabe, posachedwapa zimenezo zasintha. 1991 Yearbook of Jehovah’s Witnesses ikusimba kuti podzafika mapeto a chaka chautumiki cha 1990, Ireland inakhala ndi ziŵerengero zapamwamba 29 zotsatizanatsatizana! Mwinamwake gawo lanu tsiku lina lidzatulutsa zofananazo. Malinga ngati Yehova alola, pitirizanibe kusodza!
20. Kodi ndiliti pamene tiyenera kuloŵa m’kusodza anthu?
20 Mu Israyeli, asodzi ankasodza usiku, pamene munthu wina aliyense anali wofunda ndi kupeza bwino pakama. Iwo anatuluka, osati pamene inali nthaŵi yowakomera, koma pamene iwo akanakhoza kugwira nsomba zochuluka. Ifenso tiyenera kupenda gawo lathu kuti tisodze, titero kunena kwake, pamene anthu ambiri ali panyumba ndipo okhoza kulabadira. Izi zingakhale madzulo, kumapeto kwa mlungu, kapena panthaŵi ina iriyonse. Nthaŵi iriyonse, tiyeni tichite zonse zomwe tingathe kuti tipeze anthu a mitima yowongoka.
21. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani ngati gawo lathu limagwiridwa ntchito mobwerezabwereza?
21 Bwanji ngati gawo lathu limalalikidwa mwa kaŵirikaŵiri? Kaŵirikaŵiri ogwira ntchito yausodzi m’dzikoli amadandaula kuti kusodza kumachitidwa mopambanitsa m’madera awo osodzako. Koma kodi kusodza kwa m’madera athu auzimu kungafikire kukhala kopambanitsa? Osati kwenikweni! Magawo ambiri amakhaladi ndi chiwonjezeko ngakhale pamene afoledwa mobwerezabwereza. Ena amatulutsa zipatso zabwino kwambiri chifukwa cha kufoledwa bwino lomwe. Komabe, pamene nyumba zifikiridwa kaŵirikaŵiri, khalani otsimikiza kwambiri kuti onse osakhala panyumba akulembedwa ndi kufikiridwa pambuyo pake. Phunzirani mitu ya nkhani yokambitsirana yosiyanasiyana. Kumbukirani kuti munthu wina adzachezeranso posapita nthaŵi, chotero musakhalitse kapena kukwiitsa mwininyumba mosafunikira. Ndipo kulitsani maluso anu a ntchito ya m’khwalala ndiponso kuchitira umboni mwamwaŵi. Ponyani makoka anu auzimu panyengo iriyonse ndi m’njira iriyonse yotheka.
22. Kodi ndimwaŵi waukulu wotani umene tiri nawo panthaŵi ino?
22 Kumbukirani kuti, m’kusodza kumeneku asodzi ndi nsomba zomwe zimapindula. Ngati amene tagwirawo alimbikira, adzakhala ndi moyo kosatha. Paulo analimbikitsa Timoteo kuti: “Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe.” (1 Timoteo 4:16) Anali Yesu amene choyamba anaphunzitsa ophunzira ake kusodza kwauzimu, ndipo ntchitoyi ikuchitidwabe motsogozedwa ndi iye. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 14:14-16.) Ndimwaŵi waukulu wotani nanga womwe tiri nawo kugwira ntchito moyang’aniridwa ndi iye kuti imalizidwe! Tiyenitu tipitirize kuponya makoka malinga ndi nthaŵi yomwe Yehova walola. Kodi pangakhale ntchito ina iriyonse yoposa yakusodza anthu?
Kodi Mungakumbukire?
◻ Kodi Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuchita ntchito yanji?
◻ Kodi Yesu anasonyeza motani kuti imfa yake sinaletse ntchito yakusodza kwauzimu?
◻ Kodi Yehova anadalitsa motani ntchito yakusodza kwauzimu ya m’zaka za zana loyamba?
◻ Kodi ndinsomba zochuluka motani zimene zasodzedwa mkati mwa “tsiku la Ambuye”?
◻ Kodi ndimotani mmene ife monga munthu payekha tingakhalire asodzi a anthu achipambano koposerapo?
[Chithunzi patsamba 15]
Pambuyo pa kuuka kwa Yesu, atumwi ake anafutukula ntchito ya Mulungu ya kusodza anthu